Check out the new design

قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا * - ترجمے کی لسٹ


معانی کا ترجمہ سورت: غافر   آیت:
وَلَقَدۡ جَآءَكُمۡ يُوسُفُ مِن قَبۡلُ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَمَا زِلۡتُمۡ فِي شَكّٖ مِّمَّا جَآءَكُم بِهِۦۖ حَتَّىٰٓ إِذَا هَلَكَ قُلۡتُمۡ لَن يَبۡعَثَ ٱللَّهُ مِنۢ بَعۡدِهِۦ رَسُولٗاۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ ٱللَّهُ مَنۡ هُوَ مُسۡرِفٞ مُّرۡتَابٌ
Ndithu adakudzerani kale Yûsuf ndi zisonyezo zoonekera poyera (Mûsa asadadze). Koma simudaleke kuzikaikira zimene adadza nazo kwa inu, kufikira pamene adamwalira, mudati: “Allah sadzatumiza mneneri wina pambuyo pake.” Motero Allah amamulekelera kusokera yemwe ali opyola malire poononga, wokaikira kwambiri.
عربی تفاسیر:
ٱلَّذِينَ يُجَٰدِلُونَ فِيٓ ءَايَٰتِ ٱللَّهِ بِغَيۡرِ سُلۡطَٰنٍ أَتَىٰهُمۡۖ كَبُرَ مَقۡتًا عِندَ ٱللَّهِ وَعِندَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْۚ كَذَٰلِكَ يَطۡبَعُ ٱللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ قَلۡبِ مُتَكَبِّرٖ جَبَّارٖ
Amene akutsutsana za zisonyezo za Allah popanda umboni uliwonse umene wawadzera. (Kutsutsa zisonyezo za Allah) nchokwiitsa Allah kwakukulu ndi kwa amene akhulupirira (mwa Allah). Momwemo ndi momwe Allah amadindira pamtima wa aliyense wodzikuza, wodzitukumula.
عربی تفاسیر:
وَقَالَ فِرۡعَوۡنُ يَٰهَٰمَٰنُ ٱبۡنِ لِي صَرۡحٗا لَّعَلِّيٓ أَبۡلُغُ ٱلۡأَسۡبَٰبَ
Ndipo Farawo adati: “E iwe Haamana! Ndimangire chipilala kuti ndikafike kunjira,”
عربی تفاسیر:
أَسۡبَٰبَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ فَأَطَّلِعَ إِلَىٰٓ إِلَٰهِ مُوسَىٰ وَإِنِّي لَأَظُنُّهُۥ كَٰذِبٗاۚ وَكَذَٰلِكَ زُيِّنَ لِفِرۡعَوۡنَ سُوٓءُ عَمَلِهِۦ وَصُدَّ عَنِ ٱلسَّبِيلِۚ وَمَا كَيۡدُ فِرۡعَوۡنَ إِلَّا فِي تَبَابٖ
“Njira za kumwamba kuti ndikamuone Mulungu wa Mûsa. Koma ndithu ine ndikudziwa kuti ameneyu ngonama.” Umo ndi momwe zochita zoipa za Farawo zidakongoletsedwera kwa iye, ndipo adatsekeretsedwa ku njira yoona, ndipo chiwembu cha Farawo sichakanthu, koma choonongeka.
عربی تفاسیر:
وَقَالَ ٱلَّذِيٓ ءَامَنَ يَٰقَوۡمِ ٱتَّبِعُونِ أَهۡدِكُمۡ سَبِيلَ ٱلرَّشَادِ
Ndipo uja adakhulupirira adati: “E inu anthu anga! Nditsatireni; ndikuongolerani ku njira yoongoka.”
عربی تفاسیر:
يَٰقَوۡمِ إِنَّمَا هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَا مَتَٰعٞ وَإِنَّ ٱلۡأٓخِرَةَ هِيَ دَارُ ٱلۡقَرَارِ
“E inu anthu anga! Ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndichisangalalo (chakutha). Ndithu tsiku lachimaliziro ndiye nyumba yokhazikikamo.”
عربی تفاسیر:
مَنۡ عَمِلَ سَيِّئَةٗ فَلَا يُجۡزَىٰٓ إِلَّا مِثۡلَهَاۖ وَمَنۡ عَمِلَ صَٰلِحٗا مِّن ذَكَرٍ أَوۡ أُنثَىٰ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَدۡخُلُونَ ٱلۡجَنَّةَ يُرۡزَقُونَ فِيهَا بِغَيۡرِ حِسَابٖ
“Amene akuchita choipa sadzalipidwa chinachake koma chofanana ndi chomwe adachita. Ndipo yemwe akuchita zabwino, mwamuna kapena mkazi, uku iye ali okhulupirira, iwowo adzalowa ku Minda ya mtendere. Adzapatsidwa zopatsidwa mmenemo zopanda chiwerengero.”
عربی تفاسیر:
 
معانی کا ترجمہ سورت: غافر
سورتوں کی لسٹ صفحہ نمبر
 
قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - چیچیوا ترجمہ - خالد ابراہیم بتیالا - ترجمے کی لسٹ

خالد ابراہیم پیٹالا نے ترجمہ کیا۔

بند کریں