Check out the new design

Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala * - Mealler fihristi


Anlam tercümesi Sure: Sûratu'l-En'âm   Ayet:
ذَٰلِكُمُ ٱللَّهُ رَبُّكُمۡۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ خَٰلِقُ كُلِّ شَيۡءٖ فَٱعۡبُدُوهُۚ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ وَكِيلٞ
Ameneyu ndi Allah, Mbuye wanu; palibe wina woti nkumpembedza mwa choonadi koma Iye. Mlengi wa chinthu chilichonse. Choncho, mpembedzeni. Iye ndi Muyang’aniri wa chinthu chilichonse.
Arapça tefsirler:
لَّا تُدۡرِكُهُ ٱلۡأَبۡصَٰرُ وَهُوَ يُدۡرِكُ ٱلۡأَبۡصَٰرَۖ وَهُوَ ٱللَّطِيفُ ٱلۡخَبِيرُ
Maso samufika (kuti nkumuona); koma Iye amawafika maso (amawaona pamodzi ndi eni masowo). Iye Ngodziwa zobisika kwambiri, Ngodziwa zoonekera.
Arapça tefsirler:
قَدۡ جَآءَكُم بَصَآئِرُ مِن رَّبِّكُمۡۖ فَمَنۡ أَبۡصَرَ فَلِنَفۡسِهِۦۖ وَمَنۡ عَمِيَ فَعَلَيۡهَاۚ وَمَآ أَنَا۠ عَلَيۡكُم بِحَفِيظٖ
(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu umboni otsimikizika wakufikani kuchokera kwa Mbuye wanu, choncho amene atsekule maso ake nkuyang’ana ndiye kuti (zotsatira zake zabwino) zili pa iye mwini. Ndipo amene atseke maso ake zili pa iye mwini (zotsatira zake zoipa). Ndipo ine sindili muyang’anili wanu.”
Arapça tefsirler:
وَكَذَٰلِكَ نُصَرِّفُ ٱلۡأٓيَٰتِ وَلِيَقُولُواْ دَرَسۡتَ وَلِنُبَيِّنَهُۥ لِقَوۡمٖ يَعۡلَمُونَ
Motero tikulongosola mwatsatanetsatane zizindikiro, (kuti azindikire). Ndikuti anene: “Wachita kuphunzira (izi, si Allah amene wakuuza.” Ndipo tazibwerezabwereza chonchi) kuti tilongosole ndi kufotokoza momveka kwa anthu odziwa.
Arapça tefsirler:
ٱتَّبِعۡ مَآ أُوحِيَ إِلَيۡكَ مِن رَّبِّكَۖ لَآ إِلَٰهَ إِلَّا هُوَۖ وَأَعۡرِضۡ عَنِ ٱلۡمُشۡرِكِينَ
Tsata zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako. Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ndipo apewe opembedza mafano.
Arapça tefsirler:
وَلَوۡ شَآءَ ٱللَّهُ مَآ أَشۡرَكُواْۗ وَمَا جَعَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ حَفِيظٗاۖ وَمَآ أَنتَ عَلَيۡهِم بِوَكِيلٖ
Ndipo Allah akadafuna sakadamphatikiza (ndi mafano), ndipo sitidakuike pa iwo kukhala muyang’aniri wawo. Ndipo iwe suli muyimiliri wawo.
Arapça tefsirler:
وَلَا تَسُبُّواْ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ فَيَسُبُّواْ ٱللَّهَ عَدۡوَۢا بِغَيۡرِ عِلۡمٖۗ كَذَٰلِكَ زَيَّنَّا لِكُلِّ أُمَّةٍ عَمَلَهُمۡ ثُمَّ إِلَىٰ رَبِّهِم مَّرۡجِعُهُمۡ فَيُنَبِّئُهُم بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Ndipo usawatukwane amene akupembedza (mafano) kusiya Allah, kuopera kuti angamtukwane Allah mwamwano popanda kuzindikira. Motero taukometsera m’badwo ulionse ntchito zake. Potsiriza adzabwerera kwa Mbuye wawo, choncho, Iye adzawauza zonse zomwe adali kuchita.
Arapça tefsirler:
وَأَقۡسَمُواْ بِٱللَّهِ جَهۡدَ أَيۡمَٰنِهِمۡ لَئِن جَآءَتۡهُمۡ ءَايَةٞ لَّيُؤۡمِنُنَّ بِهَاۚ قُلۡ إِنَّمَا ٱلۡأٓيَٰتُ عِندَ ٱللَّهِۖ وَمَا يُشۡعِرُكُمۡ أَنَّهَآ إِذَا جَآءَتۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndipo (akafiri) adalumbira Allah ndi malumbiro awo amphamvu kuti ngati chitawadzera chozizwitsa ndithu adzachikhulupirira. Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah (sizili mmanja mwanga). Kodi nchinthu chanji chingakudziwitseni (inu Asilamu) kuti (ngakhale) chitaza (chozizwitsacho) iwo sangakhulupirire?”
Arapça tefsirler:
وَنُقَلِّبُ أَفۡـِٔدَتَهُمۡ وَأَبۡصَٰرَهُمۡ كَمَا لَمۡ يُؤۡمِنُواْ بِهِۦٓ أَوَّلَ مَرَّةٖ وَنَذَرُهُمۡ فِي طُغۡيَٰنِهِمۡ يَعۡمَهُونَ
Ndipo titembenuza mitima yawo ndi maso awo (kotero kuti sangathe kuchikhulupirira ngakhale atachiona chozizwitsacho) monga momwe sadaikhulupirire (Qur’an) poyamba ndipo tiwasiya akuyumbayumba m’machimo awo.
Arapça tefsirler:
 
Anlam tercümesi Sure: Sûratu'l-En'âm
Surelerin fihristi Sayfa numarası
 
Kur'an-ı Kerim meal tercümesi - Çevaca Tercüme - Halid İbrahim Pitala - Mealler fihristi

Halid İbrahim Pitala Tercümesi.

Kapat