۞ Ndithu Allah wamva mawu a (mkazi) amene akubwezeranabwezerana nawe (mawu) pa za mwamuna wake (amene adamsala); ndipo akusuma kwa Allah. Ndipo Allah akumva kukambirana kwanu; ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya (chilichonse).[347]
[347] Arabu adali ndi chizolowezi chakupatukana ndi mkazi ponena mawu akuti: “Ndikukuyerekeza ngati mayi wanga.” Choncho amangokhala naye mkazi uja, osamkhudza ndiponso osamulola kuti akwatiwe ndi mwamuna wina. Samamchitiranso zimene munthu amachitira mkazi wake monga kumveka ndi kumdyetsa. Msilamu wina adamsiya mkazi masiyidwe onga amenewa ndipo mkazi uja adapita kukakambirana naye Mtumiki (s.a.w). Choncho Chisilamu chidaletsa machitidwe onga amenewa.
Ndipo amene akuwafanizira akazi awo (ndi amayi awo) kenako nkubweza zimene adanena, apereke ufulu kwa kapolo asanakhale malo amodzi (ndi mkaziyo). Amenewa ndi malamulo a Allah kwa inu (amene) mukuchenjezedwa nawo. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita (zoonekera poyera ndi zosaonekera choncho sungani malamulo amene Allah wakhazikitsa pa inu).
Ndipo amene sadapeze (kapolo) asale miyezi iwiri yondondozana asadakhalirane pamodzi (ndi mkaziyo), koma amene sadathe kusala adyetse masikini makumi asanu ndi limodzi (60). Izi (zalamulidwa) kuti mukhulupirire mwa Allah ndi Mthenga Wake. Amenewo ndiwo malire a Allah; (malamulo okhazikitsidwa ndi Allah choncho musawalumphe). Ndipo chilango chopweteka chili pa osakhulupirira.
(Kumbuka) tsiku limene Allah adzaukitsa akufa onse ndi kuwafotokozera zimene adachita (pa moyo wa dziko lapansi: zoipa ndi zabwino); Allah adazisunga mozilemba koma iwo adaziiwala. Ndipo Allah ndi mboni wa zonse (palibe chingabisike kwa Iye).
Kodi sukudziwa (iwe, womvera wanzeru) kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zam’dziko lapansi? Sipakhala manong’onong’o a (anthu) atatu koma Iye Ngwachinayi wawo (ndi kudziwa kwake kosabisika chilichonse cha kumwamba ndi m’dziko), ngakhale a (anthu) asanu koma Iye Ngwachisanu ndi chimodzi wawo (mkudziwa Kwake), ngakhale ali ochepera kuposera pamenepa kapena ochulukira koma Iye ali nawo paliponse pomwe ati akhale (Allah ali nawo pamodzi mukudziwa Kwake kosabisika chilichonse), kenako adzawafotokozera pa tsiku la chiweruziro zimene adachita; ndithu Allah Ngodziwa chilichonse (mokwanira).[348]
[348] M’ndime iyi, Allah akutichenjeza kuti pamene tikuchita kalikonse tisamaganizire kuti Allah sakutiona. Palibe chimene chingabisike kwa Allah cha m’dziko lapansi kapena kumwamba; m’zoyankhula kapena m’zochitachita.
E inu amene mwakhulupirira! Ngati mukunong’onezana, musamanong’onezane za machimo ndi mtopola ndi kunyoza Mtumiki; koma nong’onezanani za kulungama ndi kuopa Allah ndipo muopeni Allah, kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwe (ndi kuweruzidwa).
E inu amene mwakhulupirira! Kukapemphedwa kwa inu kuti perekani malo pabwalo (pokhala), perekani malowo (kuti anzanu apeze pokhala; mukatero) Allah akuphanulirani (chifundo Chake pano pa dziko ndi kumwamba). Ndipo kukanenedwa kuti imilirani, muimilire (musanyozere, apatseni ena malo); Allah awakwezera (ulemelero) mwa inu amene akhulupirira ndi amene apatsidwa nzeru. Ndipo Allah akudziwa bwino zimene mukuchita.[350]
[350] Kuvumbulutsidwa kwa ndime iyi pali mawu akuti: Mtumiki (s.a.w) amaikira mtima kwambiri pa anthu amene adamenya nkhondo ya Badir; amgulu la Amuhajirina ndi Answari. Ndipo ena mwa iwowa adadza pa bwalo la Mtumiki ndi kupeza anthu ena atakhala kale adakhala chiimire chifukwa chosowa pokhala uku akuyembekezera kuti anzawo aja awapatseko pokhala; koma anthu adakhala kale aja sadalabadireko chilichonse. Mtumiki ataona izi zidamuwawa mu mtima ndipo adawauza omwe adakhala kale aja kuti aimilire apereke malo kwa anzawo. Achiphamaso adayamba kum’dzudzula Mtumiki (s.a.w) kuti bwanji akuchotsa anthu okhalakhala pamalo chifukwa cha anthu obwera mochedwa; sikupanda chilungamo kumeneko? Adatero achiphamaso aja. Ndipo poyankha zimenezi Allah adati: “E inu okhulupilira! Mukauzidwa kuti perekani malo kwa anzanu mupereke.” Ndipo mukauzidwa kuti imilirani, muimilire.”
M’ndime imeneyi Allah akutiphunzitsa kuti timvere Mtumiki (s.a.w) pa chilichonse chimene watilangiza popanda kuwiringula.
Kulumbira kwawo adakuchita kukhala chodzitetezera (iwo, ana awo ndi chuma chawo); choncho adatsekereza (anthu) ku njira ya Allah; choncho chilango choyalutsa chili pa iwo.[351]
Supeza anthu okhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro akukonda amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, ngakhale atakhala atate awo, ana awo abale awo ndi akumtundu wawo; kwa iwo (Allah) wazika chikhulupiliro (champhamvu) m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi mphamvu zochokera kwa Iye. Ndipo adzawalowetsa m’minda yomwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Allah adzakondwera nawo ndipo (iwonso) adzakondwera Naye. Iwowa ndi chipani cha Allah. Dziwani kuti chipani cha Allah ndichopambana.[352]
[352] M’ndime imeneyi Allah akunenetsa kuti: ‘‘Amene akukhulupilira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro, asapalane ubwenzi ndi munthu wodana ndi Allah ndi Mthenga Wake ngakhale wodana ndi Allah yo atakhala bambo wake, mwana wake ndi wina aliyense; apatukane nawo ndithu; chifukwa kupanda kutero akusonyeza kufooka kwa chikhulupiliro. Mtumiki (s.a.w) adati: “Munthu adzakhala ndi amene amamkonda pa tsiku la chiweruziro.”
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
Paieškos rezultatai:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".