Check out the new design

Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala * - Daftar isi terjemahan


Terjemahan makna Surah: Al-A'rāf   Ayah:
وَلَوۡ أَنَّ أَهۡلَ ٱلۡقُرَىٰٓ ءَامَنُواْ وَٱتَّقَوۡاْ لَفَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَرَكَٰتٖ مِّنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ وَلَٰكِن كَذَّبُواْ فَأَخَذۡنَٰهُم بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Chikhala kuti eni midziwo adakhulupirira naopa (Allah pamene aneneri adawadzera), tikadawatsekulira madalitso ochokera kumwamba ndi pansi. Koma adatsutsa (aneneri) ndipo tidawaononga chifukwa cha zoipa zomwe ankachita.[188]
[188] Apa tanthauzo lake nkuti akanapeza mtendere wambiri pompano padziko lapansi akadakhala kuti adali olungama.
Tafsir berbahasa Arab:
أَفَأَمِنَ أَهۡلُ ٱلۡقُرَىٰٓ أَن يَأۡتِيَهُم بَأۡسُنَا بَيَٰتٗا وَهُمۡ نَآئِمُونَ
Kodi anthu a m’mizinda (iyo momwe muli anthu oipa) ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango chathu sichingawadzere usiku iwo ali mtulo?
Tafsir berbahasa Arab:
أَوَأَمِنَ أَهۡلُ ٱلۡقُرَىٰٓ أَن يَأۡتِيَهُم بَأۡسُنَا ضُحٗى وَهُمۡ يَلۡعَبُونَ
Kapena anthu a m’mizindayo ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango Chathu sichingawafike masana uku iwo akusewera?
Tafsir berbahasa Arab:
أَفَأَمِنُواْ مَكۡرَ ٱللَّهِۚ فَلَا يَأۡمَنُ مَكۡرَ ٱللَّهِ إِلَّا ٱلۡقَوۡمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ
Kodi akudziika pa chitetezo ku chilango cha Allah? Sangadziike pa chitetezo ku chilango cha Allah kupatula anthu otayika basi.
Tafsir berbahasa Arab:
أَوَلَمۡ يَهۡدِ لِلَّذِينَ يَرِثُونَ ٱلۡأَرۡضَ مِنۢ بَعۡدِ أَهۡلِهَآ أَن لَّوۡ نَشَآءُ أَصَبۡنَٰهُم بِذُنُوبِهِمۡۚ وَنَطۡبَعُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ فَهُمۡ لَا يَسۡمَعُونَ
Kodi sadadziwe awa omwe alandira dziko molowa mmalo pambuyo pa eni dzikolo (anthu akale) kuti tikadafuna tikadawaika m’masautso chifukwa cha machimo awo ndi kuwadinda mitima yawo kotero iwo sakadamva (kanthu)?
Tafsir berbahasa Arab:
تِلۡكَ ٱلۡقُرَىٰ نَقُصُّ عَلَيۡكَ مِنۡ أَنۢبَآئِهَاۚ وَلَقَدۡ جَآءَتۡهُمۡ رُسُلُهُم بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا كَانُواْ لِيُؤۡمِنُواْ بِمَا كَذَّبُواْ مِن قَبۡلُۚ كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِ ٱلۡكَٰفِرِينَ
Iyo ndi midzi (ikuluikulu) yomwe tikukusimbira iwe zina mwa nkhani zake. Ndithudi, adawadzera atumiki awo ndi zizindikiro (zoonekera poyera zosonyeza kuti iwo ndi atumiki a Allah). Koma sadali oti nkukhulupirira pa zomwe adazitsutsapo kale. Umo ndi mmene Allah amadindira ndi kuitseka mitima ya osakhulupirira (kotero kuti sangathandizike ndi malangizo a mtundu uliwonse).
Tafsir berbahasa Arab:
وَمَا وَجَدۡنَا لِأَكۡثَرِهِم مِّنۡ عَهۡدٖۖ وَإِن وَجَدۡنَآ أَكۡثَرَهُمۡ لَفَٰسِقِينَ
Ndipo ambiri a iwo sitidawapeze akukwaniritsa lonjezo lililonse koma tidawapeza ambiri a iwo ali opandukira (chilamulo cha Allah).
Tafsir berbahasa Arab:
ثُمَّ بَعَثۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِم مُّوسَىٰ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَظَلَمُواْ بِهَاۖ فَٱنظُرۡ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
Kenako pambuyo pawo (aneneriwo) tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zizindikiro Zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adazikana (zizindikirozo). Choncho taona momwe adalili mathero aoononga.
Tafsir berbahasa Arab:
وَقَالَ مُوسَىٰ يَٰفِرۡعَوۡنُ إِنِّي رَسُولٞ مِّن رَّبِّ ٱلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo Mûsa adati: “E iwe Farawo! Ndithu ine ndine mthenga wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.”
Tafsir berbahasa Arab:
 
Terjemahan makna Surah: Al-A'rāf
Daftar surah Nomor Halaman
 
Terjemahan makna Alquran Alkarim - Terjemahan Berbahasa Chichewa - Khalid Ibrahim Betala - Daftar isi terjemahan

Terjemahan oleh Khalid Ibrahim Bitala.

Tutup