قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - شیشیوا ترجمہ۔ * - ترجمے کی لسٹ


معانی کا ترجمہ آیت: (39) سورت: سورۂ مریم
وَأَنذِرۡهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡحَسۡرَةِ إِذۡ قُضِيَ ٱلۡأَمۡرُ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٖ وَهُمۡ لَا يُؤۡمِنُونَ
Ndipo achenjeze (anthu) za tsiku la madandaulo, pamene chiweruzo chidzagamulidwa, (abwino kulowa ku munda wamtendere, oipa kulowa ku Moto); koma iwo (pano pa dziko lapansi) ali m’kusalabadira ndipo sakhulupirira.[270]
[270] Tsiku la Qiyâma (chimaliziro), anthu oipa adzadandaula kwambiri. Tsiku limenelo kwa iwo lidzakhala tsiku lamadandaulo okhaokha, osatinso chinachake. M’buku la swahihi la Musilim muli hadisi ya Abi Saidi Khuduriyi (r.a). Iye adati: Ndithu Mtumiki (s.a.w) adati: “Pamene anthu olungama adzalowa ku munda wa mtendere ndipo anthu oipa ku Moto, imfa idzadza tsiku la chimalizirolo. Idzaoneka ngati nkhosa yabwino. Ndipo idzaikidwa pakati pa Munda wa mtendere ndi Moto. Tsono kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Kenako kudzanenedwa: “E inu anthu a ku Moto! Kodi ichi mukuchidziwa?” Onse adzatukula makosi awo kuyang’ana nkuzati: “Inde iyo ndi imfa.” Ndipo kudzalamulidwa kuti izingidwe. Kenako kudzanenedwa: “E inu eni munda wa mtendere! Khalani muyaya m’menemo, palibe imfanso. Ndiponso inu eni Moto khalani muyaya mmenemo palibe imfanso.” Kenako Mtumiki (s.a.w) adawerenga Ayah (ndime) yakuti: “Achenjeze za tsiku lamadandaulo aakulu....”
عربی تفاسیر:
 
معانی کا ترجمہ آیت: (39) سورت: سورۂ مریم
سورتوں کی لسٹ صفحہ نمبر
 
قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - شیشیوا ترجمہ۔ - ترجمے کی لسٹ

قرآن کریم کے معانی کا شیشیوا ترجمہ، ترجمہ خالد ابراہیم بيتلا نے کیا ہے۔نسخہ ۲۰۲۰م۔

بند کریں