Check out the new design

Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима * - Таржималар мундарижаси


Маънолар таржимаси Сура: Шўро   Оят:
فَاطِرُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ جَعَلَ لَكُم مِّنۡ أَنفُسِكُمۡ أَزۡوَٰجٗا وَمِنَ ٱلۡأَنۡعَٰمِ أَزۡوَٰجٗا يَذۡرَؤُكُمۡ فِيهِۚ لَيۡسَ كَمِثۡلِهِۦ شَيۡءٞۖ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ
(Iye ndi) Mlengi wa kumwamba ndi pansi. Adakupangirani akazi kuchokera mwa inu nomwe, ndipo nazo ziweto mitundu iwiri, (zazimuna ndi zazikazi. Choncho) akukuchulukitsani mmenemo (mchikonzero Chake chanzeru) palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona zonse.
Арабча тафсирлар:
لَهُۥ مَقَالِيدُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۖ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّهُۥ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ
Makiyi a kumwamba ndi pansi ndi Ake. Amamchulukitsira rizq amene wamfuna ndipo amamchepetsera amene wamfuna. Ndithu Iye Ngodziwa chilichonse (pochiika pamalo oyenera).
Арабча тафсирлар:
۞ شَرَعَ لَكُم مِّنَ ٱلدِّينِ مَا وَصَّىٰ بِهِۦ نُوحٗا وَٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ وَمَا وَصَّيۡنَا بِهِۦٓ إِبۡرَٰهِيمَ وَمُوسَىٰ وَعِيسَىٰٓۖ أَنۡ أَقِيمُواْ ٱلدِّينَ وَلَا تَتَفَرَّقُواْ فِيهِۚ كَبُرَ عَلَى ٱلۡمُشۡرِكِينَ مَا تَدۡعُوهُمۡ إِلَيۡهِۚ ٱللَّهُ يَجۡتَبِيٓ إِلَيۡهِ مَن يَشَآءُ وَيَهۡدِيٓ إِلَيۡهِ مَن يُنِيبُ
Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo chonga chomwe adam’langiza Nuh. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) kuti: Mulimbike chipembedzo (potsatira malamulo) ndikuti musalekane pa chipembedzo. Koma ndizovuta kwa opembedza mafano (kuvomera) zimene ukuwaitanira. Allah amadzisankhira amene wam’funa ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye.
Арабча тафсирлар:
وَمَا تَفَرَّقُوٓاْ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَهُمُ ٱلۡعِلۡمُ بَغۡيَۢا بَيۡنَهُمۡۚ وَلَوۡلَا كَلِمَةٞ سَبَقَتۡ مِن رَّبِّكَ إِلَىٰٓ أَجَلٖ مُّسَمّٗى لَّقُضِيَ بَيۡنَهُمۡۚ وَإِنَّ ٱلَّذِينَ أُورِثُواْ ٱلۡكِتَٰبَ مِنۢ بَعۡدِهِمۡ لَفِي شَكّٖ مِّنۡهُ مُرِيبٖ
Ndipo sadagawikane (pa chipembedzo otsatira a aneneri oyamba) kufikira pamene kudawadzera kudziwa kwa choonadi, chifukwa chachidani ndi dumbo pakati pawo. Kukadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako pachiyambi (lowachedwetsera chilango) mpaka nthawi yoikidwa kukadaweruzidwa pakati pawo koma ndithu amene adalandira buku pambuyo pawo (makolo awo, ndipo ndikukumana ndi nthawi yako,) ali mchikaiko cholikaikira (buku lawo).
Арабча тафсирлар:
فَلِذَٰلِكَ فَٱدۡعُۖ وَٱسۡتَقِمۡ كَمَآ أُمِرۡتَۖ وَلَا تَتَّبِعۡ أَهۡوَآءَهُمۡۖ وَقُلۡ ءَامَنتُ بِمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِن كِتَٰبٖۖ وَأُمِرۡتُ لِأَعۡدِلَ بَيۡنَكُمُۖ ٱللَّهُ رَبُّنَا وَرَبُّكُمۡۖ لَنَآ أَعۡمَٰلُنَا وَلَكُمۡ أَعۡمَٰلُكُمۡۖ لَا حُجَّةَ بَيۡنَنَا وَبَيۡنَكُمُۖ ٱللَّهُ يَجۡمَعُ بَيۡنَنَاۖ وَإِلَيۡهِ ٱلۡمَصِيرُ
(Chifukwa cha umodzi wa zipembedzo ndikuti pasakhale kugawikana pa chipembedzo) choncho aitanire (ku chipembedzo chimodzi); ndipo lungama (poitanapo) monga momwe walamulidwira. Ndipo usatsatire zofuna zawo. Ndipo nena: “Ndakhulupirira mmabuku onse omwe adawavumbulutsa Allah; ndipo ndalamulidwa kuchita chilungamo pakati panu. Allah ndiye Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu; ife tili ndi ntchito zathu (zomwe tidzalipidwa nazo); inunso muli ndi ntchito zanu (zomwe mudzalipidwa nazo). Palibe kukangana pakati pa ife ndi inu (chifukwa chakuonekera poyera choona). Allah adzatisonkhanitsa (kuti atiweruze); kwa Iye yekha ndiko kobwerera.
Арабча тафсирлар:
 
Маънолар таржимаси Сура: Шўро
Суралар мундарижаси Бет рақами
 
Қуръони Карим маъноларининг таржимаси - Чевача таржима - Таржималар мундарижаси

Таржима қилган Халид Иброҳим Бетала.

Ёпиш