Check out the new design

ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا * - لیست ترجمه ها


ترجمهٔ معانی سوره: اعراف   آیه:
قَالَ يَٰمُوسَىٰٓ إِنِّي ٱصۡطَفَيۡتُكَ عَلَى ٱلنَّاسِ بِرِسَٰلَٰتِي وَبِكَلَٰمِي فَخُذۡ مَآ ءَاتَيۡتُكَ وَكُن مِّنَ ٱلشَّٰكِرِينَ
(Allah) adati: “E iwe Mûsa! Ndithu Ine ndakusankha iwe mwa anthu onse, (kukusankhira) uthenga Wanga ndi kuyankhulana Nane. Choncho landira chimene ndakupatsa, ndipo khala m’modzi wa anthu othokoza.”
تفسیرهای عربی:
وَكَتَبۡنَا لَهُۥ فِي ٱلۡأَلۡوَاحِ مِن كُلِّ شَيۡءٖ مَّوۡعِظَةٗ وَتَفۡصِيلٗا لِّكُلِّ شَيۡءٖ فَخُذۡهَا بِقُوَّةٖ وَأۡمُرۡ قَوۡمَكَ يَأۡخُذُواْ بِأَحۡسَنِهَاۚ سَأُوْرِيكُمۡ دَارَ ٱلۡفَٰسِقِينَ
Ndipo tidamlembera m’mapale (m’masileti) maphunziro aulaliki wa mtundu uliwonse wofotokoza chinthu chilichonse: “Choncho, atenge mwa mphamvu ndi kuwalamulira anthu ako kuti awagwire mwa ubwino wake. Posachedwapa ndidzakusonyezani midzi ya oipa oswa malamulo athu (momwe idaonongekera. Ndipo ndikulowetsani inu m’menemo).”
تفسیرهای عربی:
سَأَصۡرِفُ عَنۡ ءَايَٰتِيَ ٱلَّذِينَ يَتَكَبَّرُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَإِن يَرَوۡاْ كُلَّ ءَايَةٖ لَّا يُؤۡمِنُواْ بِهَا وَإِن يَرَوۡاْ سَبِيلَ ٱلرُّشۡدِ لَا يَتَّخِذُوهُ سَبِيلٗا وَإِن يَرَوۡاْ سَبِيلَ ٱلۡغَيِّ يَتَّخِذُوهُ سَبِيلٗاۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ عَنۡهَا غَٰفِلِينَ
Ndiwatembenuzira kuzilingalira zizindikiro Zanga awo omwe akudzitukumula pa dziko popanda choonadi, ndipo akaona chizindikiro chilichonse sachikhulupirira, ndipo akaona njira yolungama sakuiyesa njira (sakuitsata), koma akaona njira yosokera akuiyetsa njira (akuitsata). Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adatsutsa zizindikiro Zathu ndipo anali osazilabadira.
تفسیرهای عربی:
وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَلِقَآءِ ٱلۡأٓخِرَةِ حَبِطَتۡ أَعۡمَٰلُهُمۡۚ هَلۡ يُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndipo awo amene atsutsa zizindikiro Zathu ndi nkumano wa tsiku lachimaliziro, zochita zawo zaonongeka. Kodi adzalipidwa china kuposa zomwe adali kuchita?
تفسیرهای عربی:
وَٱتَّخَذَ قَوۡمُ مُوسَىٰ مِنۢ بَعۡدِهِۦ مِنۡ حُلِيِّهِمۡ عِجۡلٗا جَسَدٗا لَّهُۥ خُوَارٌۚ أَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّهُۥ لَا يُكَلِّمُهُمۡ وَلَا يَهۡدِيهِمۡ سَبِيلًاۘ ٱتَّخَذُوهُ وَكَانُواْ ظَٰلِمِينَ
Ndipo pambuyo pake (popita kukalandira Taurat), anthu a Mûsa adaumba (fano la) thole (mwana wa ng’ombe) kuchokera mu zodzikongoletsera zawo (zibangiri zawo za siliva ndi golide); yemwe adali ndi thupi ndi kumatuluka mawu (koma wopanda moyo). Kodi sakuona kuti ilo (fano lawolo) silikuwalankhula ndiponso silikuwaongolera njira (yabwino?) Koma adalipanga basi (kuti likhale mulungu wawo wa fano) potero adali kudzichitira okha zoipa.
تفسیرهای عربی:
وَلَمَّا سُقِطَ فِيٓ أَيۡدِيهِمۡ وَرَأَوۡاْ أَنَّهُمۡ قَدۡ ضَلُّواْ قَالُواْ لَئِن لَّمۡ يَرۡحَمۡنَا رَبُّنَا وَيَغۡفِرۡ لَنَا لَنَكُونَنَّ مِنَ ٱلۡخَٰسِرِينَ
Pamene adazindikira kulakwa kwawo, (anadandaula kwambiri) naona kuti iwo asokera, anati: “Ngati Mbuye wathu satimvera chisoni ndi kutikhululukira, ndithudi, tikhala mwa otaika (oonongeka).”
تفسیرهای عربی:
 
ترجمهٔ معانی سوره: اعراف
فهرست سوره ها شماره صفحه
 
ترجمهٔ معانی قرآن کریم - ترجمه‌ى چوایی - خالد ابراهیم بيتالا - لیست ترجمه ها

مترجم: خالد ابراهیم بیتالا.

بستن