Check out the new design

அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா * - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை


மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அல்அன்ஆம்   வசனம்:
قُلۡ أَيُّ شَيۡءٍ أَكۡبَرُ شَهَٰدَةٗۖ قُلِ ٱللَّهُۖ شَهِيدُۢ بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۚ وَأُوحِيَ إِلَيَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانُ لِأُنذِرَكُم بِهِۦ وَمَنۢ بَلَغَۚ أَئِنَّكُمۡ لَتَشۡهَدُونَ أَنَّ مَعَ ٱللَّهِ ءَالِهَةً أُخۡرَىٰۚ قُل لَّآ أَشۡهَدُۚ قُلۡ إِنَّمَا هُوَ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞ وَإِنَّنِي بَرِيٓءٞ مِّمَّا تُشۡرِكُونَ
Nena: “Kodi nchinthu chanji chomwe umboni wake uli waukulu koposa?” Nena (ngati sakuyankha): “Ndi (umboni wa) Allah basi. (Iye) ndi Mboni pakati pa ine ndi inu. Ndipo Qur’an iyi yavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni nayo ndi amene yawafika (pali ponse pamene ali). Kodi inu mukutsimikiza ndi kuikira umboni kuti pali milungu ina pamodzi ndi Allah?” Nenanso: “Koma ine sindikuikira umboni.” Nenanso: “Iye ndi Mulungu Mmodzi Yekha. Ndithudi, ine ndili kutali ndi zomwe mukumphatikiza nazo.”
அரபு விரிவுரைகள்:
ٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يَعۡرِفُونَهُۥ كَمَا يَعۡرِفُونَ أَبۡنَآءَهُمُۘ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ فَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Omwe tidawapatsa buku akumzindikira (Muhammad {s.a.w} bwinobwino) monga momwe akuwazindikilira ana awo. Koma omwe adziononga okha, iwo sangakhulupirire.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِـَٔايَٰتِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ لَا يُفۡلِحُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Kodi ndani woipitsitsa zedi woposa yemwe akum’pekera Allah bodza. Kapena kutsutsa zizindikiro Zake? Ndithudi, oipa sangapambane.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَيَوۡمَ نَحۡشُرُهُمۡ جَمِيعٗا ثُمَّ نَقُولُ لِلَّذِينَ أَشۡرَكُوٓاْ أَيۡنَ شُرَكَآؤُكُمُ ٱلَّذِينَ كُنتُمۡ تَزۡعُمُونَ
Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse pamodzi; kenako tidzati kwa omwe adali kuphatikiza (Allah ndi mafano): “Ali kuti aphatikizi anu aja omwe munkati ngothandizana ndi Allah?”
அரபு விரிவுரைகள்:
ثُمَّ لَمۡ تَكُن فِتۡنَتُهُمۡ إِلَّآ أَن قَالُواْ وَٱللَّهِ رَبِّنَا مَا كُنَّا مُشۡرِكِينَ
Ndipo dandaulo lawo silidzakhala lina koma kunena: “Tikulumbilira Allah Mbuye wathu, sitidali ophatikiza (mafano ndi Allah).” (Uku kudzakhala kuyesera kumunamiza Allah).
அரபு விரிவுரைகள்:
ٱنظُرۡ كَيۡفَ كَذَبُواْ عَلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡۚ وَضَلَّ عَنۡهُم مَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Taona momwe akudzinamizira okha ndipo zidzawasokonekera zomwe adali kuzipeka (ponena kuti izo ndi milungu zidzawapulumutsa kwa Allah).
அரபு விரிவுரைகள்:
وَمِنۡهُم مَّن يَسۡتَمِعُ إِلَيۡكَۖ وَجَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرٗاۚ وَإِن يَرَوۡاْ كُلَّ ءَايَةٖ لَّا يُؤۡمِنُواْ بِهَاۖ حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءُوكَ يُجَٰدِلُونَكَ يَقُولُ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِنۡ هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Alipo ena mwa iwo omwe akukumvetsera (ukamawerenga Qur’an), ndipo taika zitsekero pa mitima yawo kuti asazindikire (chifukwa cha machimo awo omwe akhala akuchita), ndi m’makutu mwawo kulemera kwa ugonthi; ndipo akaona chozizwitsa chilichonse, sakuchikhulupirira, kufikira akakudzera kudzakangana nawe, awo amene sadakhulupirire akuti: “Izi (zimene utilankhulazi), sikanthu koma ndi nkhani zopeka za anthu akale.”
அரபு விரிவுரைகள்:
وَهُمۡ يَنۡهَوۡنَ عَنۡهُ وَيَنۡـَٔوۡنَ عَنۡهُۖ وَإِن يُهۡلِكُونَ إِلَّآ أَنفُسَهُمۡ وَمَا يَشۡعُرُونَ
Ndipo iwo akuletsa (anthu kutsatira) izi, ndipo (eniwo) akudzitalikitsa nazo. Palibe wina akumuononga koma iwo okha, ndipo sakudziwa.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذۡ وُقِفُواْ عَلَى ٱلنَّارِ فَقَالُواْ يَٰلَيۡتَنَا نُرَدُّ وَلَا نُكَذِّبَ بِـَٔايَٰتِ رَبِّنَا وَنَكُونَ مِنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Ndipo ukadaona (tsiku la Qiyâma) pamene adzawaimitsa pa Moto nkuyamba kunena: “Ha! Tikadabwezedwa (ku dziko lapansi) ndipo sitikadatsutsanso zizindikiro za Mbuye wathu; ndipo tikadakhala mwa okhulupirira.”
அரபு விரிவுரைகள்:
 
மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அல்அன்ஆம்
அத்தியாயங்களின் அட்டவணை பக்க எண்
 
அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை

மொழிபெயர்த்தது காலித் இப்ராஹீம் பைதாலா.

மூடுக