Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима * - Таржималар мундарижаси


Маънолар таржимаси Сура: Анбиё сураси   Оят:

Анбиё сураси

ٱقۡتَرَبَ لِلنَّاسِ حِسَابُهُمۡ وَهُمۡ فِي غَفۡلَةٖ مُّعۡرِضُونَ
۞ Chiwerengero chayandikira kwa anthu pomwe iwo ali m’kusalabadira ndi M’kunyozera.
Арабча тафсирлар:
مَا يَأۡتِيهِم مِّن ذِكۡرٖ مِّن رَّبِّهِم مُّحۡدَثٍ إِلَّا ٱسۡتَمَعُوهُ وَهُمۡ يَلۡعَبُونَ
Palibe pamene ukuwadzera ulaliki watsopano wochokera kwa Mbuye wawo koma amaumvetsera uku akuchita zachibwana.
Арабча тафсирлар:
لَاهِيَةٗ قُلُوبُهُمۡۗ وَأَسَرُّواْ ٱلنَّجۡوَى ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ هَلۡ هَٰذَآ إِلَّا بَشَرٞ مِّثۡلُكُمۡۖ أَفَتَأۡتُونَ ٱلسِّحۡرَ وَأَنتُمۡ تُبۡصِرُونَ
Mitima yawo ikunyozera (osalabadira za kudza kwa Qiyâma). Ndipo akunenezana mobisa amene adzichitira zoipa; (akuuzana motere): “Kodi uyu (Muhammadiyu) ndi ndani, simunthu monga inu? Kodi mukuudzera ufiti pomwe mukuuona?”
Арабча тафсирлар:
قَالَ رَبِّي يَعۡلَمُ ٱلۡقَوۡلَ فِي ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِۖ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
(Mneneri Muhammad{s.a.w}) adati: “Mbuye wanga akudziwa zimene zikunenedwa kumwamba ndi pansi; ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa.
Арабча тафсирлар:
بَلۡ قَالُوٓاْ أَضۡغَٰثُ أَحۡلَٰمِۭ بَلِ ٱفۡتَرَىٰهُ بَلۡ هُوَ شَاعِرٞ فَلۡيَأۡتِنَا بِـَٔايَةٖ كَمَآ أُرۡسِلَ ٱلۡأَوَّلُونَ
Koma (osakhulupirira) adati: “(Izi zimene akufotokozazi) ndi maloto opanda pake.” (Ndipo nthawi zina amati:) “Koma zimenezi wazipeka.” (Penanso amati:) “Koma iyeyu ndi mlakatuli. Chonchotu, atibweretsere chizizwa monga mmene adatumiziridwa (aneneri) oyamba.”
Арабча тафсирлар:
مَآ ءَامَنَتۡ قَبۡلَهُم مِّن قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَآۖ أَفَهُمۡ يُؤۡمِنُونَ
Sadakhulupirire apatsogolo pawo, eni midzi imene tidaiononga (ngakhale kuti zozizwitsa adaziona); nanga iwo akhulupirira?
Арабча тафсирлар:
وَمَآ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ إِلَّا رِجَالٗا نُّوحِيٓ إِلَيۡهِمۡۖ فَسۡـَٔلُوٓاْ أَهۡلَ ٱلذِّكۡرِ إِن كُنتُمۡ لَا تَعۡلَمُونَ
Ndipo sitidawatume patsogolo pako, (iwe Mtumiki,) koma anthu, (osati angelo); tidawavumbulutsira (chivumbulutso Chathu.) Choncho, afunseni eni kudziwa ngati inu simukudziwa (nkhani zakale).
Арабча тафсирлар:
وَمَا جَعَلۡنَٰهُمۡ جَسَدٗا لَّا يَأۡكُلُونَ ٱلطَّعَامَ وَمَا كَانُواْ خَٰلِدِينَ
Ndipo sitidawachite (aneneriwo) kukhala matupi osadya chakudya ndipo sadalinso okhala nthawi yaitali.
Арабча тафсирлар:
ثُمَّ صَدَقۡنَٰهُمُ ٱلۡوَعۡدَ فَأَنجَيۡنَٰهُمۡ وَمَن نَّشَآءُ وَأَهۡلَكۡنَا ٱلۡمُسۡرِفِينَ
Kenako tidawatsimikizira lonjezo (la kuwathangata pa adani awo), ndipo tidawapulumutsa iwo ndi amene tidawafuna (mwa omwe adawatsata), ndipo olumpha malire (a Allah) Tidawaononga.
Арабча тафсирлар:
لَقَدۡ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ كِتَٰبٗا فِيهِ ذِكۡرُكُمۡۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
Ndithu tatumiza kwa inu buku lomwe m’kati mwake muli ulaliki wanu (malangizo kwa inu). Kodi simukuzindikira?
Арабча тафсирлар:
وَكَمۡ قَصَمۡنَا مِن قَرۡيَةٖ كَانَتۡ ظَالِمَةٗ وَأَنشَأۡنَا بَعۡدَهَا قَوۡمًا ءَاخَرِينَ
Ndi ambiri mwa eni midzi yomwe idali yosalungama, tidawaononga; ndipo pambuyo pake tidalenga anthu ena.
Арабча тафсирлар:
فَلَمَّآ أَحَسُّواْ بَأۡسَنَآ إِذَا هُم مِّنۡهَا يَرۡكُضُونَ
Pamene adazindikira za chilango chathu, pompo adayamba kuchithawa.
Арабча тафсирлар:
لَا تَرۡكُضُواْ وَٱرۡجِعُوٓاْ إِلَىٰ مَآ أُتۡرِفۡتُمۡ فِيهِ وَمَسَٰكِنِكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تُسۡـَٔلُونَ
Musathawe, (kuthawa sikukupulumutsani), koma bwererani ku zimene mwasangalatsidwa nazo ndi m’malo mwanu, kuti mufunsidwe.
Арабча тафсирлар:
قَالُواْ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ
Adanena: “Tsoka lathu ndithu! Tidali ochita zoipa.”
Арабча тафсирлар:
فَمَا زَالَت تِّلۡكَ دَعۡوَىٰهُمۡ حَتَّىٰ جَعَلۡنَٰهُمۡ حَصِيدًا خَٰمِدِينَ
Kukuwa kwawoko sikudathe, kufikira tidawapanga ngati (mbewu) zokololedwa, mpaka kupuma kwawo kudazima (adafa).
Арабча тафсирлар:
وَمَا خَلَقۡنَا ٱلسَّمَآءَ وَٱلۡأَرۡضَ وَمَا بَيۡنَهُمَا لَٰعِبِينَ
Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, mwamasewera.
Арабча тафсирлар:
لَوۡ أَرَدۡنَآ أَن نَّتَّخِذَ لَهۡوٗا لَّٱتَّخَذۡنَٰهُ مِن لَّدُنَّآ إِن كُنَّا فَٰعِلِينَ
Tikadafuna kupanga choti tiziseweretsa (sitidakapanga zomwe mukuzionazi) tikadapanga mwazomwe tili nazo, tikadakhala oti tichite (zachibwana).
Арабча тафсирлар:
بَلۡ نَقۡذِفُ بِٱلۡحَقِّ عَلَى ٱلۡبَٰطِلِ فَيَدۡمَغُهُۥ فَإِذَا هُوَ زَاهِقٞۚ وَلَكُمُ ٱلۡوَيۡلُ مِمَّا تَصِفُونَ
Koma (chimene timachita ndi ichi), timachiponya choona pa chachabe ndi kuchiswa bongo bwake, ndipo chachabecho chimachoka. Ndipo chilango chili pa inu chifukwa cha zomwe mukunena (kumnamizira Allah).
Арабча тафсирлар:
وَلَهُۥ مَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ وَمَنۡ عِندَهُۥ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ عَنۡ عِبَادَتِهِۦ وَلَا يَسۡتَحۡسِرُونَ
Onse akumwamba ndi pansi, Ngake (Allah); ndipo amene ali kwa Iye (angelo), sadzitukumula pakumulambira, ndiponso satopa (ndi mapemphero)
Арабча тафсирлар:
يُسَبِّحُونَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ لَا يَفۡتُرُونَ
Amamlemekeza usiku ndi usana, ndipo sagwidwa ndi ulesi.
Арабча тафсирлар:
أَمِ ٱتَّخَذُوٓاْ ءَالِهَةٗ مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ هُمۡ يُنشِرُونَ
Kapena adzipangira milungu yochokera m’nthaka youkitsa akufa, (kotero kuti aichita kukhala milungu yawo mmalo mwa Allah)?
Арабча тафсирлар:
لَوۡ كَانَ فِيهِمَآ ءَالِهَةٌ إِلَّا ٱللَّهُ لَفَسَدَتَاۚ فَسُبۡحَٰنَ ٱللَّهِ رَبِّ ٱلۡعَرۡشِ عَمَّا يَصِفُونَ
Kukadakhala kuti ilipo m’menemo milungu ina (kuthambo ndi pansi) kupatula Allah, (ziwirizi) zikadawonongeka, wapatukana Allah Mbuye wa Arsh (Mpando Wachifumu) ndi zimene akunena (osakhulupirira).
Арабча тафсирлар:
لَا يُسۡـَٔلُ عَمَّا يَفۡعَلُ وَهُمۡ يُسۡـَٔلُونَ
Safunsidwa pa zimene akuchita, koma iwo adzafunsidwa.
Арабча тафсирлар:
أَمِ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِهِۦٓ ءَالِهَةٗۖ قُلۡ هَاتُواْ بُرۡهَٰنَكُمۡۖ هَٰذَا ذِكۡرُ مَن مَّعِيَ وَذِكۡرُ مَن قَبۡلِيۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡلَمُونَ ٱلۡحَقَّۖ فَهُم مُّعۡرِضُونَ
Kapena adzipangira milungu ina m’malo mwa Iye? Nena: ‘“Bweretsani umboni wanu (pa zimenezi), (izi ndikuuzani) ndichikumbutso kwa awa ali pamodzi ndi ine, ndiponso ndichikumbutso kwa amene adalipo patsogolo panga.” Koma ambiri a iwo sadziwa za choonadi, tero iwo akunyozera.
Арабча тафсирлар:
وَمَآ أَرۡسَلۡنَا مِن قَبۡلِكَ مِن رَّسُولٍ إِلَّا نُوحِيٓ إِلَيۡهِ أَنَّهُۥ لَآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنَا۠ فَٱعۡبُدُونِ
Ndipo sitidatume patsogolo pako mtumiki aliyense koma tidali kumzindikiritsa kuti palibe mulungu wina wompembedza mwachoonadi, koma Ine; choncho ndilambireni.
Арабча тафсирлар:
وَقَالُواْ ٱتَّخَذَ ٱلرَّحۡمَٰنُ وَلَدٗاۗ سُبۡحَٰنَهُۥۚ بَلۡ عِبَادٞ مُّكۡرَمُونَ
Ndipo (osakhulupirira) akuti: “(Allah) Wachifundo chambiri wadzipangira mwana.” Allah wapatukana (ndi zimenezo) koma (awa angelo) ndi akapolo (a Allah) amene alemekezedwa.
Арабча тафсирлар:
لَا يَسۡبِقُونَهُۥ بِٱلۡقَوۡلِ وَهُم بِأَمۡرِهِۦ يَعۡمَلُونَ
Samutsogolera kuyankhula, ndipo iwo amachita molingana ndi malamulo Ake.
Арабча тафсирлар:
يَعۡلَمُ مَا بَيۡنَ أَيۡدِيهِمۡ وَمَا خَلۡفَهُمۡ وَلَا يَشۡفَعُونَ إِلَّا لِمَنِ ٱرۡتَضَىٰ وَهُم مِّنۡ خَشۡيَتِهِۦ مُشۡفِقُونَ
(Allah) akudziwa zapatsogolo pawo (angelowo) ndi zapambuyo pawo, ndipo (angelowo) sangaombole (aliyense) koma yekhayo (Allah) wamuyanja, ndipo iwo, chifukwa chomuopa, amanjenjemera.
Арабча тафсирлар:
۞ وَمَن يَقُلۡ مِنۡهُمۡ إِنِّيٓ إِلَٰهٞ مِّن دُونِهِۦ فَذَٰلِكَ نَجۡزِيهِ جَهَنَّمَۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo mwa iwo amene anganene kuti: “Ine ndi mulungu mmalo mwa Iye,” ndiye kuti timulipira Jahannam; umo ndi momwe timawalipirira ochita zoipa.
Арабча тафсирлар:
أَوَلَمۡ يَرَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ أَنَّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ كَانَتَا رَتۡقٗا فَفَتَقۡنَٰهُمَاۖ وَجَعَلۡنَا مِنَ ٱلۡمَآءِ كُلَّ شَيۡءٍ حَيٍّۚ أَفَلَا يُؤۡمِنُونَ
Kodi osakhulupirira sadaone kuti thambo ndi nthaka zidali zophatikizana, ndipo tidazilekanitsa? Ndipo ndi madzi tidalenga chilichonse chamoyo. Kodi sakhulupirira?
Арабча тафсирлар:
وَجَعَلۡنَا فِي ٱلۡأَرۡضِ رَوَٰسِيَ أَن تَمِيدَ بِهِمۡ وَجَعَلۡنَا فِيهَا فِجَاجٗا سُبُلٗا لَّعَلَّهُمۡ يَهۡتَدُونَ
Ndipo tidaika mapiri panthaka molimbika kuti isagwedezeke ndi iwo, ndipo m’menemo tidaikamo misewu kuti alondole njira (ndikufika komwe afuna).
Арабча тафсирлар:
وَجَعَلۡنَا ٱلسَّمَآءَ سَقۡفٗا مَّحۡفُوظٗاۖ وَهُمۡ عَنۡ ءَايَٰتِهَا مُعۡرِضُونَ
Ndipo thambo tidalipanga monga tsindwi losungidwa (kuti lisagwe). Koma iwo akuzitembenukira kumbali zizindikiro zake.
Арабча тафсирлар:
وَهُوَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ وَٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَۖ كُلّٞ فِي فَلَكٖ يَسۡبَحُونَ
Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi; chilichonse mwa izo chikusambira mozungulira m’njira mwake.
Арабча тафсирлар:
وَمَا جَعَلۡنَا لِبَشَرٖ مِّن قَبۡلِكَ ٱلۡخُلۡدَۖ أَفَإِيْن مِّتَّ فَهُمُ ٱلۡخَٰلِدُونَ
Ife sitidawachite anthu amene adalipo patsogolo pako kukhala okhala nthawi yaitali. Nanga ukafa, kodi iwo adzakhala okhala nthawi yaitali?
Арабча тафсирлар:
كُلُّ نَفۡسٖ ذَآئِقَةُ ٱلۡمَوۡتِۗ وَنَبۡلُوكُم بِٱلشَّرِّ وَٱلۡخَيۡرِ فِتۡنَةٗۖ وَإِلَيۡنَا تُرۡجَعُونَ
Chamoyo chilichonse chidzalawa imfa; ndipo tikukuyesani mayeso ndi zinthu zoipa ndi zabwino. Ndipo nonsenu mudzabwerera kwa Ife.
Арабча тафсирлар:
وَإِذَا رَءَاكَ ٱلَّذِينَ كَفَرُوٓاْ إِن يَتَّخِذُونَكَ إِلَّا هُزُوًا أَهَٰذَا ٱلَّذِي يَذۡكُرُ ءَالِهَتَكُمۡ وَهُم بِذِكۡرِ ٱلرَّحۡمَٰنِ هُمۡ كَٰفِرُونَ
Ndipo amene sadakhulupirire akakuona, akungokuchitira chipongwe. “Kodi ndi uyu yemwe akutchula milungu yanu (mwachipongwe)?” Pomwe iwo ndi amene akukana zakutchula (Allah) Wachifundo chambiri.
Арабча тафсирлар:
خُلِقَ ٱلۡإِنسَٰنُ مِنۡ عَجَلٖۚ سَأُوْرِيكُمۡ ءَايَٰتِي فَلَا تَسۡتَعۡجِلُونِ
Munthu walengedwa ndi chikhalidwe chokonda zinthu (zake zonse) mwachangu. Posachedwapa ndikusonyezani zisonyezo Zanga; choncho musandifulumizitse (kukubweretserani chilango changa).
Арабча тафсирлар:
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا ٱلۡوَعۡدُ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Ndipo (osakhulupirira) akuti: “Kodi malonjezo awa adzakwaniritsidwa liti, ngati mukunena zoona?”
Арабча тафсирлар:
لَوۡ يَعۡلَمُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ حِينَ لَا يَكُفُّونَ عَن وُجُوهِهِمُ ٱلنَّارَ وَلَا عَن ظُهُورِهِمۡ وَلَا هُمۡ يُنصَرُونَ
Chikhala kuti amene sadakhulupirire akudziwa chilango chimene chidzawapeza panthawi yomwe sangathe kutchinjiriza Moto kunkhope zawo ndi kumisana yawo ndipo kuti sadzathandizidwa, (sakadanena zimenezi.)
Арабча тафсирлар:
بَلۡ تَأۡتِيهِم بَغۡتَةٗ فَتَبۡهَتُهُمۡ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ رَدَّهَا وَلَا هُمۡ يُنظَرُونَ
Koma (Qiyâma) idzawadzera mwadzidzidzi ndi kuwadzidzimutsa; kenako sadzatha kuibweza kapena kupatsidwa danga (kuti achite zomwe sadachite.)
Арабча тафсирлар:
وَلَقَدِ ٱسۡتُهۡزِئَ بِرُسُلٖ مِّن قَبۡلِكَ فَحَاقَ بِٱلَّذِينَ سَخِرُواْ مِنۡهُم مَّا كَانُواْ بِهِۦ يَسۡتَهۡزِءُونَ
Ndipo ndithu atumiki adachitidwa chipongwe patsogolo pako; choncho amene adachita chipongwe mwa iwo, zidawadzera zomwe adali kuzichita chipongwe.
Арабча тафсирлар:
قُلۡ مَن يَكۡلَؤُكُم بِٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ مِنَ ٱلرَّحۡمَٰنِۚ بَلۡ هُمۡ عَن ذِكۡرِ رَبِّهِم مُّعۡرِضُونَ
Nena: “Kodi ndani angakutetezeni usiku ndi usana ku masautso a (Allah) Wachifundo Chambiri?” Koma iwo akunyozera kukumbuka Mbuye wawo.
Арабча тафсирлар:
أَمۡ لَهُمۡ ءَالِهَةٞ تَمۡنَعُهُم مِّن دُونِنَاۚ لَا يَسۡتَطِيعُونَ نَصۡرَ أَنفُسِهِمۡ وَلَا هُم مِّنَّا يُصۡحَبُونَ
Kapena ali nayo milungu yowatchinjiriza m’malo mwa Ife? (Milunguyo) siingathe kudzithandiza yokha (nanga ndiye ingathe kuthandiza ena?) Ndipo (milungu) imeneyo siidzasamalidwa ndi Ife.
Арабча тафсирлар:
بَلۡ مَتَّعۡنَا هَٰٓؤُلَآءِ وَءَابَآءَهُمۡ حَتَّىٰ طَالَ عَلَيۡهِمُ ٱلۡعُمُرُۗ أَفَلَا يَرَوۡنَ أَنَّا نَأۡتِي ٱلۡأَرۡضَ نَنقُصُهَا مِنۡ أَطۡرَافِهَآۚ أَفَهُمُ ٱلۡغَٰلِبُونَ
Koma awa (osakhulupirira) tidawasangalatsa ndi makolo awo kufikira nthawi ya moyo wawo idatalika; kodi saona kuti tikulidzera dziko lawo ndikulichepetsa malire ake?. Nanga kodi iwo ndiwo opambana?
Арабча тафсирлар:
قُلۡ إِنَّمَآ أُنذِرُكُم بِٱلۡوَحۡيِۚ وَلَا يَسۡمَعُ ٱلصُّمُّ ٱلدُّعَآءَ إِذَا مَا يُنذَرُونَ
Nena: “Ndithu ndikukuchenjezani ndi chivumbulutso (cha Allah). Koma agonthi samva kuitana pamene akuchenjezedwa.”
Арабча тафсирлар:
وَلَئِن مَّسَّتۡهُمۡ نَفۡحَةٞ مِّنۡ عَذَابِ رَبِّكَ لَيَقُولُنَّ يَٰوَيۡلَنَآ إِنَّا كُنَّا ظَٰلِمِينَ
Ndipo kukadawakhudza kumenya kumodzi kwa chilango cha Mbuye wako, ndithudi, (akadadzichepetsa nthawi yomweyo). Akadanena: “Tsoka kwa ife ndithu tidali osalungama.”
Арабча тафсирлар:
وَنَضَعُ ٱلۡمَوَٰزِينَ ٱلۡقِسۡطَ لِيَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ فَلَا تُظۡلَمُ نَفۡسٞ شَيۡـٔٗاۖ وَإِن كَانَ مِثۡقَالَ حَبَّةٖ مِّنۡ خَرۡدَلٍ أَتَيۡنَا بِهَاۗ وَكَفَىٰ بِنَا حَٰسِبِينَ
Ndipo tsiku la Qiyâma tidzaika masikero achilungamo, choncho mzimu uliwonse sudzachitidwa chinyengo pa chilichonse. Ngakhale (chinthucho) chili cholemera ngati njere ya mpiru, tidzachibweretsa; ndipo tikukwana (kukhala akatswiri) pa chiwerengero.
Арабча тафсирлар:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ وَهَٰرُونَ ٱلۡفُرۡقَانَ وَضِيَآءٗ وَذِكۡرٗا لِّلۡمُتَّقِينَ
Ndipo ndithu Mûsa ndi Harun tidawapatsa (buku) losiyanitsa pakati pa choonadi ndi chonama, ndiponso muuni ndi ulaliki kwa anthu oopa (Allah).
Арабча тафсирлар:
ٱلَّذِينَ يَخۡشَوۡنَ رَبَّهُم بِٱلۡغَيۡبِ وَهُم مِّنَ ٱلسَّاعَةِ مُشۡفِقُونَ
Omwe akumuopa Mbuye wawo ngakhale ali paokha, omwenso amaopa Qiyâma.
Арабча тафсирлар:
وَهَٰذَا ذِكۡرٞ مُّبَارَكٌ أَنزَلۡنَٰهُۚ أَفَأَنتُمۡ لَهُۥ مُنكِرُونَ
Ndipo iyi (Qur’an) ndi ulaliki wodalitsika umene tauvumbulutsa (kwa inu); kodi inu mukuikana?
Арабча тафсирлар:
۞ وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَآ إِبۡرَٰهِيمَ رُشۡدَهُۥ مِن قَبۡلُ وَكُنَّا بِهِۦ عَٰلِمِينَ
Ndipo ndithu Ibrahim tidampatsa kulungama kwake kuyambira kale (kuubwana), ndipo tinkamudziwa (bwinobwino).
Арабча тафсирлар:
إِذۡ قَالَ لِأَبِيهِ وَقَوۡمِهِۦ مَا هَٰذِهِ ٱلتَّمَاثِيلُ ٱلَّتِيٓ أَنتُمۡ لَهَا عَٰكِفُونَ
(Akumbutse anthu) pamene adauza bambo wake ndi anthu ake, “Nchiyani mafano awa omwe inu nthawi zonse mukupitiriza kuwapembedza.”
Арабча тафсирлар:
قَالُواْ وَجَدۡنَآ ءَابَآءَنَا لَهَا عَٰبِدِينَ
Adati: “Tidapeza makolo athu akuwapembedza. (Choncho nafenso Tikuwapembedza).”
Арабча тафсирлар:
قَالَ لَقَدۡ كُنتُمۡ أَنتُمۡ وَءَابَآؤُكُمۡ فِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٖ
(Iye) adati: “Ndithu inu ndi makolo anu mudali mkusokera koonekera.”
Арабча тафсирлар:
قَالُوٓاْ أَجِئۡتَنَا بِٱلۡحَقِّ أَمۡ أَنتَ مِنَ ٱللَّٰعِبِينَ
(Iwo) adati: “Kodi watibweretsera choonadi, kapena iwe ndi m’modzi mwa osereula?”
Арабча тафсирлар:
قَالَ بَل رَّبُّكُمۡ رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ ٱلَّذِي فَطَرَهُنَّ وَأَنَا۠ عَلَىٰ ذَٰلِكُم مِّنَ ٱلشَّٰهِدِينَ
(Iye) adati: (“Iyayi, ine siwosereula), koma Mbuye wanu, ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka amene adalenga zimenezi; ine pa zimenezi, ndine m’modzi wochitira umboni.”
Арабча тафсирлар:
وَتَٱللَّهِ لَأَكِيدَنَّ أَصۡنَٰمَكُم بَعۡدَ أَن تُوَلُّواْ مُدۡبِرِينَ
“Ndipo ndikulumbilira Allah, ndiwachitira chiwembu mafano anuwo pambuyo ponditembenukira misana kupita komwe mukupita.”
Арабча тафсирлар:
فَجَعَلَهُمۡ جُذَٰذًا إِلَّا كَبِيرٗا لَّهُمۡ لَعَلَّهُمۡ إِلَيۡهِ يَرۡجِعُونَ
Choncho adawaphwanya (mafanowo) zidutswazidutswa kupatula lalikulu lawo (sadaliswe) kuti iwo alibwelere (ndi kulifunsa zimene zachitika).
Арабча тафсирлар:
قَالُواْ مَن فَعَلَ هَٰذَا بِـَٔالِهَتِنَآ إِنَّهُۥ لَمِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ
(Iwo parnene adafika kumafano awo) adati: “Ndani wachita ichi pa milungu yathu? Ndithu iye ndi m’modzi wa ochita zoipa.”
Арабча тафсирлар:
قَالُواْ سَمِعۡنَا فَتٗى يَذۡكُرُهُمۡ يُقَالُ لَهُۥٓ إِبۡرَٰهِيمُ
Adati: “Tidamumva m’nyamata wina akuitchula (moipa); amatchedwa Ibrahim.”
Арабча тафсирлар:
قَالُواْ فَأۡتُواْ بِهِۦ عَلَىٰٓ أَعۡيُنِ ٱلنَّاسِ لَعَلَّهُمۡ يَشۡهَدُونَ
Adati: “Mubweretseni pamaso pa anthu kuti amuone.”
Арабча тафсирлар:
قَالُوٓاْ ءَأَنتَ فَعَلۡتَ هَٰذَا بِـَٔالِهَتِنَا يَٰٓإِبۡرَٰهِيمُ
Adati: “Kodi ndiwedi wachita ichi ku milungu yathu, E, iwe Ibrahim?”
Арабча тафсирлар:
قَالَ بَلۡ فَعَلَهُۥ كَبِيرُهُمۡ هَٰذَا فَسۡـَٔلُوهُمۡ إِن كَانُواْ يَنطِقُونَ
(Iye) adati: “(Iyayi), koma wachita ichi ndi mkulu wawoyu. Choncho afunseni (kuti akuuzeni zenizeni) ngati amatha kuyankhula.”
Арабча тафсирлар:
فَرَجَعُوٓاْ إِلَىٰٓ أَنفُسِهِمۡ فَقَالُوٓاْ إِنَّكُمۡ أَنتُمُ ٱلظَّٰلِمُونَ
Ndipo adadzitembenukira okha ndikunena kuti: “Ndithu inu ndinu oipa.”
Арабча тафсирлар:
ثُمَّ نُكِسُواْ عَلَىٰ رُءُوسِهِمۡ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَا هَٰٓؤُلَآءِ يَنطِقُونَ
Kenako adazyolitsa mitu yawo (ndikubwerera kuumbuli wawo) nanena kuti: “Ndithu iwe ukudziwa kuti izi siziyankhula (nchifukwa ninji ukutichita chipongwe)?”
Арабча тафсирлар:
قَالَ أَفَتَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ مَا لَا يَنفَعُكُمۡ شَيۡـٔٗا وَلَا يَضُرُّكُمۡ
(Iye) adati: “Kodi mukupembedza zomwe sizingakuthandizeni chilichonse, kusiya Allah, zomwenso sizingakupatseni masautso?”
Арабча тафсирлар:
أُفّٖ لَّكُمۡ وَلِمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِۚ أَفَلَا تَعۡقِلُونَ
“Kuyaluka nkwanu ndi zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah. Kodi simuganizira?”
Арабча тафсирлар:
قَالُواْ حَرِّقُوهُ وَٱنصُرُوٓاْ ءَالِهَتَكُمۡ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ
(Iwo) adati: “Mtentheni; ndipo pulumutsani milungu yanu, ngati inu mungathe kuchita zimenezi.”
Арабча тафсирлар:
قُلۡنَا يَٰنَارُ كُونِي بَرۡدٗا وَسَلَٰمًا عَلَىٰٓ إِبۡرَٰهِيمَ
Tidati: “E iwe Moto! Khala kuzizira ndiponso mtendere kwa Ibrahim.”
Арабча тафсирлар:
وَأَرَادُواْ بِهِۦ كَيۡدٗا فَجَعَلۡنَٰهُمُ ٱلۡأَخۡسَرِينَ
Ndipo adamfunira chiwembu; koma tidawachita kukhala otaika zedi.
Арабча тафсирлар:
وَنَجَّيۡنَٰهُ وَلُوطًا إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَا لِلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo tidampulumutsa iye ndi Luti kupita ku dziko lomwe tidalidalitsa ku zolengedwa.
Арабча тафсирлар:
وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ نَافِلَةٗۖ وَكُلّٗا جَعَلۡنَا صَٰلِحِينَ
Ndipo (Ibrahim) tidampatsa Ishaq ndi kuonjezera Ya’qub, ndipo tidawachita onse kukhala abwino.
Арабча тафсирлар:
وَجَعَلۡنَٰهُمۡ أَئِمَّةٗ يَهۡدُونَ بِأَمۡرِنَا وَأَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡهِمۡ فِعۡلَ ٱلۡخَيۡرَٰتِ وَإِقَامَ ٱلصَّلَوٰةِ وَإِيتَآءَ ٱلزَّكَوٰةِۖ وَكَانُواْ لَنَا عَٰبِدِينَ
Ndipo tidawasankha kukhala atsogoleri, owongolera mwa lamulo Lathu, ndipo tidawazindikiritsa kuchita zabwino ndi kupemphera Swala moyenera, ndi kupereka Zakaat; ndipo kwa Ife adali opembeza.
Арабча тафсирлар:
وَلُوطًا ءَاتَيۡنَٰهُ حُكۡمٗا وَعِلۡمٗا وَنَجَّيۡنَٰهُ مِنَ ٱلۡقَرۡيَةِ ٱلَّتِي كَانَت تَّعۡمَلُ ٱلۡخَبَٰٓئِثَۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمَ سَوۡءٖ فَٰسِقِينَ
Ndipo Luti tidampatsa luntha ndi kuzindikira, ndipo tidampulumutsa ku mudzi womwe anthu ake ankachita zoipa; ndithu iwo adali anthu oipa otuluka m’chilamulo (cha Allah).
Арабча тафсирлар:
وَأَدۡخَلۡنَٰهُ فِي رَحۡمَتِنَآۖ إِنَّهُۥ مِنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Ndipo tidamulowetsa mu chifundo Chathu; ndithu iye adali m’modzi wa ochita zabwino.
Арабча тафсирлар:
وَنُوحًا إِذۡ نَادَىٰ مِن قَبۡلُ فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ فَنَجَّيۡنَٰهُ وَأَهۡلَهُۥ مِنَ ٱلۡكَرۡبِ ٱلۡعَظِيمِ
Ndipo (akumbutse za) Nuh, pamene adatiitana kale (kutipempha). Ndipo Ife tidamuyankha ndi kupulumutsa iye ndi anthu ake ku sautso Ialikulu.
Арабча тафсирлар:
وَنَصَرۡنَٰهُ مِنَ ٱلۡقَوۡمِ ٱلَّذِينَ كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَآۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ قَوۡمَ سَوۡءٖ فَأَغۡرَقۡنَٰهُمۡ أَجۡمَعِينَ
Ndipo tidampulumutsa pa anthu amene adatsutsa Ayah Zathu; ndithu iwo adali anthu oipa. Ndipo onse tidawamiza (ndi chigumula chamadzi).
Арабча тафсирлар:
وَدَاوُۥدَ وَسُلَيۡمَٰنَ إِذۡ يَحۡكُمَانِ فِي ٱلۡحَرۡثِ إِذۡ نَفَشَتۡ فِيهِ غَنَمُ ٱلۡقَوۡمِ وَكُنَّا لِحُكۡمِهِمۡ شَٰهِدِينَ
Ndipo (akumbutse za) Daud ndi Sulaiman, pamene ankaweruza mlandu wa munda, pomwe mbuzi za anthu zidadya ndi kuonongaononga usiku mmenemo ndipo Ife tidali mboni pa kuweruza kwawo.
Арабча тафсирлар:
فَفَهَّمۡنَٰهَا سُلَيۡمَٰنَۚ وَكُلًّا ءَاتَيۡنَا حُكۡمٗا وَعِلۡمٗاۚ وَسَخَّرۡنَا مَعَ دَاوُۥدَ ٱلۡجِبَالَ يُسَبِّحۡنَ وَٱلطَّيۡرَۚ وَكُنَّا فَٰعِلِينَ
Tero tidamzindikiritsa za mlanduwo Sulaiman (kuposa tate wake Daud). Yense wa iwo tidampatsa kuweruza ndi kudziwa; ndipo tidagonjetsa mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Daud zikulemekeza (Allah); ndipo Ife ndi ochita chimene tafuna.
Арабча тафсирлар:
وَعَلَّمۡنَٰهُ صَنۡعَةَ لَبُوسٖ لَّكُمۡ لِتُحۡصِنَكُم مِّنۢ بَأۡسِكُمۡۖ فَهَلۡ أَنتُمۡ شَٰكِرُونَ
Ndipo tidamphunzitsa (Daud) kapangidwe ka chovala chapankhondo chifukwa cha inu kuti chikutetezeni mkumenyana kwanu; kodi simungakhale othokoza?
Арабча тафсирлар:
وَلِسُلَيۡمَٰنَ ٱلرِّيحَ عَاصِفَةٗ تَجۡرِي بِأَمۡرِهِۦٓ إِلَى ٱلۡأَرۡضِ ٱلَّتِي بَٰرَكۡنَا فِيهَاۚ وَكُنَّا بِكُلِّ شَيۡءٍ عَٰلِمِينَ
Nayenso Sulaiman tidamugonjetsera mphepo yamphamvu; inkayenda mwa lamulo lake kunka ku dziko lomwe talidalitsa (dziko la Sham); ndipo Ife pa chilichonse Ngodziwa.
Арабча тафсирлар:
وَمِنَ ٱلشَّيَٰطِينِ مَن يَغُوصُونَ لَهُۥ وَيَعۡمَلُونَ عَمَلٗا دُونَ ذَٰلِكَۖ وَكُنَّا لَهُمۡ حَٰفِظِينَ
Ndipo (tidamugonjetseranso) asatana omwe ankamubilira m’madzi (ndikumtolera ngale), ndipo ankachita ntchito zina kuonjezera pa zimenezi; ndipo Ife tidali owasunga (owateteza).
Арабча тафсирлар:
۞ وَأَيُّوبَ إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَسَّنِيَ ٱلضُّرُّ وَأَنتَ أَرۡحَمُ ٱلرَّٰحِمِينَ
Ndipo akumbutsenso za Ayubu pamene adakuwira Mbuye wake (kuti): “Ndithu mavuto andikhudza, pomwe Inu ndi Achifundo kuposa achifundo!”
Арабча тафсирлар:
فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ فَكَشَفۡنَا مَا بِهِۦ مِن ضُرّٖۖ وَءَاتَيۡنَٰهُ أَهۡلَهُۥ وَمِثۡلَهُم مَّعَهُمۡ رَحۡمَةٗ مِّنۡ عِندِنَا وَذِكۡرَىٰ لِلۡعَٰبِدِينَ
Choncho tidavomera (pempho lake); ndipo tidamchotsera mavuto omwe adali nawo, ndipo tidampatsa ana ake ofanana ndi omwe adali nawo kale ndikuonjezeranso ena onga iwo, (zonsezi monga) chifundo chochokera kwa Ife, (ndikuti zikhale) chikumbutso kwa ochita mapemphero.
Арабча тафсирлар:
وَإِسۡمَٰعِيلَ وَإِدۡرِيسَ وَذَا ٱلۡكِفۡلِۖ كُلّٞ مِّنَ ٱلصَّٰبِرِينَ
Ndipo (mutchule) Isimaila ndi Idrisa ndi Zul Kifli, onsewa adali mwa opirira.
Арабча тафсирлар:
وَأَدۡخَلۡنَٰهُمۡ فِي رَحۡمَتِنَآۖ إِنَّهُم مِّنَ ٱلصَّٰلِحِينَ
Tidawalowetsanso ku chifundo Chathu, ndithu iwo adali mwa anthu abwino.
Арабча тафсирлар:
وَذَا ٱلنُّونِ إِذ ذَّهَبَ مُغَٰضِبٗا فَظَنَّ أَن لَّن نَّقۡدِرَ عَلَيۡهِ فَنَادَىٰ فِي ٱلظُّلُمَٰتِ أَن لَّآ إِلَٰهَ إِلَّآ أَنتَ سُبۡحَٰنَكَ إِنِّي كُنتُ مِنَ ٱلظَّٰلِمِينَ
Ndipo (mtchulenso) Thun-Nun (Yunusu), pamene adachoka uku atakwiya, ndipo ankaganiza (kuti tamuloleza kusamuka) ndikuti sititha kumchita kanthu. Choncho adaitana mu mdima (mammimba mwa nsomba imene idamumeza, kuti): “Ndithu palibe mulungu wina wopembezedwa mwachoonadi koma Inu; mwayeretsedwa; ndithu ine ndidali m’modzi wa odzichitira zoipa.”
Арабча тафсирлар:
فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ وَنَجَّيۡنَٰهُ مِنَ ٱلۡغَمِّۚ وَكَذَٰلِكَ نُـۨجِي ٱلۡمُؤۡمِنِينَ
Choncho tidavomereza (pempho lake) ndi kumpulumutsa ku madandaulo; umo ndi m’mene timawapulumutsira okhulupirira.
Арабча тафсирлар:
وَزَكَرِيَّآ إِذۡ نَادَىٰ رَبَّهُۥ رَبِّ لَا تَذَرۡنِي فَرۡدٗا وَأَنتَ خَيۡرُ ٱلۡوَٰرِثِينَ
Ndipo (akumbutse za) Zakariya pamene adaitana Mbuye wake (kuti): “Mbuye wanga! Musandisiye ndekha; ndithu Inu ndinu wabwino kuposa alowa mmalo onse.”
Арабча тафсирлар:
فَٱسۡتَجَبۡنَا لَهُۥ وَوَهَبۡنَا لَهُۥ يَحۡيَىٰ وَأَصۡلَحۡنَا لَهُۥ زَوۡجَهُۥٓۚ إِنَّهُمۡ كَانُواْ يُسَٰرِعُونَ فِي ٱلۡخَيۡرَٰتِ وَيَدۡعُونَنَا رَغَبٗا وَرَهَبٗاۖ وَكَانُواْ لَنَا خَٰشِعِينَ
Choncho tidamuvomera (pempho), ndikumpatsa Yahya ndikumkonzera mkazi wake. Ndithu iwo adali achangu pochita zabwino; ankatipempha mwakhumbo ndi mwamantha, ndipo adali odzichepetsa kwa Ife.
Арабча тафсирлар:
وَٱلَّتِيٓ أَحۡصَنَتۡ فَرۡجَهَا فَنَفَخۡنَا فِيهَا مِن رُّوحِنَا وَجَعَلۡنَٰهَا وَٱبۡنَهَآ ءَايَةٗ لِّلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo (atchulire za Mariya) yemwe adauteteza umaliseche wake (podzisunga); ndipo tidauzira mwa iye Mzimu Wathu, ndipo tidamchita iye ndi mwana wake kukhala chizizwa (cha Allah) kwa zolengedwa zonse.
Арабча тафсирлар:
إِنَّ هَٰذِهِۦٓ أُمَّتُكُمۡ أُمَّةٗ وَٰحِدَةٗ وَأَنَا۠ رَبُّكُمۡ فَٱعۡبُدُونِ
Ndithu uwu mpingo wanu, ndimpingo umodzi, ndipo Ine ndine Mbuye wanu; choncho ndipembedzeni.
Арабча тафсирлар:
وَتَقَطَّعُوٓاْ أَمۡرَهُم بَيۡنَهُمۡۖ كُلٌّ إِلَيۡنَا رَٰجِعُونَ
Koma iwo adaswa chinthu chawochi pakati pawo (tero adakhala mipingo yosiyanasiyana). Onse adzabwerera kwa Ife.
Арабча тафсирлар:
فَمَن يَعۡمَلۡ مِنَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَلَا كُفۡرَانَ لِسَعۡيِهِۦ وَإِنَّا لَهُۥ كَٰتِبُونَ
Ndipo amene achite ntchito zabwino uku ali wokhulupirira, khama lake silidzakanidwa; ndithunso Ife tikumlembera zonse zimene akuchita.
Арабча тафсирлар:
وَحَرَٰمٌ عَلَىٰ قَرۡيَةٍ أَهۡلَكۡنَٰهَآ أَنَّهُمۡ لَا يَرۡجِعُونَ
Ndipo nkosatheka kwa eni mudzi umene tidauononga chifukwa cha machimo awo kuti asabwelere kwa Ife; (koma ndithu abwerera).
Арабча тафсирлар:
حَتَّىٰٓ إِذَا فُتِحَتۡ يَأۡجُوجُ وَمَأۡجُوجُ وَهُم مِّن كُلِّ حَدَبٖ يَنسِلُونَ
Kufikira pamene Yaajuju ndi Maajuju adzatsekulilidwa (mpanda wawo), ndipo iwo adzakhala akuthamanga kuchokera m’phiri lililonse.
Арабча тафсирлар:
وَٱقۡتَرَبَ ٱلۡوَعۡدُ ٱلۡحَقُّ فَإِذَا هِيَ شَٰخِصَةٌ أَبۡصَٰرُ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ يَٰوَيۡلَنَا قَدۡ كُنَّا فِي غَفۡلَةٖ مِّنۡ هَٰذَا بَلۡ كُنَّا ظَٰلِمِينَ
Ndipo lonjezo la choonadi lidzafika; pamenepo maso a omwe sadakhulupirire, adzatong’oka uku akunena: “Tsoka pa ife! Ndithu tidali osalabadira (za chinthu) ichi; koma tidali oipa, (odzichitira tokha zoipa.)”
Арабча тафсирлар:
إِنَّكُمۡ وَمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ حَصَبُ جَهَنَّمَ أَنتُمۡ لَهَا وَٰرِدُونَ
Ndithu inu ndi amene mukuwapembedza kusiya Allah, ndinu nkhuni za ku Jahannam. Ndipo inu (Jahannamyo) mudzalowa.
Арабча тафсирлар:
لَوۡ كَانَ هَٰٓؤُلَآءِ ءَالِهَةٗ مَّا وَرَدُوهَاۖ وَكُلّٞ فِيهَا خَٰلِدُونَ
Ngati awa akadakhala milungu yeniyeni, ndiye kuti sakadailowa, mmenemo onse adzakhala nthawi yaitali.
Арабча тафсирлар:
لَهُمۡ فِيهَا زَفِيرٞ وَهُمۡ فِيهَا لَا يَسۡمَعُونَ
Mmenemo iwo adzakhala akubuula ndipo iwo mmenemo sadzamva (chifukwa makutu adzagontha).
Арабча тафсирлар:
إِنَّ ٱلَّذِينَ سَبَقَتۡ لَهُم مِّنَّا ٱلۡحُسۡنَىٰٓ أُوْلَٰٓئِكَ عَنۡهَا مُبۡعَدُونَ
Ndithu amene ubwino wathu udawafika, iwo adzatalikitsidwa nawo (motowo).
Арабча тафсирлар:
لَا يَسۡمَعُونَ حَسِيسَهَاۖ وَهُمۡ فِي مَا ٱشۡتَهَتۡ أَنفُسُهُمۡ خَٰلِدُونَ
Sadzamva mavume ake, ndipo iwo adzakhala nthawi yaitali m’zomwe ikukhumba mitima yawo.
Арабча тафсирлар:
لَا يَحۡزُنُهُمُ ٱلۡفَزَعُ ٱلۡأَكۡبَرُ وَتَتَلَقَّىٰهُمُ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةُ هَٰذَا يَوۡمُكُمُ ٱلَّذِي كُنتُمۡ تُوعَدُونَ
Kugwedezeka kwakukulu sikudzawadandaulitsa; ndipo angelo adzawalandira (ndikuwauza): “Ili ndi tsiku lanu lomwe mudali kulonjezedwa.”
Арабча тафсирлар:
يَوۡمَ نَطۡوِي ٱلسَّمَآءَ كَطَيِّ ٱلسِّجِلِّ لِلۡكُتُبِۚ كَمَا بَدَأۡنَآ أَوَّلَ خَلۡقٖ نُّعِيدُهُۥۚ وَعۡدًا عَلَيۡنَآۚ إِنَّا كُنَّا فَٰعِلِينَ
(Kumbukirani) tsiku lomwe tidzakulunga thambo monga momwe amakulungira makalata okhala ndi malembo m’kati mwake; monga tidayamba kulenga zolengedwa poyamba, tidzabwerezanso (kuzilenga kachiwiri. Ndipo aliyense adzalipidwa pa zomwe adali kuchita) ili ndilonjezo lomwe lili pa Ife. Ndithu Ife ndi Ochita (zomwe tikunena.)
Арабча тафсирлар:
وَلَقَدۡ كَتَبۡنَا فِي ٱلزَّبُورِ مِنۢ بَعۡدِ ٱلذِّكۡرِ أَنَّ ٱلۡأَرۡضَ يَرِثُهَا عِبَادِيَ ٱلصَّٰلِحُونَ
Ndipo ndithu tidalemba m’zaburi (mu Masalimo buku la Daud) pambuyo polemba mu chikumbutso (Lauhil-Mahafudh) kuti: “Dziko (lapansi) adzalilowa akapolo Anga abwino.”
Арабча тафсирлар:
إِنَّ فِي هَٰذَا لَبَلَٰغٗا لِّقَوۡمٍ عَٰبِدِينَ
Ndithu pazimenezi (nkhani za aneneri), pali miyambo kwa anthu, opembedza (Allah).
Арабча тафсирлар:
وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا رَحۡمَةٗ لِّلۡعَٰلَمِينَ
Ndipo sitidakutume koma kuti ukhale mtendere kwa zolengedwa zonse.
Арабча тафсирлар:
قُلۡ إِنَّمَا يُوحَىٰٓ إِلَيَّ أَنَّمَآ إِلَٰهُكُمۡ إِلَٰهٞ وَٰحِدٞۖ فَهَلۡ أَنتُم مُّسۡلِمُونَ
Nena: “Ndithu kukuvumbulutsidwa kwa ine kuti mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi; nanga inu mudzagonjera (zofuna Zake polowa m’Chisilamu)?”
Арабча тафсирлар:
فَإِن تَوَلَّوۡاْ فَقُلۡ ءَاذَنتُكُمۡ عَلَىٰ سَوَآءٖۖ وَإِنۡ أَدۡرِيٓ أَقَرِيبٌ أَم بَعِيدٞ مَّا تُوعَدُونَ
Koma ngati anyozera, nena: “Ndalengeza (uthenga) kwa inu mofanana (popanda tsankho); sindidziwa kuti zomwe mukulonjezedwa zili pafupi kapena zili kutali.”
Арабча тафсирлар:
إِنَّهُۥ يَعۡلَمُ ٱلۡجَهۡرَ مِنَ ٱلۡقَوۡلِ وَيَعۡلَمُ مَا تَكۡتُمُونَ
“Ndithu Iye akudziwa mawu okweza, ndiponso akudziwa zomwe mukubisa.”
Арабча тафсирлар:
وَإِنۡ أَدۡرِي لَعَلَّهُۥ فِتۡنَةٞ لَّكُمۡ وَمَتَٰعٌ إِلَىٰ حِينٖ
“Ndipo sindikudziwa, mwina kuchedwetsa chilango chanu ndi mayeso akukuyesani ndikukusangalatsani ndi zokoma (za m’dziko) mpaka Idzakwane nthawi yoikidwayo.”
Арабча тафсирлар:
قَٰلَ رَبِّ ٱحۡكُم بِٱلۡحَقِّۗ وَرَبُّنَا ٱلرَّحۡمَٰنُ ٱلۡمُسۡتَعَانُ عَلَىٰ مَا تَصِفُونَ
Adati: “E Mbuye wanga! Weruzani moona.” “Ndipo Mbuye wathu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; Wopemphedwa chithandizo pa zimene mukusimbazo.”
Арабча тафсирлар:
 
Маънолар таржимаси Сура: Анбиё сураси
Суралар мундарижаси Бет рақами
 
Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима - Таржималар мундарижаси

Қуръон Карим маъноларининг чевача таржимаси, мутаржим: Холид Иброҳим Бетала, 2020 йилда нашр қилинган

Ёпиш