Alif-Lâm-Ra. (Ili ndi) buku lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti uwatulutse anthu mu mdima ndi kuwaika mkuunika - mwalamulo la Mbuye wawo - uwapititse kunjira ya Mwini mphamvu zoposa, Woyamikidwa.
Amene akukondetsa moyo wadziko lapansi kuposa moyo wa pambuyo pa imfa, ndipo amatsekereza (anthu) ku njira ya Allah ndikufuna kuikhotetsa (pomwe njirayo njosakhota). Iwo ali mkusokera kotalikana kwambiri (ndi choonadi).
Ndipo ndithu tidamtumiza Mûsa ndi zozizwitsa Zathu (tidamuuza): “Achotse anthu ako mu mdima (wa umbuli) ndi kuwaika mkuunika (kwa chikhulupiliro) ndipo uwakumbutse masiku a Allah (a masautso).” Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa yense wopirira, wothokoza.
Ndipo (akumbutse anthu ako) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu pamene adakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe adakuzunzani ndi chilango choipa. Ankazinga (kupha) ana anu aamuna ndi kuwasiya amoyo ana anu aakazi; ndithu m’zimenezi mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu.”
Ndipo Mûsa adati (kwa anthu ake): “Ngati inu mukana (pakusiya kuthokoza) pamodzi ndi onse a m’dziko, (Allah salabadira chilichonse pa zimenezo), ndithudi Allah Ngwachikwanekwane; Ngotamandidwa.”
Atumiki awo adati kwa iwo: “(Zoonadi), ife ndife anthu ngati inu, koma Allah amamchitira zabwino yemwe wamfuna mwa akapolo ake. Ndipo ife tilibe nyonga zokubweretserani chisonyezo koma mwachilolezo cha Allah. Ndipo kwa Allah yekha atsamire okhulupirira onse.”
“Nanga kwa ife kuli chiyani kuti tisatsamire kwa Allah pomwe watisonyeza njira zathu. Ndipo tipirira pa zimene mukutisautsa nazo. Choncho, kwa Allah Yekha atsamire otsamira.”
Ndipo satana adzanena chiweruzo chikadzalamulidwa (oipa kulowa ku Moto, abwino kulowa ku Munda wamtendere): “Ndithu Allah adakulonjezani lonjezo loona (ndipo wakwaniritsa). Nane ndidakulonjezani, koma sindidakukwaniritsireni. Ndidalibe mphamvu pa inu (yokukakamizirani kunditsata) koma ndimangokuitanani basi, ndipo munkandiyankha. Choncho musandidzudzule, koma dzidzudzuleni nokha. Sindingathe kukuthangatani ndiponso inu simungathe kundithangata. Ndithu ine ndidakukana kundiphatikiza kwanu ndi Allah kale. Ndithu ochita zoipa adzapeza chilango chowawa.”[242]
[242] Omasulira Qur’an adati: Chiweruzo chikadzaweruzidwa, anthu abwino nkukakhazikika ku Munda wa mtendere pomwe anthu oipa nkukalowa ku Moto, anthu a ku Moto adzayamba kumadzudzula satana ndi kumnyoza. Ndipo satana adzaimilira pakati pawo pagome la Moto m’katikati mwa Jahannam nadzanena kwa anthu onse a ku Moto kuti: “Musandidzudzule, koma dzudzulani mitima yanu. Mitima yanu ndiyomwe idakuonongani. Ine ndinkangokuitanani chabe, sindidakukakamizeni.”
Umapereka zipatso zake nthawi iliyonse mwachifuniro cha Mbuye wake. (Umo ndi momwe liwu labwino lilili, limabwera ndi zabwino). Ndipo Allah amaponyera anthu mafanizo kuti akumbukire.
Allah amawalimbikitsa amene akhulupirira ndi mawu olimba m’moyo wa dziko lapansi, ndi moyo wapambuyo pa imfa; ndipo Allah amawalekelera kusokera omwe akudzichitira okha zoipa; ndipo Allah amachita zimene wafuna.
Allah ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndipo adatsitsa madzi ku mitambo, ndi madziwo adatulutsa zipatso kuti zikhale Rizq lanu (chakudya chanu). Ndipo adakufewetserani zombo kuti ziziyenda pa nyanja mwa lamulo Lake; ndiponso adakufewetserani mitsinje.
Ndipo (kumbukani) pamene Ibrahim adanena: “Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa mtendere; ndipo ndipatuleni ine ndi ana anga ku machitidwe opembedza mafano.”
Ndipo usaganize kuti Allah waiwala zomwe akuchita oipa. Ndithudi, Iye akuwalekelera chabe mpaka tsiku lomwe maso awo adzatong’oke (chifukwa cha mantha).[243]
[243] Ndithudi machitidwe a Allah nkuwalekelera oipa pamene akuchita zoipa. Sawalanga mwachangu. Koma akafuna kuwalanga amawakhaulitsa ndi chilango choopsa. Choncho munthu asanyengeke pamene akulakwira Allah namulekelera osamulanga.
(Adzakhala) akuyenda mothamanga mitu ili m’mwamba ndipo maso awo osatha kuphethira, ndipo m’mitima mwawo muli mopanda kanthu (mopanda ganizo lililonse chifukwa cha kudzadzidwa ndi mantha).
Choncho usaganize kuti Allah Ngwakuswa lonjezo Lake kwa atumiki Ake. Ndithu Allah ndi mwini mphamvu (salephera chilichonse), Ngobwezera chilango mwaukali.
Izi zikukwana kukhala phunziro kwa anthu kuti achenjezedwe nazo, ndi kuti azindikire kuti Iye (Allah) ndi Mulungu Mmodzi basi, ndikuti eni nzeru akumbukire.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Axatrışın nəticələri:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".