Check out the new design

Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима * - Таржималар мундарижаси


Маънолар таржимаси Сура: Сажда   Оят:
وَلَوۡ تَرَىٰٓ إِذِ ٱلۡمُجۡرِمُونَ نَاكِسُواْ رُءُوسِهِمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ رَبَّنَآ أَبۡصَرۡنَا وَسَمِعۡنَا فَٱرۡجِعۡنَا نَعۡمَلۡ صَٰلِحًا إِنَّا مُوقِنُونَ
Ndipo ukadawaona oipa atazolikitsa mitu yawo kwa Mbuye wawo (uku akunena): “E Mbuye wathu! Taona, ndipo tamva. Choncho tibwezeni tikachita ntchito zabwino. Ndithu tsopano tatsimikiza (kukhulupirira).”
Арабча тафсирлар:
وَلَوۡ شِئۡنَا لَأٓتَيۡنَا كُلَّ نَفۡسٍ هُدَىٰهَا وَلَٰكِنۡ حَقَّ ٱلۡقَوۡلُ مِنِّي لَأَمۡلَأَنَّ جَهَنَّمَ مِنَ ٱلۡجِنَّةِ وَٱلنَّاسِ أَجۡمَعِينَ
Ndipo tikadafuna, tikadaupatsa mzimu ulionse chiongoko chake (moukakamiza monga momwe tidawachitira angelo, koma mzimu udapatsidwa mphamvu ndi ufulu wodzisankhira chimene ufuna; chabwino kapena choipa). Koma mawu atsimikizika ochokera kwa Ine: “Ndithu ndizadzazitsa Jahannam ziwanda ndi anthu; onse pamodzi (amene ali oipa).”
Арабча тафсирлар:
فَذُوقُواْ بِمَا نَسِيتُمۡ لِقَآءَ يَوۡمِكُمۡ هَٰذَآ إِنَّا نَسِينَٰكُمۡۖ وَذُوقُواْ عَذَابَ ٱلۡخُلۡدِ بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Choncho, lawani chifukwa cha kuyiwala (kusalabadila) kwanu kukumana ndi tsiku lanu ili. Ifenso tikusiyani (ku chilango monga ngati takuiwalani). Tero lawani chilango chamuyaya, chifukwa cha zomwe munkachita.”
Арабча тафсирлар:
إِنَّمَا يُؤۡمِنُ بِـَٔايَٰتِنَا ٱلَّذِينَ إِذَا ذُكِّرُواْ بِهَا خَرُّواْۤ سُجَّدٗاۤ وَسَبَّحُواْ بِحَمۡدِ رَبِّهِمۡ وَهُمۡ لَا يَسۡتَكۡبِرُونَ۩
Ndithu amene akukhulupirira Ayah Zathu, ndiamene akuti pamene akukumbutsidwa ndi Ayazo, amagwetsa nkhope zawo pansi (kusujudu) ndi kulemekeza Mbuye wawo pamodzi ndi kumthokoza. Ndipo iwo sadzitukumula.
Арабча тафсирлар:
تَتَجَافَىٰ جُنُوبُهُمۡ عَنِ ٱلۡمَضَاجِعِ يَدۡعُونَ رَبَّهُمۡ خَوۡفٗا وَطَمَعٗا وَمِمَّا رَزَقۡنَٰهُمۡ يُنفِقُونَ
Nthiti zawo zimalekana ndi malo ogona (usiku), uku akumpempha Mbuye wawo, moopa ndi mwachiyembekezo. Ndipo amapereka (Zakaat ndi sadaka) mzimene tawapatsa.
Арабча тафсирлар:
فَلَا تَعۡلَمُ نَفۡسٞ مَّآ أُخۡفِيَ لَهُم مِّن قُرَّةِ أَعۡيُنٖ جَزَآءَۢ بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Mzimu uliwonse sudziwa zimene aubisira zotonthoza diso (zosangalatsa moyo ku Munda wa mtendere) monga mphoto pa zimene unkachita.
Арабча тафсирлар:
أَفَمَن كَانَ مُؤۡمِنٗا كَمَن كَانَ فَاسِقٗاۚ لَّا يَسۡتَوُۥنَ
Kodi yemwe ali okhulupirira angafanane ndi wotuluka m’chilamulo cha Allah? Sangafanane.
Арабча тафсирлар:
أَمَّا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ فَلَهُمۡ جَنَّٰتُ ٱلۡمَأۡوَىٰ نُزُلَۢا بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzalandira Minda yokhalamo yokongola, monga phwando lawo pa zimene ankachita.
Арабча тафсирлар:
وَأَمَّا ٱلَّذِينَ فَسَقُواْ فَمَأۡوَىٰهُمُ ٱلنَّارُۖ كُلَّمَآ أَرَادُوٓاْ أَن يَخۡرُجُواْ مِنۡهَآ أُعِيدُواْ فِيهَا وَقِيلَ لَهُمۡ ذُوقُواْ عَذَابَ ٱلنَّارِ ٱلَّذِي كُنتُم بِهِۦ تُكَذِّبُونَ
Koma kwa amene adachita zoipa potuluka m’chilamulo cha Allah, malo awo ndi ku Moto. Nthawi iliyonse akafuna kutulukamo, azikabwezedwamo ndipo azidzauzidwa: “Lawani chilango cha Moto, chomwe munkachitsutsa.”
Арабча тафсирлар:
 
Маънолар таржимаси Сура: Сажда
Суралар мундарижаси Бет рақами
 
Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима - Таржималар мундарижаси

Таржима қилган Халид Иброҳим Бетала.

Ёпиш