કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર * - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા


શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અઝ્ ઝારિયાત   આયત:

અઝ્ ઝારિયાત

وَٱلذَّٰرِيَٰتِ ذَرۡوٗا
. Ndikulumbilira mphepo imene ikubalalitsa mitambo ya mvula.
અરબી તફસીરો:
فَٱلۡحَٰمِلَٰتِ وِقۡرٗا
Ndi imene imasenza mitolo yolemera (ya madzi).
અરબી તફસીરો:
فَٱلۡجَٰرِيَٰتِ يُسۡرٗا
Ndi kuyenda (nawo madziwo) mwaubwino.
અરબી તફસીરો:
فَٱلۡمُقَسِّمَٰتِ أَمۡرًا
Ndi awo amene amagawa rizq (limene Allah amalipereka kwa amene wamfuna).
અરબી તફસીરો:
إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَصَادِقٞ
Ndithu zimene mukulonjezedwa nzoonadi, (zidzachitika).
અરબી તફસીરો:
وَإِنَّ ٱلدِّينَ لَوَٰقِعٞ
Ndipo, ndithu malipiro (pa zochita zanu) adzapezekadi.
અરબી તફસીરો:
وَٱلسَّمَآءِ ذَاتِ ٱلۡحُبُكِ
Ndikulumbilira thambo lomwe njira zake zambiri nzoikidwa mwaluso.
અરબી તફસીરો:
إِنَّكُمۡ لَفِي قَوۡلٖ مُّخۡتَلِفٖ
Ndithu inu muli m’mau otsutsana, (pa zimene mukunena).
અરબી તફસીરો:
يُؤۡفَكُ عَنۡهُ مَنۡ أُفِكَ
(Kupyolera m’mawu amenewa) akuchotsedwa ku icho (chikhulupiliro chalonjezo loona) amene adachotsedwa (ku chikhulupilirocho).
અરબી તફસીરો:
قُتِلَ ٱلۡخَرَّٰصُونَ
Aonongeka abodza (amene akunena za tsiku lachiweruziro mongoganizira.)
અરબી તફસીરો:
ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي غَمۡرَةٖ سَاهُونَ
Iwo amene akubira mu umbuli, osalabadira (za tsiku lachimaliziro).
અરબી તફસીરો:
يَسۡـَٔلُونَ أَيَّانَ يَوۡمُ ٱلدِّينِ
Akufunsa (mwachipongwe ponena kuti) “Lidzakhala liti tsiku lamalipiro?”
અરબી તફસીરો:
يَوۡمَ هُمۡ عَلَى ٱلنَّارِ يُفۡتَنُونَ
(Limenelo ndi) tsiku lomwe iwo adzalangidwa ku Moto.
અરબી તફસીરો:
ذُوقُواْ فِتۡنَتَكُمۡ هَٰذَا ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تَسۡتَعۡجِلُونَ
(Adzawauza kuti): “Lawani chilango chanu ichi chimene munkachifulumizitsa (kuti chikufikeni).”
અરબી તફસીરો:
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٖ وَعُيُونٍ
Ndithu oopa (Allah) adzakhala (akusangalala) m’minda ndi mu akasupe okongola,
અરબી તફસીરો:
ءَاخِذِينَ مَآ ءَاتَىٰهُمۡ رَبُّهُمۡۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَبۡلَ ذَٰلِكَ مُحۡسِنِينَ
Uku akulandira zimene wawapatsa Mbuye wawo (malipiro aulemu); ndithu iwo ankachita zabwino asanapeze izi.
અરબી તફસીરો:
كَانُواْ قَلِيلٗا مِّنَ ٱلَّيۡلِ مَا يَهۡجَعُونَ
Nthawi yausiku amagona pang’ono. (Amadzuka nachita mapemphero mochulukitsa).
અરબી તફસીરો:
وَبِٱلۡأَسۡحَارِ هُمۡ يَسۡتَغۡفِرُونَ
Ndipo kum’bandakucha, iwo amapempha chikhululuko,
અરબી તફસીરો:
وَفِيٓ أَمۡوَٰلِهِمۡ حَقّٞ لِّلسَّآئِلِ وَٱلۡمَحۡرُومِ
Ndipo m’chuma chawo mudali gawo (lodziwika) la opempha ndi osapempha (mwa osauka).
અરબી તફસીરો:
وَفِي ٱلۡأَرۡضِ ءَايَٰتٞ لِّلۡمُوقِنِينَ
M’nthaka muli zizindikiro kwa otsimikiza, (zosonyeza kuti Allah alipo).
અરબી તફસીરો:
وَفِيٓ أَنفُسِكُمۡۚ أَفَلَا تُبۡصِرُونَ
Ndi mwa inu nomwe; kodi simuona?
અરબી તફસીરો:
وَفِي ٱلسَّمَآءِ رِزۡقُكُمۡ وَمَا تُوعَدُونَ
Ndipo kumwamba kuli zokuthandizani (pa moyo wanu), ndi zimene mukulonjezedwa.
અરબી તફસીરો:
فَوَرَبِّ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ إِنَّهُۥ لَحَقّٞ مِّثۡلَ مَآ أَنَّكُمۡ تَنطِقُونَ
Ndikulumbilira Mbuye wa kumwamba ndi pansi, ndithu zimenezo ndi zoona monga kulili kuyankhula kwanu.
અરબી તફસીરો:
هَلۡ أَتَىٰكَ حَدِيثُ ضَيۡفِ إِبۡرَٰهِيمَ ٱلۡمُكۡرَمِينَ
Kodi yakufika nkhani ya alendo a Ibrahim; (angelo) olemekezeka?
અરબી તફસીરો:
إِذۡ دَخَلُواْ عَلَيۡهِ فَقَالُواْ سَلَٰمٗاۖ قَالَ سَلَٰمٞ قَوۡمٞ مُّنكَرُونَ
Pamene adalowa kwa iye ndi kunena kuti: “Salaam,” (“Mtendere”)! Iye adayankha: “Salaam,” (“Mtendere) inu ndinu anthu osadziwika (achilendo).”
અરબી તફસીરો:
فَرَاغَ إِلَىٰٓ أَهۡلِهِۦ فَجَآءَ بِعِجۡلٖ سَمِينٖ
Adatembenukira kwa akunyumba ake (mwakachetechete), ndipo adadza ndi nyama ya mwana wa ng’ombe yonona (yowotcha).
અરબી તફસીરો:
فَقَرَّبَهُۥٓ إِلَيۡهِمۡ قَالَ أَلَا تَأۡكُلُونَ
Naipereka kwa iwo (koma sadadye); iye adanena (modabwa): “Kodi bwanji simukudya?”
અરબી તફસીરો:
فَأَوۡجَسَ مِنۡهُمۡ خِيفَةٗۖ قَالُواْ لَا تَخَفۡۖ وَبَشَّرُوهُ بِغُلَٰمٍ عَلِيمٖ
Mumtima mwake adadzazidwa mantha ndi iwo. Iwo adati: “Usaope,” ndipo adamuuza nkhani yabwino ya kubala mwana wodziwa.
અરબી તફસીરો:
فَأَقۡبَلَتِ ٱمۡرَأَتُهُۥ فِي صَرَّةٖ فَصَكَّتۡ وَجۡهَهَا وَقَالَتۡ عَجُوزٌ عَقِيمٞ
Adadza mkazi wake ndi mkuwe (pamene adamva nkhani yabwino ija). Adadzimenya kunkhope (ndi dzanja lake kusonyeza kudabwa ndi kusatheka). Ndipo adati: (“Ine ndine) nkhalamba (ndiponso) chumba; (ndingabereke bwanji)?”
અરબી તફસીરો:
قَالُواْ كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡحَكِيمُ ٱلۡعَلِيمُ
Iwo adati: “Momwemo, Mbuye wako wanena. Iye Ngwanzeru zakuya (pa chilichonse chimene akulamula); Ngodziwa; (palibe chimene chingabisike kwa Iye).
અરબી તફસીરો:
۞ قَالَ فَمَا خَطۡبُكُمۡ أَيُّهَا ٱلۡمُرۡسَلُونَ
۞ (Ibrahim) adati: “Kodi nkhani yanu ndiyotani E inu otumidwa?”
અરબી તફસીરો:
قَالُوٓاْ إِنَّآ أُرۡسِلۡنَآ إِلَىٰ قَوۡمٖ مُّجۡرِمِينَ
Iwo adati: “Tatumizidwa kwa anthu oipa.”
અરબી તફસીરો:
لِنُرۡسِلَ عَلَيۡهِمۡ حِجَارَةٗ مِّن طِينٖ
“Kuti tiwagende ndi miyala yotenthedwa kuchokera kudongo.”
અરબી તફસીરો:
مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَ لِلۡمُسۡرِفِينَ
“Yoikidwa chizindikiro cha aliyense wochimwa kuchokera kwa Mbuye wako.”
અરબી તફસીરો:
فَأَخۡرَجۡنَا مَن كَانَ فِيهَا مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Tidawatulutsa okhulupirira omwe adali m’mudzimo.
અરબી તફસીરો:
فَمَا وَجَدۡنَا فِيهَا غَيۡرَ بَيۡتٖ مِّنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
Sitidapeze mmenemo (okhulupirira ambiri) kupatula mnyumba imodzi ya Asilamu.
અરબી તફસીરો:
وَتَرَكۡنَا فِيهَآ ءَايَةٗ لِّلَّذِينَ يَخَافُونَ ٱلۡعَذَابَ ٱلۡأَلِيمَ
Ndipo tidasiya pamenepo chizindikiro (chosonyeza kuonongeka kwa eni mudziwo kuti chikhale lingaliro) kwa amene akuopa chilango chopweteka.
અરબી તફસીરો:
وَفِي مُوسَىٰٓ إِذۡ أَرۡسَلۡنَٰهُ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ بِسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٖ
M’nkhani ya Mûsa (muli phunziro) pamene tidamtuma kwa Farawo uku atalimbikitsidwa ndi chisonyezo choonekera.
અરબી તફસીરો:
فَتَوَلَّىٰ بِرُكۡنِهِۦ وَقَالَ سَٰحِرٌ أَوۡ مَجۡنُونٞ
Koma Farawo adanyoza (kukhulupirira Mûsa) chifukwa chotama nyonga zake, ndipo adati: “Uyu ndi wamatsenga kapena wamisala.”
અરબી તફસીરો:
فَأَخَذۡنَٰهُ وَجُنُودَهُۥ فَنَبَذۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡيَمِّ وَهُوَ مُلِيمٞ
Tidamlanga pamodzi ndi khamu lake la nkhondo ndi kuwaponya mnyanja; iye ali wodzudzulidwa.
અરબી તફસીરો:
وَفِي عَادٍ إِذۡ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلرِّيحَ ٱلۡعَقِيمَ
Ndipo m’nkhani ya Âdi (muli phunziro) pamene tidawatumizira chimphepo (chamkuntho) chopanda chabwino mkati mwake.
અરબી તફસીરો:
مَا تَذَرُ مِن شَيۡءٍ أَتَتۡ عَلَيۡهِ إِلَّا جَعَلَتۡهُ كَٱلرَّمِيمِ
Chomwe sichisiya chinthu chimene chachidutsa koma kuchichita monga chofumbwa.
અરબી તફસીરો:
وَفِي ثَمُودَ إِذۡ قِيلَ لَهُمۡ تَمَتَّعُواْ حَتَّىٰ حِينٖ
Ndipo m’nkhani ya Samudu (muli chisonyezo) pamene kudanenedwa kwa iwo kuti: “Sangalalani (mnyumba zanu) mpaka nthawi yaikika.”
અરબી તફસીરો:
فَعَتَوۡاْ عَنۡ أَمۡرِ رَبِّهِمۡ فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّٰعِقَةُ وَهُمۡ يَنظُرُونَ
Koma adadzikweza (ponyozera) lamulo la Mbuye wawo. Choncho chiphokoso chidawaononga uku akupenya.
અરબી તફસીરો:
فَمَا ٱسۡتَطَٰعُواْ مِن قِيَامٖ وَمَا كَانُواْ مُنتَصِرِينَ
Sadathe kuimilira ndi (kuthawa) ndiponso sadali wodzipulumutsa.
અરબી તફસીરો:
وَقَوۡمَ نُوحٖ مِّن قَبۡلُۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمٗا فَٰسِقِينَ
Naonso anthu a Nuh (tidawaononga) kale chifukwa iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah).
અરબી તફસીરો:
وَٱلسَّمَآءَ بَنَيۡنَٰهَا بِأَيۡيْدٖ وَإِنَّا لَمُوسِعُونَ
Thambo tidalimanga mwamphamvu (ndi luntha); ndipo tingathe kuchita zochuluka (kuposa zimenezi.)
અરબી તફસીરો:
وَٱلۡأَرۡضَ فَرَشۡنَٰهَا فَنِعۡمَ ٱلۡمَٰهِدُونَ
Ndipo nthaka tidaiyala; taonani kukonza bwino Ife amene tidakonza nthaka!
અરબી તફસીરો:
وَمِن كُلِّ شَيۡءٍ خَلَقۡنَا زَوۡجَيۡنِ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ
Ndipo m’chinthu chilichonse talenga ziwiriziwiri kuti inu mulingalire (ndi kukhulupirira mphamvu Zathu).
અરબી તફસીરો:
فَفِرُّوٓاْ إِلَى ٱللَّهِۖ إِنِّي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٞ مُّبِينٞ
Thawirani kwa Allah. Ine ndine mchenjezi woonekera kwa inu wochokera kwa Iye.
અરબી તફસીરો:
وَلَا تَجۡعَلُواْ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَۖ إِنِّي لَكُم مِّنۡهُ نَذِيرٞ مُّبِينٞ
Ndipo musadzipangire mulungu wina wompembedza ndi kumuphatikiza ndi Allah. Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera poyera kwa inu wochokera kwa Iye.
અરબી તફસીરો:
كَذَٰلِكَ مَآ أَتَى ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا قَالُواْ سَاحِرٌ أَوۡ مَجۡنُونٌ
Momwemo (ndimo idalili mibadwo yakale pamodzi ndi aneneri awo); palibe Mthenga amene adawadzera anthu akale, anthu akowa kulibe, popanda kumnena kuti: “Ndiwamatsenga kapena wamisala.”
અરબી તફસીરો:
أَتَوَاصَوۡاْ بِهِۦۚ بَلۡ هُمۡ قَوۡمٞ طَاغُونَ
Kodi adalangizana za mawuwa pakati pawo? Iyayi, koma iwo ndianthu opyola malire.
અરબી તફસીરો:
فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡ فَمَآ أَنتَ بِمَلُومٖ
Choncho apatukire iwo (amakani), iwe suli wodzudzulidwa (pakuleka kwawo kuyankha kuitana).
અરબી તફસીરો:
وَذَكِّرۡ فَإِنَّ ٱلذِّكۡرَىٰ تَنفَعُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Kumbutsa. Ndithu kukumbutsa kumawathandiza okhulupirira.
અરબી તફસીરો:
وَمَا خَلَقۡتُ ٱلۡجِنَّ وَٱلۡإِنسَ إِلَّا لِيَعۡبُدُونِ
Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza.
અરબી તફસીરો:
مَآ أُرِيدُ مِنۡهُم مِّن رِّزۡقٖ وَمَآ أُرِيدُ أَن يُطۡعِمُونِ
Sindifuna kwa iwo chithandizo ndiponso sindifuna kuti azindidyetsa.
અરબી તફસીરો:
إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلرَّزَّاقُ ذُو ٱلۡقُوَّةِ ٱلۡمَتِينُ
Ndithu Allah ndi Amene amapereka rizq; Iye ndi Mwini mphamvu zoposa; Wolimba, (salaphera kanthu).
અરબી તફસીરો:
فَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُواْ ذَنُوبٗا مِّثۡلَ ذَنُوبِ أَصۡحَٰبِهِمۡ فَلَا يَسۡتَعۡجِلُونِ
Ndithu amene adzichitira okha chinyengo (pokana ndi kutsutsa) ali nalo gawo la chilango monga gawo la anzawo (a mibadwo yakale); choncho asandifulumizitse (kutsitsa chilango nthawi yake isanafike)!
અરબી તફસીરો:
فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن يَوۡمِهِمُ ٱلَّذِي يُوعَدُونَ
Kuonongeka kuli pa amene atsutsa za tsiku lawo limene alonjezedwa.
અરબી તફસીરો:
 
શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અઝ્ ઝારિયાત
સૂરહ માટે અનુક્રમણિકા પેજ નંબર
 
કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચેવા ભાષાતર - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા

ચેવા ભાષાતરમાં

બંધ કરો