Allah (ndimmodzi), palibe winanso wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye Yekha, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi kuteteza chilichonse.[60]
[60] Allah ndiyekhayo woti nkumpembedza. Palibe wina wompembedza mwa choonadi koma Iye basi. Padziko lonse lapansi ndi kumwamba palibe mwini mphamvu zoposa wogonjetsa chilichonse koma Iye Yekha basi. Iye ndiYemwe amadzetsa zabwino ndikubweretsa zoipa, osati wina aliyense. Iye Ngwamoyo wamuyaya, moyo wopanda chiyambi ndiponso wopanda malekezero. Iye Ngwachikhalire kuyendetsa zinthu za zolengedwa Zake. Thambo ndi nthaka adazikhazikitsa. Apa nkuti mneneri Isa (Yesu) asanamlenge. Choncho, Isa (Yesu) sali Mulungu koma ndimmodzi wa aneneri.
Kale, kuti (mabukuwo) akhale chotsogolera anthu. Ndipo adavumbulutsa (Qur’an) yolekanitsa pakati pa choonadi ndi chonama.[61] Ndithudi, aja amene sadakhulupirire zizindikiro za Allah, adzakhala ndi chilango chaukali. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wobwezera (chilango mwaukali).
[61] Tanthauzo la ndime iyi nkuti yakuvumbulukira iwe Muhammad (s.a.w) iyi Qur’an mwa choonadi popanda chipeneko kuti idachokera kwa Allah. Yatsika kupyolera mkudziwa kwake kuti itsimikizire zimene zidali m’mabuku a patsogolo pake. Ndipo pa zimenezi angelo ndimboni.
Iye ndi Yemwe amakulinganizani muli m’mimba mmaonekedwe anu mmene akufunira. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye; Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Iye ndi Yemwe wakuvumbulutsira buku (ili la Qur’an), lomwe mkati mwake muli ndime zomveka zomwe ndimaziko a bukuli. Ndipo zilipo zina zokuluwika. Koma amene m’mitima mwawo muli kusokera, akutsata zomwe zili zokuluwika ndi cholinga chofuna kusokoneza anthu, ndi kufuna kudziwa tanthauzo lake lenileni. Palibe amene akudziwa tanthauzo lake lenileni koma Allah basi. Koma amene azama pa maphunziro, amanena: “Tawakhulupirira (ma Ayah amenewa). Onse ngochokera kwa Mbuye wathu.” Ndipo palibe angakumbukire koma eni nzeru basi.
(Khalidwe la awa osakhulupiira, amumbadwo wako iwe mneneri Muhammad {s.a.w}, liri) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi amene adalipo pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa zisonyezo Zathu. Choncho, Allah adawakhaulitsa chifukwa cha machimo awo. Ndipo Allah Ngolanga mwaukali.
Auze amene sadakhulupirire: “Posachedwapa mugonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa ndi kuponyedwa ku Moto. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!”[62]
[62] Mawu adalandiridwa kuchokera kwa Saîd bun Jubair omwe iye adawalandiranso kuchokera kwa Ikrima pomwe nayenso Ikrima adawalandira kuchokera kwa Ibn Abbas (Allah asangalale nawo onse). Iye adati: “Ndithudi, Mtumiki (s.a.w) pamene adagonjetsa Aquraishi pa nkhondo ya Badri nabwerera ku Madina, adawasonkhanitsa Ayuda mu msika wa Bani Qainuqaa’ nawachenjeza kuti chingawapeze chomwe chidawapeza Aquraish. Iwo adati: “Usanyengedwe ndizimenezo. Ndithudi, iwe unakumana ndi mbuli za anthu zomwe sizidziwa kamenyedwe ka nkhondo. Ndipo nchifukwa chake wawagonjetsa. Ukadamenyana ndi ife ukadadziwa kuti ife ndife anthu.”
Pachifukwa ichi idavumbulutsidwa Ayah (ndime) yakuti: “Nena (kwa iwo iwe Muhammad {s.a.w}): “Inu Ayuda mugonjetsedwa posachedwapa pompano pa dziko lapansi. Chuma chanu ndi ana anu zisakunyengeni. Kupambana sikuli pa chifukwa cha kuchuluka kwanu, koma kuli m’manja mwa Allah Woyera.”
Mawuwa adatsimikizika powapha a Bani Nadhir ndi kugonjetsa mzinda wa Khaibar.
“Ndithudi, padapezeka chisonyezo chachikulu kwa inu m’magulu awiri omwe adakumana (tsiku la nkhondo ya Badri), pomwe gulu limodzi limamenya (nkhondo) pa njira ya Allah, pamene linalo lokanira, (ndipo gululo) linkawaona (Asilamu) kukhala ochuluka kawiri kuposa ilo, poona ndi maso awo. Ndipo Allah amamlimbikitsira mphamvu ndi chipulumutso chake amene wamfuna. Ndithudi, m’zimenezo muli malingaliro (akulu) kwa eni kupenyetsetsa mwanzeru.”
Kwakometsedwa kwa anthu kukonda zilakolako (za moyo wawo) monga akazi, ana, milumilu ya chuma cha golide ndi siliva, ndi mahachi oyang’aniridwa bwino, ziweto ndi mbewu. Izo ndi zosangalatsa za moyo wa dziko lapansi (zomwe sizili kanthu). Koma kwa Allah ndiko kuli mabwelero abwino.
Allah (Mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) angelo ndi eni nzeru (kuti Iye) Ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Allah ndi Chisilamu. Ndipo amene adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) sadatsutsane koma pambuyo powabwerera kuzindikira. (Adatsutsana) chifukwa cha dumbo lomwe lidali pakati pawo. Ndipo amene akukana zisonyezo za Allah, (Allah akamulanga pa tsiku la chiweruziro). Ndithu Allah Ngwachangu powerengera.
Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la buku (la Allah)? Akuitanidwa ku buku la Allah kuti liwaweruze pakati pawo; kenako gulu lina la iwo likutembenukira kumbali iwo ali onyoza.[63]
[63] Ndimeyi anthu omasulira Qur’an akuti ikufotokoza nkhani za Ayuda pamene adadza kwa Mtumiki (s.a.w), mmodzi mwa iwo atachita chiwerewere kuti amve chilamulo cha wochita chiwerewere. Mtumiki (s.a.w) anagamula kuti amugende ndi miyala mpaka afe. Koma iwo anakana. Nati: “M’buku lathu mulibe chilamulo chotere.” Ndipo adawauza kuti abwere nalo bukulo. Atabwera nalo anapeza kuti chilamulocho chilimo. Ndipo anawagenda miyala. Zitachitika tero, Ayuda anakwiya.
Asilamu asapale ubwenzi osakhulupirira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Allah, kupatula (kupalana nawo ubwenzi mwachiphamaso) chifukwa cha kudzitchinjiriza kwa iwo. Ndipo Allah Iye Mwini akukuchenjezani (za chilango Chake). Ndipo kobwerera ndi kwa Allah (basi).
Nena: (Iwe Mtumiki) “Ngati inu mukumkonda Allah, tsatani ine; Allah akukondani ndikukukhululukirani machimo anu. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.”[65]
[65] Kungonena chabe pakamwa kuti ndikumkonda mtumiki Muhammad (s.a.w) pomwe zochita zako nzosalingana ndi malangizo a mtumiki Muhammad (s.a.w), chikondi chotere chilibe phindu la mtundu uliwonse. Ngati Muhammad (s.a.w) tikumkondadi timumvere ndi kumuyesa chitsanzo chathu pa zochita zathu zonse.
(Kumbukirani) pamene adanena mkazi wa Imran (mayi wa Mariya), m’mapemphero ake): “Mbuye wanga! Ndapereka kwa Inu chimene chili m’mimba mwanga monga “waqf” (wotumikira m’kachisi Wanu). Tero landirani ichi kwa ine. Ndithudi, Inu ndinu Akumva, Wodziwa.”[67]
[67] (Ndime 35-36) Mkazi wa Imran pamene adali ndi pakati, ankaganiza kuti adzabereka mwana wa mwamuna. Ndipo adalonjeza kwa Allah kuti mwanayo adzampereka kuti akhale wotumikira ku msikiti wa Baiti Limakadasi (Yelusalemu), ndi kutinso adzatumikire pa zinthu zina za chipembedzo. Ntchito yake idzangokhala yokhayo. Koma mmalomwake adabereka mwana wamkazi. Ndipo kuti adzakhale mwana wabwino nkutinso adzabereke ana abwino, adamutcha dzina loti Mariya (wotumikira Allah). Tero mayi Mariya adali mayi wabwino. Ndipo nayenso adabala mwana wabwino yemwe ndi mneneri Isa (Yesu). Mariya ndi mayi wolemekezeka kwabasi.
Mwadzidzidzi, mngelo adamuitana uku iye ataimilira akupemphera mchipinda cha m’kachisi: “Allah akukuuza nkhani yabwino (yakuti ubereka mwana; dzina lake) Yahya yemwe adzakhala wotsimikizira (mneneri yemwe adzabadwa) ndi liwu lochokera kwa Allah, (yemwe ndi mneneri Isa (Yesu) amene adzakhalanso wolemekezeka ndi wolungama ndi mneneri wa mwa anthu abwino.”
Ndipo (kumbukira) pamene angelo adati: “E Iwe Mariya! Ndithudi, Allah wakusankha, wakuyeretsa ndipo wakulemekeza, mwa akazi onse amitundu ya anthu.”[70]
[70] Apa patchulidwa nkhani ya mayi Mariya pomwe mngelo adamuuza nkhani yabwinoyi.
(Kumbukira) pamene angelo adati: “E iwe Mariya! Ndithu Allah akukuuza nkhani yabwino (kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu) liwu lochokera kwa Iye (Allah, lakuti: “Bereka,” ndipo nkubereka popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa oyandikitsidwa kwa Allah.
“Ndipo (adzamchita kukhala) mneneri kwa ana a Israyeli (adzakhala akuwauza kuti): “Ine ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu kuti ndikuumbireni dongo ngati chithunzi chambalame, nkuuzira m’menemo nkukhaladi mbalame mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndichiritsa osapenya chibadwire, ndiwamaangamaanga (chinawa), ndi kuukitsa akufa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndikuuzani zomwe mudye ndi zimene musunge m’nyumba zanu. Ndithudi, m’zimenezi muli zizindikiro kwa inu ngati mulidi okhulupirira.”[71]
[71] Apa akunena zina mwa zozizwitsa zomwe mneneri Isa (Yesu) anadza nazo, ndipo zina mwa izo ndikuumba ndi dongo chifanizo cha mbalame. Kenako nkuchiuzira chikhaladi mbalame yamoyo mwa chilolezo cha Allah.
Koma pamene Isa (Yesu) adazindikira mwa iwo kusakhulupirira adati: “Ndani akhale athandizi anga kwa Allah (popitiriza kufalitsa Chipembedzo Chake)?” Ophunzira ake adati: “Ife ndife athandizi a Allah (pofalitsa Chipembedzo Chake). Takhulupirira Allah; ndipo ikira umboni kuti ife ndithu ndi odzipereka kwa Allah (Asilamu).”
Ndipo (Ayuda) adakonza chiwembu (chofuna kupha Isa (Yesu), koma Allah adachiwononga chiwembu chawocho. Allah Ngokhoza bwino zedi poononga ziwembu za anthu a chiwembu.
(Kumbukirani) pamene Allah adati: “Iwe Isa (Yesu)! Ine ndikukwaniritsira nyengo yako yokhala ndi moyo (Ayuda sachita kanthu kwa iwe). Ndipo ndikunyamulira kwa Ine ndiponso ndikuyeretsa kwa anthu osakhulupirira (omwe ndi adani ako). Ndipo amene akutsata (iwe) ndiwasankha kukhala apamwamba pa amene sadakhulupirire kufikira tsiku lachimaliziro. Kenako kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo ndidzaweruza pakati panu pa zomwe mudali kusiyana.
Ndithudi, fanizo la Isa (Yesu) kwa Allah lili ngati fanizo la Adam; adamulenga ndi dothi namuuza kuti: “Khala munthu.” Ndipo adakhaladi.[72]
[72] (Ndime 59-62) Ndime izi zidavumbulutsidwa pamene nthumwi za Chikhirisitu zidadza kwa Mtumiki (s.a.w) kuchokera ku Najirani. Iwowo adakangana ndi Mtumiki wa Allah pa nkhani ya Isa (Yesu). Iwo adati kwa Mtumiki wa Allah: “Bwanji iwe ukutukwana Mneneri wathu?” Iye adati: “Kodi ndikutukwana chotani?” Iwo adati: “Iwe ukuti iyeyo ndikapolo wa Allah.” Iye adati: “Inde. Iyeyo ndi kapolo wa Allah ndiponso mawu ake omwe adawaponya mwa namwali.’ Zitatero iwo adapsa mtima ndipo anakwiya nati: “Kodi iwe udamuonapo munthu wobadwa popanda tate? Ngati ukunenadi zoona tationetsa munthu wotere.” Apa mpomwe Allah adavumbulutsa ndime yakuti “Ndithudi, fanizo la Isa (Yesu) kwa Allah lili ngati fanizo la Adam”. Kenako anawaitanira ku Chisilamu. Iwo adati: “Tidalowa kale m’Chisilamu iwe usanadze.” Mtumiki (s.a.w) adati: “Mwanama. Pali zinthu zitatu zikukuletsani kulowa m’Chisilamu:
(a) Kunena kwanu mawu oti Allah wadzipangira mwana.
(b) Kudya kwanu nyama ya nkhumba.
(c) Kulambira kwanu mtanda.”
Pamene adapitiriza kumtsutsa mneneri Muhammad (s.a.w) adawapempha kuti atembelerane ponena kuti: “E Ambuye Mulungu! Mtembelereni ndi kumlanga amene akunena zabodza mwa ife pa nkhani ya Isa (Yesu)! Pompo Mtumiki (s.a.w) adasonkhanitsa anthu ake. Koma iwo atakhala upo adagwirizana kuti asalole kuopa kuti chilango chingawatsikire. Potero zidadziwika kwa anthu kuti iwo ngabodza.
Tsopano amene akutsutsana nawe (iwe Mtumiki s.a.w) pa ichi pambuyo pokudzera kuzindikira, auze: “Bwerani tiitane ana athu ndi ana anu, akazi athu ndi akazi anu, ife ndi inu; kenako modzichepetsa tipemphe tembelero la Allah kuti likhale pa amene ali abodza (mwa ife).”
Nena: “Inu eni buku (la Allah, Ayuda ndi Akhrisitu!) Idzani ku liwu lolingana pakati pathu ndi inu (lakuti) tisapembedze aliyense koma Allah (Mmodzi Yekha), ndiponso tisamphatikize ndi chilichonse ndipo ena mwa ife asawasandutse anzawo kukhala milungu m’malo mwa Allah.” Ngati atembenuka ndi kunyoza, nenani: “Ikirani umboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera malamulo a Allah).”
Ndithu anthu omwe ali oyenera kudzilumikiza ndi Ibrahim ndi amene adamutsata (m’nyengo yake) ndi Mtumiki uyu (Muhammad {s.a.w}) ndi amene amkhulupirira (Mtumikiyu). Ndipo Allah ndi Mtetezi wa okhulupirira.
Ndipo musakhulupirire aliyense kupatula yekhayo yemwe watsata chipembedzo chanu. (Allah adauza Mtumiki {s.a.w}), nena: “Ndithudi, chiongoko chenicheni ndi chiongoko cha Allah basi.” (Amene adapatsidwa buku Adanena kwa anzawo: “Musakhulupirire) kuti angapatsidwe aliyense zofanana ndi zomwe mwapatsidwa inu (Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti angakutsutseni kwa Mbuye wanu.” (Allah adati kwa mtumiki{s.a.w}), nena: “Ndithu zabwino zonse zili m’manja mwa Allah; amazipereka kwa yemwe wamfuna. Allah ndi Mataya, Ngodziwa.”
Ndipo mwa iwo muli anthu ena oti ukawasungitsa milumilu ya chuma, akubwezera. Ndipo mwa iwo muli ena oti ukawasungitsa “dinar” (ndalama imodzi) sangakubwezere pokhapokha upitirize kwa iye kuimilira (kulonjelera). Izi nchifukwa chakuti amanena: “Palibe njira pa ife (yotidzudzulira) chifukwa chozibera mbulizi.” Koma akumnamizira Allah uku iwo akudziwa.
Ndipo ndithu mwa iwo muli gulu lomwe likukhotetsa malirime awo (powerenga) buku kuti muwaganizire (mawu awowo) kuti ndi a m’buku la Allah); pomwe si a m’buku (la Allah). Ndipo akunena: “Izi zachokera kwa Allah.” Pomwe zimenezo sizinachokere kwa Allah; ndipo akumnamizira Allah uku akudziwa.
Sikoyenera kwa munthu yemwe Allah wampatsa buku ndi chiweruzo ndi uneneri, kenako nanena kwa anthu: “Khalani opembedza ine, mmalo mwa Allah.” Koma (awauze): “Khalani opembedza Allah, anzeru, aluntha chifukwa choti mukuphunzitsa buku ndi chifukwanso cha zomwe mukaphunzira.”
Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adatenga lonjezo kwa aneneri, (n’kuwauza): “Ndikakupatsani buku ndi nzeru, nakudzerani Mtumiki wotsimikizira zomwe zili pamodzi ndi inu, mudzamkhulupirire ndi kumthangata.” (Allah) adatinso: “Kodi mwavomereza ndi kulandira pa zimenezi pangano langali?” (Iwo) adati: “Tavomereza.” (Iye) adati: “Tsono chitirani umboni, ine ndili pamodzi nanu mwa oikira umboni.”
Kodi akufuna chipembedzo chomwe si cha Allah pomwe chinthu chilichonse chili kumwamba ndi pansi chikugonjera Iye, mofuna kapena mosafuna? Ndipo onse adzabwezedwa kwa Iye.
Nena: “Takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa pa ife, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, ndi Ismail, Ishâq ndi Yaqub ndi zidzukulu (zake), ndi zimene adapatsidwa Mûsa ndi Isa (Yesu), ndi aneneri (ena) zochokera kwa Mbuye wawo. Sitisiyanitsa aliyense pakati pawo, ndipo ife kwa Iye ndi Asilamu (odzipereka kwathunthu).”
Ndithudi amene sadakhulupirire, nkumwalira pamene ali osakhulupirira, sikudzalandiridwa kwa aliyense wa iwo ngakhale atapereka dipo la golide lodzadza dziko lonse. Iwo ndi omwe adzalandire chilango chopweteka, ndipo sadzakhala ndi athandizi.
Zakudya zonse zidali zololedwa kwa ana a Israyeli kupatula chimene adadziretsa Israyeli mwini wake Taurat isadavumbulutsidwe. Nena: “Bwerani ndi Tauratiyo ndipo iwerengeni ngati mukunena zoona.”[74]
[74] Ayuda adauza Mtumiki (s.a.w) kuti: “Iwe sukutsata chikhalidwe cha Ibrahim ngakhale umadzinyenga kuti ukumtsata. Nanga bwanji ukudya nyama ya ngamira, pomwe mneneri Ibrahim sadali kudya ngamira?” Apa Allah akuwatsutsa kuti ngabodza. Ndipo buku lawo la Taurat ndilo mboni pa bodza lawoli. atavundukula buku lawo la Taurat apeza kuti yemwe adadziletsa kudya ngamira ndi Yakobo, yemwe ankadziwikanso kuti Israeli, osati mneneri Ibrahim.Yakobo njemwe adasala kudya nyama ya ngamira mwa chifuniro chake. Ndipo izi adazichita popanda kukakamizidwa ndi Allah.
Ndithudi, nyumba yoyamba yomwe idakhazikitsidwa chifukwa cha anthu (kuti azipempheramo) ndiyomwe ili pa Bakka (ku Makka); yodalitsidwa ndiponso ndichiongolo kwa anthu onse.[75]
[75] Apa akunenetsa kuti nyumba yoyamba kukhazikitsidwa kwa anthu kuti ikhale yochitira mapemphero ndi Al-Kaaba, osati Baiti Muqaddas monga momwe Ayuda amakhulupilira.
Kodi mukukanira bwanji pomwe ndime za Allah zikuwerengedwa kwa inu, pomwenso Mtumiki Wake ali pamodzi nanu? Ndipo amene agwiritse mwa Allah (bwinobwino), ndithudi iye wawongoleredwa kunjira yoongoka.
Ndipo gwiritsani chingwe (chipembedzo) cha Allah nonsenu, ndipo musagawikane. Kumbukirani mtendere wa Allah womwe uli pa inu; pamene mudali odana ndipo Iye adalunzanitsa pakati pa mitima yanu, tero mwa mtendere Wake mudakhala abale; ndipo mudali m’mphepete mwa dzenje la moto (wa Jahanama), ndipo Iye adakupulumutsanimo. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah Ake (ndime Zake) kuti muongoke.[77]
[77] Ndime izi zikuwauza Asilamu onse kuti akhale ogwirizana pamodzi m’dzina lachipembedzo chawo cha Chisilamu. Asapatukane popatsana maina atsopano kapena kuti awa akuchokera ku dziko lakutilakuti, awa ngamtundu wakutiwakuti. Kuchita zimenezo nkulakwa kwambiri. Koma pakati pa Asilamu pakhale chimvano.
Inu (Asilamu) ndinu gulu labwino limene lasankhidwa kwa anthu. Mukulamula (kuchita) zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa Allah. Ndipo aja adapatsidwa buku akadakhulupirira monga momwe (adawalamulira) kukadakhala kwabwino kwa iwo. (Koma) mwa iwo alipo okhulupirira pomwe ambiri mwa iwo ngopandukira (chilamulo cha Allah).[78]
[78] Apa akutchula zifukwa zomwe chipembedzo cha Chisilamu chapambanira zipembedzo zina. Tero tiyeni tigwirizane ndizimenezi kuti tikhaledi opambana.
Amakhulupirira Allah ndi lsiku lomaliza; ndipo amalamulira (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa; ndipo amachita changu pa zinthu zabwino. Ndipo iwo ndi omwe ali mwa anthu abwino.
Ndithudi, amene sakhulupirira, chuma chawo ngakhale ana awo, sizidzawathandiza chilichonse kwa Allah. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto basi; adzakhala mmenemo nthawi yaitali.
Fanizo la chimene akupereka mwaulere pa moyo uwu wa dziko lapansi, chili ngati mphepo yomwe mkati mwake muli chisanu chaukali, chagwera pa munda wa anthu omwe adadzichitira okha zoipa, n’kuuonongeratu. Si Allah amene adawachitira zoipa, koma iwo okha adadzichitira zoipa.[80]
[80] Tsono amene savomereza Allah potsatira malamulo ake ndi kusiya zomwe lye adaletsa, ngakhale atachita zabwino zotani sakamlipira pa tsiku lachimaliziro. Ngati nkofunika kuti amulipire, ndiye kuti amulipiliratu pompano pa dziko lapansi.
(Kumbukira) pamene unachoka m’mawa kusiya banja lako kuti uwakonzere Asilamu malo omenyanira (nkhondo). Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa.[83]
[83] Apa akunena nkhani ya nkhondo yachiwiri yaikulu kwabasi pambiri ya Chisilamu, nkhondo ya Uhudi. Nkhondo imeneyi Asilamu adakumana ndi masautso akulu chifukwa cha Asilamu ena amene adaswa lamulo la Mtumiki (s.a.w). Ndiponso chifukwa cha anthu ena omwe adalowa Chisilamu mwachiphamaso, (achiphamaso) omwe adapita ku nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) koma adakathawa kunkhondoko. Ndipo adali ochuluka gawo limodzi mwa magawo atatu a Asilamu (1/3). Pothawapo adathawa ochuluka kuposa nambala yatchulidwayi. Koma ena mwa iwo adabwerera nkudzalumikizananso ndi gulu la nkhondo la Mtumiki (s.a.w).
(Kumbukira) pamene magulu awiri mwa inu anafunitsitsa kuti athawe (chifukwa cha mantha monga momwe adathawira achinyengo). Koma Allah adali Mtetezi wa magulu awiriwo. (Choncho adawasunga kuti asathawe). Ndipo okhulupirira ayadzamire kwa Allah Yekha basi.
Allah adakupulumutsani pa (nkhondo) ya Badri pomwe inu munali ofooka (chifukwa chakuchepa ndi kusakhala ndi zida zokwanira). Choncho opani Allah kuti mumthokoze (nthawi zonse pa zomwe akukuchitirani).
Ndipo Allah sadachite izi (potumiza angelo) koma kuti ukhale uthenga wabwino kwa inu ndi kuti pakutero mitima yanu ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo chithandizo sichichokera (kwa wina aliyense) koma kwa Allah basi, Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
E inu amene mwakhulupirira! Musadye Riba (chuma cha katapira), kumangoonjezeraonjezera. Ndipo opani Allah kuti mupambane.[86]
[86] Kuipa kwina kwa malonda a katapira (Riba) ndiko kuti amangoonjezeraonjezera mpaka kuchimaliza chuma chamnzakeyo momchenjelera. Ndipo nchifukwa chake m’ndime yachiwiriyi ya 131 akunenetsa kuti ngati sasiya mchitidwe wa katapira (Riba) ndi kubweza kwa eni zomwe adalandazo, moto wa Jahanama ukuwadikira.
Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe Allah asadawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo cha Allah mwa inu ndi kuwaonetseranso poyera opirira (pa nkhondo ya Allah)?
Muhammad (s.a.w) sali chinthu china koma Mtumiki chabe. Patsogolo pake adamuka atumiki ambiri. Kodi ngati atamwalira kapena kuphedwa, mungabwelerenso m’mbuyo? Ndipo amene abwelere m’mbuyo mwake savutitsa Allah ndi chilichonse; koma Allah adzalipira othokoza.[91]
[91] Apa akunena mwatsatanetsatane kuti Mneneri Muhammad (s.a.w) ndi mtumiki basi yemwe ndimunthu monga alili anthu ena onse. Adafa monga momwe ena adafera. Koma ngakhale iye wafa anthu ena atsanzire chikhalidwe chake ndi zophunzitsa zake zomwe amaphunzitsa. Asabwelere m’mbuyo kusiya Chipembedzo poona kuti iye wafa.
Tiponya mantha m’mitima mwa amene sadakhulupirire chifukwa chakumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadatsitsire umboni (wosonyeza umulungu wawo) ndipo malo awo adzakhala ku Moto. Taonani kuipitsitsa malo a anthu ochita zoipa.
Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira.[94]
[94] Apa akulongosola chifukwa chomwe Asilamu adapezera mavuto. Iwo adapeza mavuto chifukwa choswa lamulo la Mtumiki (s.a.w) lomwe adawalamula. Mtumiki (s.a.w) adaika pa phiri anthu makumi asanu (50) omwe adali akatswiri olasa mipaliro. Adawauza kuti asachokepo kuti ateteze gulu la Asilamu kuti adani asawamenye nkhondo powadzelera kumbuyo. Adanenetsa kwa iwo kuti asachoke pamalopo ngakhale ataona kuti anzawo akupambana kapena akugonja, kufikira Mtumiki atawalamula kuti achokepo. Koma ena mwa iwo adanyoza lamuloli pamene adaona kuti anzawo chammunsi mwa phirilo akupambana ndipo akuthamangitsa adani ndi kuwapha ndikumatola zotolatola za pankhondo. Choncho, iwo anatsika paphiripo nkusakanikirana ndi anzawo nayamba kutola nawo zotola zapankhondo. Mtsogoleri wawo adayesera umu ndi umu kuwaletsa koma sadamumvere kupatula ochepa okha amene adatsala pa phiripo. Pompo ngwazi zina za m’gulu la adani awowo zitaona kuti anthu omwe adali pa phiri achokapo, zidalitembenuza gulu lawo lankhondo nkuyamba kuwamenya Asilamu chakumbuyo. Potero ambiri adaphedwa ndi kuvulala.
Ndithudi, mwa inu amene adabwerera m’mbuyo (kuthawa) tsiku lomwe magulu awiri a nkhondo adakumana (pa nkhondo ya Uhudi; gulu la osakhulupirira ndi gulu lankhondo la Asilamu), satana ndiyemwe adawaterezetsa chifukwa cha zina (zolakwa) zomwe adachita; ndipo Allah (tsopano) wawakhululukira. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngoleza koposa.
Ndipo ngati mwaphedwa pa njira ya Allah, kapena kufa, (palibe chotaika kwa inu) pakuti chikhululuko ndi chisoni zochokera kwa Allah nzabwino kuposa zomwe akuzisonkhanitsa (pa moyo wa pa dziko lapansi).
Kodi amene akutsata chokondweretsa Allah angalingane ndi yemwe wabwerera ndi mkwiyo wochokera kwa Allah, ndipo Jahannam nkukhala malo ake? Taonani kuipa kumalo obwerera!
Ndithudi, Allah adawachitira ubwino waukulu okhulupirira powatumizira Mtumiki wochokera mwa iwo yemwe akuwawerengera ma Ayah ake (ndime zake) ndikuwayeretsa ndikuwaphunzitsa buku ndi (mawu a) nzeru. Ndithudi, kale adali mkusokera koonekera.[97]
[97] Apa Allah akukumbutsa Asilamu za chisomo chomwe adawapatsa pakuwapatsa Mtumiki, pomwe Mtumikiyo asanawadzere iwo adali anthu osokera. Koma kupyolera mwa Mtumikiyo akhala olungama.
Omwenso adauzidwa ndi anthu (olembedwa ganyu ndi Akafiri aku Makka) kuti: “Anthu Akusonkhanirani. Choncho aopeni.” Koma (zonenazo) zidawaonjezera chikhulupiliro (Asilamu). Ndipo adati: “Allah akutikwanira, ndipo Iye ndi Mtetezi wabwino koposa.”
Choncho adabwerera ndi chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah. Sichidawakhudze choipa chilichonse; adatsatira zokondweretsa Allah. Ndipo Allah ndimwini ubwino waukulu.
Ndithudi, amene asinthanitsa kusakhulupirira ndi chikhulupiliro, sangathe kumvutitsa Allah ndi chilichonse. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chopweteka.
Nkosatheka kwa Allah kusiya okhulupirira momwe mulilimu, mpaka atalekanitsa (pakati pawo) oipa ndi abwino. Ndipo nkosatheka kwa Allah kukudziwitsani zinthu zamseri, koma Allah amasankha mwa atumiki ake amene wamfuna (nkumdziwitsa zina mwa zimenezo). Choncho khulupirirani Allah ndi atumiki ake. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kuopa (Allah), pa inu padzakhala malipiro aakulu.[99]
Ndipo asaganize amene akuchitira umbombo zimene Allah wawapatsa kuchokera m’zabwino Zake kuti kutero ndibwino kwa iwo, koma kutero nkoipa kwa iwo. Adzanjatidwa magoli pa zomwe adazichitira umbombo pa tsiku lachimaliziro. Ndipo um’lowam’malo wa zakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita.[100]
[100] Apa Allah akuchenjeza mbombo kuti zisaone kutsekemera umbombo wawowo. Chuma akuchichitira umbombocho chidzasanduka njoka zomwe zidzawazunza kwambiri.
Ndipo ngati akutsutsa iwe (Mtumiki Muhammad (s.a.w}, sichachilendo) adatsutsidwanso atumiki patsogolo pako omwe adadza ndi zisonyezo zoonekera ndi mabuku anzeru, ndi mabukunso ounika.
Munthu aliyense adzalawa imfa. Ndithudi, mudzalipidwa malipiro anu mokwanira tsiku lachimaliziro. Ndipo amene adzatalikitsidwe ndi Moto nalowetsedwa ku Munda wamtendere, ndiye kuti wapambana, (kupambana kwakukulu), ndipo moyo wapadziko lapansi sulikanthu koma ndichisangalalo chonyenga basi.[104]
[104] Apa anthu akuwauza kuti achite zinthu molimbika zokawalowetsa ku Munda wa mtendere ndi kupewa kuchita zinthu zokawalowetsa ku Moto. Chifukwa anthu akaponyedwa ku Moto kupyolera m’zochita zawo zoipa.
Ndithu mudzayesedwa m’chuma chanu ndi miyoyo yanu; ndipo mudzamva masautso ambiri kuchokera kwa omwe adapatsidwa mabuku kale ndiponso kuchokera kwa omwe akuphatikiza Allah ndi zinthu zina (Arab), koma ngati mupirira ndi kudzisunga ku zomwe mwaletsedwa ndi Allah, (ndiye kuti mwachita chinthu chabwino kwambiri) pakuti zinthu izi (ndi zinthu zazikulu) zofunika munthu kuikirapo mtima.
Omwe amakumbukira Allah, ali chiimire, ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; namalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (mmene Allah adazilengera, uku akuti): “E Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe. Ulemelero Ngwanu. Tichinjirizeni ku chilango cha Moto.”
Ndithudi mwa amene adapatsidwa buku, alipo amene akukhulupirira Allah ndi zimene zavumbulutsidwa kwa inu, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa iwo, uku akudzichepetsa kwa Allah; sagulitsa ndime za Allah ndi mtengo wochepa (wa pa dziko lapansi). Iwo adzalandira malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndithudi, Allah Ngwachangu pakuwerengera.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
د لټون پایلې:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".