Check out the new design

የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ * - የትርጉሞች ማዉጫ


የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አልን ኑር   አንቀጽ:
وَأَنكِحُواْ ٱلۡأَيَٰمَىٰ مِنكُمۡ وَٱلصَّٰلِحِينَ مِنۡ عِبَادِكُمۡ وَإِمَآئِكُمۡۚ إِن يَكُونُواْ فُقَرَآءَ يُغۡنِهِمُ ٱللَّهُ مِن فَضۡلِهِۦۗ وَٱللَّهُ وَٰسِعٌ عَلِيمٞ
Ndipo zikwatitseni mbeta za mwa inu (mfulu), ndi akapolo anu amene ali abwino (achimuna) ndi adzakazi anu. Ngati ali osauka Allah awalemeletsa kuchokera m’zabwino Zake. Ndipo Allah za ufulu Zake nzambiri (zopanda muyeso, ndiponso) Ngodziwa kwabasi.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلۡيَسۡتَعۡفِفِ ٱلَّذِينَ لَا يَجِدُونَ نِكَاحًا حَتَّىٰ يُغۡنِيَهُمُ ٱللَّهُ مِن فَضۡلِهِۦۗ وَٱلَّذِينَ يَبۡتَغُونَ ٱلۡكِتَٰبَ مِمَّا مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡ فَكَاتِبُوهُمۡ إِنۡ عَلِمۡتُمۡ فِيهِمۡ خَيۡرٗاۖ وَءَاتُوهُم مِّن مَّالِ ٱللَّهِ ٱلَّذِيٓ ءَاتَىٰكُمۡۚ وَلَا تُكۡرِهُواْ فَتَيَٰتِكُمۡ عَلَى ٱلۡبِغَآءِ إِنۡ أَرَدۡنَ تَحَصُّنٗا لِّتَبۡتَغُواْ عَرَضَ ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۚ وَمَن يُكۡرِههُّنَّ فَإِنَّ ٱللَّهَ مِنۢ بَعۡدِ إِكۡرَٰهِهِنَّ غَفُورٞ رَّحِيمٞ
Ndipo amene sapeza chokwatilira apewe (uve wa chiwerewere) kufikira Allah atawalemeletsa ndi zabwino Zake. Ndipo amene afuna kuti awalembere (kuti apate ufulu) mwa amene manja anu akumanja apeza, alembereni (kuti adziombole) ngati mwaona zabwino mwa iwo. Ndipo apatseni gawo la chuma cha Allah chomwe akupatsani. Musawakakamize adzakadzi anu kuchita uhule ngati akufuna kudzisunga, ncholinga choti mupeze zinthu za moyo wa dziko lapansi. Ndipo amene angawakakamize, ndithu Allah, pambuyo pokakamizidwa kwawoko, Ngokhululuka; Ngwachisoni (kwa okakamizidwawo).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكُمۡ ءَايَٰتٖ مُّبَيِّنَٰتٖ وَمَثَلٗا مِّنَ ٱلَّذِينَ خَلَوۡاْ مِن قَبۡلِكُمۡ وَمَوۡعِظَةٗ لِّلۡمُتَّقِينَ
Ndipo ndithu tatumiza kwa inu Ayah (ndime) zofotokoza (zofunika zonse) mwatsatanetsatane, ndi mafanizo (okuphanulani maso) pa za amene adamuka patsogolo panu, ndi phunziro kwa oopa (Allah).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
۞ ٱللَّهُ نُورُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ مَثَلُ نُورِهِۦ كَمِشۡكَوٰةٖ فِيهَا مِصۡبَاحٌۖ ٱلۡمِصۡبَاحُ فِي زُجَاجَةٍۖ ٱلزُّجَاجَةُ كَأَنَّهَا كَوۡكَبٞ دُرِّيّٞ يُوقَدُ مِن شَجَرَةٖ مُّبَٰرَكَةٖ زَيۡتُونَةٖ لَّا شَرۡقِيَّةٖ وَلَا غَرۡبِيَّةٖ يَكَادُ زَيۡتُهَا يُضِيٓءُ وَلَوۡ لَمۡ تَمۡسَسۡهُ نَارٞۚ نُّورٌ عَلَىٰ نُورٖۚ يَهۡدِي ٱللَّهُ لِنُورِهِۦ مَن يَشَآءُۚ وَيَضۡرِبُ ٱللَّهُ ٱلۡأَمۡثَٰلَ لِلنَّاسِۗ وَٱللَّهُ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ
Allah ndiye Kuunika kwa kuthambo ndi nthaka. Fanizo la kuunika Kwake (powaongolera akapolo Ake) lili ngati “Mishikati” (chibowo cha pa khoma choikapo nyali) yomwe mkati mwake mwaikidwa nyali. Nyali ili m’galasi. Ndipo galasilo lili ngati nyenyezi yowala. Nyali imeneyo imayatsidwa ndi mafuta ochokera ku mtengo wodalitsidwa wa mzitona, womwe suli mbali yakuvuma ngakhale kuzambwe; (umamenyedwa kwambiri ndi dzuwa pamene likutuluka, ndi parnene likulowa). Mafuta ake ngoyandikira kuwala okha (chifukwa champhamvu yake) ngakhale moto usanawakhudze. Kuunika pamwamba pa kuunika! Allah amamuongolera ku kuunika Kwake amene wamfuna. Allah amaponya mafanizo kwa anthu (kuti aganizire ndi kupeza phunziro), ndipo Allah Ngodziwa chilichonse.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فِي بُيُوتٍ أَذِنَ ٱللَّهُ أَن تُرۡفَعَ وَيُذۡكَرَ فِيهَا ٱسۡمُهُۥ يُسَبِّحُ لَهُۥ فِيهَا بِٱلۡغُدُوِّ وَٱلۡأٓصَالِ
(Apezeke akupemphera kasanu) m’nyumba zomwe Allah walamula kuti zilemekezedwe; ndipo m’menemo dzina Lake litchulidwe; azimulemekeza m’menemo (m’misikiti) kum’mawa ndi kumadzulo;
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
 
የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አልን ኑር
የምዕራፎች ማውጫ የገፅ ቁጥር
 
የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ - የትርጉሞች ማዉጫ

በኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ ተተረጎመ

መዝጋት