Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa * - Daftar isi terjemahan


Terjemahan makna Ayah: (184) Surah: Surah Al-Baqarah
أَيَّامٗا مَّعۡدُودَٰتٖۚ فَمَن كَانَ مِنكُم مَّرِيضًا أَوۡ عَلَىٰ سَفَرٖ فَعِدَّةٞ مِّنۡ أَيَّامٍ أُخَرَۚ وَعَلَى ٱلَّذِينَ يُطِيقُونَهُۥ فِدۡيَةٞ طَعَامُ مِسۡكِينٖۖ فَمَن تَطَوَّعَ خَيۡرٗا فَهُوَ خَيۡرٞ لَّهُۥۚ وَأَن تَصُومُواْ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
(Kusalaku nkwa) masiku owerengeka. Koma amene akhale odwala mwa inu kapena akhale paulendo, (namasula masiku ena), akwaniritse chiwerengerocho m’masiku ena. Ndipo kwa amene sangathe kusala apereke dipo lodyetsa masikini. Ndipo amene achite zabwino mwa chifuniro chake, kutero ndibwino kwa iye. Ndipo kusala (pamene kukulolezedwa kumasula) ndibwino kwa inu, ngati muli odziwadi (kufunika kwa kusala).[19]
[19] Amene sangathe kusala ndi awa:-
a) Okalamba kwambiri omwe abwerera ku umwana, amene sangathe kupilira
ndi njala
b) Odwala amene sangathe kusala ndipo alibe chiyembekezo choti achira. Anthu oterewa akuloledwa kusiya kusala. Ndipo tsiku lililonse aliyense wa iwo apereke chakudya chokwana kudya munthu mmodzi. Chakudya chomwe anthu m’dzikomo amadya. Koma amene ali osauka asachite zimenezi.
Allah amkhululukira pakuti Allah sakakamiza munthu kuchita chimene sangathe kuchichita.
Tsono wodwala yemwe ali ndi chiyembekezo chochira, ndi wapakati amene akuvutika ndi kusala, ndi woyamwitsa amene akuona kuti azunzika akasala, onsewa sapereka dipo lija. Koma adzalipa masiku amene adamasulawo zikawachokera zovutazo monganso zilili ndi wapaulendo. Koma masheikh ena akuti wapakati ndi woyamwitsa nawonso apereke dipo la chakudya. Tero malangizo awanso tikhoza kuwatsata.
Tsono kunena koti: “Ngati mutasala ndi bwino kwa inu...” kukusonyeza kuti kumanga silamulo lomwe Allah watikakamiza kuchita lopanda phindu kwa ife, koma nchinthu chothandiza kwa anthu, makamaka pathupi lathu.
Ndipo kuonjezera apa, Allah, pa tsiku la chimaliziro, adzatipatsa mphoto yabwino. Masiku ano madokotala onse padziko lapansi akuvomereza kuti kusala kuli ndi phindu lalikulu ku thupi la munthu. Ichi ndi chimodzi mwa zizindikiro zosonyeza kuona kwa chipembedzo cha Chisilamu.
Chinenere nkhaniyi papita zaka zambiri, ndipo tsopano omwe sali Asilamu akuvomereza.
Tafsir berbahasa Arab:
 
Terjemahan makna Ayah: (184) Surah: Surah Al-Baqarah
Daftar surah Nomor Halaman
 
Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Daftar isi terjemahan

Terjemahan Makna Al-Qur`ān Al-Karīm ke Bahasa Chichewa oleh Khalid Ibrahim Betala. Edisi 2020 M

Tutup