Check out the new design

Përkthimi i kuptimeve të Kuranit Fisnik - Përkthimi çiçevë - Khalid Ibrahim Betiala * - Përmbajtja e përkthimeve


Përkthimi i kuptimeve Surja: El A’raf   Ajeti:
قَالَ ٱدۡخُلُواْ فِيٓ أُمَمٖ قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِكُم مِّنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِ فِي ٱلنَّارِۖ كُلَّمَا دَخَلَتۡ أُمَّةٞ لَّعَنَتۡ أُخۡتَهَاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا ٱدَّارَكُواْ فِيهَا جَمِيعٗا قَالَتۡ أُخۡرَىٰهُمۡ لِأُولَىٰهُمۡ رَبَّنَا هَٰٓؤُلَآءِ أَضَلُّونَا فَـَٔاتِهِمۡ عَذَابٗا ضِعۡفٗا مِّنَ ٱلنَّارِۖ قَالَ لِكُلّٖ ضِعۡفٞ وَلَٰكِن لَّا تَعۡلَمُونَ
(Allah) adzati (pa tsiku la chiweruziro): “Lowani ku Moto pamodzi ndi mibadwo imene idamuka kale (inu musanabwere) yochokera m’ziwanda ndi mu anthu. M’badwo uliwonse pamene uzikalowa, udzatembelera unzake, kufikira pamene onse adzasonkhana m’menemo. Adzanena apambuyo kwa oyambilira awo: “Mbuye wathu! Awa, adatisokeretsa. Apatseni chilango cha Moto chochuluka.” (Allah) adzanena: “Aliyense mwa inu akhala ndi chilango chochuluka; koma izi inu simukudziwa.”[183]
[183] Aliyense adzapeza chilango chachikulu. Ndipo awo amene adasokeretsedwa: (a) Adzapeza chilango chifukwa cholola kusokeretsedwa pomwe adapatsidwa nzeru zowazindikiritsa zabwino ndi zoipa. (b) Adzapeza chilango chifukwa chochita machimowo. Tsono amene adali kusokeretsa anzawo:
a) Adzapeza chilango chifukwa chakuchita kwawo machimo.
b) Adzapeza chilango chifukwa chakuwasokeretsa anthu omwe adawasokeretsa.
c) Adzapeza chilango chifukwa chakuyambitsa machimowo.
d) Adzapeza chilango chifukwa chowasiira anzawo odza m’mbuyo mwawo machimo powatsanzira iwo.
Tefsiret në gjuhën arabe:
وَقَالَتۡ أُولَىٰهُمۡ لِأُخۡرَىٰهُمۡ فَمَا كَانَ لَكُمۡ عَلَيۡنَا مِن فَضۡلٖ فَذُوقُواْ ٱلۡعَذَابَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡسِبُونَ
Ndipo oyamba awo adzati kwa otsiriza awo: “Inunso mudalibe ubwino woposa ife; choncho, lawani chilango cha zomwe mudapeza (m’zochitachita zanu).”
Tefsiret në gjuhën arabe:
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَٱسۡتَكۡبَرُواْ عَنۡهَا لَا تُفَتَّحُ لَهُمۡ أَبۡوَٰبُ ٱلسَّمَآءِ وَلَا يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ حَتَّىٰ يَلِجَ ٱلۡجَمَلُ فِي سَمِّ ٱلۡخِيَاطِۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡمُجۡرِمِينَ
Ndithudi, amene akutsutsa zivumbulutso Zathu nadzitukumula nazo (pakukana kuzitsata), sadzatsekulidwa kwa iwo makomo a kumwamba, ndipo sadzalowa ku Munda wamtendere mpaka ngamira idzalowe pa bowo la singano. Umo ndimomwe timawalipirira anthu ochimwa.
Tefsiret në gjuhën arabe:
لَهُم مِّن جَهَنَّمَ مِهَادٞ وَمِن فَوۡقِهِمۡ غَوَاشٖۚ وَكَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلظَّٰلِمِينَ
Moto wa Jahannam ndi mphasa yawo; ndipo pamwamba pawo adzakhala ndi (chofunda cha Moto) chowaphimba. Umo ndimomwe Tikuwalipirira anthu osalungama.
Tefsiret në gjuhën arabe:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ لَا نُكَلِّفُ نَفۡسًا إِلَّا وُسۡعَهَآ أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Ndipo amene akhulupirira ndikumachita zabwino, sitikakamiza munthu aliyense koma chimene angachithe, awo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo iwo akakhala nthawi yaitali.
Tefsiret në gjuhën arabe:
وَنَزَعۡنَا مَا فِي صُدُورِهِم مِّنۡ غِلّٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهِمُ ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ وَقَالُواْ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي هَدَىٰنَا لِهَٰذَا وَمَا كُنَّا لِنَهۡتَدِيَ لَوۡلَآ أَنۡ هَدَىٰنَا ٱللَّهُۖ لَقَدۡ جَآءَتۡ رُسُلُ رَبِّنَا بِٱلۡحَقِّۖ وَنُودُوٓاْ أَن تِلۡكُمُ ٱلۡجَنَّةُ أُورِثۡتُمُوهَا بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
Ndipo tidzachotsa kusakondana (komwe kudali) m’mitima mwawo; (adzakhala okondana ngakhale pa dziko lapansi adali odana), uku pansi ndi patsogolo pawo mitsinje ikuyenda; ndipo adzanena (m’kuthokoza kwawo): “Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Yemwe adatitsogolera ku ichi (chomwe chatidzetsera mtendere). Sitikadaongoka pakadapanda Allah kutiongola. Atumiki a Mbuye wathu adadza ndi choonadi.” Ndipo adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Uwu ndi Munda wamtendere umene mwapatsidwa chifukwa cha zomwe mudali kuchita.”
Tefsiret në gjuhën arabe:
 
Përkthimi i kuptimeve Surja: El A’raf
Përmbajtja e sureve Numri i faqes
 
Përkthimi i kuptimeve të Kuranit Fisnik - Përkthimi çiçevë - Khalid Ibrahim Betiala - Përmbajtja e përkthimeve

E përktheu Khalid Ibrahim Betala.

Mbyll