Check out the new design

அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா * - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை


மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அந்நூர்   வசனம்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ جَآءُو بِٱلۡإِفۡكِ عُصۡبَةٞ مِّنكُمۡۚ لَا تَحۡسَبُوهُ شَرّٗا لَّكُمۖ بَلۡ هُوَ خَيۡرٞ لَّكُمۡۚ لِكُلِّ ٱمۡرِيٕٖ مِّنۡهُم مَّا ٱكۡتَسَبَ مِنَ ٱلۡإِثۡمِۚ وَٱلَّذِي تَوَلَّىٰ كِبۡرَهُۥ مِنۡهُمۡ لَهُۥ عَذَابٌ عَظِيمٞ
Ndithu amene adza ndi bodza (ponamizira Mayi Aisha {r.a}, yemwe ndi Mkazi wa Mtumiki {s.a.w}, kuti wachita chiwerewere), ndi gulu la mwa inu. Musaganizire zimenezo kuti nzoipa kwa inu, koma kuti zimenezo nzabwino kwa inu. Ndipo munthu aliyense wa iwo apeza (chilango) pa machimo amene wawachitawo. Ndipo yemwe wasenza gawo lalikulu la uchimowo mwa iwo, adzapeza chilango chachikulu.
அரபு விரிவுரைகள்:
لَّوۡلَآ إِذۡ سَمِعۡتُمُوهُ ظَنَّ ٱلۡمُؤۡمِنُونَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتُ بِأَنفُسِهِمۡ خَيۡرٗا وَقَالُواْ هَٰذَآ إِفۡكٞ مُّبِينٞ
Nanga bwanji pamene mudaimva (nkhani) iyi okhulupirira achimuna ndi okhulupirira achikazi saadaganizire anzawo zabwino ndikunena kuti: “Ili ndi bodza loonekera?”
அரபு விரிவுரைகள்:
لَّوۡلَا جَآءُو عَلَيۡهِ بِأَرۡبَعَةِ شُهَدَآءَۚ فَإِذۡ لَمۡ يَأۡتُواْ بِٱلشُّهَدَآءِ فَأُوْلَٰٓئِكَ عِندَ ٱللَّهِ هُمُ ٱلۡكَٰذِبُونَ
Nanga bwanji sadabweretse mboni zinayi (pa zimenezi)? Ndipo pamene alephera kubweretsa mboni, iwo ngabodza kwa Allah.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِ لَمَسَّكُمۡ فِي مَآ أَفَضۡتُمۡ فِيهِ عَذَابٌ عَظِيمٌ
Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu, pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro, chilango chachikulu chikadakukhudzani pa zomwe munkazijijirikira.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِذۡ تَلَقَّوۡنَهُۥ بِأَلۡسِنَتِكُمۡ وَتَقُولُونَ بِأَفۡوَاهِكُم مَّا لَيۡسَ لَكُم بِهِۦ عِلۡمٞ وَتَحۡسَبُونَهُۥ هَيِّنٗا وَهُوَ عِندَ ٱللَّهِ عَظِيمٞ
Pamene mudalilandira (bodzalo) ndi malirime anu ndi kumanena ndi milomo yanu zomwe inu simukuzidziwa, ndipo mumaganizira kuti ndi chinthu Chochepa pomwe icho kwa Allah ndi chinthu chachikulu.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡلَآ إِذۡ سَمِعۡتُمُوهُ قُلۡتُم مَّا يَكُونُ لَنَآ أَن نَّتَكَلَّمَ بِهَٰذَا سُبۡحَٰنَكَ هَٰذَا بُهۡتَٰنٌ عَظِيمٞ
Ndipo nanga bwanji pamene mudalimva (bodzalo) simudanene (kuti): “Sikoyenera kwa ife kuyankhula izi; kuyera nkwanu (Mbuye wathu). Ili ndi bodza lalikulu.”
அரபு விரிவுரைகள்:
يَعِظُكُمُ ٱللَّهُ أَن تَعُودُواْ لِمِثۡلِهِۦٓ أَبَدًا إِن كُنتُم مُّؤۡمِنِينَ
Allah akukulangizani kuti: “Musabwerezenso kuchita zonga zimenezi mpaka kalekale, ngati inu muli okhulupirira enieni.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡأٓيَٰتِۚ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ
Ndipo Allah akukufotokozerani Ayah (ndime) Zake mwatsatanetsatane. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يُحِبُّونَ أَن تَشِيعَ ٱلۡفَٰحِشَةُ فِي ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِۚ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ وَأَنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ
Ndithu amene akukonda kuti zoipa zifale pa amene akhulupirira, chilango chowawa chili pa iwo padziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro. Ndipo Allah ndi yemwe akudziwa (zoyenerana ndi inu), koma inu simudziwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ وَأَنَّ ٱللَّهَ رَءُوفٞ رَّحِيمٞ
Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu, (pakadapezeka zauve). Koma ndithu Allah Ngoleza; Ngwachisoni chosatha.
அரபு விரிவுரைகள்:
 
மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அந்நூர்
அத்தியாயங்களின் அட்டவணை பக்க எண்
 
அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை

மொழிபெயர்த்தது காலித் இப்ராஹீம் பைதாலா.

மூடுக