[271] Allah wapamwamba wayamba Sura iyi ndi malembo awa awiri potchalenja omwe akutsutsa zoti Qur’an idachokera kwa Allah, kuti atalemba yawo Qur’an yomwe malembo ake omwewa omwe iwo akuwadziwa bwino ndipo amawayankhula.
Koma alephera kutalitali kulemba buku ndi nzeru zawo monga ili. Ndipo kulephera kwawo kulemba buku longa ili, ndiumboni kuti bukuli lidachokera kwa Allah.
(Iye ndi Allah), Wachifundo Chambiri; pa Arsh (Mpando wachifumu) adakhazikika, (kukhazikika koyenerana ndi ulemelero Wake kopanda kukufanizira ndi kukhazikika kwa chilichonse; pakuti Iye salingana ndi chilichonse pa chikhalidwe ndi mbiri Zake).
Ndipo ngati ulankhula mokweza mawu, (iwe munthu), ndithu Iye akudziwa zobisika ndi zobisika kwambiri (zomwe mwazibisa mu mtima mwanu).[272]
[272] M’ndime iyi Allah akuuza munthu kuti Iye akudziwa zonse zimene munthu amayankhula mokweza mawu ndi zimene munthu amayankhula ndi anzake mobisa, ngakhalenso zomwe mtima wake umamnong’oneza.
Ndithu nthawi ya tsiku lachimaliziro idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuibisa dala (kwa anthu) kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita.[274]
[274] Womasulira Qur’an adati cholinga chakubisa kudza kwa tsiku la chimaliziro, ndi nthawi ya imfa ya munthu ndikuti Allah wapamwambamwamba adalamula kuti sangavomereze kulapa tsiku la chimaliziro litadza, ndi nthawi ya imfa itamufikira munthu. Anthu akadadziwa nthawi yeniyeni ya chimaliziro ndi nthawi yakudza kwa imfa yawo, akadakhala akuchita zinthu zoyipa naakhala ndi chiyembekezero choti adzalapa nthawi ikayandikira, nadzapulumuka kuchilango cha Allah. Koma Allah anabisa zimenezo kuti anthu akhale tcheru nthawi zonse ndikukhala okonzekera za imfa ndi za tsiku la chimaliziro kuti zingawadzere modzidzimutsa.
“Ndipo masulani mfundo yomwe ili ku lirime kwanga, (ndimasulireni kumangika kwa lirime langa kuti mawu anga akakhale opanda chibwibwi).”[278]
[278] Musa adali wachibwibwi koma chibwibwi chake sichinali chachibadwa. Kuyamba kwa chibwibwi chake kudali motere: Kumayambiliro amoyo wake adali kukhala m’nyumba ya Farawo. Ndipo nthawi ina Farawo adamuika pamiyendo yake iye ali mwana. Musa adakoka ndevu za Farawo ndi dzanja lake. Ndipo Farawo adakwiya natsimikiza zomupha. Ndipo Asiya, mkazi wake, adati kwa iye: “Iyeyu sazindikira. Ndipo ndikusonyeza zimenezo kuti udziwe.Yandikitsani kwa iye makala awiri ndi ngale ziwiri. Ngati atola ngalezo ndiye kuti akuzindikira. Koma akatola khala lamoto, apo uzindikira kuti ameneyu sazindikira kanthu. Choncho Farawo adamuyandikizira zonsezo ndipo iye adatola khala lamoto nkuliponya mkamwa mwake. Potero palirime lake padali kachipsera. Nkhaniyi ikupezeka m’buku la Tabariyi, volume 16 tsamba 159.
(Kuti): “Mponye (mwanayo) m’bokosi ndipo ponya bokosilo mu mtsinje; ndipo mtsinje umponya m’mbali kuti amtenge mdani wanga ndi mdani wake (ndi kuti aleredwe mwaubwino ndi Farawo); ndipo ndidaika kukondeka pa iwe kochokera kwa Ine (kuti ukhale wokondedwa ndi anthu onse) ndikuti uleredwe moyang’aniridwa ndi Ine.”
(Kumbuka) pomwe mlongo wako ankayenda (kunka kubanja la Farawo) Ndipo adati: “Kodi ndikulondolereni munthu amene angathe kumlera?” Ndipo tidakubwezera kwa mayi wako kuti maso ake atonthole, ndipo asadandaule. Ndipo kenaka udapha munthu (mwangozi), ndipo tidakupulumutsa ku madandaulo; tidakuyesa ndi mayeso ambiri. Udakhala zaka zambiri ndi anthu a ku Madiyan. Kenaka wabwera (apa) monga mwachikonzero, E, iwe Mûsa![279]
[279] Omasulira adati: Pamene adamtola Musa akubanja la Farawo sadali kuyamwa bele la mkazi aliyense, amakana, chifukwa Allah adamuletsa kuyamwa mawere aakazi ena oyamwitsa. Ndipo mayi wake adali ndi madandaulo ndi chisoni atamponya mumtsinje, ndipo adamulamula mlongo wake kunka nafufuza za mwanayo. Pamene adafika kunyumba ya Farawo, adamuona. Adati: “Kodi ndikulondolereni mkazi wokhulupirika, waulemu kuti azikuyamwitsirani mwanayo?” Ndipo iwo adati: “Pita kamtenge.” Choncho adadza ndi mayi wa Musa. Pamene adatulutsa bere lake, Musa adayamwa. Choncho mkazi wa Farawo adasangalala kwabasi namuuza make Musa: “Dzikhala pamodzi nane kunyumba yachifumu.” Iye adati: “Sindingathe kusiya nyumba yanga ndi ana anga. Koma ndimtenga ndipo ndikhala ndikudza naye nthawi iliyonse ukamufuna.” Mkazi wa Farawo adavomereza ndi kumchitira zabwino mayiyo. Ili ndilo tanthauzo la mawu a Allah akuti: “Tidakubwezera kwa mayi wako kuti diso lake litonthole, asadandaule.”
Choncho mpitireni, ndikumuuza (kuti): “Ndithu ife ndife atumiki a Mbuye wako. Asiye ana a Israyeli achoke ndi ife, ndipo usawazunze; ndithu takudzera ndi chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wako (chomwe ndi mboni yathu pa zomwe tikukuuzazi), ndipo mtendere ukhala pa yemwe atsate chiwongoko.”
(Farawo) adanena: “Ha! Mwamkhulupirira ndisadakupatseni chilolezo? Ndithu iye ndi mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga! Choncho ndikudulani manja anu ndi miyendo yanu, mosemphanitsa:; (dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wakumanzere. Pomwe wina, mkono wakumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja), ndipo kenako ndikupachikani pa mathunthu a mitengo ya kanjeza; ndithu mudziwa (panthawiyo) kuti ndani mwa ife, (ine kapena Mulungu wa Mûsa), wachilango chaukali ndi chopitilira.”[282]
“Ndithu takhulupirira Mbuye wathu kuti atikhululukire zolakwa zathu ndi matsenga amene watikakamiza (kuchita); ndipo Allah ndi Yemwe ali Wabwino ndi Wamuyaya (osati iwe).”
E inu ana a Israyeli! Ndithu tidakupulumutsani kwa mdani wanu, ndipo tidakulonjezani (kuti mudze) mbali yakudzanjadzanja ya phiri (kuti tikupatseni malamulo ndi zina), ndipo tidakutsitsirani Manna ndi Saluwa.
(Harun) adati: E iwe mwana wa mayi anga! Usagwire ndevu zanga, ngakhale mutu wanga (poukoka chifukwa cha mkwiyo). Ndithu ine ndidaopa (kuchoka ndi ena, kusiya ena) kuti ungati: “Wawagawa ana a Israyeli, ndipo sudayembekezere mawu anga.”
(Iye adati:) “Ndidaona zomwe sadazione (ena) ndipo ndidatapa pang’ono mapazi a Mtumiki (Gabriele) ndikuwaponya (mu fano la mwana wa ng’ombe). Ndipo zimenezi ndi zomwe zidakomera mtima wanga.”[285]
[285] Samiriyyu adaona Gabrieli ali kudza kwa Musa atakwera hatchi. Choncho adakondwera mu mtima mwake kutapa mapazi ake. Tero ankati akaponya zomwe adatapazo pa chinthu chilichonse chakufa chinkauka. Ndipo pamene fano la mwana wang’ombe lidakonzedwa, iye adatenga dothi la mapazi a mthengayo nkuponya pa fanolo. Choncho fanolo lidayamba kutulutsa mawu ngati mwana wa ng’ombe.
Ndithu wompembedza wanu, ndi Allah Yekha, Yemwe, palibe woti nkupembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo wakwanira pa chilichonse kuchidziwa ndi nzeru (Zake zopanda malire).
(Kumbuka Mtumiki Muhammad {s.a.w}), tsiku lomwe lipenga lidzaimbidwa. Ndipo tidzasonkhanitsa oipa tsiku limenelo maso awo ali a buluu (blue, chifukwa cha mantha).
Ife tikudziwa kwambiri zimene azidzanena pamene abwino awo pamayendedwe azidzanena: “Inu simudakhale koma tsiku limodzi basi (poyerekeza ndi kuchuluka kwa masiku a ku Moto).”
Tsiku limenelo adzamtsatira woitana; sadzatha kumpatuka, ndipo mawu (azolengedwa) adzatonthola (kuti chete) kwa (Allah) Wachifundo chambiri; ndipo sudzamva, koma kunong’ona basi (ndi mididi ya mapazi).
Ndipo tidamulangiza (Mneneri) Adam kale, koma adaiwala. Ndipo sitidapeze Mwa iye kulimba mtima (potsatira lamulo Lathu loti asadye zipatso za mtengo woletsedwa).
(Allah) adati: “Chokani nonsenu m’menemo, uku pali chidani pakati pa wina ndi mnzake, (padzakhala chidani pakati pa ana anu); koma chikadzakudzerani chiongoko kuchokera kwa Ine, tero amene adzachitsate chiongoko changacho, sadzasokera ndiponso sadzavutika.”
Choncho pirira pa zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda, dzuwa lisanatuluke (popemphera swala ya Fajr), ndiponso lisanalowe (popemphera swala ya Asr); ndiponso nthawi za usiku umulemekeze (popemphera swala ya Magrib ndi Isha), ndi pansonga za masana (pakatikati pa usana popemphera swala ya Dhuhr); kuti udzakhale wokondwa (ndi malipilo amene azakupatse tsiku la Qiyâma).
Ndipo usazitong’olere maso ako (mozidololokera zinthu) zimene tawasangalatsa nazo ena mwa anthu pakati pawo; zimenezo nzokongoletsa za moyo wa pa dziko basi, kuti tiwayese mayeso pazimenezo; koma chopatsa cha Mbuye wako (chomwe nchololedwa ngakhale chikhale chochepa) nchabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.
Ndipo lamula banja lako kupemphera Swala ndi kuipirira iwe mwini Swalayo. Sitikukupempha rizq, (chakudya) koma Ife ndi amene tikukudyetsa ndipo malekezero abwino ali mukuopa (Allah).
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
نتایج جستجو:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".