Check out the new design

Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Khaled Ibrahim Betala * - Índice de traducciones


Traducción de significados Capítulo: Ar-Room   Versículo:

Ar-Rûm

الٓمٓ
Alif-Lâm-Mîm.[306]
[306] Surayi yayamba ndi zilembo za alifabeti posonyeza kuti Qur’an yalembedwa kupyolera m’malemba amenewa omwe Arabu amawayankhula mofewa. Koma Aquraish adalephera kulemba Buku limeneli pomwe malembo ake akuwadziwa.
Las Exégesis Árabes:
غُلِبَتِ ٱلرُّومُ
Aroma agonjetsedwa (ndi Aperezi)[307]
[307] Surayi idapatsidwa dzina loti Rum chifukwa chakuti idalosera kuti Aroma adzagonjetsa Aperezi. M’menemo nkuti pamene Surayi inkavumbulutsidwa ndi kulosera kupambana kwa Aroma iwo adali atagonjetsedwa kale ndi Aperezi, kugonjetsedwa zedi kotero kuti maiko awo ambiri adalandidwa ndi Apereziwo. Surayi idavumbulutsidwa ku Makka m’chaka chachisanu nchimodzi (6) kapena chisanu ndichiwiri (7) Mtumiki asanasamuke. Aroma ndi anthu akale zedi; amalamulira maiko ambiri. Mzinda wawo waukulu umatchedwa Roma m’dziko la Italy.
Padali mkangano pakati pa mafumu awiri: Mfumu ya Aroma ndi Mfumu ya Aperezi. Mkanganowo udayamba m’chaka cha 602 A.D, ndipo pamene adamenyana nkhondo Aperezi adagonjetsa Aroma ndipo kupambana kwa Aperezi kutamveka m’Makka, Arabu opembedza mafano adakondwa kwambiri poti naonso Aperezi adali kupembedza mafano ngati iwo. Arabu opembedza mafanowo adati kwa Asilamu ndi Akhrisitu: “Anthu a mabuku ngati inu mwagonjetsedwa ndi anzathu opembedza mafano, choncho nafenso tikugonjetsani inu Asilamu posachedwa.”
Qur’an idalengeza ndime izi ziwiri zomwe mkati mwake muli ulosi uwiri: Ulosi woyamba nkuti m’nyengo yosapyolera zaka zisanu ndi zinayi (9) Aperezi adzagonjetsedwa ndi Aroma. Ndipo ulosi wachiwiri ukuti Asilamu adzagonjetsa Arabu opembedza mafano a mu mzinda wa Makka. M’chaka cha 624, Hiraqla, mfumu ya Aroma adagonjetsa mzinda wa Madiyana m’dziko la Aperezi. Ndipo m’chaka chomwecho naonso Asilamu omwe adali 313 adagonjetsa gulu lankhondo la Arabu opembedza mafano omwe kuchuluka kwawo kudali 1,000 pa nkhondo yomwe idachitikira pamalo wotchedwa Badri.
Ndipo opembedza mafanowo adagonjetsedwa moipa. Potero ulosi umene Qur’an idalosera udakwaniritsidwa. Ndipo ichi chidali chinthu chozizwitsa zedi, chomwe chimasonyeza kuti Qur’an ndi mawudi a Allah.
Las Exégesis Árabes:
فِيٓ أَدۡنَى ٱلۡأَرۡضِ وَهُم مِّنۢ بَعۡدِ غَلَبِهِمۡ سَيَغۡلِبُونَ
M’dziko loyandikira (kwa Arabu lomwe ndi dziko la Sham). Nawonso pambuyo pogonjetsedwa kwawo, adzagonjetsa (Aperezi).
Las Exégesis Árabes:
فِي بِضۡعِ سِنِينَۗ لِلَّهِ ٱلۡأَمۡرُ مِن قَبۡلُ وَمِنۢ بَعۡدُۚ وَيَوۡمَئِذٖ يَفۡرَحُ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ
Mzaka zochepa (zosapyolera 10). Zonse nza Allah, pambuyo ndi patsogolo (pankhondoyo). Ndipo tsiku limenelo okhulupirira adzasangalala.
Las Exégesis Árabes:
بِنَصۡرِ ٱللَّهِۚ يَنصُرُ مَن يَشَآءُۖ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلرَّحِيمُ
Ndi chithandizo cha Allah (chimene iwo adzapatsidwa, chomwe ndikugonjetsa Aquraish tsiku lomwelo). (Allah) amamthandiza amene wamfuna, ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha.
Las Exégesis Árabes:
 
Traducción de significados Capítulo: Ar-Room
Índice de Capítulos Número de página
 
Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Khaled Ibrahim Betala - Índice de traducciones

Traducida por Khaled Ibrahim Petala

Cerrar