Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fasaara da Yaren Pashto * - Teburin Bayani kan wasu Fassarori


Fassarar Ma'anoni Sura: Suratu Saad   Aya:

Suratu Saad

صٓۚ وَٱلۡقُرۡءَانِ ذِي ٱلذِّكۡرِ
Sad, ndikulumbira Qur’an (iyi) ya ulaliki (wothandiza).
Tafsiran larabci:
بَلِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي عِزَّةٖ وَشِقَاقٖ
Koma amene sadakhulupirire ali mkudzitukumula ndi makani.
Tafsiran larabci:
كَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِن قَبۡلِهِم مِّن قَرۡنٖ فَنَادَواْ وَّلَاتَ حِينَ مَنَاصٖ
Kodi ndimibadwo ingati taiwononga patsogolo pawo? Adakuwa kuitana (panthawi imeneyo), koma nthawi yopulumuka idali itatha.
Tafsiran larabci:
وَعَجِبُوٓاْ أَن جَآءَهُم مُّنذِرٞ مِّنۡهُمۡۖ وَقَالَ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا سَٰحِرٞ كَذَّابٌ
Ndipo anadabwa atawadzera mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adati: “Uyu ndiwamatsenga; ngwabodza lamkunkhuniza!”
Tafsiran larabci:
أَجَعَلَ ٱلۡأٓلِهَةَ إِلَٰهٗا وَٰحِدًاۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٌ عُجَابٞ
Ha! Waichita milungu yambirimbiri ija kuti ikhale Mulungu Mmodzi Yekha? Ndithu ichi nchinthu chodabwitsa.”
Tafsiran larabci:
وَٱنطَلَقَ ٱلۡمَلَأُ مِنۡهُمۡ أَنِ ٱمۡشُواْ وَٱصۡبِرُواْ عَلَىٰٓ ءَالِهَتِكُمۡۖ إِنَّ هَٰذَا لَشَيۡءٞ يُرَادُ
Ndipo adanyamuka akuluakulu a mwa iwo nati: “Nyamukani muzikapitiriza kupembedza milungu yanu. Ndithu chinthu ichi (nchoipa); chikulinga ife (kuti tisiyane ndi milungu yathu).”
Tafsiran larabci:
مَا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِي ٱلۡمِلَّةِ ٱلۡأٓخِرَةِ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا ٱخۡتِلَٰقٌ
“Sitidamve zimenezi (zakuti Mulungu Ndimmodzi ngakhale) m’chipembedzo chakale (Chikhrisitu). Ichi sikanthu, koma ndibodza lopeka.”
Tafsiran larabci:
أَءُنزِلَ عَلَيۡهِ ٱلذِّكۡرُ مِنۢ بَيۡنِنَاۚ بَلۡ هُمۡ فِي شَكّٖ مِّن ذِكۡرِيۚ بَل لَّمَّا يَذُوقُواْ عَذَابِ
“Kodi uthengawo (wakuti Mulungu Ndimmodzi) wavumbulutsidwa kwa iye pakati pathu?” Koma iwo akukaika ndi ulaliki Wanga. Koma sadalawebe chilango Changa.
Tafsiran larabci:
أَمۡ عِندَهُمۡ خَزَآئِنُ رَحۡمَةِ رَبِّكَ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡوَهَّابِ
Kodi iwo ali nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wako, Wamphamvu zoposa, Wopatsa mochuluka?
Tafsiran larabci:
أَمۡ لَهُم مُّلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَاۖ فَلۡيَرۡتَقُواْ فِي ٱلۡأَسۡبَٰبِ
Kapena ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake, ngwawo. Ngati zili choncho atakwera makwelero (kuti akafike pamalo poti akalamulire zimene akufuna, ngati angathe kutero).
Tafsiran larabci:
جُندٞ مَّا هُنَالِكَ مَهۡزُومٞ مِّنَ ٱلۡأَحۡزَابِ
Awa (Aquraish kuonjezera pa kudzitama kwawo), nkagulu kochepa ndi kofooka. Kagonjetsedwa monga makamu ankhondo (omwe adagonjetsedwa kale omwe amatsutsana ndi aneneri akale).
Tafsiran larabci:
كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ وَعَادٞ وَفِرۡعَوۡنُ ذُو ٱلۡأَوۡتَادِ
Patsogolo pawo, anthu a Nuh, Âdi ndi Farawo, mwini nyumba zitalizitali (Pyramid), adatsutsa (aneneri awo).
Tafsiran larabci:
وَثَمُودُ وَقَوۡمُ لُوطٖ وَأَصۡحَٰبُ لۡـَٔيۡكَةِۚ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلۡأَحۡزَابُ
Ndi Asamudu, ndi anthu a Luti ndi (anthu a Shuaib) eni mitengo yambiri yothothana, amenewo ndiwo makamu.
Tafsiran larabci:
إِن كُلٌّ إِلَّا كَذَّبَ ٱلرُّسُلَ فَحَقَّ عِقَابِ
Onsewa adatsutsa atumiki; basi chilango Changa chidatsimikizika (pa iwo).
Tafsiran larabci:
وَمَا يَنظُرُ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ مَّا لَهَا مِن فَوَاقٖ
Ndipo awa (Aquraish), sayembekeza china koma mkuwe umodzi wosabwereza. (Ndipo ukadzachitika, onse adzafa).
Tafsiran larabci:
وَقَالُواْ رَبَّنَا عَجِّل لَّنَا قِطَّنَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ
Ndipo akunena (mwachipongwe): “E Mbuye wathu! Tipatsirenitu gawo la chilango chathu lisanafike tsiku lachiwerengero.”
Tafsiran larabci:
ٱصۡبِرۡ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَٱذۡكُرۡ عَبۡدَنَا دَاوُۥدَ ذَا ٱلۡأَيۡدِۖ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ
Pirira (iwe Mtumiki) ku zimene akunena (kwa iwe), ndipo kumbuka kapolo wathu Daud, wamphamvu (pa chipembedzo ndi za m’dziko lapansi). Ndithu iye ngotembenukira kwa Allah kwambiri.
Tafsiran larabci:
إِنَّا سَخَّرۡنَا ٱلۡجِبَالَ مَعَهُۥ يُسَبِّحۡنَ بِٱلۡعَشِيِّ وَٱلۡإِشۡرَاقِ
Ndithu Ife tidawagonjetsa mapiri kuti pamodzi ndi iye alemekeze (Allah) mmawa ndi madzulo.
Tafsiran larabci:
وَٱلطَّيۡرَ مَحۡشُورَةٗۖ كُلّٞ لَّهُۥٓ أَوَّابٞ
Ndi mbalame zomwe zidasonkhanitsidwa zonse zimamvera iye.
Tafsiran larabci:
وَشَدَدۡنَا مُلۡكَهُۥ وَءَاتَيۡنَٰهُ ٱلۡحِكۡمَةَ وَفَصۡلَ ٱلۡخِطَابِ
Ndipo tidaulimbikitsa ufumu wake ndi kumpatsa uneneri ndi kuyankhula kwa luntha (kosiyanitsira choona ndi chonama).
Tafsiran larabci:
۞ وَهَلۡ أَتَىٰكَ نَبَؤُاْ ٱلۡخَصۡمِ إِذۡ تَسَوَّرُواْ ٱلۡمِحۡرَابَ
Kodi yakufika nkhani ya okangana pamene adakwera chipupa mpaka kuchipinda (cha Daud chochitira mapemphero)?
Tafsiran larabci:
إِذۡ دَخَلُواْ عَلَىٰ دَاوُۥدَ فَفَزِعَ مِنۡهُمۡۖ قَالُواْ لَا تَخَفۡۖ خَصۡمَانِ بَغَىٰ بَعۡضُنَا عَلَىٰ بَعۡضٖ فَٱحۡكُم بَيۡنَنَا بِٱلۡحَقِّ وَلَا تُشۡطِطۡ وَٱهۡدِنَآ إِلَىٰ سَوَآءِ ٱلصِّرَٰطِ
Pamene adamulowera Daud, adachita nawo mantha adati: “Usaope; (ife) ndife okangana awiri, mmodzi wathu wamchenjelera wina. Weruza pakati pathu mwachilungamo, usakondere, ndipo tisonyeze njira yoongoka.”
Tafsiran larabci:
إِنَّ هَٰذَآ أَخِي لَهُۥ تِسۡعٞ وَتِسۡعُونَ نَعۡجَةٗ وَلِيَ نَعۡجَةٞ وَٰحِدَةٞ فَقَالَ أَكۡفِلۡنِيهَا وَعَزَّنِي فِي ٱلۡخِطَابِ
“Ndithu uyu m’bale wanga ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi (99), pomwe ine ndili ndi imodzi.” Ndipo akuti: “Ndipatse nkhosa imodziyo kuti ndizikusungira.” Ndipo wandiposa pakuyankhula.
Tafsiran larabci:
قَالَ لَقَدۡ ظَلَمَكَ بِسُؤَالِ نَعۡجَتِكَ إِلَىٰ نِعَاجِهِۦۖ وَإِنَّ كَثِيرٗا مِّنَ ٱلۡخُلَطَآءِ لَيَبۡغِي بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٍ إِلَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَقَلِيلٞ مَّا هُمۡۗ وَظَنَّ دَاوُۥدُ أَنَّمَا فَتَنَّٰهُ فَٱسۡتَغۡفَرَ رَبَّهُۥ وَخَرَّۤ رَاكِعٗاۤ وَأَنَابَ۩
(Daud) adati: “Zoona, wakuchitira zosalungama pokupempha nkhosa yako imodzi kuti aiphatikize ndi nkhosa zake. Ndithu ambiri mwa ophatikizana nawo zinthu, ena amachenjelera ena kupatula amene akhulupirira ndi kumachita zabwino; ndipo iwo ngochepa.” Basi pamenepo Daud adaona kuti tamuyesa mayeso (ndipo sadapambane). Choncho adapempha chikhululuko kwa Mbuye wake; adagwa ndi kulambira ndi kubwerera kwa Mbuye wake.
Tafsiran larabci:
فَغَفَرۡنَا لَهُۥ ذَٰلِكَۖ وَإِنَّ لَهُۥ عِندَنَا لَزُلۡفَىٰ وَحُسۡنَ مَـَٔابٖ
Choncho tidamkhululukira iye zimenezo; ndithu iye ali nawo ulemelero kwa Ife ndi mabwelero abwino.
Tafsiran larabci:
يَٰدَاوُۥدُ إِنَّا جَعَلۡنَٰكَ خَلِيفَةٗ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱحۡكُم بَيۡنَ ٱلنَّاسِ بِٱلۡحَقِّ وَلَا تَتَّبِعِ ٱلۡهَوَىٰ فَيُضِلَّكَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ يَضِلُّونَ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ لَهُمۡ عَذَابٞ شَدِيدُۢ بِمَا نَسُواْ يَوۡمَ ٱلۡحِسَابِ
“E iwe Daud! Ndithu ife takuchita iwe kukhala woyang’anira pa dziko; choncho weruza pakati pa anthuwa mwachilungamo; ndipo usatsatire zilakolako kuopa kuti zingakusokeretse ku njira ya Allah.” Ndithu amene akusokera ku njira ya Allah (potsatira zilakolako zawo), chilango chaukali chili pa iwo chifukwa cha kuiwala kwawo tsiku la chiwerengero.
Tafsiran larabci:
وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَآءَ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا بَٰطِلٗاۚ ذَٰلِكَ ظَنُّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْۚ فَوَيۡلٞ لِّلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنَ ٱلنَّارِ
Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake popanda cholinga. Zoterezo ndi maganizo a amene sadakhulupirire. Choncho kuonongeka kwakukulu ku Moto kuli kwa iwo amene sadakhulupirire.
Tafsiran larabci:
أَمۡ نَجۡعَلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ كَٱلۡمُفۡسِدِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ نَجۡعَلُ ٱلۡمُتَّقِينَ كَٱلۡفُجَّارِ
Kodi tingawachite amene akhulupirira (Allah) ndi kuchita zabwino kukhala monga oononga pa dziko? Kapena tiwachite oopa (Allah) monga oipa?
Tafsiran larabci:
كِتَٰبٌ أَنزَلۡنَٰهُ إِلَيۡكَ مُبَٰرَكٞ لِّيَدَّبَّرُوٓاْ ءَايَٰتِهِۦ وَلِيَتَذَكَّرَ أُوْلُواْ ٱلۡأَلۡبَٰبِ
(Ili), ndibuku lochuluka madalitso lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti (anthu) azame kwambiri pomvetsetsa ndime zake; ndi kuti apeze nalo phunziro eni nzeru.
Tafsiran larabci:
وَوَهَبۡنَا لِدَاوُۥدَ سُلَيۡمَٰنَۚ نِعۡمَ ٱلۡعَبۡدُ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٌ
Ndipo Daud tidampatsa (dalitso lobereka) Sulaiman, amene adali munthu wabwino. Ndithu iye adali wochulukitsa kutembenukira kwa Allah (ndi kudzichepetsa m’chikhalidwe chake chonse).
Tafsiran larabci:
إِذۡ عُرِضَ عَلَيۡهِ بِٱلۡعَشِيِّ ٱلصَّٰفِنَٰتُ ٱلۡجِيَادُ
(Kumbuka) pamene adasonyezedwa kwa iye nthawi yamadzulo akavalo ofatsa akaima; othamanga kwambiri, akayenda.
Tafsiran larabci:
فَقَالَ إِنِّيٓ أَحۡبَبۡتُ حُبَّ ٱلۡخَيۡرِ عَن ذِكۡرِ رَبِّي حَتَّىٰ تَوَارَتۡ بِٱلۡحِجَابِ
Ndipo adati: “Ndikukonda zinthu zabwino chifukwa chokumbukira Mbuye wanga,” kufikira pomwe (akavalowo) adabisika kuseri kwa chotsekereza (poikidwa m’makola mwawo pomwe iye amafunitsitsa kumawaonabe).
Tafsiran larabci:
رُدُّوهَا عَلَيَّۖ فَطَفِقَ مَسۡحَۢا بِٱلسُّوقِ وَٱلۡأَعۡنَاقِ
(Ndipo adati): “Abwezeni kwa ine.” Kenako adayamba kuwasisita m’miyendo ndi m’makosi (mwawo).
Tafsiran larabci:
وَلَقَدۡ فَتَنَّا سُلَيۡمَٰنَ وَأَلۡقَيۡنَا عَلَىٰ كُرۡسِيِّهِۦ جَسَدٗا ثُمَّ أَنَابَ
Ndithu Sulaiman tidamuyesa (mayeso); ndipo tidaika thupi pa mpando wake wachifumu; kenako adabwerera kwa Allah.
Tafsiran larabci:
قَالَ رَبِّ ٱغۡفِرۡ لِي وَهَبۡ لِي مُلۡكٗا لَّا يَنۢبَغِي لِأَحَدٖ مِّنۢ بَعۡدِيٓۖ إِنَّكَ أَنتَ ٱلۡوَهَّابُ
Adati: “E Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndipo ndipatseni ufumu (umene) sangaupeze aliyense pambuyo panga; ndithu inu ndiwopatsa mochulukitsa.”
Tafsiran larabci:
فَسَخَّرۡنَا لَهُ ٱلرِّيحَ تَجۡرِي بِأَمۡرِهِۦ رُخَآءً حَيۡثُ أَصَابَ
Kenako tidaichita mphepo yoomba moleza kuti imgonjere, yomwe imayenda mwachifuniro chake (Sulaiman), paliponse pomwe wafuna.
Tafsiran larabci:
وَٱلشَّيَٰطِينَ كُلَّ بَنَّآءٖ وَغَوَّاصٖ
Ndiponso (tidamgonjetsera) asatana; ena mwa iwo omanga zomangamanga ndi obira m’nyanja zakuya.
Tafsiran larabci:
وَءَاخَرِينَ مُقَرَّنِينَ فِي ٱلۡأَصۡفَادِ
Ndi ena (mwa asatana) onjatidwa mmagoli ndi unyolo, (kuti asiye kusokoneza ena).
Tafsiran larabci:
هَٰذَا عَطَآؤُنَا فَٱمۡنُنۡ أَوۡ أَمۡسِكۡ بِغَيۡرِ حِسَابٖ
(Ndipo adauzidwa iye): “Izi (zomwc takudalitsa nazo) ndi zopatsa Zathu; choncho mpatse kapena mmane (amene wamfuna). Popanda kuwerengeredwa.”
Tafsiran larabci:
وَإِنَّ لَهُۥ عِندَنَا لَزُلۡفَىٰ وَحُسۡنَ مَـَٔابٖ
Ndithu (Sulaiman) ali nawo ulemelero waukulu woyandikira kwa Ife, ndi mabwelero abwino.
Tafsiran larabci:
وَٱذۡكُرۡ عَبۡدَنَآ أَيُّوبَ إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَسَّنِيَ ٱلشَّيۡطَٰنُ بِنُصۡبٖ وَعَذَابٍ
Kumbuka, (iwe Mtumiki {s.a.w}) kapolo Wathu Ayubu, pamene adaitana Mbuye wake: “Ine wandikhudza satana ndi masautso ndi zowawa!”
Tafsiran larabci:
ٱرۡكُضۡ بِرِجۡلِكَۖ هَٰذَا مُغۡتَسَلُۢ بَارِدٞ وَشَرَابٞ
(Tidamuyankha kuitana kwake, ndipo tidamuuza): “Menyetsa miyendo yako (panthaka; patuluka madzi) ozizira osamba ndi kumwa (zikuchokera zomwe uli nazo).”
Tafsiran larabci:
وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ أَهۡلَهُۥ وَمِثۡلَهُم مَّعَهُمۡ رَحۡمَةٗ مِّنَّا وَذِكۡرَىٰ لِأُوْلِي ٱلۡأَلۡبَٰبِ
Ndipo tidamubwezera anthu ake, ndi kumpatsanso ena onga iwo (m’kuchuluka kwawo) powaphatikiza ndi omwe adali nawo; (tidachita zimenezi) chifukwa cha chifundo chochokera kwa Ife ndi kuti chikhale chikumbutso kwa eni nzeru.
Tafsiran larabci:
وَخُذۡ بِيَدِكَ ضِغۡثٗا فَٱضۡرِب بِّهِۦ وَلَا تَحۡنَثۡۗ إِنَّا وَجَدۡنَٰهُ صَابِرٗاۚ نِّعۡمَ ٱلۡعَبۡدُ إِنَّهُۥٓ أَوَّابٞ
“Ndipo gwira m’dzanja lako mtolo wa zikoti; menya ndi mtolowo ndipo usaswe lonjezo.” Ndithu Ife tidampeza ali wopirira. Taonani kukhala bwino kapolo! Ndithu iye ngotembenukira kwambiri kwa Allah.[343]
[343] Ayubu adalumbira kuti adzamenya mkazi wake ndi zikoti zingapo pamene adamupsera mtima chifukwa cha kuchedwa kufika kwa iye pomwe adakasaka mkaziyo chakudya panthawi yomwe ayubu amadwala. Ndipo Allah adamasula kulumbira kwake kuti atenge mtolo wa zikoti zomwe m’kati mwake mudali chiwerengero chomwe adalumbilira kuti adzammenya nacho, ndipo ammenye ndi mtolowo kuti akwaniritse kulumbira kwakeko. Allah adamchitira Ayubu chifundo chimenechi chifukwa chakuti adapilira pa masautso ake, komanso adamchitira chifundo mkaziyo chifukwa anali mkazi wochita zabwino.
Tafsiran larabci:
وَٱذۡكُرۡ عِبَٰدَنَآ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ أُوْلِي ٱلۡأَيۡدِي وَٱلۡأَبۡصَٰرِ
Kumbukira, (iwe Mtumiki {s.a.w}) akapolo athu Ibrahim, Ishâq ndi Ya’qub, eni mphamvu (pa ntchito yachipembedzo) ndi kuyang’ana kozindikira.
Tafsiran larabci:
إِنَّآ أَخۡلَصۡنَٰهُم بِخَالِصَةٖ ذِكۡرَى ٱلدَّارِ
Ndithu Ife tidawasankha powapatsa chikhalidwe chabwino (chomwe) ndi kukumbukira Nyumba yomaliza (nthawi zonse).
Tafsiran larabci:
وَإِنَّهُمۡ عِندَنَا لَمِنَ ٱلۡمُصۡطَفَيۡنَ ٱلۡأَخۡيَارِ
Ndithu kwa Ife iwo adali mwa anthu abwino omwe adasankhidwa.
Tafsiran larabci:
وَٱذۡكُرۡ إِسۡمَٰعِيلَ وَٱلۡيَسَعَ وَذَا ٱلۡكِفۡلِۖ وَكُلّٞ مِّنَ ٱلۡأَخۡيَارِ
Ndipo kumbuka Ismail, Alyasa’ (Eliya), ndi Thulkifl (Yesaya); ndipo onsewo adali mwa anthu abwino.
Tafsiran larabci:
هَٰذَا ذِكۡرٞۚ وَإِنَّ لِلۡمُتَّقِينَ لَحُسۡنَ مَـَٔابٖ
Ichi ndichikumbutso (kwa iwe ndi anthu ako). Ndipo ndithu oopa Allah ali ndi mabwelero abwino.
Tafsiran larabci:
جَنَّٰتِ عَدۡنٖ مُّفَتَّحَةٗ لَّهُمُ ٱلۡأَبۡوَٰبُ
(Awakonzera iwo) minda yamuyaya yotsekulidwa makomo ake kwa iwo.
Tafsiran larabci:
مُتَّكِـِٔينَ فِيهَا يَدۡعُونَ فِيهَا بِفَٰكِهَةٖ كَثِيرَةٖ وَشَرَابٖ
(Azidzakhala m’menemo) uku atatsamira (makama amtengo wapatali, ndipo adzakhala akusangalala) akuitanitsa mmenemo zipatso ndi zakumwa zambiri.
Tafsiran larabci:
۞ وَعِندَهُمۡ قَٰصِرَٰتُ ٱلطَّرۡفِ أَتۡرَابٌ
Ndipo (ku Munda wamtenderewo) adzakhala ndi akazi oyang’ana amuna awo okha basi, ofanana misinkhu.
Tafsiran larabci:
هَٰذَا مَا تُوعَدُونَ لِيَوۡمِ ٱلۡحِسَابِ
Izi ndi zomwe mukulonjezedwa pa tsiku la chiweruziro.
Tafsiran larabci:
إِنَّ هَٰذَا لَرِزۡقُنَا مَا لَهُۥ مِن نَّفَادٍ
Ndithu izi ndizopatsa Zathu zosatha.
Tafsiran larabci:
هَٰذَاۚ وَإِنَّ لِلطَّٰغِينَ لَشَرَّ مَـَٔابٖ
Awa ndimalipiro (a oopa Allah)! Koma opyola malire (ndi kunyoza aneneri awo), ali ndi mabwelero oipa.
Tafsiran larabci:
جَهَنَّمَ يَصۡلَوۡنَهَا فَبِئۡسَ ٱلۡمِهَادُ
(Omwe ndi) Jahannam adzailowa (ndi kupseleramo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!
Tafsiran larabci:
هَٰذَا فَلۡيَذُوقُوهُ حَمِيمٞ وَغَسَّاقٞ
Awa ndimadzi wotentha kwambiri, ndi mafinya (a anthu a ku Moto). Choncho awalaweko!
Tafsiran larabci:
وَءَاخَرُ مِن شَكۡلِهِۦٓ أَزۡوَٰجٌ
Ndi zilango zina zambiri zonga zimenezi zamitundumitundu.
Tafsiran larabci:
هَٰذَا فَوۡجٞ مُّقۡتَحِمٞ مَّعَكُمۡ لَا مَرۡحَبَۢا بِهِمۡۚ إِنَّهُمۡ صَالُواْ ٱلنَّارِ
(Kudzanenedwa kwa opyola malire, omwe ndiatsogoleri a opembedza mafano): “Gulu ili lalikulu, lilowa nanu ku Moto; (omwe adali okutsatirani. Ndipo atsogoleri adzati): Siolandiridwa (mwamtendere). Ndithu iwo ngolowa ku Moto.”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ بَلۡ أَنتُمۡ لَا مَرۡحَبَۢا بِكُمۡۖ أَنتُمۡ قَدَّمۡتُمُوهُ لَنَاۖ فَبِئۡسَ ٱلۡقَرَارُ
(Otsatira adzanena): “Ndithu tembeleroli likuyenera inu, (limene mukutitembelera ife) chifukwa inu ndiamene mudadzetsa chilangochi potinyenga ife (ndi kutiitanira kunjira yopotoka), taonani kuipa malo okhazikikamo (Jahannam)!”
Tafsiran larabci:
قَالُواْ رَبَّنَا مَن قَدَّمَ لَنَا هَٰذَا فَزِدۡهُ عَذَابٗا ضِعۡفٗا فِي ٱلنَّارِ
(Otsatira) adzanena: “E Mbuye wathu! Muonjezereni chilango ku Moto pamwamba pa chilango amene watidzetsera chilangochi.”
Tafsiran larabci:
وَقَالُواْ مَا لَنَا لَا نَرَىٰ رِجَالٗا كُنَّا نَعُدُّهُم مِّنَ ٱلۡأَشۡرَارِ
Ndipo (anthu a ku Moto) adzanena: “Kodi nchifukwa ninji sitikuwaona anthu aja omwe timawawerengera kuti ngoipa (pa dziko lapansi)?
Tafsiran larabci:
أَتَّخَذۡنَٰهُمۡ سِخۡرِيًّا أَمۡ زَاغَتۡ عَنۡهُمُ ٱلۡأَبۡصَٰرُ
Kodi tidawachitira chipongwe (pa dziko lapansi koma taonani sadalowe nafe ku Moto). Kapena kuti maso athu sakuwaona?”
Tafsiran larabci:
إِنَّ ذَٰلِكَ لَحَقّٞ تَخَاصُمُ أَهۡلِ ٱلنَّارِ
Ndithu zimenezo, zokangana anthu a ku Moto nzoona.
Tafsiran larabci:
قُلۡ إِنَّمَآ أَنَا۠ مُنذِرٞۖ وَمَا مِنۡ إِلَٰهٍ إِلَّا ٱللَّهُ ٱلۡوَٰحِدُ ٱلۡقَهَّارُ
Nena (kwa iwo): “Ndithu ine ndine mchenjezi (wochenjeza za chilango cha Allah). Palibe wopembedzedwa mwachoonadi, koma Allah Mmodzi Yekha Wopambana.
Tafsiran larabci:
رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَا ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡغَفَّٰرُ
Mbuye wathambo ndi nthaka, ndi zapakati pake; wamphamvu zoposa; Wokhululuka machimo kwambiri (kwa yemwe walapa ndi kumkhulupirira).”
Tafsiran larabci:
قُلۡ هُوَ نَبَؤٌاْ عَظِيمٌ
Nena (kwa iwo iwe Mtumiki {s.a.w}): “Ichi (chimene ndakuchenjezani nachochi) ndinkhani yaikulu.”
Tafsiran larabci:
أَنتُمۡ عَنۡهُ مُعۡرِضُونَ
“Inu, za chimenechi, mukunyozera!”
Tafsiran larabci:
مَا كَانَ لِيَ مِنۡ عِلۡمِۭ بِٱلۡمَلَإِ ٱلۡأَعۡلَىٰٓ إِذۡ يَخۡتَصِمُونَ
“Sindimadziwa chilichonse za akuluakulu a pamwamba (angelo) pamene amakangana (za kulengedwa kwa Adam).”
Tafsiran larabci:
إِن يُوحَىٰٓ إِلَيَّ إِلَّآ أَنَّمَآ أَنَا۠ نَذِيرٞ مُّبِينٌ
Palibe china chimene chavumbulutsidwa kwa ine, koma (kuti ndikuuzeni mawu awa oti): “Ine ndine mchenjezi (wanu) woonekera.”
Tafsiran larabci:
إِذۡ قَالَ رَبُّكَ لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنِّي خَٰلِقُۢ بَشَرٗا مِّن طِينٖ
(Akumbutse) pamene Mbuye wako adanena kwa angelo: “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi, (yemwe ndi Adam).”
Tafsiran larabci:
فَإِذَا سَوَّيۡتُهُۥ وَنَفَخۡتُ فِيهِ مِن رُّوحِي فَقَعُواْ لَهُۥ سَٰجِدِينَ
“Ndikammaliza ndi kumuuzira mzimu wochokera kwa Ine, igwani pansi momulemekeza.”
Tafsiran larabci:
فَسَجَدَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ كُلُّهُمۡ أَجۡمَعُونَ
Choncho angelo onse anagwa pansi momulemekeza.
Tafsiran larabci:
إِلَّآ إِبۡلِيسَ ٱسۡتَكۡبَرَ وَكَانَ مِنَ ٱلۡكَٰفِرِينَ
Kupatula Iblis; adadzikweza, ndipo adali mmodzi mwa okana.
Tafsiran larabci:
قَالَ يَٰٓإِبۡلِيسُ مَا مَنَعَكَ أَن تَسۡجُدَ لِمَا خَلَقۡتُ بِيَدَيَّۖ أَسۡتَكۡبَرۡتَ أَمۡ كُنتَ مِنَ ٱلۡعَالِينَ
(Allah) adati: “E iwe Iblis! Nchiyani chakuletsa kugwa pansi ndi kuchilemekeza chimene ndachilenga ndi manja Anga (popanda kutuma wina)? Kodi wadzikweza kapena uli mmodzi wa odziika pamwamba?”
Tafsiran larabci:
قَالَ أَنَا۠ خَيۡرٞ مِّنۡهُ خَلَقۡتَنِي مِن نَّارٖ وَخَلَقۡتَهُۥ مِن طِينٖ
(Iblis) adanena: “Ine ndine wabwino kuposa iye (Adam); chifukwa ine mudandilenga kuchokera ku Moto, ndipo iye mudamulenga kuchokera kudongo.”
Tafsiran larabci:
قَالَ فَٱخۡرُجۡ مِنۡهَا فَإِنَّكَ رَجِيمٞ
(Allah) adanena (kwa Iblis): “Tuluka m’menemo (m’gulu la angelo apamwamba); ndithu iwe ngopirikitsidwa (ku chifundo cha Allah).”
Tafsiran larabci:
وَإِنَّ عَلَيۡكَ لَعۡنَتِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلدِّينِ
“Ndipo ndithu matembelero Anga akhala pa iwe kufikira tsiku lamalipiro.”
Tafsiran larabci:
قَالَ رَبِّ فَأَنظِرۡنِيٓ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ
(Iblis) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nthawi kufikira tsiku louka ku imfa.”
Tafsiran larabci:
قَالَ فَإِنَّكَ مِنَ ٱلۡمُنظَرِينَ
(Allah) adati: “Ndithu iwe ndiwe mmodzi wa wopatsidwa nthawi.”
Tafsiran larabci:
إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡوَقۡتِ ٱلۡمَعۡلُومِ
“Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (imene yaikidwa).”
Tafsiran larabci:
قَالَ فَبِعِزَّتِكَ لَأُغۡوِيَنَّهُمۡ أَجۡمَعِينَ
(Iblis) adati: “Choncho kupyolera mu ulemelero Wanu ndikulumbira kuti ndiwasokoneza onse.”
Tafsiran larabci:
إِلَّا عِبَادَكَ مِنۡهُمُ ٱلۡمُخۡلَصِينَ
“Kupatula akapolo Anu omwe ali osankhidwa (oyeretsedwa) mwa iwo. (Pa iwo ndilibe nyonga zilizonse).”
Tafsiran larabci:
قَالَ فَٱلۡحَقُّ وَٱلۡحَقَّ أَقُولُ
(Allah) adati: “Ndikulumbira mwachoonadi ndipo ndikunena choona.”
Tafsiran larabci:
لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنكَ وَمِمَّن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ أَجۡمَعِينَ
“Ndithudi, ndidzazadzitsa Jahannam ndi ochokera ku mtundu wako ndi omwe adzakutsate mwa iwo (ana a Adam) onse.”
Tafsiran larabci:
قُلۡ مَآ أَسۡـَٔلُكُمۡ عَلَيۡهِ مِنۡ أَجۡرٖ وَمَآ أَنَا۠ مِنَ ٱلۡمُتَكَلِّفِينَ
Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}, kwa anthu ako): “Sindikukupemphani malipiro pa zimenezi ndiponso ine simmodzi wa odzikakamiza (pa zinthu zosandiyenera).
Tafsiran larabci:
إِنۡ هُوَ إِلَّا ذِكۡرٞ لِّلۡعَٰلَمِينَ
(Qur’an) sichina koma ndichikumbutso ndi chiphunzitso kwa zolengedwa zonse.
Tafsiran larabci:
وَلَتَعۡلَمُنَّ نَبَأَهُۥ بَعۡدَ حِينِۭ
Ndipo posachedwa mudziwa, (inu otsutsa, kuona kwa) nkhani zake.”
Tafsiran larabci:
 
Fassarar Ma'anoni Sura: Suratu Saad
Teburin Jerin Sunayen Surori Lambar shafi
 
Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fasaara da Yaren Pashto - Teburin Bayani kan wasu Fassarori

Fassarar Maanonin Alurani mai girma zuwa Yaren shishiwa wanda Khalid Ibrahim Bitala kwafi na Shekarar 2020 Miladiyya

Rufewa