Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation * - Translations’ Index


Translation of the meanings Ayah: (35) Surah: Al-An‘ām
وَإِن كَانَ كَبُرَ عَلَيۡكَ إِعۡرَاضُهُمۡ فَإِنِ ٱسۡتَطَعۡتَ أَن تَبۡتَغِيَ نَفَقٗا فِي ٱلۡأَرۡضِ أَوۡ سُلَّمٗا فِي ٱلسَّمَآءِ فَتَأۡتِيَهُم بِـَٔايَةٖۚ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَجَمَعَهُمۡ عَلَى ٱلۡهُدَىٰۚ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ
Ndipo ngati nkovuta kwa iwe kudzipatula kwawoku (ndi zomwe wadza nazozi pomwe iwo akukuumiriza kuti uwabweretsere chozizwitsa, nawe nkumafuna; zikadatero, pomwe Ine sindikufuna), choncho ngati uli wokhoza kufunafuna njira ya pansi penipeni m’nthaka (kukafuna zozizwitsazo), kapena (ungathe kupeza) makwelero nkukwera kumwamba nkubwera ndi chozizwitsa (chimene akufuna, chita). Allah Akadafuna akadawasonkhanitsa onse ku chiwongoko. Choncho, usakhale mwa osazindikira zinthu.
Arabic explanations of the Qur’an:
 
Translation of the meanings Ayah: (35) Surah: Al-An‘ām
Surahs’ Index Page Number
 
Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Translations’ Index

Translation of the Quran meanings into Chewa by Khaled Ibrahim Betala (ed. 2020)

close