Check out the new design

அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா * - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை


மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அல்பகரா   வசனம்:
وَإِذۡ نَجَّيۡنَٰكُم مِّنۡ ءَالِ فِرۡعَوۡنَ يَسُومُونَكُمۡ سُوٓءَ ٱلۡعَذَابِ يُذَبِّحُونَ أَبۡنَآءَكُمۡ وَيَسۡتَحۡيُونَ نِسَآءَكُمۡۚ وَفِي ذَٰلِكُم بَلَآءٞ مِّن رَّبِّكُمۡ عَظِيمٞ
Ndipo (kumbukirani) pamene tidakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe amakuzunzani ndi chilango choipa; adali kuzinga (kupha) ana anu achimuna ndikuwasiya moyo achikazi. Ndipo m’zimenezo mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذۡ فَرَقۡنَا بِكُمُ ٱلۡبَحۡرَ فَأَنجَيۡنَٰكُمۡ وَأَغۡرَقۡنَآ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ وَأَنتُمۡ تَنظُرُونَ
Ndipo (kumbukiraninso) pamene tidailekanitsa nyanja chifukwa cha inu (kuti muoloke pa mchenga wouma), potero tidakupulumutsani ndi kuwamiza anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini) uku inu mukuona; (chomwe chidali chizizwa choonekera).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذۡ وَٰعَدۡنَا مُوسَىٰٓ أَرۡبَعِينَ لَيۡلَةٗ ثُمَّ ٱتَّخَذۡتُمُ ٱلۡعِجۡلَ مِنۢ بَعۡدِهِۦ وَأَنتُمۡ ظَٰلِمُونَ
(Kumbukiraninso) pamene tidamulonjeza Mûsa masiku makumi anayi (kuti tidzampatsa buku la Taurat patapita masiku makumi anayi pambuyo pa kupulumuka kwanu ndi kuonongeka kwa Farawo); kenako inu mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe) pambuyo pake, (iye kulibe, atapita ku chipangano cha Mbuye wake). Ndipo inu muli ochita zoipa.
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ عَفَوۡنَا عَنكُم مِّنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Kenako tidakukhululukirani pambuyo pa zimenezo, kuti muthokoze (mtendere wa Allah).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَٱلۡفُرۡقَانَ لَعَلَّكُمۡ تَهۡتَدُونَ
Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa tidampatsa buku lolekanitsa choonadi ndi chonama kuti inu muongoke (polilingalira ndi kutsatira malamulo ake).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذۡ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوۡمِهِۦ يَٰقَوۡمِ إِنَّكُمۡ ظَلَمۡتُمۡ أَنفُسَكُم بِٱتِّخَاذِكُمُ ٱلۡعِجۡلَ فَتُوبُوٓاْ إِلَىٰ بَارِئِكُمۡ فَٱقۡتُلُوٓاْ أَنفُسَكُمۡ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ عِندَ بَارِئِكُمۡ فَتَابَ عَلَيۡكُمۡۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلتَّوَّابُ ٱلرَّحِيمُ
Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti “E inu anthu anga! Ndithudi, inu mwadzichitira nokha zoipa pompembedza thole (mwana wa ng’ombe). Choncho lapani kwa Mlengi wanu, ndipo iphanani nokha (amene ali abwino aphe oipa). Kutero ndi bwino kwa inu pamaso pa Mlengi wanu.” Choncho (Allah) wavomera kulapa kwanu. Ndithudi, Iye Ngovomera kulapa mochuluka, Wachisoni chosatha.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَإِذۡ قُلۡتُمۡ يَٰمُوسَىٰ لَن نُّؤۡمِنَ لَكَ حَتَّىٰ نَرَى ٱللَّهَ جَهۡرَةٗ فَأَخَذَتۡكُمُ ٱلصَّٰعِقَةُ وَأَنتُمۡ تَنظُرُونَ
Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mudati: “E iwe Mûsa!; Sitingakukhulupirire iwe mpaka timuone Allah masomphenya.” Ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona.
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ بَعَثۡنَٰكُم مِّنۢ بَعۡدِ مَوۡتِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَشۡكُرُونَ
Kenako tidakuukitsani ku imfa pambuyo pakufa kwanu, kuti muyamike.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَظَلَّلۡنَا عَلَيۡكُمُ ٱلۡغَمَامَ وَأَنزَلۡنَا عَلَيۡكُمُ ٱلۡمَنَّ وَٱلسَّلۡوَىٰۖ كُلُواْ مِن طَيِّبَٰتِ مَا رَزَقۡنَٰكُمۡۚ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ
Ndipo tidakuphimbani ndi mthunzi wa mitambo (pamene mudali kuoloka chipululu cha mchenga), ndipo tidakutsitsirani Mana (zakumwa zotsekemera ngati uchi) ndi Salwa (zinziri), ndi kukuuzani: “Idyani zinthu zabwino izi zimene takupatsani.” Komatu sadatichitire Ife choipa koma adali kudzichitira okha zoipa.
அரபு விரிவுரைகள்:
 
மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அல்பகரா
அத்தியாயங்களின் அட்டவணை பக்க எண்
 
அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை

மொழிபெயர்த்தது காலித் இப்ராஹீம் பைதாலா.

மூடுக