Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Čevų k. vertimas * - Vertimų turinys


Reikšmių vertimas Sūra: Sūra Al-Mu’minūn   Aja (Korano eilutė):

Sūra Al-Mu’minūn

قَدۡ أَفۡلَحَ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ
۞ Ndithu apambana okhulupirira (mwa Allah).
Tafsyrai arabų kalba:
ٱلَّذِينَ هُمۡ فِي صَلَاتِهِمۡ خَٰشِعُونَ
Amene amakhudzumuka pa mapemphero awo (poipereka mitima yawo kwa Allah modzichepetsa).
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَنِ ٱللَّغۡوِ مُعۡرِضُونَ
Ndi omwe amapewa zinthu zopanda pake (zachabe).
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِلزَّكَوٰةِ فَٰعِلُونَ
Ndi omwe amakwaniritsa (nsanamira ya) chopereka (Zakaat).
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِفُرُوجِهِمۡ حَٰفِظُونَ
Ndi omwe amasunga umaliseche wawo.
Tafsyrai arabų kalba:
إِلَّا عَلَىٰٓ أَزۡوَٰجِهِمۡ أَوۡ مَا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُهُمۡ فَإِنَّهُمۡ غَيۡرُ مَلُومِينَ
Kupatula kwa akazi awo ndi adzakazi omwe manja awo akumanja apeza. Choncho iwo (pakukumana ndi amenewo) saali odzudzulidwa.
Tafsyrai arabų kalba:
فَمَنِ ٱبۡتَغَىٰ وَرَآءَ ذَٰلِكَ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡعَادُونَ
Koma omwe angafune zosemphana ndi izi (kulumikizana ndi mkazi posiya njira ziwirizi) iwowo ndiwo opyola malire (a Allah).
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ لِأَمَٰنَٰتِهِمۡ وَعَهۡدِهِمۡ رَٰعُونَ
Ndi amene amasunga malonjezo awo ndi zomwe akhulupirika nazo.
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ هُمۡ عَلَىٰ صَلَوَٰتِهِمۡ يُحَافِظُونَ
Ndi omwe akusunga mapemphero awo (popemphera mu nthawi zake ndi kutsata malamulo ake uku ali odzichepetsa).
Tafsyrai arabų kalba:
أُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡوَٰرِثُونَ
Iwo ndi olandira (zabwino tsiku la Qiyâma).
Tafsyrai arabų kalba:
ٱلَّذِينَ يَرِثُونَ ٱلۡفِرۡدَوۡسَ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Amene adzalandira Munda wamtendere (wotchedwa) Fir’dausi (Munda wapamwamba kwambiri). M’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِن سُلَٰلَةٖ مِّن طِينٖ
Ndipo ndithu tidamlenga munthu kuchokera ku dongo labwino.
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ جَعَلۡنَٰهُ نُطۡفَةٗ فِي قَرَارٖ مَّكِينٖ
Kenako tidalenga ana ake ndi dontho lamadzi (ambewu ya munthu) lomwe lidaikidwa pamalo osungidwa.
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ خَلَقۡنَا ٱلنُّطۡفَةَ عَلَقَةٗ فَخَلَقۡنَا ٱلۡعَلَقَةَ مُضۡغَةٗ فَخَلَقۡنَا ٱلۡمُضۡغَةَ عِظَٰمٗا فَكَسَوۡنَا ٱلۡعِظَٰمَ لَحۡمٗا ثُمَّ أَنشَأۡنَٰهُ خَلۡقًا ءَاخَرَۚ فَتَبَارَكَ ٱللَّهُ أَحۡسَنُ ٱلۡخَٰلِقِينَ
Kenako tidalisintha dontholo kukhala magazi oundana; ndipo kenako magaziwo tidawasintha kukhala m’nofu; ndipo kenako m’nofu tidausintha kukhala mafupa; ndipo mafupawo tidawaveka minofu, kenako tidamsintha kukhala cholengedwa china. Choncho watukuka Allah, Wabwino polenga.
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ إِنَّكُم بَعۡدَ ذَٰلِكَ لَمَيِّتُونَ
Kenako ndithu inu pambuyo pa zimenezo mudzamwalira.
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ إِنَّكُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ تُبۡعَثُونَ
Ndithu inu, kenako mudzaukitsidwa pa tsiku la Qiyâma.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَقَدۡ خَلَقۡنَا فَوۡقَكُمۡ سَبۡعَ طَرَآئِقَ وَمَا كُنَّا عَنِ ٱلۡخَلۡقِ غَٰفِلِينَ
Ndipo ndithu tapanga njira zisanu ndi ziwiri (mitambo) pamwamba panu, ndipo ndithu (Ife) sitisiya kulabadira zolengedwa.
Tafsyrai arabų kalba:
وَأَنزَلۡنَا مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءَۢ بِقَدَرٖ فَأَسۡكَنَّٰهُ فِي ٱلۡأَرۡضِۖ وَإِنَّا عَلَىٰ ذَهَابِۭ بِهِۦ لَقَٰدِرُونَ
Ndipo tatsitsa madzi mwamuyeso kuchokera kumwamba, ndi kuwakhazikitsa m’nthaka; ndipo ndithu Ife ndi okhoza kuwachotsa (kuti musathandizike nawo, koma sitidachite zimenezo chifukwa chokuchitirani chifundo).
Tafsyrai arabų kalba:
فَأَنشَأۡنَا لَكُم بِهِۦ جَنَّٰتٖ مِّن نَّخِيلٖ وَأَعۡنَٰبٖ لَّكُمۡ فِيهَا فَوَٰكِهُ كَثِيرَةٞ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ
Ndi madzi amenewo, tidakupangirani minda ya kanjedza ndi mpesa, m’menemo inu mulinazo zipatso zambiri; ndipo mwazimenezo mumadya.
Tafsyrai arabų kalba:
وَشَجَرَةٗ تَخۡرُجُ مِن طُورِ سَيۡنَآءَ تَنۢبُتُ بِٱلدُّهۡنِ وَصِبۡغٖ لِّلۡأٓكِلِينَ
Ndipo (tidakupangirani) mtengo womera pa phiri la Sinai, womwe umatulutsa mafuta; ndipo ndindiwo kwa amene amadya. (Mtengo wake ndi mzitona).
Tafsyrai arabų kalba:
وَإِنَّ لَكُمۡ فِي ٱلۡأَنۡعَٰمِ لَعِبۡرَةٗۖ نُّسۡقِيكُم مِّمَّا فِي بُطُونِهَا وَلَكُمۡ فِيهَا مَنَٰفِعُ كَثِيرَةٞ وَمِنۡهَا تَأۡكُلُونَ
Ndipo ndithu m’ziweto muli lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwake; ndipo m’zimenezo mukupeza zothandiza zambiri; ndipo zina mwa izo mumadya.
Tafsyrai arabų kalba:
وَعَلَيۡهَا وَعَلَى ٱلۡفُلۡكِ تُحۡمَلُونَ
Ndipo pa msana pa izo ndi pamwamba pa zombo, mumanyamulidwa.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ فَقَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۚ أَفَلَا تَتَّقُونَ
Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah! Mulibe mulungu wina woti nkumpembedza kupatula Iye. Kodi simuopa (chilango Chake?)
Tafsyrai arabų kalba:
فَقَالَ ٱلۡمَلَؤُاْ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِن قَوۡمِهِۦ مَا هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡ يُرِيدُ أَن يَتَفَضَّلَ عَلَيۡكُمۡ وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ لَأَنزَلَ مَلَٰٓئِكَةٗ مَّا سَمِعۡنَا بِهَٰذَا فِيٓ ءَابَآئِنَا ٱلۡأَوَّلِينَ
Akuluakulu mwa anthu ake amene sadakhulupirire, adati: “Uyu sali kanthu, koma ndi munthu ngati inu; akufuna kuti adzipezere ubwino pa inu; ndipo Allah akadafuna (kukuphunzitsani) akadatuma angelo. Zoterezi sitidamvepo kumakolo athu akale.”
Tafsyrai arabų kalba:
إِنۡ هُوَ إِلَّا رَجُلُۢ بِهِۦ جِنَّةٞ فَتَرَبَّصُواْ بِهِۦ حَتَّىٰ حِينٖ
“Uyu sali kanthu, koma ndi munthu wamisala; choncho muyembekezereni mpaka nthawi (yofera.”)
Tafsyrai arabų kalba:
قَالَ رَبِّ ٱنصُرۡنِي بِمَا كَذَّبُونِ
(Nuh) adati: “Mbuye wanga ndipulumutseni pazomwe anditsutsa!”
Tafsyrai arabų kalba:
فَأَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡهِ أَنِ ٱصۡنَعِ ٱلۡفُلۡكَ بِأَعۡيُنِنَا وَوَحۡيِنَا فَإِذَا جَآءَ أَمۡرُنَا وَفَارَ ٱلتَّنُّورُ فَٱسۡلُكۡ فِيهَا مِن كُلّٖ زَوۡجَيۡنِ ٱثۡنَيۡنِ وَأَهۡلَكَ إِلَّا مَن سَبَقَ عَلَيۡهِ ٱلۡقَوۡلُ مِنۡهُمۡۖ وَلَا تُخَٰطِبۡنِي فِي ٱلَّذِينَ ظَلَمُوٓاْ إِنَّهُم مُّغۡرَقُونَ
Choncho tidamuvumbulutsira (mawu akuti): “Panga chombo moyang’aniridwa ndi kudziwitsidwa ndi Ife.” Ndipo lamulo Lathu likadza ndi kufwamphuka madzi mu uvuni, lowetsa mkati mwake (mwa chombocho) chilichonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi ndi banja lako, kupatula yemwe liwu latsogola pa iye kuti aonongeke mwa iwo. Ndipo usandilankhule za omwe adzichitira (okha) zoipa ndithu iwo amizidwa (m’madzi).
Tafsyrai arabų kalba:
فَإِذَا ٱسۡتَوَيۡتَ أَنتَ وَمَن مَّعَكَ عَلَى ٱلۡفُلۡكِ فَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي نَجَّىٰنَا مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo ukakhazikika m’chombocho, iwe ndi amene uli nawo, nena: “Tikuthokoza Allah, amene watipulumutsa ku anthu osalungama.”
Tafsyrai arabų kalba:
وَقُل رَّبِّ أَنزِلۡنِي مُنزَلٗا مُّبَارَكٗا وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡمُنزِلِينَ
Ndipo (potsika), nena: “E Mbuye wanga! Nditsitseni; kutsitsa kwa madalitso, pakuti Inu ndinu wotsitsa bwino kwambiri kuposa otsitsa.”
Tafsyrai arabų kalba:
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ وَإِن كُنَّا لَمُبۡتَلِينَ
Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo. Ndithu Ife tili (ndi udindo) wowayesa ndi mayeso osiyanasiyana.
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ أَنشَأۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِمۡ قَرۡنًا ءَاخَرِينَ
Kenako tidabweretsa m’badwo wina pambuyo pawo (omwe ndi Âdi).
Tafsyrai arabų kalba:
فَأَرۡسَلۡنَا فِيهِمۡ رَسُولٗا مِّنۡهُمۡ أَنِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مَا لَكُم مِّنۡ إِلَٰهٍ غَيۡرُهُۥٓۚ أَفَلَا تَتَّقُونَ
Ndipo tidatuma kwa iwo mtumiki (Hûd) wochokera mwa iwo, (yemwe ankati): “Pembedzani Allah! Mulibe mulungu wina kupatula Iye. Kodi simuopa?
Tafsyrai arabų kalba:
وَقَالَ ٱلۡمَلَأُ مِن قَوۡمِهِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَكَذَّبُواْ بِلِقَآءِ ٱلۡأٓخِرَةِ وَأَتۡرَفۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَا مَا هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡ يَأۡكُلُ مِمَّا تَأۡكُلُونَ مِنۡهُ وَيَشۡرَبُ مِمَّا تَشۡرَبُونَ
Ndipo akuluakulu a mwa anthu ake amene adali osakhulupirira, ndikutsutsa za kukumana ndi tsiku la chimaliziro, omwe tidawapatsa kulemera pa moyo wa padziko lapansi, adati: “Uyu saali kanthu, koma ndi munthu monga inu; amadya zimene inu mumadya, ndi kumwa zomwe inu mumamwa.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَئِنۡ أَطَعۡتُم بَشَرٗا مِّثۡلَكُمۡ إِنَّكُمۡ إِذٗا لَّخَٰسِرُونَ
Koma ngati mumvera munthu wonga inu, ndiye kuti mukhala otaika (oluza).
Tafsyrai arabų kalba:
أَيَعِدُكُمۡ أَنَّكُمۡ إِذَا مِتُّمۡ وَكُنتُمۡ تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَنَّكُم مُّخۡرَجُونَ
Kodi akukulonjezani kuti mukadzafa ndikusanduka dothi ndi mafupa, mudzaukitsidwanso (m’manda)?
Tafsyrai arabų kalba:
۞ هَيۡهَاتَ هَيۡهَاتَ لِمَا تُوعَدُونَ
Sizingachitike, sizingachitike, zimene mukulonjezedwazi!
Tafsyrai arabų kalba:
إِنۡ هِيَ إِلَّا حَيَاتُنَا ٱلدُّنۡيَا نَمُوتُ وَنَحۡيَا وَمَا نَحۡنُ بِمَبۡعُوثِينَ
Palibe (moyo wina) koma moyo wathu wapadziko lapansiwu basi! Tikufa ndiponso kukhala ndi moyo! Ndipo sitidzaukitsidwa m’manda.
Tafsyrai arabų kalba:
إِنۡ هُوَ إِلَّا رَجُلٌ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗا وَمَا نَحۡنُ لَهُۥ بِمُؤۡمِنِينَ
Uyu saali kanthu (amene akudzitcha kuti ndi Mtumiki) koma ndi munthu basi, akupekera Allah bodza, ndipo ife sitimkhulupirira.”
Tafsyrai arabų kalba:
قَالَ رَبِّ ٱنصُرۡنِي بِمَا كَذَّبُونِ
(Mtumikiyo) adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni pachifukwa chakuti anditsutsa.”
Tafsyrai arabų kalba:
قَالَ عَمَّا قَلِيلٖ لَّيُصۡبِحُنَّ نَٰدِمِينَ
(Allah) adati: “Posachedwapa akhala odzinena.”
Tafsyrai arabų kalba:
فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلصَّيۡحَةُ بِٱلۡحَقِّ فَجَعَلۡنَٰهُمۡ غُثَآءٗۚ فَبُعۡدٗا لِّلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
Choncho, mkuwe wa (chilango) choonadi udawaononga, ndipo tidawachita ngati zinyalala (zongotengedwa ndi madzi). Choncho, kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osalungama.
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ أَنشَأۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِمۡ قُرُونًا ءَاخَرِينَ
Ndipo titatero tidalenga mibadwo ina pambuyo pawo.
Tafsyrai arabų kalba:
مَا تَسۡبِقُ مِنۡ أُمَّةٍ أَجَلَهَا وَمَا يَسۡتَـٔۡخِرُونَ
Palibe mtundu ungaifulumizitse kapena kuichedwetsa nthawi yake yofera,
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ أَرۡسَلۡنَا رُسُلَنَا تَتۡرَاۖ كُلَّ مَا جَآءَ أُمَّةٗ رَّسُولُهَا كَذَّبُوهُۖ فَأَتۡبَعۡنَا بَعۡضَهُم بَعۡضٗا وَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَحَادِيثَۚ فَبُعۡدٗا لِّقَوۡمٖ لَّا يُؤۡمِنُونَ
Kenaka tidatuma atumiki Athu motsatizana; (wina pambuyo pa mnzake). Ndipo mbadwo uliwonse pamene adaufikira mtumiki wake, udamtsutsa; ndipo tidawaononga motsatana; ndipo tidawachita kukhala nkhani (za anthu.) Ndipo kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osakhulupirira.
Tafsyrai arabų kalba:
ثُمَّ أَرۡسَلۡنَا مُوسَىٰ وَأَخَاهُ هَٰرُونَ بِـَٔايَٰتِنَا وَسُلۡطَٰنٖ مُّبِينٍ
Zitatero tidatuma Mûsa ndi m’bale wake Harun ndi zozizwitsa Zathu, ndi umboni woonekera poyera,
Tafsyrai arabų kalba:
إِلَىٰ فِرۡعَوۡنَ وَمَلَإِيْهِۦ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ وَكَانُواْ قَوۡمًا عَالِينَ
Kwa Farawo ndi nduna zake. Koma onse adadzitukumula; ndipo adali anthu odzikweza.
Tafsyrai arabų kalba:
فَقَالُوٓاْ أَنُؤۡمِنُ لِبَشَرَيۡنِ مِثۡلِنَا وَقَوۡمُهُمَا لَنَا عَٰبِدُونَ
Ndipo adati: “Ha! Tikhulupirire anthu awiri onga ife, omwe mtundu wawo ndi akapolo athu!”
Tafsyrai arabų kalba:
فَكَذَّبُوهُمَا فَكَانُواْ مِنَ ٱلۡمُهۡلَكِينَ
Choncho adawatsutsa onse awiri, ndipo adali m’gulu la oonongedwa.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ لَعَلَّهُمۡ يَهۡتَدُونَ
Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku kuti iwo aongoke.
Tafsyrai arabų kalba:
وَجَعَلۡنَا ٱبۡنَ مَرۡيَمَ وَأُمَّهُۥٓ ءَايَةٗ وَءَاوَيۡنَٰهُمَآ إِلَىٰ رَبۡوَةٖ ذَاتِ قَرَارٖ وَمَعِينٖ
Ndipo tidamchita mwana wa Mariya ndi mayi wake kukhala chisonyezo (choonetsa kukhoza kwathu). Ndipo tidawapatsa malo othawirapo, pachikweza, chokhazikika pomwenso padali akasupe.
Tafsyrai arabų kalba:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلرُّسُلُ كُلُواْ مِنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَٱعۡمَلُواْ صَٰلِحًاۖ إِنِّي بِمَا تَعۡمَلُونَ عَلِيمٞ
E inu Atumiki! Idyani zakudya zabwino, ndipo chitani zabwino. Ndithu Ine ndi Wodziwa zonse zimene muchita.
Tafsyrai arabų kalba:
وَإِنَّ هَٰذِهِۦٓ أُمَّتُكُمۡ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ وَأَنَا۠ رَبُّكُمۡ فَٱتَّقُونِ
(Tidauza mibadwo yawo): “Ndithu mpingo wanuwu ndi mpingo umodzi, ndipo Ine Ndine Mbuye wanu; choncho ndiopeni.”
Tafsyrai arabų kalba:
فَتَقَطَّعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡ زُبُرٗاۖ كُلُّ حِزۡبِۭ بِمَا لَدَيۡهِمۡ فَرِحُونَ
Koma adadula chinthu chawochi (chipembedzo chawo) pakati pawo mipatukomipatuko; gulu lililonse limasangalalira chimene lili nacho.
Tafsyrai arabų kalba:
فَذَرۡهُمۡ فِي غَمۡرَتِهِمۡ حَتَّىٰ حِينٍ
Choncho, asiye mu umbuli wawo kufikira nthawi (yakufa kwawo).
Tafsyrai arabų kalba:
أَيَحۡسَبُونَ أَنَّمَا نُمِدُّهُم بِهِۦ مِن مَّالٖ وَبَنِينَ
Kodi akuganiza kuti tikamawapatsa chuma ndi ana,
Tafsyrai arabų kalba:
نُسَارِعُ لَهُمۡ فِي ٱلۡخَيۡرَٰتِۚ بَل لَّا يَشۡعُرُونَ
Tikuwafulumizitsira zabwino? Sichoncho, koma iwo sakuzindikira.
Tafsyrai arabų kalba:
إِنَّ ٱلَّذِينَ هُم مِّنۡ خَشۡيَةِ رَبِّهِم مُّشۡفِقُونَ
Ndithu amene amakhala amantha chifukwa choopa Mbuye wawo, (ndi m’mene mathero awo adzakhalire);
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ هُم بِـَٔايَٰتِ رَبِّهِمۡ يُؤۡمِنُونَ
Ndi omwe amakhulupirira Ayah za Mbuye wawo;
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ هُم بِرَبِّهِمۡ لَا يُشۡرِكُونَ
Ndi omwenso saphatikiza Mbuye wawo ndi mafano;
Tafsyrai arabų kalba:
وَٱلَّذِينَ يُؤۡتُونَ مَآ ءَاتَواْ وَّقُلُوبُهُمۡ وَجِلَةٌ أَنَّهُمۡ إِلَىٰ رَبِّهِمۡ رَٰجِعُونَ
Ndi omwenso amapereka (Zakaat ndi sadaka kuchokera m’chuma) chimene apatsidwa, uku mitima yawo ili yoopa kuti adzabwerera kwa Mbuye wawo;
Tafsyrai arabų kalba:
أُوْلَٰٓئِكَ يُسَٰرِعُونَ فِي ٱلۡخَيۡرَٰتِ وَهُمۡ لَهَا سَٰبِقُونَ
Amenewa ndiamene akuchita changu pa zinthu zabwino, ndipo iwo akutsogolera (ena) pa zimenezo.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَاۚ وَلَدَيۡنَا كِتَٰبٞ يَنطِقُ بِٱلۡحَقِّ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
Ndipo sitikakamiza munthu, koma chimene angathe (kuchichita). Ndipo tili naye kaundula (wosunga chilichonse) yemwe adzayankhula choonadi ndipo iwo sadzaponderezedwa.
Tafsyrai arabų kalba:
بَلۡ قُلُوبُهُمۡ فِي غَمۡرَةٖ مِّنۡ هَٰذَا وَلَهُمۡ أَعۡمَٰلٞ مِّن دُونِ ذَٰلِكَ هُمۡ لَهَا عَٰمِلُونَ
Koma mitima yawo ili m’kusalabadira mu ichi; ndipo iwo ali ndi ntchito zimene akuchita, osati izi.
Tafsyrai arabų kalba:
حَتَّىٰٓ إِذَآ أَخَذۡنَا مُتۡرَفِيهِم بِٱلۡعَذَابِ إِذَا هُمۡ يَجۡـَٔرُونَ
Kufikira tikadzawaika m’chilango amene ali opeza bwino awo, pompo adzakuwa (ndi kupempha chipulumutso).
Tafsyrai arabų kalba:
لَا تَجۡـَٔرُواْ ٱلۡيَوۡمَۖ إِنَّكُم مِّنَّا لَا تُنصَرُونَ
(Kudzanenedwa kwa iwo): “Musalire lero (ndi kupempha chipulumutso)! Ndithu inu simupulumutsidwa ndi Ife.”
Tafsyrai arabų kalba:
قَدۡ كَانَتۡ ءَايَٰتِي تُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فَكُنتُمۡ عَلَىٰٓ أَعۡقَٰبِكُمۡ تَنكِصُونَ
“Ndipo Ayah Zanga zinkawerengedwa kwa inu koma munkadzibwezera kumbuyo ndi zidendene zanu,
Tafsyrai arabų kalba:
مُسۡتَكۡبِرِينَ بِهِۦ سَٰمِرٗا تَهۡجُرُونَ
Uku mukudzikweza; nkumakambirana usiku za chabechabe zoinyoza (Qur’an).”
Tafsyrai arabų kalba:
أَفَلَمۡ يَدَّبَّرُواْ ٱلۡقَوۡلَ أَمۡ جَآءَهُم مَّا لَمۡ يَأۡتِ ءَابَآءَهُمُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Kodi sadaganizire liwu (ili limene wadza nalo Mtumiki{s.a.w}), kapena zawadzera zomwe sizidawadzerepo makolo awo akale?
Tafsyrai arabų kalba:
أَمۡ لَمۡ يَعۡرِفُواْ رَسُولَهُمۡ فَهُمۡ لَهُۥ مُنكِرُونَ
Kodi kapena sadam’dziwe Mtumiki wawoyu (makhalidwe ake) kotero kuti iwo akum’kana?
Tafsyrai arabų kalba:
أَمۡ يَقُولُونَ بِهِۦ جِنَّةُۢۚ بَلۡ جَآءَهُم بِٱلۡحَقِّ وَأَكۡثَرُهُمۡ لِلۡحَقِّ كَٰرِهُونَ
Kapena akunena kuti: “Ngwamisala?” Koma wawadzera ndi choonadi, ndipo ambiri a iwo amachida choonadi.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَوِ ٱتَّبَعَ ٱلۡحَقُّ أَهۡوَآءَهُمۡ لَفَسَدَتِ ٱلسَّمَٰوَٰتُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهِنَّۚ بَلۡ أَتَيۡنَٰهُم بِذِكۡرِهِمۡ فَهُمۡ عَن ذِكۡرِهِم مُّعۡرِضُونَ
Ndipo choonadi chikadatsatira zofuna zawo, ndiye kuti thambo ndi nthaka ndi za m’menemo zikadaonongeka! Koma tawabweretsera chikumbutso chawo, koma iwo akuchipewa chikumbutso chawocho.
Tafsyrai arabų kalba:
أَمۡ تَسۡـَٔلُهُمۡ خَرۡجٗا فَخَرَاجُ رَبِّكَ خَيۡرٞۖ وَهُوَ خَيۡرُ ٱلرَّٰزِقِينَ
Kodi kapena ukuwapempha malipiro (nchifukwa chake akuchikana chipembedzochi)? Koma malipiro a Mbuye wako ndiwo abwino; ndipo Iye ndi Wopereka Wabwino kuposa opereka.
Tafsyrai arabų kalba:
وَإِنَّكَ لَتَدۡعُوهُمۡ إِلَىٰ صِرَٰطٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Ndipo ndithu iwe ukuwaitanira ku njira yolunjika; (supempha malipiro kwa iwo pa kuitanako).
Tafsyrai arabų kalba:
وَإِنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ عَنِ ٱلصِّرَٰطِ لَنَٰكِبُونَ
Ndipo ndithu amene sakhulupirira tsiku la chimaliziro, ali kutali ndi njira ya choonadi.
Tafsyrai arabų kalba:
۞ وَلَوۡ رَحِمۡنَٰهُمۡ وَكَشَفۡنَا مَا بِهِم مِّن ضُرّٖ لَّلَجُّواْ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ
Ndipo tikadawachitira chifundo ndi kuwachotsera masautso omwe ali nawo, ndithu akadapitiriza kuyumbayumba m’kuchita kwawo zoipa.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَقَدۡ أَخَذۡنَٰهُم بِٱلۡعَذَابِ فَمَا ٱسۡتَكَانُواْ لِرَبِّهِمۡ وَمَا يَتَضَرَّعُونَ
Ndipo ndithu tidawalanga ndi chilango (chaukali), koma sadacheukire kwa Mbuye wawo ndikudzichepetsa.
Tafsyrai arabų kalba:
حَتَّىٰٓ إِذَا فَتَحۡنَا عَلَيۡهِم بَابٗا ذَا عَذَابٖ شَدِيدٍ إِذَا هُمۡ فِيهِ مُبۡلِسُونَ
Kufikira pamene tidawatsekulira khomo la chilango chaukali; pamenepo ndipo adataya mtima.
Tafsyrai arabų kalba:
وَهُوَ ٱلَّذِيٓ أَنشَأَ لَكُمُ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡأَبۡصَٰرَ وَٱلۡأَفۡـِٔدَةَۚ قَلِيلٗا مَّا تَشۡكُرُونَ
Ndipo Iye ndi Yemwe adakupangirani makutu, maso ndi mitima; nzochepa zimene mukuthokoza.
Tafsyrai arabų kalba:
وَهُوَ ٱلَّذِي ذَرَأَكُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَإِلَيۡهِ تُحۡشَرُونَ
Iyenso ndi Yemwe wakufalitsani pa dziko; kenako mudzasonkhanitsidwa kwa Iye.
Tafsyrai arabų kalba:
وَهُوَ ٱلَّذِي يُحۡيِۦ وَيُمِيتُ وَلَهُ ٱخۡتِلَٰفُ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
Ndipo Iye ndi Yemwe amapatsa moyo ndi imfa, ndipo kusinthana kwa usiku ndi usana Nkwake. Kodi simuzindikira?
Tafsyrai arabų kalba:
بَلۡ قَالُواْ مِثۡلَ مَا قَالَ ٱلۡأَوَّلُونَ
Koma akunena monga (anthu) oyamba adanenera.
Tafsyrai arabų kalba:
قَالُوٓاْ أَءِذَا مِتۡنَا وَكُنَّا تُرَابٗا وَعِظَٰمًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ
Akunena: “Kodi tikadzafa ndikukhala dothi ndi mafupa, tidzaukitsidwanso?”
Tafsyrai arabų kalba:
لَقَدۡ وُعِدۡنَا نَحۡنُ وَءَابَآؤُنَا هَٰذَا مِن قَبۡلُ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
“Ndithudi ife ndi makolo athu kale tidalonjezedwa zimenezi, izi sikanthu koma nkhambakamwa za anthu akale.”
Tafsyrai arabų kalba:
قُل لِّمَنِ ٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهَآ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
Nena: “Kodi nthaka njayani ndi zomwe zili m’menemo, ngati inu mukudziwa (kanthu)!”
Tafsyrai arabų kalba:
سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَذَكَّرُونَ
Adzanena kuti: “Nza Allah!” Nena: “Nanga bwanji simukumkumbukira (kuti Iye Ngokhoza chilichonse)?
Tafsyrai arabų kalba:
قُلۡ مَن رَّبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ ٱلسَّبۡعِ وَرَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡعَظِيمِ
Nena: “Kodi ndani Mbuye wa thambo zisanu ndi ziwiri, ndi Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) yaikulu?”
Tafsyrai arabų kalba:
سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ أَفَلَا تَتَّقُونَ
Anena (kuti): “Nza Allah.” Nena: “Nanga bwanji simukumuopa?”
Tafsyrai arabų kalba:
قُلۡ مَنۢ بِيَدِهِۦ مَلَكُوتُ كُلِّ شَيۡءٖ وَهُوَ يُجِيرُ وَلَا يُجَارُ عَلَيۡهِ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
Nena: “Kodi ndani yemwe m’manja mwake muli mphamvu yolamulira chinthu chilichonse? Ndipo Iye amateteza zonse. Ndipo palibe chimene chingatetezedwe kuchilango Chake. Ngati inu mukudziwa.”
Tafsyrai arabų kalba:
سَيَقُولُونَ لِلَّهِۚ قُلۡ فَأَنَّىٰ تُسۡحَرُونَ
Anena (kuti): “Ndi Allah.” Nena: “Nanga mukulodzedwa bwanji (ndi satana)?”
Tafsyrai arabų kalba:
بَلۡ أَتَيۡنَٰهُم بِٱلۡحَقِّ وَإِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ
Koma tawabweretsera choonadi; ndithu iwo ngabodza (potsutsana ndi choonadicho).
Tafsyrai arabų kalba:
مَا ٱتَّخَذَ ٱللَّهُ مِن وَلَدٖ وَمَا كَانَ مَعَهُۥ مِنۡ إِلَٰهٍۚ إِذٗا لَّذَهَبَ كُلُّ إِلَٰهِۭ بِمَا خَلَقَ وَلَعَلَا بَعۡضُهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۚ سُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ عَمَّا يَصِفُونَ
Allah sadadzipangire mwana, ndipo padalibe pamodzi ndi Iye mulungu (wina), ngati zikadakhala choncho ndiye kuti mulungu aliyense akadatenga zimene adalenga, ndipo milungu ina ikadaipambana milungu inzawo (polimbanirana ufumu), Allah wapatukana nazo kwambiri zimene akusimbazo.
Tafsyrai arabų kalba:
عَٰلِمِ ٱلۡغَيۡبِ وَٱلشَّهَٰدَةِ فَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Wodziwa zamseri ndi zapoyera; watukuka ku zimene akumphatikiza nazozo.
Tafsyrai arabų kalba:
قُل رَّبِّ إِمَّا تُرِيَنِّي مَا يُوعَدُونَ
Nena: “E Mbuye wanga! Ngati mungandionetse zomwe akulonjezedwa (ndikadali ndi moyo),
Tafsyrai arabų kalba:
رَبِّ فَلَا تَجۡعَلۡنِي فِي ٱلۡقَوۡمِ ٱلظَّٰلِمِينَ
E Mbuye wanga! Musandiyike m’gulu la anthu osalungama.”
Tafsyrai arabų kalba:
وَإِنَّا عَلَىٰٓ أَن نُّرِيَكَ مَا نَعِدُهُمۡ لَقَٰدِرُونَ
Ndipo ndithu Ife ndi Wokhoza kukuonetsa (chilango) chimene tikuwalonjeza.
Tafsyrai arabų kalba:
ٱدۡفَعۡ بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ ٱلسَّيِّئَةَۚ نَحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَصِفُونَ
Chotsa zoipa (zimene akukuchitira) powabwezera zabwino; Ife tikudziwa zimene akunena.
Tafsyrai arabų kalba:
وَقُل رَّبِّ أَعُوذُ بِكَ مِنۡ هَمَزَٰتِ ٱلشَّيَٰطِينِ
Ndipo nena: “E Mbuye wanga! Ndikudzitchinjiriza ndi Inu kumanong’onong’o a satana.”
Tafsyrai arabų kalba:
وَأَعُوذُ بِكَ رَبِّ أَن يَحۡضُرُونِ
“Ndiponso ndikudzitchinjiriza ndi inu Mbuye wanga kuti asandidzere.”
Tafsyrai arabų kalba:
حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَ أَحَدَهُمُ ٱلۡمَوۡتُ قَالَ رَبِّ ٱرۡجِعُونِ
Kufikira m’modzi wawo ikam’dzera imfa, amanena: “Mbuye wanga! Ndibwezereni (ku moyo wa pa dziko),”
Tafsyrai arabų kalba:
لَعَلِّيٓ أَعۡمَلُ صَٰلِحٗا فِيمَا تَرَكۡتُۚ كَلَّآۚ إِنَّهَا كَلِمَةٌ هُوَ قَآئِلُهَاۖ وَمِن وَرَآئِهِم بَرۡزَخٌ إِلَىٰ يَوۡمِ يُبۡعَثُونَ
“Kuti ndikachite zabwino pa zimene ndidasiya.” (Angelo amayankha kuti): “Iyayi! Ndithu awa ndi mawu basi amene iye akuyankhula (imfa ikamfika).” Ndipo patsogolo pawo pali chiyembekezo; (moyo wamasautso kwa oipa; ndipo wamtendere kwa abwino) kufikira tsiku limene adzaukitsidwa.
Tafsyrai arabų kalba:
فَإِذَا نُفِخَ فِي ٱلصُّورِ فَلَآ أَنسَابَ بَيۡنَهُمۡ يَوۡمَئِذٖ وَلَا يَتَسَآءَلُونَ
Choncho, lipenga likadzaimbidwa, sipadzakhala chibale pakati pawo tsiku limenelo, ndipo sadzafunsana.
Tafsyrai arabų kalba:
فَمَن ثَقُلَتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡمُفۡلِحُونَ
Tsono omwe mlingo (wa zochita zawo zabwino) udzalemere, iwowo ndiwo opambana.
Tafsyrai arabų kalba:
وَمَنۡ خَفَّتۡ مَوَٰزِينُهُۥ فَأُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فِي جَهَنَّمَ خَٰلِدُونَ
Ndipo omwe miyeso yawo (ya zochita zabwino) idzatsike, iwowo ndi omwe adadziluzitsa okha; adzakhala ku Jahannam nthawi yaitali.
Tafsyrai arabų kalba:
تَلۡفَحُ وُجُوهَهُمُ ٱلنَّارُ وَهُمۡ فِيهَا كَٰلِحُونَ
Moto ukawawula nkhope zawo, ndipo adzakhala m’menemo uku mano ali pamtunda.
Tafsyrai arabų kalba:
أَلَمۡ تَكُنۡ ءَايَٰتِي تُتۡلَىٰ عَلَيۡكُمۡ فَكُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ
(Adzauzidwa): “Kodi Ayah Zanga sizidali kuwerengedwa kwa inu ndipo inu nkumazitsutsa?”
Tafsyrai arabų kalba:
قَالُواْ رَبَّنَا غَلَبَتۡ عَلَيۡنَا شِقۡوَتُنَا وَكُنَّا قَوۡمٗا ضَآلِّينَ
Adzati: “Mbuye wathu! Zoipa zathu zidatigonjetsa, choncho tidali anthu osokera.”
Tafsyrai arabų kalba:
رَبَّنَآ أَخۡرِجۡنَا مِنۡهَا فَإِنۡ عُدۡنَا فَإِنَّا ظَٰلِمُونَ
Mbuye wathu! Titulutseni umu (m’moto ndikutibwezera ku dziko lapansi kuti tikachite ntchito yabwino); ngati titabwerezanso kuchita zoipa, ndiye kuti tidzakhaladi oipa (odziononga tokha).”
Tafsyrai arabų kalba:
قَالَ ٱخۡسَـُٔواْ فِيهَا وَلَا تُكَلِّمُونِ
(Allah) adzati: “Khalani chete m’menemo, monyozeka! Ndipo musandilankhule!”
Tafsyrai arabų kalba:
إِنَّهُۥ كَانَ فَرِيقٞ مِّنۡ عِبَادِي يَقُولُونَ رَبَّنَآ ءَامَنَّا فَٱغۡفِرۡ لَنَا وَٱرۡحَمۡنَا وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلرَّٰحِمِينَ
Ndithu mwa akapolo anga lidalipo gulu lomwe linkanena: “Mbuye wathu! Takhulupirira; choncho tikhululukireni ndi kutichitira chifundo; ndipo inu Ngabwino kwambiri kuposa (ena onse) ochita chifundo.”
Tafsyrai arabų kalba:
فَٱتَّخَذۡتُمُوهُمۡ سِخۡرِيًّا حَتَّىٰٓ أَنسَوۡكُمۡ ذِكۡرِي وَكُنتُم مِّنۡهُمۡ تَضۡحَكُونَ
“Koma inu mudawachita chipongwe kufikira adakuiwalitsani kundikumbuka uku muli kuwaseka.”
Tafsyrai arabų kalba:
إِنِّي جَزَيۡتُهُمُ ٱلۡيَوۡمَ بِمَا صَبَرُوٓاْ أَنَّهُمۡ هُمُ ٱلۡفَآئِزُونَ
“Ndithu Ine lero ndawalipira (Munda wamtendere) chifukwa cha kupirira kwawo; kuti ndithu iwo ndiwo opambana.”
Tafsyrai arabų kalba:
قَٰلَ كَمۡ لَبِثۡتُمۡ فِي ٱلۡأَرۡضِ عَدَدَ سِنِينَ
Adzanena: “Kodi mudakhala nthawi yotani padziko pa chiwerengero cha zaka?”
Tafsyrai arabų kalba:
قَالُواْ لَبِثۡنَا يَوۡمًا أَوۡ بَعۡضَ يَوۡمٖ فَسۡـَٔلِ ٱلۡعَآدِّينَ
Adzayankha: “Tidakhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku; afunse owerengera.” (Adzatero poyerekeza ndi kutalika kwa moyo wamasautso ku Moto).
Tafsyrai arabų kalba:
قَٰلَ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلٗاۖ لَّوۡ أَنَّكُمۡ كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
Adzanena: “Inu simudakhale (kudzikoko) koma pang’ono basi, mukadakhala mukudziwa (chilango chomwe chakufikanichi, sibwenzi mukuchita zoipa).”
Tafsyrai arabų kalba:
أَفَحَسِبۡتُمۡ أَنَّمَا خَلَقۡنَٰكُمۡ عَبَثٗا وَأَنَّكُمۡ إِلَيۡنَا لَا تُرۡجَعُونَ
Kodi mumaganiza kuti tidakulengani chabe, ndikuti simudzabwerera kwa Ife?
Tafsyrai arabų kalba:
فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ ٱلۡمَلِكُ ٱلۡحَقُّۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ رَبُّ ٱلۡعَرۡشِ ٱلۡكَرِيمِ
Watukuka Allah, Mfumu ya choonadi; palibe wompembedza mwachoonadi koma Iye, Bwana wa Arsh (Mpando wachifumu) yolemekezeka (kwambiri).
Tafsyrai arabų kalba:
وَمَن يَدۡعُ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ لَا بُرۡهَٰنَ لَهُۥ بِهِۦ فَإِنَّمَا حِسَابُهُۥ عِندَ رَبِّهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلۡكَٰفِرُونَ
Ndipo amene apembedza mulungu wina pomphatikiza ndi Allah, chikhalirecho iye alibe umboni pa zimenezo; basi chiwerengero chake chili kwa Mbuye wake. Ndithu osakhulupirira sangapambane.
Tafsyrai arabų kalba:
وَقُل رَّبِّ ٱغۡفِرۡ وَٱرۡحَمۡ وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلرَّٰحِمِينَ
Choncho nena: “Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndikundichitira Chifundo! Inu Ngabwino kuposa achifundo.”
Tafsyrai arabų kalba:
 
Reikšmių vertimas Sūra: Sūra Al-Mu’minūn
Sūrų turinys Puslapio numeris
 
Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Čevų k. vertimas - Vertimų turinys

Kilniojo Korano reikšmių vertimas į čevų k., išvertė Khaled Ibrahim Betala. 2020 m. leidimas.

Uždaryti