Check out the new design

Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Khaled Ibrahim Betala * - Índice de traducciones


Traducción de significados Capítulo: Al-Baqara   Versículo:
۞ مَا نَنسَخۡ مِنۡ ءَايَةٍ أَوۡ نُنسِهَا نَأۡتِ بِخَيۡرٖ مِّنۡهَآ أَوۡ مِثۡلِهَآۗ أَلَمۡ تَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ
Ayah (ndime) iliyonse yomwe tikuifafaniza kapena kuiiwalitsa (mu mtima wako) tikubweretsa yabwino kuposa iyo, kapena yofanana nayo. Kodi sukudziwa kuti Allah Ngokhoza chinthu chilichonse?
Las Exégesis Árabes:
أَلَمۡ تَعۡلَمۡ أَنَّ ٱللَّهَ لَهُۥ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِن وَلِيّٖ وَلَا نَصِيرٍ
Kodi siudziwa kuti ufumu wakumwamba ndi pansi ngwa Allah? Ndipo inu kupatula Iye Allah mulibe mtetezi ngakhale mthandizi.
Las Exégesis Árabes:
أَمۡ تُرِيدُونَ أَن تَسۡـَٔلُواْ رَسُولَكُمۡ كَمَا سُئِلَ مُوسَىٰ مِن قَبۡلُۗ وَمَن يَتَبَدَّلِ ٱلۡكُفۡرَ بِٱلۡإِيمَٰنِ فَقَدۡ ضَلَّ سَوَآءَ ٱلسَّبِيلِ
Kodi mukufuna kumfunsa Mtumiki wanu (inu Asilamu) monga momwe Mûsa adafunsidwira kale (mafunso achipongwe)? Ndipo amene angasinthitse chikhulupiliro ndi kusakhulupirira, ndithudi wasokera njira yolingana (yopanda majiga).
Las Exégesis Árabes:
وَدَّ كَثِيرٞ مِّنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ لَوۡ يَرُدُّونَكُم مِّنۢ بَعۡدِ إِيمَٰنِكُمۡ كُفَّارًا حَسَدٗا مِّنۡ عِندِ أَنفُسِهِم مِّنۢ بَعۡدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُمُ ٱلۡحَقُّۖ فَٱعۡفُواْ وَٱصۡفَحُواْ حَتَّىٰ يَأۡتِيَ ٱللَّهُ بِأَمۡرِهِۦٓۗ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Ambiri mwa amene anapatsidwa mabuku, akufuna kukubwezani (kukutembenuzani) kuti mukhale osakhulupirira pambuyo pa chikhulupiliro chanu, chifukwa chadumbo lomwe lili m’mitima mwawo (lomwe lawapeza) pambuyo powaonekera choonadi poyera. Choncho akhululukireni ndi kuwasiya kufikira Allah adzabweretse lamulo Lake[5]; ndithudi Allah Ngokhoza chilichonse.
[5] Lamulo lake ndilakuwaloleza Asilamu kubwezera pamene aputidwa kapena kuchitidwa mtopola.
Las Exégesis Árabes:
وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَۚ وَمَا تُقَدِّمُواْ لِأَنفُسِكُم مِّنۡ خَيۡرٖ تَجِدُوهُ عِندَ ٱللَّهِۗ إِنَّ ٱللَّهَ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرٞ
Ndipo pempherani Swala moyenera ndiponso perekani Zakaat. Ndipo chilichonse chabwino chimene mukudzitsogozera mukachipeza kwa Allah. Ndithudi, Allah akuona zonse zimene mukuchita.
Las Exégesis Árabes:
وَقَالُواْ لَن يَدۡخُلَ ٱلۡجَنَّةَ إِلَّا مَن كَانَ هُودًا أَوۡ نَصَٰرَىٰۗ تِلۡكَ أَمَانِيُّهُمۡۗ قُلۡ هَاتُواْ بُرۡهَٰنَكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Eti akunena: “Palibe amene adzalowe ku Munda wamtendere koma amene ali Myuda Kapena Mkhirisitu.” Zimenezo nzokhumba zawo chabe. Nena: “Bweretsani umboni wanu ngati mukunena zoona.”
Las Exégesis Árabes:
بَلَىٰۚ مَنۡ أَسۡلَمَ وَجۡهَهُۥ لِلَّهِ وَهُوَ مُحۡسِنٞ فَلَهُۥٓ أَجۡرُهُۥ عِندَ رَبِّهِۦ وَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ
Ayi, koma amene nkhope yake yagonjera kwa Allah uku akuchita zabwino (kwa anthu anzawo) iye ndi amene adzapeza mphoto yake kwa Mbuye wake. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso iwo sadzadandaula.
Las Exégesis Árabes:
 
Traducción de significados Capítulo: Al-Baqara
Índice de Capítulos Número de página
 
Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Khaled Ibrahim Betala - Índice de traducciones

Khaled Ibrahim Petala la tradujo.

Cerrar