የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - ቸዋኛ ትርጉም * - የትርጉሞች ማዉጫ


የይዘት ትርጉም አንቀጽ: (181) ምዕራፍ: ሱረቱ አል-በቀራህ
فَمَنۢ بَدَّلَهُۥ بَعۡدَ مَا سَمِعَهُۥ فَإِنَّمَآ إِثۡمُهُۥ عَلَى ٱلَّذِينَ يُبَدِّلُونَهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٞ
Ndipo amene asinthe malangizowo pambuyo pakuwamva; uchimo wake uli pa amene akusinthawo. Ndithudi, Allah Ngwakumva; Ngodziwa.[18]
[18] Apa akuwachenjeza amene auzidwa wasiyawo kuti asasinthepo kanthu. Ndipo akunenetsa kuti ngati wasiyawo uwonongedwa ndiye kuti anthu omwe adalandira wasiyawo akhala ndi uchimo chifukwa chosintha wasiyawo. Koma ngati wasiyawo udalembedwa mopanda chilungamo, monga kuti iye adati: “Chuma changa m’dzawapatse ana anga aamuna okha basi,” nkusiya kutchulapo aakazi, apo Allah akuloleza olandira wasiyawo kuti aukonze ndi kuwagawira ana onsewo mwachilungamo.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
 
የይዘት ትርጉም አንቀጽ: (181) ምዕራፍ: ሱረቱ አል-በቀራህ
የምዕራፎች ማውጫ የገፅ ቁጥር
 
የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - ቸዋኛ ትርጉም - የትርጉሞች ማዉጫ

የተከበረው ቁርአን ቸዋኛ መልዕክተ ትርጉም፤ በኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ የ 2020 ቅጅ

መዝጋት