કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર * - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા


શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અન્ નમલ   આયત:

અન્ નમલ

طسٓۚ تِلۡكَ ءَايَٰتُ ٱلۡقُرۡءَانِ وَكِتَابٖ مُّبِينٍ
Tâ-Sîn. Izi ndi Ayah (ndime) (za Qur’an buku lodzazidwa ndi zothandiza), ndiponso buku lofotokoza (chilichonse chauzimu ndi chamoyo wadziko).
અરબી તફસીરો:
هُدٗى وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُؤۡمِنِينَ
(Qur’an) nchiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
ٱلَّذِينَ يُقِيمُونَ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُونَ ٱلزَّكَوٰةَ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ يُوقِنُونَ
Amene akupemphera Swala (zisanu, modzichepetsa ndi mokwaniritsa malamulo ake) ndi kumapereka Zakaat (m’nthawi yake), ndipo iwo ali ndi chitsimikizo champhamvu cha (moyo wa) tsiku la chimaliziro.
અરબી તફસીરો:
إِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ زَيَّنَّا لَهُمۡ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَهُمۡ يَعۡمَهُونَ
Ndithu amene sakhulupirira za (moyo wa) tsiku la chimaliziro, tawakometsera zochita zoipa kukhala ngati zabwino; choncho iwo akungoyumbayumba (m’kusokera kwawo).
અરબી તફસીરો:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَهُمۡ سُوٓءُ ٱلۡعَذَابِ وَهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ هُمُ ٱلۡأَخۡسَرُونَ
Iwowo ndiamene adzapeza chilango choipa; iwo tsiku lachimaliziro ngotayika zedi, (adzaonongeka ku Moto motheratu).
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّكَ لَتُلَقَّى ٱلۡقُرۡءَانَ مِن لَّدُنۡ حَكِيمٍ عَلِيمٍ
Ndipo ndithu iwe ukuphunzitsidwa Qur’an kuchokera kwa mwini nzeru zakuya, Wodziwa kwambiri.
અરબી તફસીરો:
إِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِأَهۡلِهِۦٓ إِنِّيٓ ءَانَسۡتُ نَارٗا سَـَٔاتِيكُم مِّنۡهَا بِخَبَرٍ أَوۡ ءَاتِيكُم بِشِهَابٖ قَبَسٖ لَّعَلَّكُمۡ تَصۡطَلُونَ
(Kumbuka) Mûsa pamene adauza banja lake (mkazi wake): “Ndithu ine ndaona moto; posachedwapa ndikubweretserani nkhani za kumeneko, kapena ndikubweretserani chikuni cha moto kuti inu muothe.
અરબી તફસીરો:
فَلَمَّا جَآءَهَا نُودِيَ أَنۢ بُورِكَ مَن فِي ٱلنَّارِ وَمَنۡ حَوۡلَهَا وَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Choncho pamene adaudzera (motowo) kudaitanidwa: “Wadalitsidwa yemwe ali m’moto ndi yemwe ali m’mphepete mwake; ndipo walemekezeka Allah Mbuye wa zolengedwa.
અરબી તફસીરો:
يَٰمُوسَىٰٓ إِنَّهُۥٓ أَنَا ٱللَّهُ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
E iwe Mûsa! Ndithu ine ndine Allah, Wamphamvu zoposa; Wanzeru zakuya.
અરબી તફસીરો:
وَأَلۡقِ عَصَاكَۚ فَلَمَّا رَءَاهَا تَهۡتَزُّ كَأَنَّهَا جَآنّٞ وَلَّىٰ مُدۡبِرٗا وَلَمۡ يُعَقِّبۡۚ يَٰمُوسَىٰ لَا تَخَفۡ إِنِّي لَا يَخَافُ لَدَيَّ ٱلۡمُرۡسَلُونَ
Ndipo ponya (pansi) ndodo yako! (Pamene adaiponya idasanduka njoka), tero pamene adaiwona ikugwedezeka (ndodo ija) ngati njoka, adatembenuka kuthawa, ndipo sadacheuke (kapena kudikira kuti amve mawu omvekawo): “E iwe Mûsa! Usaope. Ndithu Ine, saopa kwa Ine atumiki.”
અરબી તફસીરો:
إِلَّا مَن ظَلَمَ ثُمَّ بَدَّلَ حُسۡنَۢا بَعۡدَ سُوٓءٖ فَإِنِّي غَفُورٞ رَّحِيمٞ
“Koma amene wadzichitira yekha zoipa, kenako nkusintha (pochita) zabwino pambuyo pa zoipa, (ndimkhululukira) pakuti Ine ndine Wokhululuka kwabasi, Wachifundo chambiri.”
અરબી તફસીરો:
وَأَدۡخِلۡ يَدَكَ فِي جَيۡبِكَ تَخۡرُجۡ بَيۡضَآءَ مِنۡ غَيۡرِ سُوٓءٖۖ فِي تِسۡعِ ءَايَٰتٍ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَقَوۡمِهِۦٓۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمٗا فَٰسِقِينَ
“Ndipo lowetsa dzanja lako palisani la mkanjo wako, ndipo lituluka lili loyera, (kuyera) kopanda matenda. (Ziwirizi) zili m’gulu la zododometsa zisanu ndi zinayi. Pita nazo kwa Farawo ndi anthu ake; ndithu iwo ndianthu otuluka m’chilamulo cha Allah.”
અરબી તફસીરો:
فَلَمَّا جَآءَتۡهُمۡ ءَايَٰتُنَا مُبۡصِرَةٗ قَالُواْ هَٰذَا سِحۡرٞ مُّبِينٞ
Tero pamene zidawadzera zizindikiro Zathu zosonyeza (kuti iye ndimtumiki wa Allah) adati: “Awa ndimatsenga woonekera.”
અરબી તફસીરો:
وَجَحَدُواْ بِهَا وَٱسۡتَيۡقَنَتۡهَآ أَنفُسُهُمۡ ظُلۡمٗا وَعُلُوّٗاۚ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
Ndipo adazitsutsa (zisonyezozo) mwachinyengo ndi modzikuza chikhalirecho mitima yawo idatsimikiza (kuti ndizoona zochokera kwa Allah); choncho, yang’ana adali bwanji malekezero a oononga!
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ عِلۡمٗاۖ وَقَالَا ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي فَضَّلَنَا عَلَىٰ كَثِيرٖ مِّنۡ عِبَادِهِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo ndithu Daud ndi Sulaiman tidawapatsa nzeru (zazikulu; adayamika Allah) adati: “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah Yemwe watichitira ubwino kuposa ambiri mwa akapolo ake okhulupirira.”
અરબી તફસીરો:
وَوَرِثَ سُلَيۡمَٰنُ دَاوُۥدَۖ وَقَالَ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّاسُ عُلِّمۡنَا مَنطِقَ ٱلطَّيۡرِ وَأُوتِينَا مِن كُلِّ شَيۡءٍۖ إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ ٱلۡفَضۡلُ ٱلۡمُبِينُ
Ndipo Sulaiman adalowa mmalo mwa Daud pa nzeru ndi uneneri ndipo (Sulaiman) adati: “E inu anthu! Ndithu taphunzitsidwa (mpaka tikudziwa) chiyankhulo cha mbalame, ndiponso tapatsidwa chilichonse; ndithu umenewu ndiubwino wopenyeka.
અરબી તફસીરો:
وَحُشِرَ لِسُلَيۡمَٰنَ جُنُودُهُۥ مِنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ وَٱلطَّيۡرِ فَهُمۡ يُوزَعُونَ
Ndipo adasonkhanitsidwa kwa Sulaiman ankhondo ake ochokera m’ziwanda, anthu ndi mbalame, ndipo adawandandika m’magulumagulu.
અરબી તફસીરો:
حَتَّىٰٓ إِذَآ أَتَوۡاْ عَلَىٰ وَادِ ٱلنَّمۡلِ قَالَتۡ نَمۡلَةٞ يَٰٓأَيُّهَا ٱلنَّمۡلُ ٱدۡخُلُواْ مَسَٰكِنَكُمۡ لَا يَحۡطِمَنَّكُمۡ سُلَيۡمَٰنُ وَجُنُودُهُۥ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Kufikira pamene adadza pachigwa chanyelere, nyelere idanena (kuuza zinzake): “E inu nyelere, lowani m’nyumba zanu poopa kuti angakupondeni Sulaiman ndi magulu ake ankhondo pomwe iwo sakudziwa (za inu).”
અરબી તફસીરો:
فَتَبَسَّمَ ضَاحِكٗا مِّن قَوۡلِهَا وَقَالَ رَبِّ أَوۡزِعۡنِيٓ أَنۡ أَشۡكُرَ نِعۡمَتَكَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ وَعَلَىٰ وَٰلِدَيَّ وَأَنۡ أَعۡمَلَ صَٰلِحٗا تَرۡضَىٰهُ وَأَدۡخِلۡنِي بِرَحۡمَتِكَ فِي عِبَادِكَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Choncho adamwetulira, mosekelera chifukwa cha mawu ake aja (mawu a nyelere); ndipo (Sulaiman) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nyonga zakuti ndizithokozera mtendere wanu umene mwandidalitsa nawo pamodzi ndi makolo anga, ndi kuti ndizichita zabwino (zomwe) mukuziyanja; Kupyolera m’chifundo chanu, ndiponso ndilowetseni m’gulu la akapolo anu abwino.”
અરબી તફસીરો:
وَتَفَقَّدَ ٱلطَّيۡرَ فَقَالَ مَالِيَ لَآ أَرَى ٱلۡهُدۡهُدَ أَمۡ كَانَ مِنَ ٱلۡغَآئِبِينَ
Ndipo adayamba kuyendera mbalame, adati: “Kodi bwanji sindikumuona Huduhudu? Kapena ali m’gulu la amene pano palibe?”
અરબી તફસીરો:
لَأُعَذِّبَنَّهُۥ عَذَابٗا شَدِيدًا أَوۡ لَأَاْذۡبَحَنَّهُۥٓ أَوۡ لَيَأۡتِيَنِّي بِسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٖ
“Ndithu ndimulanga chilango chokhwima, kapena ndimzinga (ndimdula khosi) pokhapokha andibweletsere umboni womveka (wosonyeza kuti adachoka pazifukwa zomveka).”
અરબી તફસીરો:
فَمَكَثَ غَيۡرَ بَعِيدٖ فَقَالَ أَحَطتُ بِمَا لَمۡ تُحِطۡ بِهِۦ وَجِئۡتُكَ مِن سَبَإِۭ بِنَبَإٖ يَقِينٍ
Choncho (Hudhud) sadakhalitse nthawi yaitali; ndipo adati (kwa Sulaiman): “Ndatulukira zomwe iwe sudazitulukire, ndipo ndakubweletsera nkhani yotsimikizika kuchokera ku Saba.”
અરબી તફસીરો:
إِنِّي وَجَدتُّ ٱمۡرَأَةٗ تَمۡلِكُهُمۡ وَأُوتِيَتۡ مِن كُلِّ شَيۡءٖ وَلَهَا عَرۡشٌ عَظِيمٞ
“Ndithu ine ndapeza mkazi akuwalamulira (anthu a ku dziko la Saba), ndipo wapatsidwa chilichonse; ndiponso ali ndi chimpando chachifumu chachikulu.”
અરબી તફસીરો:
وَجَدتُّهَا وَقَوۡمَهَا يَسۡجُدُونَ لِلشَّمۡسِ مِن دُونِ ٱللَّهِ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَصَدَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ فَهُمۡ لَا يَهۡتَدُونَ
“Ndampeza iye ndi anthu ake akulambira dzuwa kusiya Allah; ndipo satana wawakometsera zochita zawo zoipa; choncho wawatsekereza ku njira yolungama, tero sadaongoke.”
અરબી તફસીરો:
أَلَّاۤ يَسۡجُدُواْۤ لِلَّهِ ٱلَّذِي يُخۡرِجُ ٱلۡخَبۡءَ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَيَعۡلَمُ مَا تُخۡفُونَ وَمَا تُعۡلِنُونَ
“Kuti asamlambire Allah yemwe amatulutsa zobisika kumwamba ndi pansi; ndipo akudziwa zimene mukubisa ndi zimene muonetsa poyera.”
અરબી તફસીરો:
ٱللَّهُ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ رَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡعَظِيمِ۩
“Allah! Palibe wina wopembedzedwa mwachoona koma Iye basi; Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) waukulu.”
અરબી તફસીરો:
۞ قَالَ سَنَنظُرُ أَصَدَقۡتَ أَمۡ كُنتَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ
(Sulaiman) adati “Tiona ngati wanena zoona kapena ngati) uli m’gulu la onama.”
અરબી તફસીરો:
ٱذۡهَب بِّكِتَٰبِي هَٰذَا فَأَلۡقِهۡ إِلَيۡهِمۡ ثُمَّ تَوَلَّ عَنۡهُمۡ فَٱنظُرۡ مَاذَا يَرۡجِعُونَ
“Pita ndi kalata yangayi, kaiponye kwa iwo; kenako ukadzipatule kwa iwo (ukakhale pambali) ndi kuona momwe azikayankhira.”
અરબી તફસીરો:
قَالَتۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ إِنِّيٓ أُلۡقِيَ إِلَيَّ كِتَٰبٞ كَرِيمٌ
(Mfumukazi) idati; “E inu nduna! Ndithu kalata yolemekezeka yaponyedwa kwa ine.”
અરબી તફસીરો:
إِنَّهُۥ مِن سُلَيۡمَٰنَ وَإِنَّهُۥ بِسۡمِ ٱللَّهِ ٱلرَّحۡمَٰنِ ٱلرَّحِيمِ
“Yachokera kwa Sulaiman, ndipo mawu ake ndi awa: ‘Mdzina la Allah, Wachifundo chambiri, Wachisoni.’
અરબી તફસીરો:
أَلَّا تَعۡلُواْ عَلَيَّ وَأۡتُونِي مُسۡلِمِينَ
‘Musadzikweze kwa ine, ndipo idzani kwa ine muli ogonjera malamulo anga.”
અરબી તફસીરો:
قَالَتۡ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ أَفۡتُونِي فِيٓ أَمۡرِي مَا كُنتُ قَاطِعَةً أَمۡرًا حَتَّىٰ تَشۡهَدُونِ
(Mfumukazi idaonjezera) kunena: “E inu nduna! ndilangizeni pankhani yangayi; sindilamula kanthu mpaka inu mutandibwerera.”
અરબી તફસીરો:
قَالُواْ نَحۡنُ أُوْلُواْ قُوَّةٖ وَأُوْلُواْ بَأۡسٖ شَدِيدٖ وَٱلۡأَمۡرُ إِلَيۡكِ فَٱنظُرِي مَاذَا تَأۡمُرِينَ
(Nduna) zidati: “Ife ndife eni nyonga ndi eni kumenya nkhondo mwaukali; koma zonse zili ndi inu; choncho yang’anani mmene mungalamulire.”
અરબી તફસીરો:
قَالَتۡ إِنَّ ٱلۡمُلُوكَ إِذَا دَخَلُواْ قَرۡيَةً أَفۡسَدُوهَا وَجَعَلُوٓاْ أَعِزَّةَ أَهۡلِهَآ أَذِلَّةٗۚ وَكَذَٰلِكَ يَفۡعَلُونَ
(Mfumukazi) idati: “Ndithu mafumu akamalowa m’mudzi (wa anthu), amauononga motheratu, ndi kuwachita olemekezeka a m’menemo kukhala onyozeka. Mmenemo ndimomwe amachitira (nthawi zonse).”
અરબી તફસીરો:
وَإِنِّي مُرۡسِلَةٌ إِلَيۡهِم بِهَدِيَّةٖ فَنَاظِرَةُۢ بِمَ يَرۡجِعُ ٱلۡمُرۡسَلُونَ
“Koma ine nditumiza mitulo kwa iwo ndi kuyembekezera zimene abwere nazo otumidwawo.”
અરબી તફસીરો:
فَلَمَّا جَآءَ سُلَيۡمَٰنَ قَالَ أَتُمِدُّونَنِ بِمَالٖ فَمَآ ءَاتَىٰنِۦَ ٱللَّهُ خَيۡرٞ مِّمَّآ ءَاتَىٰكُمۚ بَلۡ أَنتُم بِهَدِيَّتِكُمۡ تَفۡرَحُونَ
Choncho pamene adafika (wamthenga wamkulu) kwa Sulaiman (ndi kupereka mphatso zija, Sulaiman adazikana) nati: “Mukundithandiza ndi chuma? zimene Allah wandipatsa ndizabwino kuposa zimene wakupatsani. Koma inu mukusangalala ndi mphatso zanu.”
અરબી તફસીરો:
ٱرۡجِعۡ إِلَيۡهِمۡ فَلَنَأۡتِيَنَّهُم بِجُنُودٖ لَّا قِبَلَ لَهُم بِهَا وَلَنُخۡرِجَنَّهُم مِّنۡهَآ أَذِلَّةٗ وَهُمۡ صَٰغِرُونَ
Bwerera (nazo) kwa iwo; ndithu tiwadzera ndi gulu lankhondo lomwe iwo sangathe kulimbana nalo; mtheradi, tikawatulutsa m’menemo ali onyozeka ndi oyaluka.”
અરબી તફસીરો:
قَالَ يَٰٓأَيُّهَا ٱلۡمَلَؤُاْ أَيُّكُمۡ يَأۡتِينِي بِعَرۡشِهَا قَبۡلَ أَن يَأۡتُونِي مُسۡلِمِينَ
(Sulaiman adasonkhanitsa nduna zake) nati: “E inu nduna! Ndani abwere ndi mpando wake wachifumuwo kwa ine asadandidzere ali ogonja?”
અરબી તફસીરો:
قَالَ عِفۡرِيتٞ مِّنَ ٱلۡجِنِّ أَنَا۠ ءَاتِيكَ بِهِۦ قَبۡلَ أَن تَقُومَ مِن مَّقَامِكَۖ وَإِنِّي عَلَيۡهِ لَقَوِيٌّ أَمِينٞ
Chiwanda chotchedwa Ifrit chidati: “Ine ndikubweletsera chimenecho usadaimilire pamalo ako (oweruzira). Ndipo ndithu ine pa icho (chimpando) ndine wanyonga, wokhulupirika.”
અરબી તફસીરો:
قَالَ ٱلَّذِي عِندَهُۥ عِلۡمٞ مِّنَ ٱلۡكِتَٰبِ أَنَا۠ ءَاتِيكَ بِهِۦ قَبۡلَ أَن يَرۡتَدَّ إِلَيۡكَ طَرۡفُكَۚ فَلَمَّا رَءَاهُ مُسۡتَقِرًّا عِندَهُۥ قَالَ هَٰذَا مِن فَضۡلِ رَبِّي لِيَبۡلُوَنِيٓ ءَأَشۡكُرُ أَمۡ أَكۡفُرُۖ وَمَن شَكَرَ فَإِنَّمَا يَشۡكُرُ لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ رَبِّي غَنِيّٞ كَرِيمٞ
Yemwe adali ndi maphunziro (akuya) a m’buku adati: “Ine ndikubweletsera (chimpandocho) maso ako asadaphetire (usadatsinzine ndi kupenya).” Pamene adachiona chitakhazikitsidwa patsogolo pake, adati: “Izi nchifukwa cha ufulu wa Mbuye wanga kuti andiyese mayeso kodi ndithokoza kapena ndiusuliza (ufulu Wake). Ndipo amene akuthokoza ndithu ubwino wa kuthokozako udzakhala pa iye mwini. Ndipo amene akukana (mtendere wa Allah posathokoza), ndithu Mbuye wanga Ngokhupuka; Waulemu, (sasaukira chilichonse kwa anthu).”
અરબી તફસીરો:
قَالَ نَكِّرُواْ لَهَا عَرۡشَهَا نَنظُرۡ أَتَهۡتَدِيٓ أَمۡ تَكُونُ مِنَ ٱلَّذِينَ لَا يَهۡتَدُونَ
(Sulaiman) adati: “Msinthireni (maonekedwe a) mpando wake wachifumuwo kuti tione kodi auzindikira kapena akhala mwa omwe sazindikira (chinthu).
અરબી તફસીરો:
فَلَمَّا جَآءَتۡ قِيلَ أَهَٰكَذَا عَرۡشُكِۖ قَالَتۡ كَأَنَّهُۥ هُوَۚ وَأُوتِينَا ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهَا وَكُنَّا مُسۡلِمِينَ
Choncho pamene (mfumukazi) idadza, kudanenedwa: “Kodi mpando wako wachifumu uli ngati uwu?” Idati: “Uli ngati umenewu, ndithu ndipo ife tidapatsidwa kuzindikira (za uneneri wanu) tisadaone chozizwitsa ichi; ndipo, ndithu tidadzipereka (kwa Allah).”
અરબી તફસીરો:
وَصَدَّهَا مَا كَانَت تَّعۡبُدُ مِن دُونِ ٱللَّهِۖ إِنَّهَا كَانَتۡ مِن قَوۡمٖ كَٰفِرِينَ
Ndipo (Sulaiman) adamuletsa zomwe amazipembedza kusiya Allah. Ndithu (mfumukaziyo) idali mwa anthu osakhulupirira (Allah).
અરબી તફસીરો:
قِيلَ لَهَا ٱدۡخُلِي ٱلصَّرۡحَۖ فَلَمَّا رَأَتۡهُ حَسِبَتۡهُ لُجَّةٗ وَكَشَفَتۡ عَن سَاقَيۡهَاۚ قَالَ إِنَّهُۥ صَرۡحٞ مُّمَرَّدٞ مِّن قَوَارِيرَۗ قَالَتۡ رَبِّ إِنِّي ظَلَمۡتُ نَفۡسِي وَأَسۡلَمۡتُ مَعَ سُلَيۡمَٰنَ لِلَّهِ رَبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
(Mfumukazi ija) idauzidwa kuti: “Lowa mkhonde la nyumba.” Koma pamene adaliona adaliganizira kuti ndidziwe; adakweza nsalu kumiyendo yake. (Sulaiman) adati: “Ndithu limeneli ndikhonde lomwe laziridwa ndi magalasi.” (Mfumukazi) idati: “E Mbuye wanga! Ndadzichitira ndekha chinyengo; choncho, ndagonjera kwa Allah, Mbuye wazolengedwa pamodzi ndi Sulaiman.”
અરબી તફસીરો:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَآ إِلَىٰ ثَمُودَ أَخَاهُمۡ صَٰلِحًا أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ فَإِذَا هُمۡ فَرِيقَانِ يَخۡتَصِمُونَ
Ndipo ndithu Asamudu tidawatumizira m’bale wawo Swalih kuti awauze: “Mpembedzeni Allah.” Choncho adali magulu awiri omwe amakangana. (Ena adam’tsata pomwe ena adam’kana).
અરબી તફસીરો:
قَالَ يَٰقَوۡمِ لِمَ تَسۡتَعۡجِلُونَ بِٱلسَّيِّئَةِ قَبۡلَ ٱلۡحَسَنَةِۖ لَوۡلَا تَسۡتَغۡفِرُونَ ٱللَّهَ لَعَلَّكُمۡ تُرۡحَمُونَ
(Swaleh) adati: “E inu anthu anga chifukwa ninji inu mukufulumizitsa choipa (kuti chidze) musanachite chabwino? Bwanji simukupempha chikhululuko kwa Allah kuti muchitiridwe chifundo?”
અરબી તફસીરો:
قَالُواْ ٱطَّيَّرۡنَا بِكَ وَبِمَن مَّعَكَۚ قَالَ طَٰٓئِرُكُمۡ عِندَ ٱللَّهِۖ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ تُفۡتَنُونَ
(Iwo) adati: “Tapeza masoka oipa chifukwa cha iwe ndi omwe uli nawo.” (Iye) adati: “Tsoka lanu lili kwa Allah (chifukwa cha zolakwa zanu); koma inu ndinu anthu amene mukuyesedwa (ndi Allah kuti aone ngati mutsatire Mtumiki Wake kapena simutsatira).”
અરબી તફસીરો:
وَكَانَ فِي ٱلۡمَدِينَةِ تِسۡعَةُ رَهۡطٖ يُفۡسِدُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا يُصۡلِحُونَ
Ndipo m’mudzimo adalipo anthu asanu ndi anayi omwe amaononga pa dziko, ndipo samakonza (chilichonse koma kuchiononga).
અરબી તફસીરો:
قَالُواْ تَقَاسَمُواْ بِٱللَّهِ لَنُبَيِّتَنَّهُۥ وَأَهۡلَهُۥ ثُمَّ لَنَقُولَنَّ لِوَلِيِّهِۦ مَا شَهِدۡنَا مَهۡلِكَ أَهۡلِهِۦ وَإِنَّا لَصَٰدِقُونَ
(Iwo) adati: “Aliyense wa ife alumbire kwa Allah (kuti) iye (Swaleh) ndi banja lake timthira nkhondo usiku, ndipo kenako Timuuza mlowam’malo wake (kuti): “Sitidaone kuonongeka kwa m’bale wake; ndithu ife tikunena zoona.”
અરબી તફસીરો:
وَمَكَرُواْ مَكۡرٗا وَمَكَرۡنَا مَكۡرٗا وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
Ndipo adakonza chiwembu ndi kutchera misampha yamphamvu, nafenso tidawatchera misampha yowaononga, iwo asakudziwa.
અરબી તફસીરો:
فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ مَكۡرِهِمۡ أَنَّا دَمَّرۡنَٰهُمۡ وَقَوۡمَهُمۡ أَجۡمَعِينَ
Tsono tayang’ana, kodi malekezero a chiwembu chawo adali otani! Tidawaononga iwo ndi anthu awo onse.
અરબી તફસીરો:
فَتِلۡكَ بُيُوتُهُمۡ خَاوِيَةَۢ بِمَا ظَلَمُوٓاْۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ
Izo ndinyumba zawo (zomwe zasanduka) mabwinja chifukwa cha chinyengo chawo. Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa odziwa.
અરબી તફસીરો:
وَأَنجَيۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ
Ndipo tidawapulumutsa amene adakhulupirira pakuti amamuopa (Allah).
અરબી તફસીરો:
وَلُوطًا إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ أَتَأۡتُونَ ٱلۡفَٰحِشَةَ وَأَنتُمۡ تُبۡصِرُونَ
Ndipo (akumbutse nkhani ya) Luti pamene adanena kwa anthu ake: “Kodi mukuchita zadama uku inu mukuziona?”
અરબી તફસીરો:
أَئِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلرِّجَالَ شَهۡوَةٗ مِّن دُونِ ٱلنِّسَآءِۚ بَلۡ أَنتُمۡ قَوۡمٞ تَجۡهَلُونَ
“Kodi inu mukugona ndi amuna pokwaniritsa chilakolako (cha chilengedwe) kusiya akazi? koma inu ndinu mbuli.”
અરબી તફસીરો:
۞ فَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ أَخۡرِجُوٓاْ ءَالَ لُوطٖ مِّن قَرۡيَتِكُمۡۖ إِنَّهُمۡ أُنَاسٞ يَتَطَهَّرُونَ
۞ Koma anthu ake sadayankhe yankho lina koma ili (lakuti): “Apirikitseni otsatira Luti m’mudzi mwanumu; ndithu iwo ndianthu odziyeretsa (asakhale pamodzi ndi ife adama).”
અરબી તફસીરો:
فَأَنجَيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥٓ إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ قَدَّرۡنَٰهَا مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ
Choncho tidampulumutsa iye ndi otsatira kupatula mkazi wake; tidamkozera kukhala mmodzi mwa otsalira (kuti aonongedwe pamodzi ndi oonongedwa, chifukwa cha ntchito zake zoipa ngakhale kuti adali mkazi wa mneneri).
અરબી તફસીરો:
وَأَمۡطَرۡنَا عَلَيۡهِم مَّطَرٗاۖ فَسَآءَ مَطَرُ ٱلۡمُنذَرِينَ
Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji mvula ya ochenjezedwa (koma osachenjezeka)!
અરબી તફસીરો:
قُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ وَسَلَٰمٌ عَلَىٰ عِبَادِهِ ٱلَّذِينَ ٱصۡطَفَىٰٓۗ ءَآللَّهُ خَيۡرٌ أَمَّا يُشۡرِكُونَ
Nena: “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, ndipo mtendere ukhale pa akapolo Ake omwe adawasankha. Kodi wabwino ndi Allah kapena zimene akumphatikiza nazozo?”
અરબી તફસીરો:
أَمَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَأَنزَلَ لَكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَنۢبَتۡنَا بِهِۦ حَدَآئِقَ ذَاتَ بَهۡجَةٖ مَّا كَانَ لَكُمۡ أَن تُنۢبِتُواْ شَجَرَهَآۗ أَءِلَٰهٞ مَّعَ ٱللَّهِۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٞ يَعۡدِلُونَ
(E iwe Mtumiki! Pitiriza kuwafunsa) kodi kapena (wabwino) ndiamene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zam’menemo) ndi kukutsitsirani madzi (mvula yothandiza) kuchokera kumwamba, choncho ndi madziwo timameretsa madimba okongola. Inu simungathe kumeretsa mitengo yake. Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu (wina)? Koma iwo (Akafiri) ndi anthu opotoka.
અરબી તફસીરો:
أَمَّن جَعَلَ ٱلۡأَرۡضَ قَرَارٗا وَجَعَلَ خِلَٰلَهَآ أَنۡهَٰرٗا وَجَعَلَ لَهَا رَوَٰسِيَ وَجَعَلَ بَيۡنَ ٱلۡبَحۡرَيۡنِ حَاجِزًاۗ أَءِلَٰهٞ مَّعَ ٱللَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
Kodi kapena (wabwino) ndiamene adapanga nthaka kukhala malo okhazikika ndi kuika mitsinje pakati pake ndi kuipangira mapiri, ndi kuika chitsekerezo pakati pa nyanja ziwiri (nyanja ya madzi amchere, ndi yamadzi ozizira)? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Koma ambiri a iwo sadziwa.
અરબી તફસીરો:
أَمَّن يُجِيبُ ٱلۡمُضۡطَرَّ إِذَا دَعَاهُ وَيَكۡشِفُ ٱلسُّوٓءَ وَيَجۡعَلُكُمۡ خُلَفَآءَ ٱلۡأَرۡضِۗ أَءِلَٰهٞ مَّعَ ٱللَّهِۚ قَلِيلٗا مَّا تَذَكَّرُونَ
Kapena (wabwino) ndiyemwe amamuyankha wozunzika akamampempha ndi kumchotsera masautso ake ndi kukuchitani inu kukhala oyendetsa dziko lapansi? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Ndithu kulangizika kwanu nkochepa.
અરબી તફસીરો:
أَمَّن يَهۡدِيكُمۡ فِي ظُلُمَٰتِ ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ وَمَن يُرۡسِلُ ٱلرِّيَٰحَ بُشۡرَۢا بَيۡنَ يَدَيۡ رَحۡمَتِهِۦٓۗ أَءِلَٰهٞ مَّعَ ٱللَّهِۚ تَعَٰلَى ٱللَّهُ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Kapena (wabwino) ndiyemwe amakuongolerani mu mdima wa pamtunda ndi panyanja ndi kutumiza mphepo kuti ikudzetsereni nkhani yabwino patsogolo pa chifundo chake (mvula isanagwe)? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Allah watukuka ku zimene akumuphatikiza nazo.
અરબી તફસીરો:
أَمَّن يَبۡدَؤُاْ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥ وَمَن يَرۡزُقُكُم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۗ أَءِلَٰهٞ مَّعَ ٱللَّهِۚ قُلۡ هَاتُواْ بُرۡهَٰنَكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Kapena (wabwino) ndiamene adayambitsa zolengedwa, (ndipo) kenako adzazibweza, kapenanso amene amakupatsani rizq (chakudya) kuchokera kumwamba ndi m’nthaka? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu winanso? Nena: “Bweretsani umboni wanu ngati mukunena zoona (wotsimikizira kuti Allah ali ndi mnzake).”
અરબી તફસીરો:
قُل لَّا يَعۡلَمُ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ ٱلۡغَيۡبَ إِلَّا ٱللَّهُۚ وَمَا يَشۡعُرُونَ أَيَّانَ يُبۡعَثُونَ
Nena: “Palibe amene alipo kumwamba ndi pansi akudziwa zam’seri (zomwe zisanadze) kupatula Allah basi. Ndipo (amene akuwapembedza) sadziwa kuti ndiliti adzaukitsidwa ku imfa.”
અરબી તફસીરો:
بَلِ ٱدَّٰرَكَ عِلۡمُهُمۡ فِي ٱلۡأٓخِرَةِۚ بَلۡ هُمۡ فِي شَكّٖ مِّنۡهَاۖ بَلۡ هُم مِّنۡهَا عَمُونَ
Kwakhwima liti kudziwa kwawo (za kudza) kwa tsiku la chimaliziro? Koma iwo ali mchikaiko ndi za tsikulo; koma iwo ngakhungu pa zatsikulo.
અરબી તફસીરો:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا تُرَٰبٗا وَءَابَآؤُنَآ أَئِنَّا لَمُخۡرَجُونَ
Ndipo adanena omwe adatsutsa (za Allah): “Kodi tikadzakhala dothi, ife ndi makolo athu akale, (nzoona) tidzatulutsidwanso (m’manda tili amoyo)?”
અરબી તફસીરો:
لَقَدۡ وُعِدۡنَا هَٰذَا نَحۡنُ وَءَابَآؤُنَا مِن قَبۡلُ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Ndithu tidalonjezedwa izi, ife ndi makolo athu kale, izi sichina koma ndi nthano (zabodza) za anthu akale.”
અરબી તફસીરો:
قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُجۡرِمِينَ
Nena: “Yendani pa dziko ndi kuona momwe adalili mapeto a oipa.”
અરબી તફસીરો:
وَلَا تَحۡزَنۡ عَلَيۡهِمۡ وَلَا تَكُن فِي ضَيۡقٖ مِّمَّا يَمۡكُرُونَ
Ndipo usawadandaulire, ndiponso usakhale wobanika chifukwa cha ziwembu zomwe akuchita.
અરબી તફસીરો:
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Ndipo (iwo) akuti: “Kodi lonjezoli lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”
અરબી તફસીરો:
قُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ رَدِفَ لَكُم بَعۡضُ ٱلَّذِي تَسۡتَعۡجِلُونَ
Nena: “Kapena zina mwa zomwe mukuzifulumizitsa zili pafupi kukupezani.”
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّ رَبَّكَ لَذُو فَضۡلٍ عَلَى ٱلنَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَشۡكُرُونَ
Ndipo ndithu Mbuye wako ndi mwini kupereka ubwino (waukulu) kwa anthu; koma ambiri a iwo sathokoza.
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّ رَبَّكَ لَيَعۡلَمُ مَا تُكِنُّ صُدُورُهُمۡ وَمَا يُعۡلِنُونَ
Ndipo ndithu Mbuye wako akudziwa zomwe zikubisa zifuwa zawo ndi zomwe akuonetsera poyera.
અરબી તફસીરો:
وَمَا مِنۡ غَآئِبَةٖ فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ إِلَّا فِي كِتَٰبٖ مُّبِينٍ
Ndiponso palibe chobisika kumwamba ndi m’nthaka koma chili m’buku lofotokoza chilichonse.
અરબી તફસીરો:
إِنَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ يَقُصُّ عَلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ أَكۡثَرَ ٱلَّذِي هُمۡ فِيهِ يَخۡتَلِفُونَ
Ndithu Qur’an iyi, ikufotokoza kwambiri za ana a Israyeli pa zambiri zomwe iwo akutsutsana.
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّهُۥ لَهُدٗى وَرَحۡمَةٞ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo ndithu iyi (Qur’an) ndichiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
إِنَّ رَبَّكَ يَقۡضِي بَيۡنَهُم بِحُكۡمِهِۦۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo ndi chiweruzo chake (choona); ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa Ngodziwa chilichonse.
અરબી તફસીરો:
فَتَوَكَّلۡ عَلَى ٱللَّهِۖ إِنَّكَ عَلَى ٱلۡحَقِّ ٱلۡمُبِينِ
Choncho tsamira kwa Allah; ndithu iwe uli pa njira yachoonadi yoonekera.
અરબી તફસીરો:
إِنَّكَ لَا تُسۡمِعُ ٱلۡمَوۡتَىٰ وَلَا تُسۡمِعُ ٱلصُّمَّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا وَلَّوۡاْ مُدۡبِرِينَ
Ndithu iwe sungathe kuwachititsa kuti amve kuitana kwako akufa, ndiponso sungathe kuwachititsa kuti agonthi amve kuitanako, pamene akucheuka kutembenuza misana (osafuna kumva ulaliki wako).
અરબી તફસીરો:
وَمَآ أَنتَ بِهَٰدِي ٱلۡعُمۡيِ عَن ضَلَٰلَتِهِمۡۖ إِن تُسۡمِعُ إِلَّا مَن يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُم مُّسۡلِمُونَ
Ndiponso suli owaongola akhungu m’kusokera kwawo, ndipo sungachititse kuti amve (uthenga wako) kupatula yemwe akukhulupirira Ayah (ndime) Zathu; iwowo ndiwo Asilamu (ogonjera malamulo Athu).
અરબી તફસીરો:
۞ وَإِذَا وَقَعَ ٱلۡقَوۡلُ عَلَيۡهِمۡ أَخۡرَجۡنَا لَهُمۡ دَآبَّةٗ مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ تُكَلِّمُهُمۡ أَنَّ ٱلنَّاسَ كَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا لَا يُوقِنُونَ
Ndipo mawu (onena kudza kwa Qiyâma) akadzatsimikizika pa iwo, tidzawatulutsira chinyama m’nthaka chimene chidzawayankhula kuti ndithu anthu adalibe chitsimikizo pa Ayah (ndime) Zathu.
અરબી તફસીરો:
وَيَوۡمَ نَحۡشُرُ مِن كُلِّ أُمَّةٖ فَوۡجٗا مِّمَّن يُكَذِّبُ بِـَٔايَٰتِنَا فَهُمۡ يُوزَعُونَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku lormwe tidzasonkhanitsa magulumagulu mu m’badwo uliwonse omwe amatsutsa Ayah (ndime) Zathu. Ndipo iwo adzakhala magulumagulu.
અરબી તફસીરો:
حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُو قَالَ أَكَذَّبۡتُم بِـَٔايَٰتِي وَلَمۡ تُحِيطُواْ بِهَا عِلۡمًا أَمَّاذَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Kufikira pomwe adzaza; (Allah) adzati: “Kodi inu mudazitsutsa Ayah (ndime) Zanga popanda kuzidziwa bwinobwino, nanga mumachita chiyani?”
અરબી તફસીરો:
وَوَقَعَ ٱلۡقَوۡلُ عَلَيۡهِم بِمَا ظَلَمُواْ فَهُمۡ لَا يَنطِقُونَ
Ndipo mawu onena za kuonongeka adzatsimikizika pa iwo, chifukwa cha chinyengo chawo (chodzichitira okha) ndipo iwo sadzawiringula.
અરબી તફસીરો:
أَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا جَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ لِيَسۡكُنُواْ فِيهِ وَٱلنَّهَارَ مُبۡصِرًاۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Kodi saona kuti Ife tapanga usiku ndi cholinga chakuti apumule m’menemo, ndinso usana woyera (kuti aone)? Ndithu mu zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
وَيَوۡمَ يُنفَخُ فِي ٱلصُّورِ فَفَزِعَ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ إِلَّا مَن شَآءَ ٱللَّهُۚ وَكُلٌّ أَتَوۡهُ دَٰخِرِينَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku limene lipenga (la chiweruziro) lidzaimbidwa, adzadzidzimuka amene ali kumwamba ndi amene ali pansi kupatula yemwe Allah wamfuna (kuti adzadzidzimuke); ndipo onse adzamdzera (Allah) ali odzichepetsa (ofooka).
અરબી તફસીરો:
وَتَرَى ٱلۡجِبَالَ تَحۡسَبُهَا جَامِدَةٗ وَهِيَ تَمُرُّ مَرَّ ٱلسَّحَابِۚ صُنۡعَ ٱللَّهِ ٱلَّذِيٓ أَتۡقَنَ كُلَّ شَيۡءٍۚ إِنَّهُۥ خَبِيرُۢ بِمَا تَفۡعَلُونَ
Ndipo udzawaona mapiri ndi kuwaganizira kuti akhazikika pomwe akuyenda kuyenda kwa mitambo. Chimenecho ndichikonzero cha Allah chimene adakonzera chinthu chilichonse. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene muchita.
અરબી તફસીરો:
مَن جَآءَ بِٱلۡحَسَنَةِ فَلَهُۥ خَيۡرٞ مِّنۡهَا وَهُم مِّن فَزَعٖ يَوۡمَئِذٍ ءَامِنُونَ
Amene adzadza ndi chabwino, adzalandira mphoto yoposa chabwinocho; ndikuopsa kwa tsiku limenelo, iwo adzakhala nako mwamtendere.
અરબી તફસીરો:
وَمَن جَآءَ بِٱلسَّيِّئَةِ فَكُبَّتۡ وُجُوهُهُمۡ فِي ٱلنَّارِ هَلۡ تُجۡزَوۡنَ إِلَّا مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Koma amene adzadza ndi choipa, adzaponyedwa ku Moto champhumi (ndipo kudzanenedwa kwa iwo): “Kodi mungalipidwe (zina) osati zomwe mumachita?”
અરબી તફસીરો:
إِنَّمَآ أُمِرۡتُ أَنۡ أَعۡبُدَ رَبَّ هَٰذِهِ ٱلۡبَلۡدَةِ ٱلَّذِي حَرَّمَهَا وَلَهُۥ كُلُّ شَيۡءٖۖ وَأُمِرۡتُ أَنۡ أَكُونَ مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu ndalamulidwa kumpembedza Mbuye wa mzinda uwu, Yemwe adaukhazika wopatulika. Ndipo zinthu zonse nza Iye (Allah), ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa ogonjera (Allah).”
અરબી તફસીરો:
وَأَنۡ أَتۡلُوَاْ ٱلۡقُرۡءَانَۖ فَمَنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَقُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُنذِرِينَ
“Ndiponso (ndalamulidwa) kuti ndiwerenge Qur’an.” Ndipo amene waongoka, ubwino wa kuongokako uli pa iye; ndipo amene wasokera, (wadzisokeretsa yekha). Nena: “Ndithu ine sikanthu koma ndine mmodzi wa achenjezi. (Ndilibe udindo wina woposa uwu).”
અરબી તફસીરો:
وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ سَيُرِيكُمۡ ءَايَٰتِهِۦ فَتَعۡرِفُونَهَاۚ وَمَا رَبُّكَ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ
Ndipo nena: “Kuyamikidwa konse (kwabwino) nkwa Allah; posachedwapa akusonyezani zizindikiro Zake, ndipo muzizindikira.” Ndipo Mbuye wako sali woiwala zimene mukuchita.
અરબી તફસીરો:
 
શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અન્ નમલ
સૂરહ માટે અનુક્રમણિકા પેજ નંબર
 
કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા

ચેવા ભાષાતરમાં

બંધ કરો