Check out the new design

قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا * - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى


مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: نۇر   ئايەت:
رِجَالٞ لَّا تُلۡهِيهِمۡ تِجَٰرَةٞ وَلَا بَيۡعٌ عَن ذِكۡرِ ٱللَّهِ وَإِقَامِ ٱلصَّلَوٰةِ وَإِيتَآءِ ٱلزَّكَوٰةِ يَخَافُونَ يَوۡمٗا تَتَقَلَّبُ فِيهِ ٱلۡقُلُوبُ وَٱلۡأَبۡصَٰرُ
Anthu omwe malonda ogulitsa ndi kugula sawatangwanitsa posiya kukumbukira Allah ndi kupemphera (Swala) ndi kupereka chopereka (Zakaat) naopa tsiku lomwe mitima ndi maso zidzatembenukatembenuka.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
لِيَجۡزِيَهُمُ ٱللَّهُ أَحۡسَنَ مَا عَمِلُواْ وَيَزِيدَهُم مِّن فَضۡلِهِۦۗ وَٱللَّهُ يَرۡزُقُ مَن يَشَآءُ بِغَيۡرِ حِسَابٖ
Kuti Allah adzawalipire zabwino pa zomwe adachita ndi kuwaonjezera zabwino Zake. Ndipo Allah amampatsa amene wamfuna popanda chiwerengero.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَعۡمَٰلُهُمۡ كَسَرَابِۭ بِقِيعَةٖ يَحۡسَبُهُ ٱلظَّمۡـَٔانُ مَآءً حَتَّىٰٓ إِذَا جَآءَهُۥ لَمۡ يَجِدۡهُ شَيۡـٔٗا وَوَجَدَ ٱللَّهَ عِندَهُۥ فَوَفَّىٰهُ حِسَابَهُۥۗ وَٱللَّهُ سَرِيعُ ٱلۡحِسَابِ
Ndipo amene sadakhulupirire, ntchito zawo (zimene akuziona ngati zabwino) zidzakhala ngati zideruderu m’chipululu chamchenga; waludzu nkumaganizira kuti ndimadzi; ndipo akapita pamenepo, osapezapo chilichonse. (Nawonso pomwe adzadza kuzochita zawo zabwino patsiku la Qiyâma sadzapeza mphotho iliyonse, chifukwa chakuti adachimenya nkhondo Chisilamu). Ndipo adzapeza Allah kumeneko, ndipo adzamkwaniritsira chiwerengero chake ndipo Allah Ngwachangu powerengera.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
أَوۡ كَظُلُمَٰتٖ فِي بَحۡرٖ لُّجِّيّٖ يَغۡشَىٰهُ مَوۡجٞ مِّن فَوۡقِهِۦ مَوۡجٞ مِّن فَوۡقِهِۦ سَحَابٞۚ ظُلُمَٰتُۢ بَعۡضُهَا فَوۡقَ بَعۡضٍ إِذَآ أَخۡرَجَ يَدَهُۥ لَمۡ يَكَدۡ يَرَىٰهَاۗ وَمَن لَّمۡ يَجۡعَلِ ٱللَّهُ لَهُۥ نُورٗا فَمَا لَهُۥ مِن نُّورٍ
Kapena (ntchito zawo zoipazo) zili ngati m’dima mkati mwa nyanja yamadzi ochuluka yomwe yaphimbidwa ndi mafunde, ndipo pamwamba pa mafundewo pali mafundenso. Ndiponso pamwamba pake (mafundewo) pali mitambo. M’dima uwu pamwamba pa m’dima uwu. Akatulutsa mkono wake, sangathe kuuona (chifukwa cha kuchindikala kwa m’dima). Ndipo amene Allah sadampatse kuunika, sakhala nako kuunika.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يُسَبِّحُ لَهُۥ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَٱلطَّيۡرُ صَٰٓفَّٰتٖۖ كُلّٞ قَدۡ عَلِمَ صَلَاتَهُۥ وَتَسۡبِيحَهُۥۗ وَٱللَّهُ عَلِيمُۢ بِمَا يَفۡعَلُونَ
Kodi suona kuti zonse zopezeka kumwamba ndi pansi zikumulemekeza Allah, kudzanso mbalame zikatambasula mapiko ake (ngakhalenso zikapanda kutambasula). Chilichonse (mwa zimenezo) chikudziwa pemphero lake ndi m’mene chingamulemekezere (Mlengi wake). Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene akuchita.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
وَلِلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَإِلَى ٱللَّهِ ٱلۡمَصِيرُ
Ufumu wakumwamba ndi pansi, ngwa Allah (Yekha); ndipo kobwerera kwa zonse nkwa Allah.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
أَلَمۡ تَرَ أَنَّ ٱللَّهَ يُزۡجِي سَحَابٗا ثُمَّ يُؤَلِّفُ بَيۡنَهُۥ ثُمَّ يَجۡعَلُهُۥ رُكَامٗا فَتَرَى ٱلۡوَدۡقَ يَخۡرُجُ مِنۡ خِلَٰلِهِۦ وَيُنَزِّلُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مِن جِبَالٖ فِيهَا مِنۢ بَرَدٖ فَيُصِيبُ بِهِۦ مَن يَشَآءُ وَيَصۡرِفُهُۥ عَن مَّن يَشَآءُۖ يَكَادُ سَنَا بَرۡقِهِۦ يَذۡهَبُ بِٱلۡأَبۡصَٰرِ
Kodi suona kuti Allah akuyendetsa mitambo, kenako nkuikumanitsa pamodzi, ndipo kenako nkuikhazika m’milumilu? Nuona mvula ikutuluka pakati pa iyo. Iye akutsitsa mapiri amitambo kuchokera kumwamba momwe muli mvula yamatalala; ndipo amamenya nawo amene wamfuna, ndikumpewetsa amene wamfuna. Kung’anima kwake kumayandikira kuchititsa khungu.
ئەرەپچە تەپسىرلەر:
 
مەنالار تەرجىمىسى سۈرە: نۇر
سۈرە مۇندەرىجىسى بەت نومۇرى
 
قۇرئان كەرىم مەنىلىرىنىڭ تەرجىمىسى - شىيشىيۋاچە تەرجىمىسى - خالىد ئىبراھىم بىيتالا - تەرجىمىلەر مۇندەرىجىسى

خالىد ئىبراھىم بېيتالا تەرجىمىسى.

تاقاش