Check out the new design

કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચિચેવા ભાષામાં અનુવાદ - ખાલિદ ઇબ્રાહિમ બૈતાલા * - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા


શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અલ્ અઅરાફ   આયત:
وَلَقَدۡ ذَرَأۡنَا لِجَهَنَّمَ كَثِيرٗا مِّنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِۖ لَهُمۡ قُلُوبٞ لَّا يَفۡقَهُونَ بِهَا وَلَهُمۡ أَعۡيُنٞ لَّا يُبۡصِرُونَ بِهَا وَلَهُمۡ ءَاذَانٞ لَّا يَسۡمَعُونَ بِهَآۚ أُوْلَٰٓئِكَ كَٱلۡأَنۡعَٰمِ بَلۡ هُمۡ أَضَلُّۚ أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡغَٰفِلُونَ
Ndithudi, ziwanda zambiri ndi anthu tidawalengera kukalowa ku (Moto wa) Jahannam. Mitima ali nayo koma sazindikira nayo kanthu; ndipo maso ali nawo koma sapenyera nawo (zodabwitsa za Allah); ndipo makutu ali nawo koma samvera nawo (zowapindulitsa). Iwo ali ngati ziweto, kapena iwo ndi osokera zedi kuposa Ziweto. Iwo ndi osalabadira.
અરબી તફસીરો:
وَلِلَّهِ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰ فَٱدۡعُوهُ بِهَاۖ وَذَرُواْ ٱلَّذِينَ يُلۡحِدُونَ فِيٓ أَسۡمَٰٓئِهِۦۚ سَيُجۡزَوۡنَ مَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndipo Allah ali nawo maina abwino. Choncho, muitaneni ndi mainawo. Alekeni amene akupotoza maina Ake posachedwapa alipidwa zomwe akhala akuchita.
અરબી તફસીરો:
وَمِمَّنۡ خَلَقۡنَآ أُمَّةٞ يَهۡدُونَ بِٱلۡحَقِّ وَبِهِۦ يَعۡدِلُونَ
Ndipo mwa amene tidawalenga, alipo anthu oongolera (anzawo) ku choonadi. Ndipo kupyolera mchoonadicho akuchita chilungamo.
અરબી તફસીરો:
وَٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا سَنَسۡتَدۡرِجُهُم مِّنۡ حَيۡثُ لَا يَعۡلَمُونَ
Ndipo amene atsutsa zivumbulutso zathu, tiwalekelera pang’onopang’ono, kenako nkuwakhaulitsa kuchokera momwe iwo sakudziwa.
અરબી તફસીરો:
وَأُمۡلِي لَهُمۡۚ إِنَّ كَيۡدِي مَتِينٌ
Ndipo ndiwapatsa kanthawi. Ndithu kukhaulitsa kwanga nkokhwima.
અરબી તફસીરો:
أَوَلَمۡ يَتَفَكَّرُواْۗ مَا بِصَاحِبِهِم مِّن جِنَّةٍۚ إِنۡ هُوَ إِلَّا نَذِيرٞ مُّبِينٌ
Kodi sadalingalire kuti munthu wawoyo (mneneri Muhammad {s.a.w}) alibe misala? Iye sali koma mchenjezi woonekera poyera.
અરબી તફસીરો:
أَوَلَمۡ يَنظُرُواْ فِي مَلَكُوتِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا خَلَقَ ٱللَّهُ مِن شَيۡءٖ وَأَنۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ قَدِ ٱقۡتَرَبَ أَجَلُهُمۡۖ فَبِأَيِّ حَدِيثِۭ بَعۡدَهُۥ يُؤۡمِنُونَ
Kodi saona ufumu wa kumwamba ndi pansi, ndi zinthu zomwe Allah adalenga? Mwina mwake nthawi yawo yofera yayandikira. (Nanga adzalingalira liti zolengedwa za Allah)? Kodi ndi nkhani iti pambuyo pa iyi (Qur’an) imene adzaikhulupirira?
અરબી તફસીરો:
مَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَلَا هَادِيَ لَهُۥۚ وَيَذَرُهُمۡ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ
Amene Allah wamulekelera kusokera, alibe muongoli. Ndipo Allah akuwasiya akuyumbayumba m’kusokera kwawo.
અરબી તફસીરો:
يَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلسَّاعَةِ أَيَّانَ مُرۡسَىٰهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ رَبِّيۖ لَا يُجَلِّيهَا لِوَقۡتِهَآ إِلَّا هُوَۚ ثَقُلَتۡ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ لَا تَأۡتِيكُمۡ إِلَّا بَغۡتَةٗۗ يَسۡـَٔلُونَكَ كَأَنَّكَ حَفِيٌّ عَنۡهَاۖ قُلۡ إِنَّمَا عِلۡمُهَا عِندَ ٱللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَ ٱلنَّاسِ لَا يَعۡلَمُونَ
Akukufunsa za nthawi (ya Qiyâma) kuti idzakhalako liti? Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Mbuye wanga. palibe amene angaionetse poyera nthawi yake koma Iye. Nkovuta kwambiri kumwamba ndi pansi (kuizindikira nthawi yake). Siidzakudzerani koma mwadzidzidzi.” Akukufunsa ngati kuti iwe ukudziwa bwino za nthawiyo. Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Allah. Koma anthu ambiri sadziwa.”
અરબી તફસીરો:
 
શબ્દોનું ભાષાંતર સૂરહ: અલ્ અઅરાફ
સૂરહ માટે અનુક્રમણિકા પેજ નંબર
 
કુરઆન મજીદના શબ્દોનું ભાષાંતર - ચિચેવા ભાષામાં અનુવાદ - ખાલિદ ઇબ્રાહિમ બૈતાલા - ભાષાંતરોની અનુક્રમણિકા

તેનું અનુવાદ ખાલીદ ઈબ્રાહીમ બૈતાલા દ્વારા કરવામાં આવ્યું.

બંધ કરો