Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Čevų k. vertimas * - Vertimų turinys


Reikšmių vertimas Sūra: Sūra Al-Fath   Aja (Korano eilutė):

Sūra Al-Fath

إِنَّا فَتَحۡنَا لَكَ فَتۡحٗا مُّبِينٗا
Ndithu takugonjetsera (iwe Mtumiki{s.a.w}mzinda wa Makka) kugonjetsa kwakukulu koonekera poyera.[346]
[346] M’chaka cha chisanu ndi chimodzi chisamukire Mtumiki (s.a.w), Mtumiki (s.a.w) adapita ku Makka kuchokera ku Madina pamodzi ndi omtsatira ake kuti akachite Umrah imene ndi Hajj yaing’ono. Koma atayandikira ku Makka, Aquraish adamuletsa kulowa mu mzindamo kuti asachite mapemphero a Umrah. Ndipo atakambiranakambirana adamvana mfundo zingapo, zina mwa izo ndi:-
(i) Asamenyane nthawi imeneyo.
(ii) Abwelere ndipo adzabwere chaka chotsatiracho mwezi wonga umenewo kudzachita mapemphero. Panthawiyo sadzawaletsa kulowa mu mzindawo.
(iii) Asiye kumenyana pakati pawo kwa zaka khumi, ndi kumayenderana m’mene angafunire; Aquraish azipita ku Madina ngati atafuna, popanda kuzunzidwa.
(iv) Mafuko ena a Arabu adaloledwa kulowa nawo m’pangano limeneli kuti asamthire nkhondo Mtumiki (s.a.w), ndipo iyenso asawathire nkhondo.
Tafsyrai arabų kalba:
لِّيَغۡفِرَ لَكَ ٱللَّهُ مَا تَقَدَّمَ مِن ذَنۢبِكَ وَمَا تَأَخَّرَ وَيُتِمَّ نِعۡمَتَهُۥ عَلَيۡكَ وَيَهۡدِيَكَ صِرَٰطٗا مُّسۡتَقِيمٗا
Kuti Allah akukhululukire zolakwa zako zapatsogolo ndi zapambuyo, ndi kukukwaniritsira mtendere Wake, ndi kukuongolera kunjira yolunjika.
Tafsyrai arabų kalba:
وَيَنصُرَكَ ٱللَّهُ نَصۡرًا عَزِيزًا
Ndikuti Allah akuteteze ndi chitetezo champhamvu.
Tafsyrai arabų kalba:
هُوَ ٱلَّذِيٓ أَنزَلَ ٱلسَّكِينَةَ فِي قُلُوبِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ لِيَزۡدَادُوٓاْ إِيمَٰنٗا مَّعَ إِيمَٰنِهِمۡۗ وَلِلَّهِ جُنُودُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلِيمًا حَكِيمٗا
Iye ndiamene adatsitsa chikhazikiko (kudekha) m’mitima mwa okhulupirira kuti awonjezera chikhulupiliro pachikhulupiro chawo. Makamu ankhondo akumwamba ndi pansi, nga Allah, (monga angelo, ziwanda, nyama ziphaliwali, mphepo yamkuntho ndi zivomerezi ndi zina zotero); ndipo Allah Ngodziwa chilichonse, ndiponso Wanzeru zakuya.
Tafsyrai arabų kalba:
لِّيُدۡخِلَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَا وَيُكَفِّرَ عَنۡهُمۡ سَيِّـَٔاتِهِمۡۚ وَكَانَ ذَٰلِكَ عِندَ ٱللَّهِ فَوۡزًا عَظِيمٗا
(Wachita izi) kuti okhulupirira aamuna ndi aakazi akawalowetse m’minda yomwe pansi pake ikuyenda mitsinje; adzakhala nthawi yaitali mmenemo, ndi kuti awafafanizire zolakwa zawo; kumeneko, kwa Allah ndiko kupambana kwakukulu.
Tafsyrai arabų kalba:
وَيُعَذِّبَ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ وَٱلۡمُنَٰفِقَٰتِ وَٱلۡمُشۡرِكِينَ وَٱلۡمُشۡرِكَٰتِ ٱلظَّآنِّينَ بِٱللَّهِ ظَنَّ ٱلسَّوۡءِۚ عَلَيۡهِمۡ دَآئِرَةُ ٱلسَّوۡءِۖ وَغَضِبَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡ وَلَعَنَهُمۡ وَأَعَدَّ لَهُمۡ جَهَنَّمَۖ وَسَآءَتۡ مَصِيرٗا
Ndi kuti awalange achiphamaso aamuna ndi aakazi ndi omphatikiza Allah aamuna ndi aakazi oganizira Allah maganizo achabe. Kutembenuka koipa kuli kwa iwo ndipo Allah wawakwiyira ndiponso wawatembelera ndi kuwakonzera Jahannamu. Ndipo kumeneko nkobwerera koipa.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلِلَّهِ جُنُودُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمًا
Ndipo magulu ankhondo akumwamba ndi pansi nga Allah; ndipo Allah ndi Wamphamvu zoposa, Wa nzeru zakuya.
Tafsyrai arabų kalba:
إِنَّآ أَرۡسَلۡنَٰكَ شَٰهِدٗا وَمُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا
Ndithu takutumiza kuti ukhale mboni ndi wolengeza nkhani zabwino ndiponso mchenjezi.
Tafsyrai arabų kalba:
لِّتُؤۡمِنُواْ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ وَتُعَزِّرُوهُ وَتُوَقِّرُوهُۚ وَتُسَبِّحُوهُ بُكۡرَةٗ وَأَصِيلًا
Ncholinga choti mumkhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kuti mumtukule ndi kumulemekeza (Mtumiki) ndi kutinso mumtamande (Allah) m’mawa ndi madzulo.
Tafsyrai arabų kalba:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُبَايِعُونَكَ إِنَّمَا يُبَايِعُونَ ٱللَّهَ يَدُ ٱللَّهِ فَوۡقَ أَيۡدِيهِمۡۚ فَمَن نَّكَثَ فَإِنَّمَا يَنكُثُ عَلَىٰ نَفۡسِهِۦۖ وَمَنۡ أَوۡفَىٰ بِمَا عَٰهَدَ عَلَيۡهُ ٱللَّهَ فَسَيُؤۡتِيهِ أَجۡرًا عَظِيمٗا
Ndithu amene akukulonjeza, ndiye kuti akulonjeza Allah. Dzanja la Allah lili pamwamba pa manja awo. Amene ati aswe lonjezo, ndiye kuti wadziswera yekha (mavuto ali pa iye). Koma yemwe akwaniritse zomwe adalonjeza kwa Allah, amulipira malipiro aakulu.
Tafsyrai arabų kalba:
سَيَقُولُ لَكَ ٱلۡمُخَلَّفُونَ مِنَ ٱلۡأَعۡرَابِ شَغَلَتۡنَآ أَمۡوَٰلُنَا وَأَهۡلُونَا فَٱسۡتَغۡفِرۡ لَنَاۚ يَقُولُونَ بِأَلۡسِنَتِهِم مَّا لَيۡسَ فِي قُلُوبِهِمۡۚ قُلۡ فَمَن يَمۡلِكُ لَكُم مِّنَ ٱللَّهِ شَيۡـًٔا إِنۡ أَرَادَ بِكُمۡ ضَرًّا أَوۡ أَرَادَ بِكُمۡ نَفۡعَۢاۚ بَلۡ كَانَ ٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ خَبِيرَۢا
Adzanena kwa iwe Arabu am’midzi otsala (ku nkhondo, amene adalibe zifukwa zomveka m’kutsala kwawo): “Chuma ndi ana athu zidatitangwanitsa; choncho tipemphereni chikhululuko.” Akunena ndi malirime awo (mawu) omwe m’mitima mwawo mulibe. Nena: “Kodi ndani angathe kukuthandizani chilichonse kwa Allah ngati atafuna kukupatsani masautso, kapena atafuna kukupatsani zabwino? Koma Allah Akudziwa zonse zimene mukuchita.”
Tafsyrai arabų kalba:
بَلۡ ظَنَنتُمۡ أَن لَّن يَنقَلِبَ ٱلرَّسُولُ وَٱلۡمُؤۡمِنُونَ إِلَىٰٓ أَهۡلِيهِمۡ أَبَدٗا وَزُيِّنَ ذَٰلِكَ فِي قُلُوبِكُمۡ وَظَنَنتُمۡ ظَنَّ ٱلسَّوۡءِ وَكُنتُمۡ قَوۡمَۢا بُورٗا
“Koma mudali kuganiza kuti Mtumiki ndi okhulupirira sabwereranso ku maanja awo, (akaphedwa konko); zimenezo zidakukondweretsani m’mitima mwanu, ndipo mumaganiza ganizo loipa; ndipo mudali anthu oonongeka.”
Tafsyrai arabų kalba:
وَمَن لَّمۡ يُؤۡمِنۢ بِٱللَّهِ وَرَسُولِهِۦ فَإِنَّآ أَعۡتَدۡنَا لِلۡكَٰفِرِينَ سَعِيرٗا
Ndipo amene sakhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu Ife tawakonzera okanira chilango cha Moto woyaka.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ يَغۡفِرُ لِمَن يَشَآءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَآءُۚ وَكَانَ ٱللَّهُ غَفُورٗا رَّحِيمٗا
Ndipo ufumu wakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Amakhululukira amene wamfuna (ngati atatembenukira kwa Iye) ndi kumlanga amene wamfuna (ngati sanatembenukire kwa Iye). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.
Tafsyrai arabų kalba:
سَيَقُولُ ٱلۡمُخَلَّفُونَ إِذَا ٱنطَلَقۡتُمۡ إِلَىٰ مَغَانِمَ لِتَأۡخُذُوهَا ذَرُونَا نَتَّبِعۡكُمۡۖ يُرِيدُونَ أَن يُبَدِّلُواْ كَلَٰمَ ٱللَّهِۚ قُل لَّن تَتَّبِعُونَا كَذَٰلِكُمۡ قَالَ ٱللَّهُ مِن قَبۡلُۖ فَسَيَقُولُونَ بَلۡ تَحۡسُدُونَنَاۚ بَلۡ كَانُواْ لَا يَفۡقَهُونَ إِلَّا قَلِيلٗا
Otsala (kunkhondo) aja, mukapita kukatenga zotola za a nkhondo, adzanena: “Tiloleni tikutsatireni.” Akufuna kuti asinthe mawu a Allah. Nena: “Simutitsatira! Umo ndimo Allah adanenera kale.” (Apo) adzanena (kuti): “Koma mukutichitira dumbo.” Iyayi, koma nzochepa zomwe adali kuzindikira.
Tafsyrai arabų kalba:
قُل لِّلۡمُخَلَّفِينَ مِنَ ٱلۡأَعۡرَابِ سَتُدۡعَوۡنَ إِلَىٰ قَوۡمٍ أُوْلِي بَأۡسٖ شَدِيدٖ تُقَٰتِلُونَهُمۡ أَوۡ يُسۡلِمُونَۖ فَإِن تُطِيعُواْ يُؤۡتِكُمُ ٱللَّهُ أَجۡرًا حَسَنٗاۖ وَإِن تَتَوَلَّوۡاْ كَمَا تَوَلَّيۡتُم مِّن قَبۡلُ يُعَذِّبۡكُمۡ عَذَابًا أَلِيمٗا
Nena kwa otsala (kunkhondo) mwa Arabu a m’midzi: “Mudzaitanidwa (kukamenyana) ndi anthu eni mphamvu zaukali; mudzamenyana nawo kapena adzagonja (ndi kulowa m’Chisilamu). Ngati mudzamvera, Allah adzakulipirani malipiro abwino, koma ngati mutembenuka monga mudatembenukira kale adzakulangani ndi chilango chowawa.”
Tafsyrai arabų kalba:
لَّيۡسَ عَلَى ٱلۡأَعۡمَىٰ حَرَجٞ وَلَا عَلَى ٱلۡأَعۡرَجِ حَرَجٞ وَلَا عَلَى ٱلۡمَرِيضِ حَرَجٞۗ وَمَن يُطِعِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ يُدۡخِلۡهُ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ وَمَن يَتَوَلَّ يُعَذِّبۡهُ عَذَابًا أَلِيمٗا
Palibe tchimo pa wakhungu, palibenso tchimo pa olumala, palibenso tchimo pa wodwala (atasiya kupita ku nkhondo). Ndipo amene angamumvere Allah ndi Mtumiki Wake, adzam’lowetsa m’minda momwe mukuyenda mitsinje pansi pake; ndipo amene anyozere, amulanga ndi chilango chowawa.
Tafsyrai arabų kalba:
۞ لَّقَدۡ رَضِيَ ٱللَّهُ عَنِ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ إِذۡ يُبَايِعُونَكَ تَحۡتَ ٱلشَّجَرَةِ فَعَلِمَ مَا فِي قُلُوبِهِمۡ فَأَنزَلَ ٱلسَّكِينَةَ عَلَيۡهِمۡ وَأَثَٰبَهُمۡ فَتۡحٗا قَرِيبٗا
Ndithu Allah adawayanja okhulupirira pamene amagwirana nawe (Mtumiki) chanza pansi pa mtengo pomwe amakulonjeza (kuti adzamenya nkhondo mpaka imfa) Allah adadziwa zomwe zidali m’mitima mwawo ndipo adatsitsa pa iwo kukhazikika (ndi kudekha;) ndipo adawalipira kupambana kwapafupi.
Tafsyrai arabų kalba:
وَمَغَانِمَ كَثِيرَةٗ يَأۡخُذُونَهَاۗ وَكَانَ ٱللَّهُ عَزِيزًا حَكِيمٗا
Ndipo zofunkha zambiri za pa nkhondo adzazitenga; ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
Tafsyrai arabų kalba:
وَعَدَكُمُ ٱللَّهُ مَغَانِمَ كَثِيرَةٗ تَأۡخُذُونَهَا فَعَجَّلَ لَكُمۡ هَٰذِهِۦ وَكَفَّ أَيۡدِيَ ٱلنَّاسِ عَنكُمۡ وَلِتَكُونَ ءَايَةٗ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ وَيَهۡدِيَكُمۡ صِرَٰطٗا مُّسۡتَقِيمٗا
Allah wakulonjezani zofunkha zambiri zapankhondo (zomwe) mudzazitenga, ndipo wachita changu kukupatsani izi, (zinazo asanakupatseni). Ndipo watsekereza manja a anthu pa inu (kuti asakumenyeni). Ndi kuti chikhale chisonyezo cha okhulupirira (amene akudza pambuyo panu), ndi kuti akuongolereni kunjira yolunjika.
Tafsyrai arabų kalba:
وَأُخۡرَىٰ لَمۡ تَقۡدِرُواْ عَلَيۡهَا قَدۡ أَحَاطَ ٱللَّهُ بِهَاۚ وَكَانَ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٗا
Ndi zina zimene simudazithe (kuzipeza); Allah wazidziwa. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.
Tafsyrai arabų kalba:
وَلَوۡ قَٰتَلَكُمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لَوَلَّوُاْ ٱلۡأَدۡبَٰرَ ثُمَّ لَا يَجِدُونَ وَلِيّٗا وَلَا نَصِيرٗا
Ndipo akadayesa kumenyana nanu amene sadakhulupirire; akadatembenuza misana kuthawa; kenako sakadapeza mthandizi kapena mtetezi.
Tafsyrai arabų kalba:
سُنَّةَ ٱللَّهِ ٱلَّتِي قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلُۖ وَلَن تَجِدَ لِسُنَّةِ ٱللَّهِ تَبۡدِيلٗا
Iyi ndinjira ya Allah imene idapita kale, ndipo sungapeze kusintha pa njira ya Allah.
Tafsyrai arabų kalba:
وَهُوَ ٱلَّذِي كَفَّ أَيۡدِيَهُمۡ عَنكُمۡ وَأَيۡدِيَكُمۡ عَنۡهُم بِبَطۡنِ مَكَّةَ مِنۢ بَعۡدِ أَنۡ أَظۡفَرَكُمۡ عَلَيۡهِمۡۚ وَكَانَ ٱللَّهُ بِمَا تَعۡمَلُونَ بَصِيرًا
Ndipo Iye ndi amene adatsekereza manja awo pa inu; ndi manja anu pa iwo, pa chigwa cha Makka, pambuyo pokupambanitsani pa iwo. Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita.
Tafsyrai arabų kalba:
هُمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَصَدُّوكُمۡ عَنِ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ وَٱلۡهَدۡيَ مَعۡكُوفًا أَن يَبۡلُغَ مَحِلَّهُۥۚ وَلَوۡلَا رِجَالٞ مُّؤۡمِنُونَ وَنِسَآءٞ مُّؤۡمِنَٰتٞ لَّمۡ تَعۡلَمُوهُمۡ أَن تَطَـُٔوهُمۡ فَتُصِيبَكُم مِّنۡهُم مَّعَرَّةُۢ بِغَيۡرِ عِلۡمٖۖ لِّيُدۡخِلَ ٱللَّهُ فِي رَحۡمَتِهِۦ مَن يَشَآءُۚ لَوۡ تَزَيَّلُواْ لَعَذَّبۡنَا ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡهُمۡ عَذَابًا أَلِيمًا
Iwowo ndiamene sadakhulupirire, ndipo adakutsekerezani kulowa mu Msikiti Wopatulika pomwe nyama zansembe zidangomangika osakafika pamalo pake. Kukadakhala kuti kulibe amuna okhulupirira ndi akazi okhulupirira omwe simudawadziwe kuti mungawaponde potero inu kukanakupezani kudzudzulidwa kuchokera kwa iwo popanda kudziwa, (Allah akadakulolezani kumenyana nawo. Koma wachita izi) kuti Iye amulowetse ku mtendere Wake amene wamfuna. Akadadzipatula, tikadawalanga ndi chilango chowawa amene sadakhulupirire pakati pawo.
Tafsyrai arabų kalba:
إِذۡ جَعَلَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فِي قُلُوبِهِمُ ٱلۡحَمِيَّةَ حَمِيَّةَ ٱلۡجَٰهِلِيَّةِ فَأَنزَلَ ٱللَّهُ سَكِينَتَهُۥ عَلَىٰ رَسُولِهِۦ وَعَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ وَأَلۡزَمَهُمۡ كَلِمَةَ ٱلتَّقۡوَىٰ وَكَانُوٓاْ أَحَقَّ بِهَا وَأَهۡلَهَاۚ وَكَانَ ٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٗا
Pamene omwe sadakhulupirire adaika mkwiyo m’mitima, mkwiyo waumbuli, Allah adatsitsa chikhazikiko Chake ndi kudekha pa Mtumiki Wake ndi pa okhulupirira, ndipo adawalimbikitsa ndi mawu woopa Allah; ndipo adali eni mawuwo ndi oyenerana nawo. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.
Tafsyrai arabų kalba:
لَّقَدۡ صَدَقَ ٱللَّهُ رَسُولَهُ ٱلرُّءۡيَا بِٱلۡحَقِّۖ لَتَدۡخُلُنَّ ٱلۡمَسۡجِدَ ٱلۡحَرَامَ إِن شَآءَ ٱللَّهُ ءَامِنِينَ مُحَلِّقِينَ رُءُوسَكُمۡ وَمُقَصِّرِينَ لَا تَخَافُونَۖ فَعَلِمَ مَا لَمۡ تَعۡلَمُواْ فَجَعَلَ مِن دُونِ ذَٰلِكَ فَتۡحٗا قَرِيبًا
Ndithu Allah adamtsimikizira Mtumiki Wake za maloto ake owona: “Ndithu inu mudzalowa mu Msikiti Wopatulika mwamtendere Allah akafuna; mutameta mitu yanu mpala kapena (ena) kuyepula (tsitsi lawo), simudzaopa (nthawi imeneyo); ndipo Allah amadziwa zimene simumazidziwa, ndipo zisanapezeke zimenezo, akupatsani kupambana kumene kuli pafupi.
Tafsyrai arabų kalba:
هُوَ ٱلَّذِيٓ أَرۡسَلَ رَسُولَهُۥ بِٱلۡهُدَىٰ وَدِينِ ٱلۡحَقِّ لِيُظۡهِرَهُۥ عَلَى ٱلدِّينِ كُلِّهِۦۚ وَكَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدٗا
Iye ndi Yemwe adatumiza Mtumiki Wake ndi chiongoko ndi chipembedzo choona kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse. Ndipo Allah akukwanira kukhala mboni (yake).
Tafsyrai arabų kalba:
مُّحَمَّدٞ رَّسُولُ ٱللَّهِۚ وَٱلَّذِينَ مَعَهُۥٓ أَشِدَّآءُ عَلَى ٱلۡكُفَّارِ رُحَمَآءُ بَيۡنَهُمۡۖ تَرَىٰهُمۡ رُكَّعٗا سُجَّدٗا يَبۡتَغُونَ فَضۡلٗا مِّنَ ٱللَّهِ وَرِضۡوَٰنٗاۖ سِيمَاهُمۡ فِي وُجُوهِهِم مِّنۡ أَثَرِ ٱلسُّجُودِۚ ذَٰلِكَ مَثَلُهُمۡ فِي ٱلتَّوۡرَىٰةِۚ وَمَثَلُهُمۡ فِي ٱلۡإِنجِيلِ كَزَرۡعٍ أَخۡرَجَ شَطۡـَٔهُۥ فَـَٔازَرَهُۥ فَٱسۡتَغۡلَظَ فَٱسۡتَوَىٰ عَلَىٰ سُوقِهِۦ يُعۡجِبُ ٱلزُّرَّاعَ لِيَغِيظَ بِهِمُ ٱلۡكُفَّارَۗ وَعَدَ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ مِنۡهُم مَّغۡفِرَةٗ وَأَجۡرًا عَظِيمَۢا
Muhammad (s.a.w) ndi Mtumiki wa Allah; ndipo amene ali pamodzi ndi iye ngamphamvu kwa osakhulupirira (Allah), ngachifundo chambiri pakati pawo. Uwaona akugwira m’maondo ndi kugwetsa nkhope zawo pansi ncholinga chofuna zabwino za Allah ndi chikondi (Chake). Zizindikiro zawo zili pa nkhope zawo zosonyeza kulambira kwawo. Ili ndi fanizo lawo m’Chipangano chakale, Ndipo fanizo lawo m’Chipangano chatsopano nkuti iwo ali monga mmera womwe watulutsa nthambi zake; kenako (nthambizo) nkuulimbitsa ndi kukhala waukulu ndi kuima bwinobwino ndi tsinde lake, nkuwasangalatsa omwe adaubzala. (Choncho) zotsatira zake, nkuwakwiyitsa osakhulupirira chifukwa cha iwo. Allah walonjeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa) amene akhulupirira ndi kuchita zabwino mwa iwo.
Tafsyrai arabų kalba:
 
Reikšmių vertimas Sūra: Sūra Al-Fath
Sūrų turinys Puslapio numeris
 
Kilniojo Korano reikšmių vertimas - Čevų k. vertimas - Vertimų turinys

Kilniojo Korano reikšmių vertimas į čevų k., išvertė Khaled Ibrahim Betala. 2020 m. leidimas.

Uždaryti