Check out the new design

የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ * - የትርጉሞች ማዉጫ


የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አልን ኑር   አንቀጽ:
۞ يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَتَّبِعُواْ خُطُوَٰتِ ٱلشَّيۡطَٰنِۚ وَمَن يَتَّبِعۡ خُطُوَٰتِ ٱلشَّيۡطَٰنِ فَإِنَّهُۥ يَأۡمُرُ بِٱلۡفَحۡشَآءِ وَٱلۡمُنكَرِۚ وَلَوۡلَا فَضۡلُ ٱللَّهِ عَلَيۡكُمۡ وَرَحۡمَتُهُۥ مَا زَكَىٰ مِنكُم مِّنۡ أَحَدٍ أَبَدٗا وَلَٰكِنَّ ٱللَّهَ يُزَكِّي مَن يَشَآءُۗ وَٱللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٞ
E inu amene mwakhulupiliira! Musatsatire mapazi a satana. Ndipo amene atsatire mapazi a satana (asokera) ndithudi iye akulamula zauve ndi zoipa. Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu, sakadayera aliyense mwa inu mpaka kalekale. Koma Allah amamuyeretsa amene wamfuna. Ndipo Allah Ngwakumva zonse; Wodziwa kwambiri.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَا يَأۡتَلِ أُوْلُواْ ٱلۡفَضۡلِ مِنكُمۡ وَٱلسَّعَةِ أَن يُؤۡتُوٓاْ أُوْلِي ٱلۡقُرۡبَىٰ وَٱلۡمَسَٰكِينَ وَٱلۡمُهَٰجِرِينَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۖ وَلۡيَعۡفُواْ وَلۡيَصۡفَحُوٓاْۗ أَلَا تُحِبُّونَ أَن يَغۡفِرَ ٱللَّهُ لَكُمۡۚ وَٱللَّهُ غَفُورٞ رَّحِيمٌ
Ndipo ochita zabwino (pa dziko lapansi), ndiponso eni kupeza bwino mwa inu, asalumbire kuti aleka kupatsa achinansi, masikini, ndi osamuka pa njira ya Allah. Koma akhululuke ndikuleka zimenezo. Kodi simufuna kuti Allah akukhululukireni? Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha (choncho, nanunso teroni).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّ ٱلَّذِينَ يَرۡمُونَ ٱلۡمُحۡصَنَٰتِ ٱلۡغَٰفِلَٰتِ ٱلۡمُؤۡمِنَٰتِ لُعِنُواْ فِي ٱلدُّنۡيَا وَٱلۡأٓخِرَةِ وَلَهُمۡ عَذَابٌ عَظِيمٞ
Ndithu amene akunamizira akazi oyera (kumachitidwe achiwerewere), odziteteza kumachitidwe oipa, okhulupirira, atembeleredwa pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro. Ndipo chilango chachikulu chili pa iwo.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
يَوۡمَ تَشۡهَدُ عَلَيۡهِمۡ أَلۡسِنَتُهُمۡ وَأَيۡدِيهِمۡ وَأَرۡجُلُهُم بِمَا كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
Tsiku lomwe malirime awo, mikono yawo ndi miyendo yawo zidzawachitira umboni pazomwe adali kuchita.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
يَوۡمَئِذٖ يُوَفِّيهِمُ ٱللَّهُ دِينَهُمُ ٱلۡحَقَّ وَيَعۡلَمُونَ أَنَّ ٱللَّهَ هُوَ ٱلۡحَقُّ ٱلۡمُبِينُ
Tsiku limenelo Allah adzawapatsa mphotho yawo ya choonadi, ndipo adzadziwa kuti Allah ndiye Mwini kulipira kwa choonadi koonekera poyera.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
ٱلۡخَبِيثَٰتُ لِلۡخَبِيثِينَ وَٱلۡخَبِيثُونَ لِلۡخَبِيثَٰتِۖ وَٱلطَّيِّبَٰتُ لِلطَّيِّبِينَ وَٱلطَّيِّبُونَ لِلطَّيِّبَٰتِۚ أُوْلَٰٓئِكَ مُبَرَّءُونَ مِمَّا يَقُولُونَۖ لَهُم مَّغۡفِرَةٞ وَرِزۡقٞ كَرِيمٞ
Akazi oipa ndi a amuna oipa, naonso amuna oipa ndi a akazi oipa; ndipo akazi abwino ndi a amuna abwino, naonso amuna abwino ndi a akazi abwino. Iwowa ngopatulidwa kuzimene akunenazo. Iwo adzapeza chikhululuko ndi rizq laulemu (ku Munda wamtendere).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لَا تَدۡخُلُواْ بُيُوتًا غَيۡرَ بُيُوتِكُمۡ حَتَّىٰ تَسۡتَأۡنِسُواْ وَتُسَلِّمُواْ عَلَىٰٓ أَهۡلِهَاۚ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ لَعَلَّكُمۡ تَذَكَّرُونَ
E inu amene mwakhulupirira! Musalowe m’nyumba zomwe sinyumba zanu kufikira mutapempha chilolezo poodira ndikupereka Salaam kwa eni nyumbazo. Kutero ndi kwa bwino kwa inu kuti mukumbukire (nkuona kuti zomwe mukuuzidwa nzabwino).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
 
የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አልን ኑር
የምዕራፎች ማውጫ የገፅ ቁጥር
 
የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ - የትርጉሞች ማዉጫ

ተርጓሙ በኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ።

መዝጋት