Check out the new design

د قرآن کریم د معناګانو ژباړه - چیچوایي ژباړه - خالد ابراهیم بتیالا * - د ژباړو فهرست (لړلیک)


د معناګانو ژباړه سورت: فصلت   آیت:
فَقَضَىٰهُنَّ سَبۡعَ سَمَٰوَاتٖ فِي يَوۡمَيۡنِ وَأَوۡحَىٰ فِي كُلِّ سَمَآءٍ أَمۡرَهَاۚ وَزَيَّنَّا ٱلسَّمَآءَ ٱلدُّنۡيَا بِمَصَٰبِيحَ وَحِفۡظٗاۚ ذَٰلِكَ تَقۡدِيرُ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡعَلِيمِ
Choncho adakwaniritsa kulenga thambo zisanu ndi ziwiri mmasiku awiri, ndipo thambo lililonse adalidziwitsa ntchito yake (polilamula zochita zake). Ndipo tidakongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi nyenyezi (zounikira dziko lapansi), ndiponso kuti zizilondera kumwamha (kuti ziwanda zisamapite kukamvera za kumwamba). Uwu ndi muyeso wa Mwini mphamvu, Wodziwa kwambiri.
عربي تفسیرونه:
فَإِنۡ أَعۡرَضُواْ فَقُلۡ أَنذَرۡتُكُمۡ صَٰعِقَةٗ مِّثۡلَ صَٰعِقَةِ عَادٖ وَثَمُودَ
Koma ngati anyozera (kukhulupirira), nena: “Ndikukuchenjezani za chilango monga chilango cha Âdi ndi Samud.”
عربي تفسیرونه:
إِذۡ جَآءَتۡهُمُ ٱلرُّسُلُ مِنۢ بَيۡنِ أَيۡدِيهِمۡ وَمِنۡ خَلۡفِهِمۡ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَۖ قَالُواْ لَوۡ شَآءَ رَبُّنَا لَأَنزَلَ مَلَٰٓئِكَةٗ فَإِنَّا بِمَآ أُرۡسِلۡتُم بِهِۦ كَٰفِرُونَ
Pamene aneneri adawadzera patsogolo pawo ndi pambuyo pawo (ndikuwauza): “Musapembedze (milungu ina), koma Allah,” adati: “Mbuye wathu akadafuna, akadatsitsa angelo (kudzatilalikira, osati anthu monga inu). Choncho ndithu ife tikuzikana zimene mwatumidwa nazozo.”
عربي تفسیرونه:
فَأَمَّا عَادٞ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَقَالُواْ مَنۡ أَشَدُّ مِنَّا قُوَّةًۖ أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ ٱلَّذِي خَلَقَهُمۡ هُوَ أَشَدُّ مِنۡهُمۡ قُوَّةٗۖ وَكَانُواْ بِـَٔايَٰتِنَا يَجۡحَدُونَ
Tsono Âdi adadzikweza pa dziko mosayenera, ndipo adati: “Ndani wamphamvu kuposa ife?” Kodi saona kuti Allah Yemwe adawalenga ndi Mwini mphamvu zambiri kuposa iwo? Koma adapitiriza kukanira zozizwitsa Zathu.
عربي تفسیرونه:
فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِيحٗا صَرۡصَرٗا فِيٓ أَيَّامٖ نَّحِسَاتٖ لِّنُذِيقَهُمۡ عَذَابَ ٱلۡخِزۡيِ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَلَعَذَابُ ٱلۡأٓخِرَةِ أَخۡزَىٰۖ وَهُمۡ لَا يُنصَرُونَ
Choncho tidawatumizira mphepo ya mkuntho yozizira kwabasi mmasiku amatsoka, kuti tiwalawitse chilango chowasambula pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo chilango cha tsiku lachimaliziro ndi choyalutsa kwambiri; ndipo iwo sadzapulumutsidwa.
عربي تفسیرونه:
وَأَمَّا ثَمُودُ فَهَدَيۡنَٰهُمۡ فَٱسۡتَحَبُّواْ ٱلۡعَمَىٰ عَلَى ٱلۡهُدَىٰ فَأَخَذَتۡهُمۡ صَٰعِقَةُ ٱلۡعَذَابِ ٱلۡهُونِ بِمَا كَانُواْ يَكۡسِبُونَ
Naonso Asamudu tidawasonyeza (njira yabwino ndi njira yoipa), ndipo adakonda ndi kusankha kusokera kusiya chiongoko; ndipo udawapeza nkuwe wa chilango choyalutsa chifukwa cha machimo amene adali kuchita.
عربي تفسیرونه:
وَنَجَّيۡنَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَكَانُواْ يَتَّقُونَ
Koma tidawapulumutsa (ku chilango chimenechi) amene adakhulupirira ndipo anali kumuopa (Allah).
عربي تفسیرونه:
وَيَوۡمَ يُحۡشَرُ أَعۡدَآءُ ٱللَّهِ إِلَى ٱلنَّارِ فَهُمۡ يُوزَعُونَ
Ndipo (akumbutse, iwe Mtumiki), tsiku lomwe adani a Allah adzasonkhanitsidwa kunka nawo ku Moto, uku akukusidwa (onse, oyamba ndi omalizira),
عربي تفسیرونه:
حَتَّىٰٓ إِذَا مَا جَآءُوهَا شَهِدَ عَلَيۡهِمۡ سَمۡعُهُمۡ وَأَبۡصَٰرُهُمۡ وَجُلُودُهُم بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Kufikira pomwe adzaufikira (Moto); makutu awo ndi maso awo ndi khungu lawo zidzawachitira umboni pa zomwe adali kuchita (pa dziko lapansi).
عربي تفسیرونه:
 
د معناګانو ژباړه سورت: فصلت
د سورتونو فهرست (لړلیک) د مخ نمبر
 
د قرآن کریم د معناګانو ژباړه - چیچوایي ژباړه - خالد ابراهیم بتیالا - د ژباړو فهرست (لړلیک)

خالد إبراهيم بيتالا ژباړلی دی.

بندول