Iye ndi Yemwe adakulengani ndi dongo, kenako adaika nthawi (yothera cholengedwa chilichonse), ndi nthawi ina yodziwika kwa Iye (yomwe njoukitsira zolengedwa ku imfa). Ndipo pa izi inu (osakhulupirira) mukukaikira.
Ndipo Iye ndi Allah (Wopembedzedwa) kumwamba ndi pansi. Akudziwa za mkati mwanu ndi zakunja kwanu, ndipo akudziwa zimene mukupeza (kuchokera mzochitachita zanu, zabwino kapena zoipa).
Nena: “Ndidzipangire mtetezi wanga kusiya Allah, Mlengi wa thambo ndi nthaka? Iye Njemwe amadyetsa ndipo sadyetsedwa.” Nena: “Ndalamulidwa kukhala woyamba mwa olowa m’Chisilamu.” Ndipo (ndauzidwa kuti): “Usakhale mwa ophatikiza (Allah ndi mafano)”
Ngati Allah atakukhudza ndi mazunzo, palibe aliyense angathe kukuchotsera, koma Iye basi; ndipo ngati atakukhudza ndi zabwino (palibe amene angakutsekereze ku zabwinozo). Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse.[171]
[171] Mu Ayah iyi Allah akuuza Mtumiki Wake ndi omtsatira ake kuti ngati masautso, umphawi ndi matenda zitampeza, palibe amene angamchotsere zimenezi koma Allah basi. Ndiponso ngati zitamkhudza zabwino, monga kukhala ndi moyo wangwiro ndi chuma chambiri, palibe amene angazichotse zimenezi kwa iye ngati Allah safuna. Choncho tiyeni tiike chikhulupiliro chathu chonse mwa Allah.
Nena: “Kodi nchinthu chanji chomwe umboni wake uli waukulu koposa?” Nena (ngati sakuyankha): “Ndi (umboni wa) Allah basi. (Iye) ndi Mboni pakati pa ine ndi inu. Ndipo Qur’an iyi yavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni nayo ndi amene yawafika (pali ponse pamene ali). Kodi inu mukutsimikiza ndi kuikira umboni kuti pali milungu ina pamodzi ndi Allah?” Nenanso: “Koma ine sindikuikira umboni.” Nenanso: “Iye ndi Mulungu Mmodzi Yekha. Ndithudi, ine ndili kutali ndi zomwe mukumphatikiza nazo.”
Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse pamodzi; kenako tidzati kwa omwe adali kuphatikiza (Allah ndi mafano): “Ali kuti aphatikizi anu aja omwe munkati ngothandizana ndi Allah?”
Ndithudi, ataika ndi kuonongeka amene akutsutsa zokumana ndi Allah, mpaka mwadzidzidzi nthawi ya Qiyama itawafikira, adzati: “Ho! Masautso pa ife chifukwa chakusalabadira kwathu za zimenezi, uku iwo atasenza mitolo ya machimo kumisana kwao. Taonani kuipa kwa zomwe akusenza.
Ndipo moyo wadziko lapansi sikanthu, koma ndi masewera ndi chibwana. Koma nyumba yomaliza ndiyabwino koposa, (siyofanana ndi chisangalalo cha pa dziko lapansi) kwa omwe akuopa Allah. Bwanji simuzindikira?
Ndipo akumanena: “Bwanji sichinatsitsidwe chozizwitsa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Ndithudi, Allah Ngokhoza kutsitsa chozizwitsa koma ambiri a iwo sadziwa (zomwe Allah afuna).”
Ndipo palibe nyama ili yonse pa nthaka, ngakhale mbalame yowuluka ndi mapiko ake awiri koma ndi magulu a zolengedwa ngati inu (zomwe Allah adazilenga). Sitinasiye chinthu chilichonse kapena kuchinyozera chilichonse m’buku (chomwe nchofunika koma tachifotokoza). Ndipo tero kwa Mbuye wawo adzasonkhanitsidwa.
Ndipo amene atsutsa zizindikiro Zathu, ndiagonthi ndiponso abubu, ali mu m’dima (wa umbuli). Amene Allah wamfuna amamlekelera kusokera. Ndipo amene wamfuna amamuika pa njira yolunjika (yomwe ndi njira ya Chisilamu).
Nena: “Tandiuzani ngati mazunzo a Allah atakufikani (pompano pa dziko lapansi), kapena kukufikani nthawi (ya chilango cha tsiku lachimaliziro) kodi mudzaitana yemwe sali Allah (kuti akupulumutseni) ngati inu muli owona.”
Nena: “Ine sindikukuuzani kuti ndili nazo nkhokwe za Allah kapena kuti ndikudziwa zamseri, ndiponso sindikukuuzani kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsata china koma zomwe zikuvumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi wakhungu ndi wopenya angafanane? Bwanji simukuganizira?”
Ndipo momwemo tawasankha ena (osauka) kukhala mayeso a ena (olemera) kuti (osauka) anene: “Kodi awa ndi omwe Allah wawasankhira ubwino mwa ife (ndikutisiya ife?)” Kodi Allah sali Wodziwa zedi amene akumthokoza?
Nena: “Ndithu ine ndili ndi umboni wowoneka wochokera kwa Mbuye wanga (wotsimikizira zomwe ndikunenazi), koma inu mwautsutsa. Ndilibe (chilango) chimene mukuchifulumizitsacho. Palibe kulamula koma nkwa Allah. Amakamba zoona zokhazokha; Iye Ngwabwino mwa oweruza (onse).”
Nena: “Ndikadakhala nacho chimene mukuchifulumizitsacho, ndiye kuti chinthucho chikadachitika pakati pa ine ndi inu (ndikadakuonongani koma ndilibe nyonga). Ndipo Allah akuwadziwa bwino anthu ochita zoipa.”
Ndipo Iye (Allah) ali nawo Makiyi a zobisika palibe akuwadziwa koma Iye basi. Ndipo akudziwa za pamtunda ndi za panyanja. Ndipo palibe tsamba limene limagwa koma amalidziwa. Ndipo (siigwa) njere mu mdima wa m’nthaka (koma iye akudziwa). Ndipo (sichigwa) chachiwisi ngakhale chouma, koma chili m’buku loonetsa chilichonse.
Nena: “Kodi ndani amakupulumutsani m’masautso a pamtunda ndi panyanja?” Mumampempha modzichepetsa ndi motsitsa mawu (kuti): “Ngati atipulumutsa m’mazunzo awa, ndithudi tidzakhala mwa othokoza.”
Ndithu ine ndalungamitsa nkhope yanga kwa Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndapendekera kwa Iye Yekha. Ndipo ine sindili mwa om’phatikiza (Allah ndi mafano).
Ichi ndi chiongoko cha Allah. Ndi icho akuongolera yemwe wamfuna mwa akapolo Ake. Akadakhala kuti (aneneriwo) adamphatikiza (Allah ndi zina) zikadawaonongekera zimene ankachita.
Iwo ndi omwe Allah adawaongola choncho, tsatira chiongoko chawo. Nena: “Sindikukupemphani malipiro pa izi (zomwe ndikukuphunzitsanizi, koma ndikungotumikira Allah). Ichi sichina koma ndi ulaliki kwa zolengedwa (majini ndi anthu).”
Kodi ndani woipitsitsa koposa yemwe wampekera bodza Allah kapena wonena: “Kwavumbulutsidwa kwa ine,” pomwe sikunavumbulutsidwe kwa iye chilichonse; ndi yemwe akunena: ‘“Ndivumbulutsa monga chimene Allah wavumbulutsa.” Ukadawaona anthu ochita zoipa akuthatha ndi imfa, nawo angelo atatambasula manja awo (powamenya uku akuwauza): “Tulutsani moyo wanu; lero mulipidwa chilango chonyozetsa chifukwa cha zomwe mudali kunenera Allah popanda choonadi, ndi kudzitukumula kwanu pa zizindikiro zake.” (Ukadaona zoopsa kwabasi).
Ndithu Allah ndi Yemwe amang’amba njere ndi mbewu ya zipatso (kuti zimere). Amatulutsa chamoyo m’chakufa. Ndiponso Ngotulutsa chakufa m’chamoyo. Ameneyu ndi Allah, nanga mukutembenuzidwa chotani?
Iye ndi Yemwe ali Wotsekula m’bandakucha, ndipo amaupanga usiku kukhala wabata (nthawi yopumula) ndi dzuwa ndi mwezi kukhala zowerengera masiku ndi zaka (kalendala). Ichi nchikonzero cha Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri.
Iye ndi amene anakupangirani nyenyezi kuti mulondole njira kudzera mwa izo mu m’dima wa pamtunda ndi panyanja. Ndithu talongosola mokwanira zizindikiro (zathu) kwa anthu odziwa.
Ndipo Iye ndi yemwe adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi. (Kwa inu) alipo malo okhalapo (dziko lapansi kapena m’mimba mwa mayi) ndiponso posungirapo (mmanda kapena munsana mwa bambo). Ndithu tafotokoza zizindikiro (Zathu) kwa anthu ozindikira.
Ndipo (pamwamba pa izi) anthu ampangira Allah ziwanda kukhala athandizi (Ake), pomwe Iye ndi Yemwe adazilenga. Ndipo akumnamizira kuti ali ndi ana aamuna ndi aakazi popanda kudziwa. Ali kutali Wolemekezekayo, ndipo watukuka kuzimene akusimbazo.
Iye ndiye Mlengi wathambo ndi nthaka, zingatheke bwanji kukhala ndi mwana pomwe Iye alibe mkazi? Ndipo ndi Yemwe adalenga chinthu chilichonse. Ndiponso Iye Ngodziwa zedi chinthu chilichonse.
Ameneyu ndi Allah, Mbuye wanu; palibe wina woti nkumpembedza mwa choonadi koma Iye. Mlengi wa chinthu chilichonse. Choncho, mpembedzeni. Iye ndi Muyang’aniri wa chinthu chilichonse.
(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu umboni otsimikizika wakufikani kuchokera kwa Mbuye wanu, choncho amene atsekule maso ake nkuyang’ana ndiye kuti (zotsatira zake zabwino) zili pa iye mwini. Ndipo amene atseke maso ake zili pa iye mwini (zotsatira zake zoipa). Ndipo ine sindili muyang’anili wanu.”
Ndi kuti ipendekere ku mawu amenewo mitima ya anthu osakhulupirira tsiku la chimaliziro, ndi kuyanjana nawo (mawuo) ndikutinso apeze (machimo) omwe amawapeza.
(Nena:) “Kodi ndifune woweruza wina kusiya Allah, pomwe Iye ndi Yemwe adavumbulutsa buku kwa inu lofotokoza chilichonse?” Ndipo omwe tidawapatsa buku akudziwa kuti (Qur’an) yavumbulutsidwa ndi Mbuye wako mwachoonadi. Choncho, usakhale mwa okaikira.
Mungasiirenji kudya (nyama) imene poizinga dzina la Allah latchulidwapo, pomwe wakufotokozerani momveka chomwe wachiletsa kwa inu, kupatula (mukadya choletsedwacho) mosimidwa ndi kukakamizidwa (chifukwa cha njala)? Koma ndithu ambiri akusokeretsa (ena) mwa zifuniro zawo popanda kudziwa. Ndithu Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa bwino za olumpha malire.
Kodi yemwe adali wakufa, kenako nkumuukitsa ndi kumpangira kuunika; choncho ndi kuunikako nkumayenda kwa anthu, kodi angafanane ndi yemwe chikhalidwe chake chili mu mdima (wa umbuli) ndipo sakutha kutuluka m’menemo? Motero zakometsedwa kwa osakhulupirira (zoipa) zomwe akhala akuchita.
Ampangira Allah (amugawira) gawo m’zomera ndi ziweto zimene (Allah) adalenga. Akunena: “Gawo ili ndi la Allah.” Mkuyankhula kwawo kwachabe: “Ndipo gawo ili ndi la aja omwe tikuwaphatikiza ndi Allah.” Choncho zomwe alinga kuwapatsa aphatikizi awo, sizingafike kwa Allah. Ndipo zimene zili za Allah, ndizomwe zingafike kwa aphatikizi awo (mafano awo). Kwaipitsitsa kuweruza kwaoku.[174]
[174] Kale anthu osakhulupilira pamene ankalima akafuna kubzala, minda yawo adali kuigawa zigawo ziwiri. Ankati: ‘‘Mbewu za chigawo ichi nza Allah, kuti mbewu zakezo adzazigwiritsa ntchito powapatsa masikini, ana a masiye ndi osowa. Ndipo ankatinso: “Mbewu za gawo ili nzamafano athu omwe ankati ngamnzake a Allah kuti zinthu zotuluka m’menemo ziperekedwe kwa anthu ogwira ntchito m’menemo. Choncho ngati patapezeka mliri pachigawo chomwe ankati zokolola zake nzamafano awo, amatenga chigawo chomwe amati dzinthu dzake nza Allah napereka ku mafano. Koma mliri ukagwera pa chigawo cha Allah, sadali kutenga zamafano nkupereka kwa Allah. Izi amachita ngati mafano ngabwino kuposa Allah.
Momwemo milungu yawo imawakometsera ambiri mwa ophatikiza Allah ndi mafano kupha ana awo (monga nsembe ya mafanowo) kuti awaononge ndikuwabweretsera chisokonezo pa chipembedzo chawo. Ndipo ngati Allah akadafuna, sakadachita zimenezo. Choncho asiye ndi izo zomwe akupeka.
Ndipo amanenanso: “Zimene zili m’mimba mwa ziweto izi, ndi za amuna okha; ndipo nzoletsedwa kwa akazi athu.” Koma ngati chili chibudu, onse adali kugawana (amuna ndi akazi). Ndithudi, adzawalipira ndi zonena zawozo. Ndithu Iye (Allah), Ngwanzeru zakuya, Wodziwa kwambiri.
Ndipo Iye (Allah) ndi amene adapanga minda (ya mitengo) yothaza ndi yosathaza; ndipo (adapanga) mitengo yakanjedza ndi mmera wazipatso zosiyanasiyana makomedwe ake ndipo adapanganso mzitona ndi makomamanga, zofanana (mmaonekedwe) ndi zosiyana (mmakomemedwe). Idyani zipatso zake pamene zikupatsa. Ndipo perekani chopereka chake tsiku lokolola (powapatsa masikini ndi ogundizana nawo nyumba). Ndipo musaziononge pakudya mopyoza muyeso. Ndithu Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso.
(Adakulengerani) mitundu isanu ndi itatu ya nyama (pophatikiza zazimuna ndi zazikazi); nkhosa (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi); mbuzi (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi Iye adakuletsani zazimuna zonse ziwiri, (mbuzi ndi nkhosa) kapena zazikazi ziwiri, (nkhosa ndi mbuzi), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Ndiuzeni mwa nzeru ngati mukunenazi nzoona (kuti Allah adatero).
Ndipo Mûsa tidampatsa buku (kukhala) lokwaniritsa (chisomo) kwa yemwe wachita zabwino, lofotokoza chinthu chilichonse, chiongoko ndi chifundo, kuti iwo akhulupirire za kukumana ndi Mbuye wawo.
Kapena kuti musadzati: “Likadavumbulutsidwa buku kwa ife, ndithudi, tikadakhala oongoka kuposa iwo.” Choncho, chakudzerani chizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu, ndi chiongoko ndi mtendere. Kodi ndani woipitsitsa kwambiri kuposa amene watsutsa zizindikiro za Allah ndi kutembenukira kutali Nazo? Tidzawalipira amene akutembenukira kutali ndi zizindikiro zathu, chilango choipa, chifukwa cha kudziika kwawo kutali.
[176] China mwa chifundo cha Allah pa zolengedwa zake ndiko kuti adzamulipira munthu pa tsiku la chimaliziro mosiyanitsa pakati pa chabwino ndi choipa. Ngati adachita chabwino chimodzi, adzamulipira mphoto ya zinthu khumi zoposera pa chabwino chimodzicho ndipo ngati adachita choipa, sadzamuonjezera malipiro a choipacho koma adzamulipira chofanana ndi choipacho. Tanthauzo lake nkuti chabwino chimodzi malipiro ake ndi zabwino khumi; pomwe choipa chimodzi mphoto yake ndi choipanso chimodzi.
Nena: “Ndithudi, ine Mbuye wanga wandiongolera ku njira yoongoka, kuchipembedzo cholingana, chomwe ndi chipembedzo cha Ibrahim, yemwe adali wolungama. Sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano).
Ndipo Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala am’lowam’malo pa dziko (kulowa m’malo mwa anzanu omwe adaonongeka). Ndipo wawatukula pa ulemelero (ndi pa chuma) ena a inu pamwamba pa ena kuti akuyeseni pa zomwe wakupatsani. (Amene apatsidwa chuma ndi ulemelero athandize amene sadapatsidwe. Ndipo amene sadapatsidwe apirire asalande chinthu chamwini). Ndithudi, Mbuye wako Ngwachangu pokhaulitsa. Ndiponso Iye Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha.[177]
[177] Ndime iyi ikusonyeza kuti kukhupuka ndi ulemelero, sindizo zizindikiro zosonyeza kuti munthuyo ngofunika kwa Allah. Ndiponso kusauka ndi kunyozeka sizizindikiro kuti munthuyo ngosafunika kwa Allah kapena wonyozeka kwa Allah. Koma kulemera, ulemelero, kusauka ndi kunyozeka.zonsezi amazipereka m’njira ya mayeso.
Contents of the translations can be downloaded and re-published, with the following terms and conditions:
1. No modification, addition, or deletion of the content.
2. Clearly referring to the publisher and the source (QuranEnc.com).
3. Mentioning the version number when re-publishing the translation.
4. Keeping the transcript information inside the document.
5. Notifying the source (QuranEnc.com) of any note on the translation.
6. Updating the translation according to the latest version issued from the source (QuranEnc.com).
7. Inappropriate advertisements must not be included when displaying translations of the meanings of the Noble Quran.
అన్వేషణ ఫలితాలు:
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/v1/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-...] (Aya number in the sura)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".