Check out the new design

قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا * - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى


مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: نۇر   ئايەت:

An-Nûr

سُورَةٌ أَنزَلۡنَٰهَا وَفَرَضۡنَٰهَا وَأَنزَلۡنَا فِيهَآ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖ لَّعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ
Iyi ndi Sura; taivumbulutsa, ndipo taikamo malamulo. Ndipo m’menemo tatumizamo Ayah (ndime) zomveka kuti mukumbukire (malamulo ndi kuchita nawo m’njira yoyenera).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
ٱلزَّانِيَةُ وَٱلزَّانِي فَٱجۡلِدُواْ كُلَّ وَٰحِدٖ مِّنۡهُمَا مِاْئَةَ جَلۡدَةٖۖ وَلَا تَأۡخُذۡكُم بِهِمَا رَأۡفَةٞ فِي دِينِ ٱللَّهِ إِن كُنتُمۡ تُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَٱلۡيَوۡمِ ٱلۡأٓخِرِۖ وَلۡيَشۡهَدۡ عَذَابَهُمَا طَآئِفَةٞ مِّنَ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Mkazi wachiwerewere ndi mwamuna wa chiwerewere aliyense wa iwo mkwapuleni zikoti zana limodzi (100). Musagwidwe chisoni ndi iwo pa chipembedzo (malamulo) cha Allah, ngati inu mukukhulupiriradi mwa Allah ndi tsiku la chimaliziro. Ndipo gulu la okhulupirira lionelere chilango chawo.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
ٱلزَّانِي لَا يَنكِحُ إِلَّا زَانِيَةً أَوۡ مُشۡرِكَةٗ وَٱلزَّانِيَةُ لَا يَنكِحُهَآ إِلَّا زَانٍ أَوۡ مُشۡرِكٞۚ وَحُرِّمَ ذَٰلِكَ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Mwamuna wa chiwerewere sakwatira mkazi (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena mkazi wopembedza mafano. Nayenso mkazi wachiwerewere sakwatiwa ndi mwamuna (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena wopembedza mafano. Ndipo zimenezi zaletsedwa kwa okhulupirira.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَٱلَّذِينَ يَرۡمُونَ ٱلۡمُحۡصَنَٰتِ ثُمَّ لَمۡ يَأۡتُواْ بِأَرۡبَعَةِ شُهَدَآءَ فَٱجۡلِدُوهُمۡ ثَمَٰنِينَ جَلۡدَةٗ وَلَا تَقۡبَلُواْ لَهُمۡ شَهَٰدَةً أَبَدٗاۚ وَأُوْلَٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡفَٰسِقُونَ
Ndipo amene akunamizira akazi odziteteza (powanamizira kuti achita chiwerewere), ndipo osabwera nazo mboni zinayi, akwapuleni zikoti 80; ndiponso musauvomereze umboni wawo mpaka kalekale. Iwo ngotuluka m’chilamulo cha Allah,
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
إِلَّا ٱلَّذِينَ تَابُواْ مِنۢ بَعۡدِ ذَٰلِكَ وَأَصۡلَحُواْ فَإِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
Kupatula amene alapa pambuyo pa zimenezo, ndipo nkukonza (zochita zawo), ndithu Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni, (awakhululukira).
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَٱلَّذِينَ يَرۡمُونَ أَزۡوَٰجَهُمۡ وَلَمۡ يَكُن لَّهُمۡ شُهَدَآءُ إِلَّآ أَنفُسُهُمۡ فَشَهَٰدَةُ أَحَدِهِمۡ أَرۡبَعُ شَهَٰدَٰتِۭ بِٱللَّهِ إِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
Ndipo amene akunamizira akazi awo (kuti achita chiwerewere) ndipo iwo nkukhala opanda mboni, koma (iwo) okha, choncho umboni wa mmodzi wa iwo (umene ungamchotsere chilango chomenyedwa zikoti 80), ndikupereka umboni kanayi polumbilira Allah kuti ndithu iye ndi mmodzi mwa onena zoona.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَٱلۡخَٰمِسَةُ أَنَّ لَعۡنَتَ ٱللَّهِ عَلَيۡهِ إِن كَانَ مِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ
Ndipo kachisanu (alumbire) kuti matembelero a Allah akhale pa iye ngati (iye) ali m’modzi mwa onama.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَيَدۡرَؤُاْ عَنۡهَا ٱلۡعَذَابَ أَن تَشۡهَدَ أَرۡبَعَ شَهَٰدَٰتِۭ بِٱللَّهِ إِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلۡكَٰذِبِينَ
Ndipo (mkazi) chilango amchotsera atapereka umboni kanayi polumbilira Allah kuti (uyu mwamuna) ndi mmodzi mwa onama.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَٱلۡخَٰمِسَةَ أَنَّ غَضَبَ ٱللَّهِ عَلَيۡهَآ إِن كَانَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
Ndipo kachisanu (alumbire) kuti mkwiyo wa Allah ukhale pa iye ngati (mwamuna wake) ali mmodzi mwa onena zoona.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ وَأَنَّ ٱللَّهَ تَوَّابٌ حَكِيمٌ
Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu (mukadavutika). Ndipo ndithu Allah Ngolandira kulapa;. Wanzeru zakuya.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
 
مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: نۇر
سۈرە مۇندەرىجىسى بەت نومۇرى
 
قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى

خالىد ئىبراھىم بېيتالا تەرجىمىسى.

تاقاش