Check out the new design

அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா * - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை


மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அல்அஃராப்   வசனம்:
فَإِذَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡحَسَنَةُ قَالُواْ لَنَا هَٰذِهِۦۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةٞ يَطَّيَّرُواْ بِمُوسَىٰ وَمَن مَّعَهُۥٓۗ أَلَآ إِنَّمَا طَٰٓئِرُهُمۡ عِندَ ٱللَّهِ وَلَٰكِنَّ أَكۡثَرَهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ
(Adali chonchi): Ubwino ukawadzera, amati: “Ubwinowu nchifukwa cha zochita zathu zabwino.” Ndipo choipa chikawadzera, amakankhira kwa Mûsa ndi amene adali naye. (Amati iye ndiye wadzetsa tsokalo chifukwa choisambula milungu yawo). Dziwani kuti tsoka lawo limachokera kwa Allah (chifukwa cha zochita zawo zoipa). Koma ambiri a iwo sazindikira.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَقَالُواْ مَهۡمَا تَأۡتِنَا بِهِۦ مِنۡ ءَايَةٖ لِّتَسۡحَرَنَا بِهَا فَمَا نَحۡنُ لَكَ بِمُؤۡمِنِينَ
Ndipo adati (kwa Mûsa): “Chisonyezo chilichonse chimene ungatibweretsere kuti utilodze nacho (siupindula kanthu). Ifetu sitikukhulupirira.”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَأَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمُ ٱلطُّوفَانَ وَٱلۡجَرَادَ وَٱلۡقُمَّلَ وَٱلضَّفَادِعَ وَٱلدَّمَ ءَايَٰتٖ مُّفَصَّلَٰتٖ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ وَكَانُواْ قَوۡمٗا مُّجۡرِمِينَ
Choncho, tidawatumizira chigumula, (mliri wa) dzombe, nsabwe, achule ndi magazi monga zizindikiro zosiyanasiyana. Koma adadzikuza; ndipo adali anthu oipa.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَلَمَّا وَقَعَ عَلَيۡهِمُ ٱلرِّجۡزُ قَالُواْ يَٰمُوسَى ٱدۡعُ لَنَا رَبَّكَ بِمَا عَهِدَ عِندَكَۖ لَئِن كَشَفۡتَ عَنَّا ٱلرِّجۡزَ لَنُؤۡمِنَنَّ لَكَ وَلَنُرۡسِلَنَّ مَعَكَ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ
Pamene chilango chidawakhudza, amati: “E iwe Mûsa! Tipemphere kwa Mbuye wako pa zomwe adakulonjeza. Ngati utichotsera chilangochi, ndithudi tikukhulupirira, ndipo tiwatumiza pamodzi nawe ana a Israyeli (kuti unke nawo kumene ukufuna).”
அரபு விரிவுரைகள்:
فَلَمَّا كَشَفۡنَا عَنۡهُمُ ٱلرِّجۡزَ إِلَىٰٓ أَجَلٍ هُم بَٰلِغُوهُ إِذَا هُمۡ يَنكُثُونَ
Koma pamene tidawachotsera chilangocho kufikira nthawi yawo yomwe iwo amayenera kuifika, pompo iwo adaswa lonjezo.
அரபு விரிவுரைகள்:
فَٱنتَقَمۡنَا مِنۡهُمۡ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡيَمِّ بِأَنَّهُمۡ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَكَانُواْ عَنۡهَا غَٰفِلِينَ
Choncho, tidawabwezera chilango ndikuwamiza m’nyanja chifukwa chakuti iwo adatsutsa zizindikiro Zathu, ndipo sadali ozilabadira.
அரபு விரிவுரைகள்:
وَأَوۡرَثۡنَا ٱلۡقَوۡمَ ٱلَّذِينَ كَانُواْ يُسۡتَضۡعَفُونَ مَشَٰرِقَ ٱلۡأَرۡضِ وَمَغَٰرِبَهَا ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَاۖ وَتَمَّتۡ كَلِمَتُ رَبِّكَ ٱلۡحُسۡنَىٰ عَلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ بِمَا صَبَرُواْۖ وَدَمَّرۡنَا مَا كَانَ يَصۡنَعُ فِرۡعَوۡنُ وَقَوۡمُهُۥ وَمَا كَانُواْ يَعۡرِشُونَ
Ndipo anthu omwe adali kuponderezedwa tidawachita kukhala amlowammalo a kuvuma kwa dziko ndi kuzambwe kwake, lomwe tidaikamo madalitso (ambiri). Ndipo mawu abwino a Mbuye wako adakwaniritsidwa kwa ana a Israyeli chifukwa cha kupirira kwawo (pa zomwe adakumana nazo). Ndipo tidazigumula ndi kuziononga zomwe Farawo ndi anthu ake ankapanga ndi zomwe ankamanga.
அரபு விரிவுரைகள்:
 
மொழிபெயர்ப்பு அத்தியாயம்: அல்அஃராப்
அத்தியாயங்களின் அட்டவணை பக்க எண்
 
அல்குர்ஆன் மொழிபெயர்ப்பு - ஷேவா(Chewa) மொழிபெயர்ப்பு - காலித் இப்ராஹிம் பேடாலா - மொழிபெயர்ப்பு அட்டவணை

மொழிபெயர்த்தது காலித் இப்ராஹீம் பைதாலா.

மூடுக