Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa * - Índice de traducciones


Traducción de significados Capítulo: Sura Al-Mulk   Versículo:

Sura Al-Mulk

تَبَٰرَكَ ٱلَّذِي بِيَدِهِ ٱلۡمُلۡكُ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٌ
۞ Watukuka ndi kudalitsika (Allah) Amene m’manja Mwake muli ufumu (wochita chilichonse pazolengedwa zonse); ndipo Iye ali ndi mphamvu yokwanira pachilichonse.[370]
[370] Sura imeneyi, Mtumiki (s.a.w) amafuna kuti msilamu aliyense ailoweze pamtima ndi kuzindikira bwino tanthauzo lake. Mtumiki (s.a.w) adali ndi chizolowezi chomawerenga Surayi asanagone. M’sura imeneyi muli chikumbutso chosonyeza kuti Allah Ngwamphamvu amachita mmene angafunire. Chimene wafuna chichitika ngakhale anthu sakufuna. Ndipo chimene sanafune kuti chichitike sichingachitike ngakhale anthu atafunitsitsa kuti chichitike. Zonse zakumwamba ndi zam’nthaka ndiZake.
Las Exégesis Árabes:
ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلۡمَوۡتَ وَٱلۡحَيَوٰةَ لِيَبۡلُوَكُمۡ أَيُّكُمۡ أَحۡسَنُ عَمَلٗاۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفُورُ
Amene adalenga imfa ndi moyo kuti akuyeseni (mayeso) ndani mwa inu ali wochita zabwino (kwambiri). Ndipo Iye ndiWopambana m’mphamvu (salephera kanthu) ndiponso Wokhululukira (olakwa).[371]
[371] M’ma Ayah awa:- Allah akutilangiza kuti tikhale oganizira zomwe adalenga zimene zingatisonyeze nzeru Zake ndi mphamvu Zake zakuya. Tilingalire m’zolengedwa Zake, tisalingalire mwa Iye mwini chifukwa sitingathe kumlingalira mmene alili pomwe tikulephera kuulingalira mzimu wathu momwe ulili.
Las Exégesis Árabes:
ٱلَّذِي خَلَقَ سَبۡعَ سَمَٰوَٰتٖ طِبَاقٗاۖ مَّا تَرَىٰ فِي خَلۡقِ ٱلرَّحۡمَٰنِ مِن تَفَٰوُتٖۖ فَٱرۡجِعِ ٱلۡبَصَرَ هَلۡ تَرَىٰ مِن فُطُورٖ
Amene adalenga thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikana (kapena zolingana mkalengedwe kake). Suona kusiyana m’zolenga za Wachifundo chambiri. Bwereza kuyang’ana, kodi ukuona pena pong’ambika?
Las Exégesis Árabes:
ثُمَّ ٱرۡجِعِ ٱلۡبَصَرَ كَرَّتَيۡنِ يَنقَلِبۡ إِلَيۡكَ ٱلۡبَصَرُ خَاسِئٗا وَهُوَ حَسِيرٞ
Bwerezanso kuyang’ana kachiwiri, kuyang’anako kukubwerera wekha (uku maso) ali olobodoka ndiponso otopa. (Suona polakwika paliponse).
Las Exégesis Árabes:
وَلَقَدۡ زَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِمَصَٰبِيحَ وَجَعَلۡنَٰهَا رُجُومٗا لِّلشَّيَٰطِينِۖ وَأَعۡتَدۡنَا لَهُمۡ عَذَابَ ٱلسَّعِيرِ
Ndipo ndithu talikongoletsa thambo loyandikirali ndi nyali (nyenyezi) ndipo tazichita kukhala (mochokera zenje) zolasila asatana. Ndipo tawakonzera (patsiku lachimaliziro) chilango cha Moto woyaka.
Las Exégesis Árabes:
وَلِلَّذِينَ كَفَرُواْ بِرَبِّهِمۡ عَذَابُ جَهَنَّمَۖ وَبِئۡسَ ٱلۡمَصِيرُ
Ndipo kwa amene sakhulupirira Mbuye wawo ali nacho chilango cha Jahannam; ndipo kuipirenji kobwerera!
Las Exégesis Árabes:
إِذَآ أُلۡقُواْ فِيهَا سَمِعُواْ لَهَا شَهِيقٗا وَهِيَ تَفُورُ
Akadzaponyedwa m’menemo adzamva mavume ake (oipa) uku ukuwira mwaukali.
Las Exégesis Árabes:
تَكَادُ تَمَيَّزُ مِنَ ٱلۡغَيۡظِۖ كُلَّمَآ أُلۡقِيَ فِيهَا فَوۡجٞ سَأَلَهُمۡ خَزَنَتُهَآ أَلَمۡ يَأۡتِكُمۡ نَذِيرٞ
Udzayandikira kudukaduka chifukwa cha mkwiyo (kukwiira oipa); nthawi iliyonse gulu (la oipa) likadzaponyedwa m’menemo, Angelo oyang’anira Motowo adzawafunsa (mowadzudzula): “Kodi sadakufikeni mchenjezi (wokuchenjezani za tsikuli?).”
Las Exégesis Árabes:
قَالُواْ بَلَىٰ قَدۡ جَآءَنَا نَذِيرٞ فَكَذَّبۡنَا وَقُلۡنَا مَا نَزَّلَ ٱللَّهُ مِن شَيۡءٍ إِنۡ أَنتُمۡ إِلَّا فِي ضَلَٰلٖ كَبِيرٖ
Adzayankha “Inde, adatifika mchenjezi koma tidatsutsa, ndipo tidati: ‘Allah sadavumbulutse chilichonse (kwa iwe ngakhale kwa anzako). Koma inu muli m’kusokera kwakukulu.”
Las Exégesis Árabes:
وَقَالُواْ لَوۡ كُنَّا نَسۡمَعُ أَوۡ نَعۡقِلُ مَا كُنَّا فِيٓ أَصۡحَٰبِ ٱلسَّعِيرِ
Ndipo adzanena: “Tikadakhala kuti tidamvera (zimene ankatiuza) kapena kuziganizira mwanzeru sitikadakhala m’gulu la anthu a ku Moto.”
Las Exégesis Árabes:
فَٱعۡتَرَفُواْ بِذَنۢبِهِمۡ فَسُحۡقٗا لِّأَصۡحَٰبِ ٱلسَّعِيرِ
Choncho adzavomereza machimo awo (koma sipadzakhala chopindula;) tero kuonongeka ndi kukhala kutali (ndi chifundo cha Allah) kuli pa anthu a ku Moto!
Las Exégesis Árabes:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُم بِٱلۡغَيۡبِ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَأَجۡرٞ كَبِيرٞ
Ndithudi amene akumuopa Mbuye wawo pomwe iwo sakumuona, adzapeza chikhululuko pa machimo awo ndi malipiro aakulu (pa zabwino zomwe ankachita).
Las Exégesis Árabes:
وَأَسِرُّواْ قَوۡلَكُمۡ أَوِ ٱجۡهَرُواْ بِهِۦٓۖ إِنَّهُۥ عَلِيمُۢ بِذَاتِ ٱلصُّدُورِ
Ndipo bisani mawu anu, kapena aonetseni poyera; (zonsezi nchimodzimodzi kwa Allah) ndithudi Iye Ngodziwa zobisika za m’mitima.
Las Exégesis Árabes:
أَلَا يَعۡلَمُ مَنۡ خَلَقَ وَهُوَ ٱللَّطِيفُ ٱلۡخَبِيرُ
Kodi asadziwe amene adalenga (zinthu zonse)? Pomwe Iye Ngodziwa zinthu zingo’nozing’no kwambiri mmene zilili (ndiponso) Ngodziwa nkhani zonse.
Las Exégesis Árabes:
هُوَ ٱلَّذِي جَعَلَ لَكُمُ ٱلۡأَرۡضَ ذَلُولٗا فَٱمۡشُواْ فِي مَنَاكِبِهَا وَكُلُواْ مِن رِّزۡقِهِۦۖ وَإِلَيۡهِ ٱلنُّشُورُ
Iye ndi Amene wakupangirani nthaka kuti ikhale yogonjera (pa chilichonse chimene mufuna). Choncho yendani mbali zake zonse; ndipo idyani rizq lake, (limene Allah akukutulutsirani). Ndipo kwa Iye Yekha ndiko kobwerera kwanu (nonse mutapatsidwa moyo wachiwiri).
Las Exégesis Árabes:
ءَأَمِنتُم مَّن فِي ٱلسَّمَآءِ أَن يَخۡسِفَ بِكُمُ ٱلۡأَرۡضَ فَإِذَا هِيَ تَمُورُ
Kodi muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakukwilireni m’nthaka (ndikukudzidzimutsani) pamene nthaka ikugwedezeka molimba?
Las Exégesis Árabes:
أَمۡ أَمِنتُم مَّن فِي ٱلسَّمَآءِ أَن يُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ حَاصِبٗاۖ فَسَتَعۡلَمُونَ كَيۡفَ نَذِيرِ
Kapena muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakutumizireni mphepo yamkuntho ya miyala (ndi kukuonongani ndi miyalayo?) Choncho mdzadziwa mmene lilili chenjezo Langa (pa inu).
Las Exégesis Árabes:
وَلَقَدۡ كَذَّبَ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡ فَكَيۡفَ كَانَ نَكِيرِ
Ndithudi amene adalipo kale iwo asanabadwe adakana mithenga yawo. Nanga udali bwanji mkwiyo Wanga pa iwo (pakuwaononga onse)!
Las Exégesis Árabes:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ إِلَى ٱلطَّيۡرِ فَوۡقَهُمۡ صَٰٓفَّٰتٖ وَيَقۡبِضۡنَۚ مَا يُمۡسِكُهُنَّ إِلَّا ٱلرَّحۡمَٰنُۚ إِنَّهُۥ بِكُلِّ شَيۡءِۭ بَصِيرٌ
Kodi, sadaone mbalame pamwamba pawo mmene zikutambasulira (mapiko ake) ndi kuwafumbata. Palibe amene akuzigwira kuti zisagwe koma (Allah) Wachifundo chambiri; ndithudi Iye pachilichonse Ngopenya.
Las Exégesis Árabes:
أَمَّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي هُوَ جُندٞ لَّكُمۡ يَنصُرُكُم مِّن دُونِ ٱلرَّحۡمَٰنِۚ إِنِ ٱلۡكَٰفِرُونَ إِلَّا فِي غُرُورٍ
Kodi ndani amene ali asilikali anu okutetezani kuchilango posakhala (Allah) Wachifimdo chambiri? Ndithudi osakhulupirira ali mkunyengeka (pa zimene akuganizira).
Las Exégesis Árabes:
أَمَّنۡ هَٰذَا ٱلَّذِي يَرۡزُقُكُمۡ إِنۡ أَمۡسَكَ رِزۡقَهُۥۚ بَل لَّجُّواْ فِي عُتُوّٖ وَنُفُورٍ
Kodi ndani uyo amene angakupatseni rizq (limene mungakhalire ndi moyo ndi kupezera mtendere) ngati Iye atatsekereza rizq Lake (kwa inu)? Koma Akafiri akupitiriza kudzikweza kwawo, ndi kudziika kutali ndi choonadi.
Las Exégesis Árabes:
أَفَمَن يَمۡشِي مُكِبًّا عَلَىٰ وَجۡهِهِۦٓ أَهۡدَىٰٓ أَمَّن يَمۡشِي سَوِيًّا عَلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Kodi amene akuyenda mozyolika ndi nkhope yake angakhale wolungama kapena amene akuyenda moongoka panjira yosakhota?
Las Exégesis Árabes:
قُلۡ هُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَكُمۡ وَجَعَلَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ
Nena: “Iye ndi Amene adakulengani (pomwe simudali kanthu) ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima, (zimene mukhoza kupeza nazo mtendere). Koma kuyamika kwanu (kwa Yemwe adakupatsani zimenezi) nkochepa kwambiri.
Las Exégesis Árabes:
قُلۡ هُوَ ٱلَّذِي ذَرَأَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ
Nena: “Iye ndi amene adakuchulukitsani pa dziko ndipo kwa Iye (Yekha) ndiko mudzasonkhanitsidwa (kuti adzakuwerengereni ndi kukulipirani).
Las Exégesis Árabes:
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Akunena (monyada osakhulupirira za kuuka): “Ndiliti (lidzakwaniritsidwa) lonjezo ili ngati inu muli owona?”
Las Exégesis Árabes:
قُلۡ إِنَّمَا ٱلۡعِلۡمُ عِندَ ٱللَّهِ وَإِنَّمَآ أَنَا۠ نَذِيرٞ مُّبِينٞ
Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}): “Ndithu kudziwa (kwa izi) nkwa Allah yekha, ndipo ndithudi ine, ndine mchenjezi wowonekera.”
Las Exégesis Árabes:
فَلَمَّا رَأَوۡهُ زُلۡفَةٗ سِيٓـَٔتۡ وُجُوهُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَقِيلَ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تَدَّعُونَ
Koma akadzaziona (zimene akulonjezedwazo) zili pafupi (ndi iwo), nkhope za amene sadakhulupirire zidzakhumudwa ndikuyaluka kwambiri, ndipo kudzanenedwa (mowadzudzula): “Izi ndi zija mudali kuzipempha (kuti zidze, zadza tsopano).
Las Exégesis Árabes:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِنۡ أَهۡلَكَنِيَ ٱللَّهُ وَمَن مَّعِيَ أَوۡ رَحِمَنَا فَمَن يُجِيرُ ٱلۡكَٰفِرِينَ مِنۡ عَذَابٍ أَلِيمٖ
Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}): “Tandiuzani ngati Allah atandiononga pamodzi ndi amene ndili nawo (monga momwe mukufunira) kapena kutichitira chifundo (ndikutalikitsa nthawi ya moyo wathu). Nanga ndani amene adzawateteza wosakhulupirira ku chilango chowawa?”
Las Exégesis Árabes:
قُلۡ هُوَ ٱلرَّحۡمَٰنُ ءَامَنَّا بِهِۦ وَعَلَيۡهِ تَوَكَّلۡنَاۖ فَسَتَعۡلَمُونَ مَنۡ هُوَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
Nena: “Iye ndiye (Allah) Wachifundo chambiri, takhulupirira mwa Iye ndiponso kwa Iye ndikumene tatsamira. Choncho posachedwapa mudziwa (chilango chikatsika kuti) ndani (m’magulu awiriwa) yemwe ali m’kusokera koonekera.”
Las Exégesis Árabes:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِنۡ أَصۡبَحَ مَآؤُكُمۡ غَوۡرٗا فَمَن يَأۡتِيكُم بِمَآءٖ مَّعِينِۭ
Nena: “Tandiuzani ngati madzi anuwa ataphwa (kulowelera pansi penipeni); choncho ndani amene angakubweretsereni madzi oyenda (ochokera mkati mwanthaka?)
Las Exégesis Árabes:
 
Traducción de significados Capítulo: Sura Al-Mulk
Índice de Capítulos Número de página
 
Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Índice de traducciones

Traducción del significado del Corán al chewa por Khaled Ibrahim Betala (ed.2020)

Cerrar