Check out the new design

Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala * - Teburin Bayani kan wasu Fassarori


Fassarar Ma'anoni Sura: Al'ma'ida   Aya:
وَمِنَ ٱلَّذِينَ قَالُوٓاْ إِنَّا نَصَٰرَىٰٓ أَخَذۡنَا مِيثَٰقَهُمۡ فَنَسُواْ حَظّٗا مِّمَّا ذُكِّرُواْ بِهِۦ فَأَغۡرَيۡنَا بَيۡنَهُمُ ٱلۡعَدَاوَةَ وَٱلۡبَغۡضَآءَ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِۚ وَسَوۡفَ يُنَبِّئُهُمُ ٱللَّهُ بِمَا كَانُواْ يَصۡنَعُونَ
Naonso aja amene akuti: “Ife ndife Akhrisitu,” tidalandira pangano lawo koma adasiya gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Tero tidabzala pakati pawo chidani ndi kusakondana mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah adzawawuza zimene adali kuchita.[160]
[160] Ndime iyi ikusonyeza kupatukana komwe kuli pakati pawo kotero kuti mpingo wina umayesa unzake monga wakunja. Monga mpingo wa Roman Catholic umaiona mipingo ina monga ya Protestant, Orthodox ndi yambiri ngati mipingo ya chikunja. Zonsezi nchifukwa cha kusatsatira zophunzitsa zenizeni za Chikhrisitu.
Tafsiran larabci:
يَٰٓأَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ قَدۡ جَآءَكُمۡ رَسُولُنَا يُبَيِّنُ لَكُمۡ كَثِيرٗا مِّمَّا كُنتُمۡ تُخۡفُونَ مِنَ ٱلۡكِتَٰبِ وَيَعۡفُواْ عَن كَثِيرٖۚ قَدۡ جَآءَكُم مِّنَ ٱللَّهِ نُورٞ وَكِتَٰبٞ مُّبِينٞ
E inu anthu a buku! Ndithudi wakufikani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani poyera zambiri zomwe munkabisa za m’buku. Koma akusiya zambiri (posazilongosola). Ndithudi kwakudzerani kuunika kochokera kwa Allah ndi buku lomwe likufotokoza mwatchutchutchu (chinthu chilichonse).
Tafsiran larabci:
يَهۡدِي بِهِ ٱللَّهُ مَنِ ٱتَّبَعَ رِضۡوَٰنَهُۥ سُبُلَ ٱلسَّلَٰمِ وَيُخۡرِجُهُم مِّنَ ٱلظُّلُمَٰتِ إِلَى ٱلنُّورِ بِإِذۡنِهِۦ وَيَهۡدِيهِمۡ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Ndi bukulo Allah akuwatsogolera kunjira zamtendere amene akutsata chiyanjano chake ndikuwatulutsa mu m’dima ndi kuwaika m’kuunika mwa lamulo Lake, ndi kuwatsogolera kunjira yoongoka.
Tafsiran larabci:
لَّقَدۡ كَفَرَ ٱلَّذِينَ قَالُوٓاْ إِنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡمَسِيحُ ٱبۡنُ مَرۡيَمَۚ قُلۡ فَمَن يَمۡلِكُ مِنَ ٱللَّهِ شَيۡـًٔا إِنۡ أَرَادَ أَن يُهۡلِكَ ٱلۡمَسِيحَ ٱبۡنَ مَرۡيَمَ وَأُمَّهُۥ وَمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ جَمِيعٗاۗ وَلِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَمَا بَيۡنَهُمَاۚ يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ وَٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Ndithudi, amukana (Allah) amene akunena kuti Mulungu ndiye Mesiya Mwana wa Mariya. Nena: “Ndani akadatha kuletsa chilichonse kwa Allah ngati Iye akadafuna kuononga Mesiya mwana wa Mariya ndi mayi wakeyo, ndi onse omwe ali m’dziko lapansi? Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake ngwa Allah. Amalenga chimene wafuna. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.”[161]
[161] Mndime iyi atchula zoyankhula zawo za machimo zoti Isa (Yesu) ndi mwana wa Mulungu, kapena ndi Mulungu amene, kapena ndi mmodzi mmilungu itatu. Ndipo akunenetsa za kufooka kwa mneneri Isa (Yesu) pamaso pa Allah monga kulili kufookanso kwa zolengedwa zina.
Ndimeyi ikunenetsanso kuti Allah monga amalenga mkalengedwe kamene Iye wafuna, mchosadabwitsa kwa Iye kulenga Isa (Yesu) popanda tate. Ndipo nchosadabwitsanso kwa Iye kulenga Adam popanda tate ndi mayi. Nanga nchotani kuti Akhrisitu azimuyesa Mneneri Isa (Yesu) kuti ndi mwana wa Mulungu kamba koti alibe tate? Bwanji nanga Adam naye sakumuyesa mwana wa Mulungu poti nayenso alibe tate ndi mayi? Ndibwino kutsata choonadi ngakhale choonadicho chikuchokera kwa mdani. Choonadi ndi choonadi.
Tafsiran larabci:
 
Fassarar Ma'anoni Sura: Al'ma'ida
Teburin Jerin Sunayen Surori Lambar shafi
 
Fassarar Ma'anonin Alqura'ni - Fassara da harshan Shishiyo - Khalid Ibrahim Bitala - Teburin Bayani kan wasu Fassarori

Fassararta Khalid Ibrahim Bitala.

Rufewa