قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - شیشیوا ترجمہ۔ * - ترجمے کی لسٹ


معانی کا ترجمہ سورت: سورۂ احقاف   آیت:

سورۂ احقاف

حمٓ
۞ Hâ-Mîm.
عربی تفاسیر:
تَنزِيلُ ٱلۡكِتَٰبِ مِنَ ٱللَّهِ ٱلۡعَزِيزِ ٱلۡحَكِيمِ
Chivumbulutso cha bukuli nchochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.
عربی تفاسیر:
مَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَآ إِلَّا بِٱلۡحَقِّ وَأَجَلٖ مُّسَمّٗىۚ وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ عَمَّآ أُنذِرُواْ مُعۡرِضُونَ
Sitidangolenga thambo ndi nthaka ndiponso zonse zapakati pa izo koma mwachoonadi ndi nyengo yoikidwa (yodziwika). Koma amene akana kukhulupirira (Allah) ngonyozera zimene achenjezedwa.
عربی تفاسیر:
قُلۡ أَرَءَيۡتُم مَّا تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَرُونِي مَاذَا خَلَقُواْ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ لَهُمۡ شِرۡكٞ فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِۖ ٱئۡتُونِي بِكِتَٰبٖ مِّن قَبۡلِ هَٰذَآ أَوۡ أَثَٰرَةٖ مِّنۡ عِلۡمٍ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Nena: Tandiuzani amene mukuwapembedza ndi kumusiya Allah, ndisonyezeni chimene adalenga panthaka? Kapena ali ndi gawo la kuthangata polenga thambo? Ndibweretsereni buku limene lidadza kale, ili lisanadze, kapena zizindikiro zanzeru, ngati inu mukunena zoona.
عربی تفاسیر:
وَمَنۡ أَضَلُّ مِمَّن يَدۡعُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَن لَّا يَسۡتَجِيبُ لَهُۥٓ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ وَهُمۡ عَن دُعَآئِهِمۡ غَٰفِلُونَ
Kodi ndindani amene ali osokera kwambiri kuposa amene akupembedza zina kusiya Allah zomwe sizingathe kumuyankha mpaka tsiku la chiweruziro ndipo izo (zimafano) sizikuzindikira za mapemphero awo.
عربی تفاسیر:
وَإِذَا حُشِرَ ٱلنَّاسُ كَانُواْ لَهُمۡ أَعۡدَآءٗ وَكَانُواْ بِعِبَادَتِهِمۡ كَٰفِرِينَ
Ndipo anthu onse akadzasonkhanitsidwa adzakhala adani awo ndikuwakanira mapemphero awo.
عربی تفاسیر:
وَإِذَا تُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ ءَايَٰتُنَا بَيِّنَٰتٖ قَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُمۡ هَٰذَا سِحۡرٞ مُّبِينٌ
Ndipo pamene zikuwerengedwa kwa iwo Ayah Zathu zolongosola chilichonse (cha m’chipembedzo), amene sadakhulupirire amanena pa choonadi chikawadzera: “Awa ndi matsenga oonekera.”
عربی تفاسیر:
أَمۡ يَقُولُونَ ٱفۡتَرَىٰهُۖ قُلۡ إِنِ ٱفۡتَرَيۡتُهُۥ فَلَا تَمۡلِكُونَ لِي مِنَ ٱللَّهِ شَيۡـًٔاۖ هُوَ أَعۡلَمُ بِمَا تُفِيضُونَ فِيهِۚ كَفَىٰ بِهِۦ شَهِيدَۢا بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۖ وَهُوَ ٱلۡغَفُورُ ٱلرَّحِيمُ
Kapena akunena kuti: “Waipeka (Qur’an)?” Nena: “Ngati ine ndaipeka, tero simungapeze chondithandizira nacho kwa Allah (ku chilango Chake). Iye ndiwodziwa kwambiri zimene mukuzijijirikira. Iye akukwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu ndipo Iye Ngokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha.”
عربی تفاسیر:
قُلۡ مَا كُنتُ بِدۡعٗا مِّنَ ٱلرُّسُلِ وَمَآ أَدۡرِي مَا يُفۡعَلُ بِي وَلَا بِكُمۡۖ إِنۡ أَتَّبِعُ إِلَّا مَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّ وَمَآ أَنَا۠ إِلَّا نَذِيرٞ مُّبِينٞ
Nena: “Ine sindine woyamba pa aneneri, ndipo sindikudziwa zimene zidzachitike kwa ine ngakhale kwa inu. Sinditsatira koma zokhazo zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine; ndipo ine sindili kanthu koma mchenjezi wolongosola (zofunika).”
عربی تفاسیر:
قُلۡ أَرَءَيۡتُمۡ إِن كَانَ مِنۡ عِندِ ٱللَّهِ وَكَفَرۡتُم بِهِۦ وَشَهِدَ شَاهِدٞ مِّنۢ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ عَلَىٰ مِثۡلِهِۦ فَـَٔامَنَ وَٱسۡتَكۡبَرۡتُمۡۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَا يَهۡدِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلظَّٰلِمِينَ
Nena: “Tandiuzani, ngati (buku ili) litachokera kwa Allah, ndipo inu nkulikana uku mboni yochokera mu ana a Israyeli itachitira umboni kuti idaliona longa limeneli, ndipo iyo nkulikhulupirira (bukuli) pomwe inu mwadzitukumula, ndithu Allah saongola anthu osalungama.”
عربی تفاسیر:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَوۡ كَانَ خَيۡرٗا مَّا سَبَقُونَآ إِلَيۡهِۚ وَإِذۡ لَمۡ يَهۡتَدُواْ بِهِۦ فَسَيَقُولُونَ هَٰذَآ إِفۡكٞ قَدِيمٞ
Ndipo amene sadakhulupirire adanena kwa amene adakhulupirira: “(Chipembedzo ichi) chikadakhala chabwino, awa sakadakhala otsogola ku chimenechi pa ife.” Ndipo chifukwa choti sadaongoke nalo (bukuli), akhala akunena: “Ili ndi bodza lakale.”
عربی تفاسیر:
وَمِن قَبۡلِهِۦ كِتَٰبُ مُوسَىٰٓ إِمَامٗا وَرَحۡمَةٗۚ وَهَٰذَا كِتَٰبٞ مُّصَدِّقٞ لِّسَانًا عَرَبِيّٗا لِّيُنذِرَ ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ وَبُشۡرَىٰ لِلۡمُحۡسِنِينَ
Ndipo lisadadze ili lidalipo buku la Mûsa monga mtsogoleri ndi chifundo. Ndipo buku ili likuikira umboni (za bukulo) m’chiyankhulo cha Chiarabu kuti liwachenjeze amene adzichitira okha chinyengo, ndi kuti likhale uthenga wabwino kwa ochita zabwino.
عربی تفاسیر:
إِنَّ ٱلَّذِينَ قَالُواْ رَبُّنَا ٱللَّهُ ثُمَّ ٱسۡتَقَٰمُواْ فَلَا خَوۡفٌ عَلَيۡهِمۡ وَلَا هُمۡ يَحۡزَنُونَ
Ndithu amene anena (kuti): “Mbuye wathu ndi Allah.” Kenako ndikulungama, sadzakhala ndi mantha (tsiku lakufa kwawo ngakhale pambuyo pake), ndiponso sadzadandaula.
عربی تفاسیر:
أُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلۡجَنَّةِ خَٰلِدِينَ فِيهَا جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Iwowo ndiwo anthu aku Jannah adzakhala kumeneko nthawi yaitali kukhala mphoto ya zimene amachita.
عربی تفاسیر:
وَوَصَّيۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ بِوَٰلِدَيۡهِ إِحۡسَٰنًاۖ حَمَلَتۡهُ أُمُّهُۥ كُرۡهٗا وَوَضَعَتۡهُ كُرۡهٗاۖ وَحَمۡلُهُۥ وَفِصَٰلُهُۥ ثَلَٰثُونَ شَهۡرًاۚ حَتَّىٰٓ إِذَا بَلَغَ أَشُدَّهُۥ وَبَلَغَ أَرۡبَعِينَ سَنَةٗ قَالَ رَبِّ أَوۡزِعۡنِيٓ أَنۡ أَشۡكُرَ نِعۡمَتَكَ ٱلَّتِيٓ أَنۡعَمۡتَ عَلَيَّ وَعَلَىٰ وَٰلِدَيَّ وَأَنۡ أَعۡمَلَ صَٰلِحٗا تَرۡضَىٰهُ وَأَصۡلِحۡ لِي فِي ذُرِّيَّتِيٓۖ إِنِّي تُبۡتُ إِلَيۡكَ وَإِنِّي مِنَ ٱلۡمُسۡلِمِينَ
Ndipo tamulangiza munthu kuchitira zabwino makolo ake. Mayi wake adatenga pathupi pake mwamasautso; ndipo adam’bala mwamasautso. Kutenga pakati pake ndi kumsiitsa kuyamwa ndi miyezi makumi atatu. Kufikira atakula nsinkhu nkukwana zaka makumi anayi, (akakhala mwana wabwino) amanena: “E Mbuye wanga! Ndilimbikitseni kuthokoza mtendere Wanu umene mwandipatsa pamodzi ndi makolo anga, ndipo ndilimbitseni kuti ndizichita zabwino zimene (Inu) muziyanja ndipo ndikonzereni ndi kundilungamitsira ana anga. Ine ndatembenukira kwa Inu; ndiponso ine ndine m’modzi mwa ogonjera (Inu).”
عربی تفاسیر:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ نَتَقَبَّلُ عَنۡهُمۡ أَحۡسَنَ مَا عَمِلُواْ وَنَتَجَاوَزُ عَن سَيِّـَٔاتِهِمۡ فِيٓ أَصۡحَٰبِ ٱلۡجَنَّةِۖ وَعۡدَ ٱلصِّدۡقِ ٱلَّذِي كَانُواْ يُوعَدُونَ
Iwowo ndiamene tikuwalandira zabwino zimene adachita ndipo tikuwakhululukira zolakwa zawo. Adzakhala m’gulu la anthu a ku Jannah. Ili ndi lonjezo loona lomwe adalonjezedwa.
عربی تفاسیر:
وَٱلَّذِي قَالَ لِوَٰلِدَيۡهِ أُفّٖ لَّكُمَآ أَتَعِدَانِنِيٓ أَنۡ أُخۡرَجَ وَقَدۡ خَلَتِ ٱلۡقُرُونُ مِن قَبۡلِي وَهُمَا يَسۡتَغِيثَانِ ٱللَّهَ وَيۡلَكَ ءَامِنۡ إِنَّ وَعۡدَ ٱللَّهِ حَقّٞ فَيَقُولُ مَا هَٰذَآ إِلَّآ أَسَٰطِيرُ ٱلۡأَوَّلِينَ
Tsono (mwana woipa) amene akunena kwa makolo ake, (akamuitanira ku chikhulupiliro kuti): “Ndithu ndinu oipa (pa zimene mukundiitanirazi)! Mukundilonjeza kuti ndidzatulutsidwa mmanda ndili wamoyo, chikhalirecho mibadwo ndi mibadwo idapita kumanda ine kulibe (koma mpaka lero siidauke)?” Ndipo uku makolo ake akupempha Allah kuti ampulumutse ndi kumuongola ndi kunena kwa iye: “Tsoka kwa iwe khulupirira (Allah ndi kuuka ku imfa, ngati sutero waonongeka). Ndithu lonjezo la Allah ndiloona.” Koma iye nkumanena (kuti): “Mukunenazi sikanthu koma ndi nthano za anthu akale.”
عربی تفاسیر:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ حَقَّ عَلَيۡهِمُ ٱلۡقَوۡلُ فِيٓ أُمَمٖ قَدۡ خَلَتۡ مِن قَبۡلِهِم مِّنَ ٱلۡجِنِّ وَٱلۡإِنسِۖ إِنَّهُمۡ كَانُواْ خَٰسِرِينَ
Iwowo ndiamene latsimikizika pa iwo liwu (la chilango) pamodzi ndi mibadwo ya ziwanda ndi anthu, imene idanka kale iwo kulibe; ndithu iwo adali otaika.
عربی تفاسیر:
وَلِكُلّٖ دَرَجَٰتٞ مِّمَّا عَمِلُواْۖ وَلِيُوَفِّيَهُمۡ أَعۡمَٰلَهُمۡ وَهُمۡ لَا يُظۡلَمُونَ
Ndipo aliyense wokhulupirira adzakhala ndi nyota molingana ndi zimene adachita, ndi kuti (Allah) awalipire zochita zawo ndipo iwo sadzaponderezedwa.
عربی تفاسیر:
وَيَوۡمَ يُعۡرَضُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ عَلَى ٱلنَّارِ أَذۡهَبۡتُمۡ طَيِّبَٰتِكُمۡ فِي حَيَاتِكُمُ ٱلدُّنۡيَا وَٱسۡتَمۡتَعۡتُم بِهَا فَٱلۡيَوۡمَ تُجۡزَوۡنَ عَذَابَ ٱلۡهُونِ بِمَا كُنتُمۡ تَسۡتَكۡبِرُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ بِغَيۡرِ ٱلۡحَقِّ وَبِمَا كُنتُمۡ تَفۡسُقُونَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku limene adzaikidwa pafupi ndi moto amene sadakhulupirire (adzawauza kuti) “Mudaononga zabwino zanu mmoyo wa dziko lapansi, (choncho lero simuzipezanso), ndipo inu mudasangalala nazo zimenezo, choncho lero mupatsidwa chilango chokusambulani chifukwa cha kudzikweza kwanu pa dziko popanda choona, ndiponso chifukwa cha kulakwa kwanu.”
عربی تفاسیر:
۞ وَٱذۡكُرۡ أَخَا عَادٍ إِذۡ أَنذَرَ قَوۡمَهُۥ بِٱلۡأَحۡقَافِ وَقَدۡ خَلَتِ ٱلنُّذُرُ مِنۢ بَيۡنِ يَدَيۡهِ وَمِنۡ خَلۡفِهِۦٓ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّا ٱللَّهَ إِنِّيٓ أَخَافُ عَلَيۡكُمۡ عَذَابَ يَوۡمٍ عَظِيمٖ
Ndipo kumbuka za m’bale wa Âdi, (mtumiki Hûd) pamene adachenjeza anthu ake kudziko la milu ya mchenga. Ndithu adaliponso achenjezi iye asadadze ndiponso iye atapita. (Iye adawauza anthu ake): “Musampembedze aliyense koma Allah; ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”[345]
[345] Dziko la milu ya mchenga: Awa ndi malo omwe akupezeka kummwera kwa mzinda wa Hadra Mauti pakati pa dziko la Omman ndi Yemen kwao kwa Âdi.
عربی تفاسیر:
قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا لِتَأۡفِكَنَا عَنۡ ءَالِهَتِنَا فَأۡتِنَا بِمَا تَعِدُنَآ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّٰدِقِينَ
Adanena: “Ha! Kodi watidzera kuti utipatule ku milungu yathu? Choncho tibweretsere zimene ukutilonjezazo ngati uli mwa onena zoona.”
عربی تفاسیر:
قَالَ إِنَّمَا ٱلۡعِلۡمُ عِندَ ٱللَّهِ وَأُبَلِّغُكُم مَّآ أُرۡسِلۡتُ بِهِۦ وَلَٰكِنِّيٓ أَرَىٰكُمۡ قَوۡمٗا تَجۡهَلُونَ
Adanena (Hûd): “Ndithu kudziwa (kwenikweni kwa zimenezo) kuli kwa Allah; ndipo ine ndikungofikitsa kwa inu zimene ndatumidwa koma ine ndikukuonani kuti inu ndinu anthu amene mukuchita (zinthu za) umbuli!.
عربی تفاسیر:
فَلَمَّا رَأَوۡهُ عَارِضٗا مُّسۡتَقۡبِلَ أَوۡدِيَتِهِمۡ قَالُواْ هَٰذَا عَارِضٞ مُّمۡطِرُنَاۚ بَلۡ هُوَ مَا ٱسۡتَعۡجَلۡتُم بِهِۦۖ رِيحٞ فِيهَا عَذَابٌ أَلِيمٞ
Kenako pamene adauona (mtambo) ukulunjika ku zigwa zawo, adanena: “(Mtambo) uwu ndi wotivumbwitsira mvula!” (Adauzidwa): “Iyayi, chimenechi ndichimene mudachifulumizitsa chija (kuti chidze mwachangu), mphepo (ya mkutho) yomwe mkati mwake muli chilango chowawa!
عربی تفاسیر:
تُدَمِّرُ كُلَّ شَيۡءِۭ بِأَمۡرِ رَبِّهَا فَأَصۡبَحُواْ لَا يُرَىٰٓ إِلَّا مَسَٰكِنُهُمۡۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلۡقَوۡمَ ٱلۡمُجۡرِمِينَ
Yoononga chinthu chilichonse mwa lamulo la Mbuye wake!” Kenako adali osaonedwanso, kupatula nyumba zawo (ndizimene zidatsalira). Umo ndim’mene timawalipirira anthu oipa.
عربی تفاسیر:
وَلَقَدۡ مَكَّنَّٰهُمۡ فِيمَآ إِن مَّكَّنَّٰكُمۡ فِيهِ وَجَعَلۡنَا لَهُمۡ سَمۡعٗا وَأَبۡصَٰرٗا وَأَفۡـِٔدَةٗ فَمَآ أَغۡنَىٰ عَنۡهُمۡ سَمۡعُهُمۡ وَلَآ أَبۡصَٰرُهُمۡ وَلَآ أَفۡـِٔدَتُهُم مِّن شَيۡءٍ إِذۡ كَانُواْ يَجۡحَدُونَ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَحَاقَ بِهِم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndipo ndithu tidawapatsa mphamvu (yochitira zinthu ndi kukhala ndi chuma chambiri ndi moyo wautali) zomwe sitidakupatseni inu (Aquraish) ndipo tidawapatsa makutu ndi maso ndi mitima, koma makutu awo ndi maso awo ndi mitima yawo sizidawapindulire chilichonse chifukwa chotsutsa Ayah za Allah; ndipo zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe.
عربی تفاسیر:
وَلَقَدۡ أَهۡلَكۡنَا مَا حَوۡلَكُم مِّنَ ٱلۡقُرَىٰ وَصَرَّفۡنَا ٱلۡأٓيَٰتِ لَعَلَّهُمۡ يَرۡجِعُونَ
Ndithu tidaiononga midzi imene yakuzungulirani; ndipo tidawafotokozera momveka Ayah Zathu kuti abwelere.
عربی تفاسیر:
فَلَوۡلَا نَصَرَهُمُ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ قُرۡبَانًا ءَالِهَةَۢۖ بَلۡ ضَلُّواْ عَنۡهُمۡۚ وَذَٰلِكَ إِفۡكُهُمۡ وَمَا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
Chifukwa chiyani siidawapulumutse milungu imene adaipangayo kusiya Allah kuti iwayandikitse kwa Iye (Allah)? Koma idasoweka kwa iwo (pomwe iwo adali pamavuto ofuna kulandira chithandizo). Ndipo zimenezo ndizo zotsatira zabodza lawo ndi zomwe adali kupeka.
عربی تفاسیر:
وَإِذۡ صَرَفۡنَآ إِلَيۡكَ نَفَرٗا مِّنَ ٱلۡجِنِّ يَسۡتَمِعُونَ ٱلۡقُرۡءَانَ فَلَمَّا حَضَرُوهُ قَالُوٓاْ أَنصِتُواْۖ فَلَمَّا قُضِيَ وَلَّوۡاْ إِلَىٰ قَوۡمِهِم مُّنذِرِينَ
Ndipo (kumbuka iwe Mtumiki{s.a.w}) pamene tidakutumizira gulu la ziwanda (majini) kudzamvera Qur’an ndipo pamene izo zidafika pamalopo zidanena pakati pawo: “Khalani chete!” Pomwe kuwerenga (kwa Qur’an) kudatha, zidabwerera ku mtundu wawo kukawachenjeza (za chilango cha Allah).
عربی تفاسیر:
قَالُواْ يَٰقَوۡمَنَآ إِنَّا سَمِعۡنَا كِتَٰبًا أُنزِلَ مِنۢ بَعۡدِ مُوسَىٰ مُصَدِّقٗا لِّمَا بَيۡنَ يَدَيۡهِ يَهۡدِيٓ إِلَى ٱلۡحَقِّ وَإِلَىٰ طَرِيقٖ مُّسۡتَقِيمٖ
Zidanena: “E inu anzathu! Ife tamva (zowerengedwa) za m’buku (lolemekezeka) lomwe lavumbulutsidwa pambuyo pa Mûsa, loikira umboni zimene zidalitsogolera; likuongolera ku choona ndi kunjira yolunjika.”
عربی تفاسیر:
يَٰقَوۡمَنَآ أَجِيبُواْ دَاعِيَ ٱللَّهِ وَءَامِنُواْ بِهِۦ يَغۡفِرۡ لَكُم مِّن ذُنُوبِكُمۡ وَيُجِرۡكُم مِّنۡ عَذَابٍ أَلِيمٖ
“E inu anzathu! Muvomereni woitana wa Allah, ndipo mkhulupirireni; (Allah) akukhululukirani machimo anu ndi kukutetezani ku chilango chowawa.
عربی تفاسیر:
وَمَن لَّا يُجِبۡ دَاعِيَ ٱللَّهِ فَلَيۡسَ بِمُعۡجِزٖ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَيۡسَ لَهُۥ مِن دُونِهِۦٓ أَوۡلِيَآءُۚ أُوْلَٰٓئِكَ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ
Ngati wina samuvomera woitanira kwa Allah, sangamulepheretse (Allah) pa dziko (akafuna kumuchita kanthu), ndipo iye alibe atetezi ena kupatula Iye (Allah). Otere akusokera koonekera poyera.”
عربی تفاسیر:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَلَمۡ يَعۡيَ بِخَلۡقِهِنَّ بِقَٰدِرٍ عَلَىٰٓ أَن يُحۡـِۧيَ ٱلۡمَوۡتَىٰۚ بَلَىٰٓۚ إِنَّهُۥ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
Kodi iwo saona kuti Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka, ndipo sadatope pozilenga, ndi Wakutha kuwaukitsa anthu ku irnfa? Inde, ndithu Iye Ngokhoza kuchita chilichonse.
عربی تفاسیر:
وَيَوۡمَ يُعۡرَضُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ عَلَى ٱلنَّارِ أَلَيۡسَ هَٰذَا بِٱلۡحَقِّۖ قَالُواْ بَلَىٰ وَرَبِّنَاۚ قَالَ فَذُوقُواْ ٱلۡعَذَابَ بِمَا كُنتُمۡ تَكۡفُرُونَ
Ndipo (akumbutse za) tsiku limene adzaperekedwa ku moto amene sadakhulupirire (uku akuuzidwa): “Kodi izi sizoona?” Adzanena: “Inde, pali Mbuye wathu!” (Allah) adzanena: “Choncho, lawani chilango chifukwa cha kukana kwanu (choonadi).”
عربی تفاسیر:
فَٱصۡبِرۡ كَمَا صَبَرَ أُوْلُواْ ٱلۡعَزۡمِ مِنَ ٱلرُّسُلِ وَلَا تَسۡتَعۡجِل لَّهُمۡۚ كَأَنَّهُمۡ يَوۡمَ يَرَوۡنَ مَا يُوعَدُونَ لَمۡ يَلۡبَثُوٓاْ إِلَّا سَاعَةٗ مِّن نَّهَارِۭۚ بَلَٰغٞۚ فَهَلۡ يُهۡلَكُ إِلَّا ٱلۡقَوۡمُ ٱلۡفَٰسِقُونَ
Choncho pirira (Mtumiki {s.a.w}) monga adapirira aneneri, eni mphamvu ndi kulimba pa chipembedzo, (monga Nuh. Ibrahimu, Mûsa ndi Isa (Yesu); ndipo usawachitire changu. Tsiku limene adzaziona zimene adalonjezedwa kudzakhala monga iwo sadakhalitse pa dziko koma ngati adakhala ola limodzi lokha lamasana. (Zomwe mukuuzidwazi) ndi ulaliki okwana. Palibe adzaonongedwe (ndi chilango cha Allah), kupatula anthu ochimwa (otuluka m’chilamulo cha Allah).
عربی تفاسیر:
 
معانی کا ترجمہ سورت: سورۂ احقاف
سورتوں کی لسٹ صفحہ نمبر
 
قرآن کریم کے معانی کا ترجمہ - شیشیوا ترجمہ۔ - ترجمے کی لسٹ

قرآن کریم کے معانی کا شیشیوا ترجمہ، ترجمہ خالد ابراہیم بيتلا نے کیا ہے۔نسخہ ۲۰۲۰م۔

بند کریں