அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு * - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை


மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: ஸூரா முஹம்மத்   வசனம்:

ஸூரா முஹம்மத்

ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ أَضَلَّ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Amene adam’kana (Allah ndi Mthenga Wake) ndi kutsekereza anthu kuyenda panjira ya Allah (powaletsa kulowa m’Chisilamu), Allah waononga zonse zabwino zimene adachita.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَءَامَنُواْ بِمَا نُزِّلَ عَلَىٰ مُحَمَّدٖ وَهُوَ ٱلۡحَقُّ مِن رَّبِّهِمۡ كَفَّرَ عَنۡهُمۡ سَيِّـَٔاتِهِمۡ وَأَصۡلَحَ بَالَهُمۡ
Ndipo amene akhulupirira nkumachita zabwino, nkuzikhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa Muhammad (s.a.w), zimene zili zoona zochokera kwa Mbuye wawo, wawafafanizira zolakwa zawo, ndipo awakonzera chikhalidwe chawo (patsiku lachimaliziro ndi padziko lapansi).
அரபு விரிவுரைகள்:
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ ٱتَّبَعُواْ ٱلۡبَٰطِلَ وَأَنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّبَعُواْ ٱلۡحَقَّ مِن رَّبِّهِمۡۚ كَذَٰلِكَ يَضۡرِبُ ٱللَّهُ لِلنَّاسِ أَمۡثَٰلَهُمۡ
Zimenezi nchifukwa chakuti amene sadakhulupirire adatsata chonama, ndipo amene adakhulupirira adatsatira choonadi chochokera kwa Mbuye wawo. M’menemu ndim’mene Allah akuperekera kwa anthu mafanizo awo (kuti alingalire ndi kupeza phunziro).
அரபு விரிவுரைகள்:
فَإِذَا لَقِيتُمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَضَرۡبَ ٱلرِّقَابِ حَتَّىٰٓ إِذَآ أَثۡخَنتُمُوهُمۡ فَشُدُّواْ ٱلۡوَثَاقَ فَإِمَّا مَنَّۢا بَعۡدُ وَإِمَّا فِدَآءً حَتَّىٰ تَضَعَ ٱلۡحَرۡبُ أَوۡزَارَهَاۚ ذَٰلِكَۖ وَلَوۡ يَشَآءُ ٱللَّهُ لَٱنتَصَرَ مِنۡهُمۡ وَلَٰكِن لِّيَبۡلُوَاْ بَعۡضَكُم بِبَعۡضٖۗ وَٱلَّذِينَ قُتِلُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ فَلَن يُضِلَّ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Ndipo mukakumana nawo pankhondo amene sanakhulupirire amenyeni makosi awo (aduleni), mpaka mwafooketse pochuluka ophedwa mwa iwo; kenako amangeni ndi zingwe (otsalawo). Ngati mutafuna kuwamasula popanda dipo kapena kuti apereke dipo, (zili kwa inu). Kufikira nkhondo itatha. Limenelo ndi lamulo la Allah. Ndithu Allah akadafuna akadathana nawo Iye mwini powaononga onse psiti; koma (wakulamulani kuti muchite nkhondo) ncholinga choti awayese mayeso ena a inu pa ena (okhulupirira pa okanitsitsawo). Ndipo amene aphedwa panjira ya Allah, ntchito yawo sadzaipititsa pachabe.
அரபு விரிவுரைகள்:
سَيَهۡدِيهِمۡ وَيُصۡلِحُ بَالَهُمۡ
Awaongolera (ku zimene zingawapindulitse pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro) ndi kuwakonzera zinthu zawo ndi chikhalidwe chawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيُدۡخِلُهُمُ ٱلۡجَنَّةَ عَرَّفَهَا لَهُمۡ
Ndi kukawalowetsa ku Munda wamtendere umene adawadziwitsa.
அரபு விரிவுரைகள்:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِن تَنصُرُواْ ٱللَّهَ يَنصُرۡكُمۡ وَيُثَبِّتۡ أَقۡدَامَكُمۡ
E inu amene mwakhulupirira! Ngati muteteza chipembedzo cha Allah, (Iye) adzakutetezani (kwa adani anu) ndi kulimbikitsa mapazi anu (pa nkhondo).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ فَتَعۡسٗا لَّهُمۡ وَأَضَلَّ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Koma amene akana (Allah ndi Ayah Zake) kuwonongeka nkwawo ndipo awaonongera zochita zawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ كَرِهُواْ مَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ فَأَحۡبَطَ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Zimenezo nchifukwa chakuti iwo azida zomwe Allah adavumbulutsa (monga Qur’an ndi malamulo ake;) choncho waziononga zochita zawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
۞ أَفَلَمۡ يَسِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَيَنظُرُواْ كَيۡفَ كَانَ عَٰقِبَةُ ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۖ دَمَّرَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِمۡۖ وَلِلۡكَٰفِرِينَ أَمۡثَٰلُهَا
Kodi sadayendeyende padziko nkuona kuti adali bwanji mapeto a amene adawatsogolera (monga Âdi ndi Samudi, ndi anthu a Luti ndi ena otero)? Allah adawaononga psiti, ndipo chilango ngati chimenecho chidzakhalanso kwa osakhulupirira.
அரபு விரிவுரைகள்:
ذَٰلِكَ بِأَنَّ ٱللَّهَ مَوۡلَى ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَأَنَّ ٱلۡكَٰفِرِينَ لَا مَوۡلَىٰ لَهُمۡ
Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, koma osakhulupirira alibe mtetezi.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱللَّهَ يُدۡخِلُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ جَنَّٰتٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُۖ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يَتَمَتَّعُونَ وَيَأۡكُلُونَ كَمَا تَأۡكُلُ ٱلۡأَنۡعَٰمُ وَٱلنَّارُ مَثۡوٗى لَّهُمۡ
Ndithu Allah adzawalowetsa ku Minda ya mtendere amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, (momwe) pansi pake ikuyenda mitsinje; koma amene sadakhulupirire akusangalala (padziko lapansi) ndi kudya momwe zidyera ziweto (popanda lingaliro lililonse kupatula lingaliro la mimba zawo ndi kukwaniritsa zilakolako za chilengedwe chawo); ndipo Moto ndiwo malo awo.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَكَأَيِّن مِّن قَرۡيَةٍ هِيَ أَشَدُّ قُوَّةٗ مِّن قَرۡيَتِكَ ٱلَّتِيٓ أَخۡرَجَتۡكَ أَهۡلَكۡنَٰهُمۡ فَلَا نَاصِرَ لَهُمۡ
Ndi ambiri mwa eni mizinda (yakale) omwe adali amphamvu kuposa eni mzinda wakowu umene akutulutsamo (eni ake,) tidawaononga (ndi zilango zosiyanasiyana) koma padalibe wowateteza (kwa Ife).
அரபு விரிவுரைகள்:
أَفَمَن كَانَ عَلَىٰ بَيِّنَةٖ مِّن رَّبِّهِۦ كَمَن زُيِّنَ لَهُۥ سُوٓءُ عَمَلِهِۦ وَٱتَّبَعُوٓاْ أَهۡوَآءَهُم
Kodi angafanane, (polandira mphoto,) amene ali ndi umboni wodziwika wochokera kwa Mbuye wake, (kotero kuti nkumamumvera, ndi amene wakometsedwa ndi zochita zake zoipa natsatira zilakolako zawo?
அரபு விரிவுரைகள்:
مَّثَلُ ٱلۡجَنَّةِ ٱلَّتِي وُعِدَ ٱلۡمُتَّقُونَۖ فِيهَآ أَنۡهَٰرٞ مِّن مَّآءٍ غَيۡرِ ءَاسِنٖ وَأَنۡهَٰرٞ مِّن لَّبَنٖ لَّمۡ يَتَغَيَّرۡ طَعۡمُهُۥ وَأَنۡهَٰرٞ مِّنۡ خَمۡرٖ لَّذَّةٖ لِّلشَّٰرِبِينَ وَأَنۡهَٰرٞ مِّنۡ عَسَلٖ مُّصَفّٗىۖ وَلَهُمۡ فِيهَا مِن كُلِّ ٱلثَّمَرَٰتِ وَمَغۡفِرَةٞ مِّن رَّبِّهِمۡۖ كَمَنۡ هُوَ خَٰلِدٞ فِي ٱلنَّارِ وَسُقُواْ مَآءً حَمِيمٗا فَقَطَّعَ أَمۡعَآءَهُمۡ
Fanizo la Munda wamtendere (Jannah) umene alonjezedwa oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa, udzakhala chonchi): M’menemo muli mitsinje yamadzi osasintha fungo lake; ndi mitsinje yamkaka wosasasa mkakomedwe kake; ndi mitsinje yavinyo wokoma kwa akumwa ndi mitsinje ya uchi woyeretsedwa (ku phula), ndiponso iwo adzapeza m’menemo mtundu uliwonse wa zipatso ndi chikhululuko chochokera kwa Mbuye wawo. Angafanane ndi wokhala nthawi yaitali ku Moto, ndi kumwetsedwa madzi owira omwe akadula matumbo awo?
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمِنۡهُم مَّن يَسۡتَمِعُ إِلَيۡكَ حَتَّىٰٓ إِذَا خَرَجُواْ مِنۡ عِندِكَ قَالُواْ لِلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ مَاذَا قَالَ ءَانِفًاۚ أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ طَبَعَ ٱللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ وَٱتَّبَعُوٓاْ أَهۡوَآءَهُمۡ
Ndipo ena mwa iwo (okana Allah) amamvetsera kwa iwe, (popanda kupindula chilichonse), ndipo akachoka pamalo pakopo, amanena kwa amene apatsidwa nzeru (mwa omtsatira ake): “Kodi (Mtumiki) wanena chiyani posachedwapa?” Iwowo ndiamene Allah wawadinda m’mitima mwawo (ndi chidindo chokana Allah), ndipo amatsatira zilakolako zawo (zachabe).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَٱلَّذِينَ ٱهۡتَدَوۡاْ زَادَهُمۡ هُدٗى وَءَاتَىٰهُمۡ تَقۡوَىٰهُمۡ
Ndipo amene aongoka, (Allah) amawaonjezera chiongoko ndi kuwapatsa kuopa kwawo (komuopa Allah).
அரபு விரிவுரைகள்:
فَهَلۡ يَنظُرُونَ إِلَّا ٱلسَّاعَةَ أَن تَأۡتِيَهُم بَغۡتَةٗۖ فَقَدۡ جَآءَ أَشۡرَاطُهَاۚ فَأَنَّىٰ لَهُمۡ إِذَا جَآءَتۡهُمۡ ذِكۡرَىٰهُمۡ
Kodi pali chimene akuyembekezera posakhala tsiku lachiweruziro limene liwadzere mwadzidzidzi (uku iwo ali otanganidwa ndi zam’dziko)? Ndithu zizindikiro zake zadza kale; kodi kudzawapindulira chiyani kukumbuka kwawo likadzawadzera (tsikulo)?
அரபு விரிவுரைகள்:
فَٱعۡلَمۡ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا ٱللَّهُ وَٱسۡتَغۡفِرۡ لِذَنۢبِكَ وَلِلۡمُؤۡمِنِينَ وَٱلۡمُؤۡمِنَٰتِۗ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مُتَقَلَّبَكُمۡ وَمَثۡوَىٰكُمۡ
Dziwa kuti palibe wompembedza m’choonadi koma Allah, ndipo pempha chikhululuko pa zolakwa zako ndi zolakwa za okhulupirira aamuna ndi aakazi; ndipo Allah akudziwa malo anu opita ndi kubwera ndi malo anu Wokhazikika.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيَقُولُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَوۡلَا نُزِّلَتۡ سُورَةٞۖ فَإِذَآ أُنزِلَتۡ سُورَةٞ مُّحۡكَمَةٞ وَذُكِرَ فِيهَا ٱلۡقِتَالُ رَأَيۡتَ ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٞ يَنظُرُونَ إِلَيۡكَ نَظَرَ ٱلۡمَغۡشِيِّ عَلَيۡهِ مِنَ ٱلۡمَوۡتِۖ فَأَوۡلَىٰ لَهُمۡ
Ndipo amene akhulupirira akunena (chifukwa cha mazunzo omwe amawapeza kuchokera kwa osakhulupirira kuti) kodi nchifukwa ninji siikuvumbulutsidwa sura (yotiloleza kumenyana ndi osakhulupirira Allah amene akutiputa)? Koma ikavumbulutsidwa Sura yokhazikika (lamulo lake), ndipo mkati mwake ndi kutchulidwa nkhani zankhondo, uwaona amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akukuyang’ana m’mayang’anidwe a yemwe akukomoka ndi imfa, (chifukwa cha kulida lamulo lomenyana ndi osakhulupirira), basi kuonongeka ndi kwawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
طَاعَةٞ وَقَوۡلٞ مَّعۡرُوفٞۚ فَإِذَا عَزَمَ ٱلۡأَمۡرُ فَلَوۡ صَدَقُواْ ٱللَّهَ لَكَانَ خَيۡرٗا لَّهُمۡ
(Zofunika ndi) kumvera ndi mawu abwino ndi kuti chinthu chikatsimikizika (achichite). Ngati akadamumvera Allah, ndithu zikadakhala zabwino kwa iwo.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَهَلۡ عَسَيۡتُمۡ إِن تَوَلَّيۡتُمۡ أَن تُفۡسِدُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَتُقَطِّعُوٓاْ أَرۡحَامَكُمۡ
Mwina mwake inu mukanyoza (Chisilamu), mubwerera m’mbuyo ku zomwe mudali nazo (m’nthawi ya umbuli) monga kuononga pa dziko ndi machimo) ndi kudula chibale chanu.
அரபு விரிவுரைகள்:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ لَعَنَهُمُ ٱللَّهُ فَأَصَمَّهُمۡ وَأَعۡمَىٰٓ أَبۡصَٰرَهُمۡ
Oterewo ndiamene Allah wawatembelera ndi kuwagonthetsa ndi kuwachititsa khungu maso awo.
அரபு விரிவுரைகள்:
أَفَلَا يَتَدَبَّرُونَ ٱلۡقُرۡءَانَ أَمۡ عَلَىٰ قُلُوبٍ أَقۡفَالُهَآ
Kodi sakuilingalira Qur’an? Kapena m’mitima mwawo m’motsekedwa ndi akabali (maloko) ake?
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ٱرۡتَدُّواْ عَلَىٰٓ أَدۡبَٰرِهِم مِّنۢ بَعۡدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُمُ ٱلۡهُدَى ٱلشَّيۡطَٰنُ سَوَّلَ لَهُمۡ وَأَمۡلَىٰ لَهُمۡ
Ndithu amene akubwerera m’mbuyo (kusiya chipembedzo chawo nkubwerera ku zosakhulupirira Allah) chiongoko chitawaonekera poyera satana ndiamene wawanyenga, ndipo Allah akuwapatsa nthawi.
அரபு விரிவுரைகள்:
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ قَالُواْ لِلَّذِينَ كَرِهُواْ مَا نَزَّلَ ٱللَّهُ سَنُطِيعُكُمۡ فِي بَعۡضِ ٱلۡأَمۡرِۖ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ إِسۡرَارَهُمۡ
Zimenezo nkaamba kakuti iwo adanena kwa omwe amada zimene Allah wavumbulutsa (kuti): “Tidzakumverani m’zinthu zina (zimene mukutsutsana ndi Mtumiki{s.a.w}).” Ndipo Allah akudziwa zobisika zawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَكَيۡفَ إِذَا تَوَفَّتۡهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ يَضۡرِبُونَ وُجُوهَهُمۡ وَأَدۡبَٰرَهُمۡ
Kodi adzakhala bwanji pamene angelo azidzatenga mizimu yawo uku akumenya nkhope zawo ndi misana yawo?
அரபு விரிவுரைகள்:
ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمُ ٱتَّبَعُواْ مَآ أَسۡخَطَ ٱللَّهَ وَكَرِهُواْ رِضۡوَٰنَهُۥ فَأَحۡبَطَ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Zimenezi (imfa yoopsayi) nkaamba kakuti iwo adatsata zomwe zidakwiitsa Allah ndi kuda zomusangalatsa (Allah); choncho adaziwononga zochita zawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
أَمۡ حَسِبَ ٱلَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ أَن لَّن يُخۡرِجَ ٱللَّهُ أَضۡغَٰنَهُمۡ
Kodi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akuganiza kuti Allah sangaonetsere poyera kaduka kawo?
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡ نَشَآءُ لَأَرَيۡنَٰكَهُمۡ فَلَعَرَفۡتَهُم بِسِيمَٰهُمۡۚ وَلَتَعۡرِفَنَّهُمۡ فِي لَحۡنِ ٱلۡقَوۡلِۚ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ أَعۡمَٰلَكُمۡ
Ndipo tikadafuna tikadakuonetsa iwo (amene akuchitira kaduka Chisilamu) ndipo ukadawadziwa ndi zizindikiro zawo. Koma ndithu uwadziwa m’kayankhulidwe (kawo) kokometsa ndipo Allah akudziwa zochita zanu zonse.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَنَبۡلُوَنَّكُمۡ حَتَّىٰ نَعۡلَمَ ٱلۡمُجَٰهِدِينَ مِنكُمۡ وَٱلصَّٰبِرِينَ وَنَبۡلُوَاْ أَخۡبَارَكُمۡ
Ndipo ndithu tikuyesani mayeso mpaka tiwaonetsere poyera (adziwike) amene akumenya nkhondo mwa inu (chifukwa cha dini) ndi opirira (pamavuto); ndi kuzionetsera poyera nkhani zanu (zochita zanu).
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ وَشَآقُّواْ ٱلرَّسُولَ مِنۢ بَعۡدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُمُ ٱلۡهُدَىٰ لَن يَضُرُّواْ ٱللَّهَ شَيۡـٔٗا وَسَيُحۡبِطُ أَعۡمَٰلَهُمۡ
Ndithu amene akana (Mtumiki {s.a.w}) ndi kuwatsekereza anthu ku njira ya Allah, ndi kutsutsana ndi Mtumiki chiongoko chitadziwika kwa iwo, sangamsautse Allah ndi chilichonse, koma adzawaonongera ntchito zawo.
அரபு விரிவுரைகள்:
۞ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ أَطِيعُواْ ٱللَّهَ وَأَطِيعُواْ ٱلرَّسُولَ وَلَا تُبۡطِلُوٓاْ أَعۡمَٰلَكُمۡ
E inu amene mwakhulupirira! Mvereni Allah ndiponso mvereni mtumiki (Wake) ndipo musaononge ntchito zanu.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ وَصَدُّواْ عَن سَبِيلِ ٱللَّهِ ثُمَّ مَاتُواْ وَهُمۡ كُفَّارٞ فَلَن يَغۡفِرَ ٱللَّهُ لَهُمۡ
Ndithu amene sadakhulupirire ndi kwatsekereza anthu kunjira ya Allah, kenako nkufa uku ali osakhulupirira Allah sadzawakhululukira (zolakwa zawo).
அரபு விரிவுரைகள்:
فَلَا تَهِنُواْ وَتَدۡعُوٓاْ إِلَى ٱلسَّلۡمِ وَأَنتُمُ ٱلۡأَعۡلَوۡنَ وَٱللَّهُ مَعَكُمۡ وَلَن يَتِرَكُمۡ أَعۡمَٰلَكُمۡ
Musafooke ndi kufuna chimvano, (koma menyanani ndi adani anu); inu ndinu opambana. Ndipo Allah ali nanu (pokuthangatani ndi kukupulumutsani,) ndipo sakuchepetserani (mphoto ya) ntchito zanu.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِنَّمَا ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا لَعِبٞ وَلَهۡوٞۚ وَإِن تُؤۡمِنُواْ وَتَتَّقُواْ يُؤۡتِكُمۡ أُجُورَكُمۡ وَلَا يَسۡـَٔلۡكُمۡ أَمۡوَٰلَكُمۡ
Ndithu moyo wapadziko lapansi ndi masewera ndi chibwana. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kudzipatula kumachimo (Allah) akupatsani malipiro anu, ndipo sakukupemphani chuma chanu.
அரபு விரிவுரைகள்:
إِن يَسۡـَٔلۡكُمُوهَا فَيُحۡفِكُمۡ تَبۡخَلُواْ وَيُخۡرِجۡ أَضۡغَٰنَكُمۡ
Ngati akadachifuna (kuchokera) kwa inu chumacho ndi kukuchulukitsirani (chopereka),mukadachita umbombo (ndi chumacho), ndipo akadatulutsira (poyera) kaduka kanu.
அரபு விரிவுரைகள்:
هَٰٓأَنتُمۡ هَٰٓؤُلَآءِ تُدۡعَوۡنَ لِتُنفِقُواْ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِ فَمِنكُم مَّن يَبۡخَلُۖ وَمَن يَبۡخَلۡ فَإِنَّمَا يَبۡخَلُ عَن نَّفۡسِهِۦۚ وَٱللَّهُ ٱلۡغَنِيُّ وَأَنتُمُ ٱلۡفُقَرَآءُۚ وَإِن تَتَوَلَّوۡاْ يَسۡتَبۡدِلۡ قَوۡمًا غَيۡرَكُمۡ ثُمَّ لَا يَكُونُوٓاْ أَمۡثَٰلَكُم
Ha! Ndinu amene mukuitanidwa kuti mupereke (chuma) mu njira ya Allah. Koma alipo ena a inu akuumira ndipo amene akuumira akuzimana yekha. Allah Ngwachikwanekwane ndipo inu ndinu amphawi. Ngati munyoza (Chisilamu) ndi kubwerera m’mbuyo posakhulupirira) Allah adzabweretsa m’malo mwanu anthu ena; iwo sadzakhala ngati inu.
அரபு விரிவுரைகள்:
 
மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: ஸூரா முஹம்மத்
அத்தியாயங்களின் அட்டவணை பக்க எண்
 
அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை

புனித அல் குர்ஆனுக்கான ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு- காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா மூலம் மொழிபெயர்க்கப்பட்டது.

மூடுக