Check out the new design

የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ * - የትርጉሞች ማዉጫ


የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አል ቀመር   አንቀጽ:

Al-Qamar

ٱقۡتَرَبَتِ ٱلسَّاعَةُ وَٱنشَقَّ ٱلۡقَمَرُ
Nthawi ya chimaliziro (Qiyâma) yayandikira ndipo mwezi wagawikana.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَإِن يَرَوۡاْ ءَايَةٗ يُعۡرِضُواْ وَيَقُولُواْ سِحۡرٞ مُّسۡتَمِرّٞ
Koma akaona chozizwitsa akunyoza ndi kunena kuti: “Awa ndi matsenga womkeramkera patsogolo.”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَكَذَّبُواْ وَٱتَّبَعُوٓاْ أَهۡوَآءَهُمۡۚ وَكُلُّ أَمۡرٖ مُّسۡتَقِرّٞ
Ndipo adatsutsa (choonadi) ndi kutsatira zilakolako (zawo zoipa) koma chinthu chilichonse (cha Allah) nchokhazikika.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ جَآءَهُم مِّنَ ٱلۡأَنۢبَآءِ مَا فِيهِ مُزۡدَجَرٌ
Ndipo ndithu zidawafika nkhani zomwe zili zokwanira kuwaopseza.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
حِكۡمَةُۢ بَٰلِغَةٞۖ فَمَا تُغۡنِ ٱلنُّذُرُ
Nzeru zokwana koma machenjezo (kwa iwo) sanawathandize.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَتَوَلَّ عَنۡهُمۡۘ يَوۡمَ يَدۡعُ ٱلدَّاعِ إِلَىٰ شَيۡءٖ نُّكُرٍ
Choncho, apewe (iwe Mtumiki) osakhulupirira, (yembekezani) tsiku loitana woitana (wa Allah) ku chinthu chovuta kwambiri, (chodedwa ndi mitima).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
خُشَّعًا أَبۡصَٰرُهُمۡ يَخۡرُجُونَ مِنَ ٱلۡأَجۡدَاثِ كَأَنَّهُمۡ جَرَادٞ مُّنتَشِرٞ
Maso awo ali zyoli chifukwa chakuopsa; adzatuluka m’manda uku ali ngati dzombe lobalalika (chifukwa cha kuchuluka),
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
مُّهۡطِعِينَ إِلَى ٱلدَّاعِۖ يَقُولُ ٱلۡكَٰفِرُونَ هَٰذَا يَوۡمٌ عَسِرٞ
Akuthamangira kwa woitana (uku atatukula mitu yawo, osatha kucheukira kwina). Adzanena osakhulupirira (tsiku lachiweruziro): “Ili nditsiku lovuta kwambiri.”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
۞ كَذَّبَتۡ قَبۡلَهُمۡ قَوۡمُ نُوحٖ فَكَذَّبُواْ عَبۡدَنَا وَقَالُواْ مَجۡنُونٞ وَٱزۡدُجِرَ
Patsogolo pawo (Aquraishi) anthu a Nuh nawo adatsutsa, adamtsutsa kapolo Wathu nanena kuti: “Uyu ngwamisala!” Ndipo adaopsezedwa (ndi kuzunzidwa ndi mazunzo osiyanasiyana).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَدَعَا رَبَّهُۥٓ أَنِّي مَغۡلُوبٞ فَٱنتَصِرۡ
(Nuh) adaitana Mbuye wake (nati): “Ine ndagonjetsedwa (ndi anthu anga); choncho ndipulumutseni (kwa iwo).”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَفَتَحۡنَآ أَبۡوَٰبَ ٱلسَّمَآءِ بِمَآءٖ مُّنۡهَمِرٖ
Tero tidatsekula makomo akumwamba ndi madzi otsika mopitiriza, mwamphamvu.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَفَجَّرۡنَا ٱلۡأَرۡضَ عُيُونٗا فَٱلۡتَقَى ٱلۡمَآءُ عَلَىٰٓ أَمۡرٖ قَدۡ قُدِرَ
Ndipo tidaing’amba nthaka kukhala ndi akasupe (ofwamphuka madzi mwamphamvu). Choncho adakumana madzi (akumwamba ndi am’nthaka kuti awaononge) pamuyeso wopimidwa ndi kulamulidwa (ndi Allah).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَحَمَلۡنَٰهُ عَلَىٰ ذَاتِ أَلۡوَٰحٖ وَدُسُرٖ
Ndipo tidamnyamula Nuh pa chombo chamatabwa chokhomedwa ndi misomali (yamitengo).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
تَجۡرِي بِأَعۡيُنِنَا جَزَآءٗ لِّمَن كَانَ كُفِرَ
Chinkayandama pamadzi ndi kuyang’aniridwa ndi Ife. Iyi ndi mphoto ya (Nuh) yemwe adakanidwa ndi anthu ake.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَد تَّرَكۡنَٰهَآ ءَايَةٗ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ
Ndipo ndithu tidachisiya (chigumula) kukhala phunziro (pakuonongeka kwa osakhulupirira ndi kupulumuka kwa okhulupirira). Kodi alipo wolikumbukira (ndi kupeza nalo malango abwino?)
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ
Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza!)
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ
Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino?)
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
كَذَّبَتۡ عَادٞ فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ
Âdi adamtsutsa (mneneri wawo Hud), kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)!
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ رِيحٗا صَرۡصَرٗا فِي يَوۡمِ نَحۡسٖ مُّسۡتَمِرّٖ
Ndithu Ife tidawatumizira mphepo yozizira, yaphokoso, m’tsiku latsoka lopitilira,
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
تَنزِعُ ٱلنَّاسَ كَأَنَّهُمۡ أَعۡجَازُ نَخۡلٖ مُّنقَعِرٖ
Idawazula anthu (kuchoka m’malo mwawo ndi kuwaponya panthaka ali akufa) ngati matsinde a mitengo yakanjedza ozulidwa m’malo mwake.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ
Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)!
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ
Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino?)
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
كَذَّبَتۡ ثَمُودُ بِٱلنُّذُرِ
Asamudu adatsutsa machenjezo.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَقَالُوٓاْ أَبَشَرٗا مِّنَّا وَٰحِدٗا نَّتَّبِعُهُۥٓ إِنَّآ إِذٗا لَّفِي ضَلَٰلٖ وَسُعُرٍ
Ndipo adati: “Kodi titsatire munthu mmodzi wochokera mwa ife? Ndithu ife ngati titamtsatira ndiye kuti tili nkusokera ndiponso misala.”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
أَءُلۡقِيَ ٱلذِّكۡرُ عَلَيۡهِ مِنۢ بَيۡنِنَا بَلۡ هُوَ كَذَّابٌ أَشِرٞ
Kodi am’vumbulutsira iye chikumbutso pakati pathu, (pomwe tili nawo oposa iye pa ulemelero)? Koma iye ndiwabodza ndi wodzitukumu.”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
سَيَعۡلَمُونَ غَدٗا مَّنِ ٱلۡكَذَّابُ ٱلۡأَشِرُ
Mawa lino adzadziwa (tsiku lakuwatsikira chilango,) kuti ndiyani wabodza wodzitukumula (iwo kapena Swaleh).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّا مُرۡسِلُواْ ٱلنَّاقَةِ فِتۡنَةٗ لَّهُمۡ فَٱرۡتَقِبۡهُمۡ وَٱصۡطَبِرۡ
(Tidamuuza mneneriyo kuti) ndithu Ife titumiza ngamira yaikazi kuti ikhale mayeso kwa iwo. Choncho adikire, ndipo pirira.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَنَبِّئۡهُمۡ أَنَّ ٱلۡمَآءَ قِسۡمَةُۢ بَيۡنَهُمۡۖ كُلُّ شِرۡبٖ مُّحۡتَضَرٞ
Ndipo auze kuti madzi agawidwa pakati pawo (ndi ngamira). Aliyense ali ndi tsiku lopita kukatunga.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَنَادَوۡاْ صَاحِبَهُمۡ فَتَعَاطَىٰ فَعَقَرَ
Koma adaitana mnzawo (wa mphulupulu). Choncho adakonzeka kupha ngamirayo ndipo adaipha.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَكَيۡفَ كَانَ عَذَابِي وَنُذُرِ
Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa anthu otsutsa)!
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ صَيۡحَةٗ وَٰحِدَةٗ فَكَانُواْ كَهَشِيمِ ٱلۡمُحۡتَظِرِ
Ndithu tidawatumizira nkuwe umodzi choncho adakhala ngati udzu ndi mitengo youma yaomanga khola.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ
Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino?)
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
كَذَّبَتۡ قَوۡمُ لُوطِۭ بِٱلنُّذُرِ
Anthu a Luti adatsutsa machenjezo (a mneneri wawo).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّآ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِمۡ حَاصِبًا إِلَّآ ءَالَ لُوطٖۖ نَّجَّيۡنَٰهُم بِسَحَرٖ
Ndithu Ife tidawatumizira chimphepo champhamvu choulutsa miyala (ndi kuwagenda), kupatula akubanja la Luti; tidawapulumutsa (ku chilangocho) m’bandakucha,
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
نِّعۡمَةٗ مِّنۡ عِندِنَاۚ كَذَٰلِكَ نَجۡزِي مَن شَكَرَ
(Choncho kupulumukako kudali) chisomo chochokera kwa Ife (pa iwo). Momwemo ndimo timamlipirira wothokoza.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ أَنذَرَهُم بَطۡشَتَنَا فَتَمَارَوۡاْ بِٱلنُّذُرِ
Ndipo ndithu (Luti) adawachenjeza anthu ake za kulanga Kwathu koopsa. Koma adakaikira machenjezo (ake ndi kumtsutsa).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ رَٰوَدُوهُ عَن ضَيۡفِهِۦ فَطَمَسۡنَآ أَعۡيُنَهُمۡ فَذُوقُواْ عَذَابِي وَنُذُرِ
Ndipo ndithu adafuna kwa iye kuti awapatse alendo ake (kuti achite nawo zauve), koma tidafafaniza maso awo (kuti ikhale mphoto pa zimene adafunazo). (Ndipo tidawauza): “Choncho lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ صَبَّحَهُم بُكۡرَةً عَذَابٞ مُّسۡتَقِرّٞ
Ndipo ndithu chidawadzera mwadzidzidzi chilango chokhazikika, nthawi yam’mamawa.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فَذُوقُواْ عَذَابِي وَنُذُرِ
Choncho (kudanenedwa kwa iwo) “Lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ يَسَّرۡنَا ٱلۡقُرۡءَانَ لِلذِّكۡرِ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ
Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an (kuti ikhale chikumbutso). Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)?
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ جَآءَ ءَالَ فِرۡعَوۡنَ ٱلنُّذُرُ
Ndipo ndithu machenjezo (ondondozana) adawadzera anthu a Farawo (ndi iye mwini).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
كَذَّبُواْ بِـَٔايَٰتِنَا كُلِّهَا فَأَخَذۡنَٰهُمۡ أَخۡذَ عَزِيزٖ مُّقۡتَدِرٍ
Adatsutsa zozizwitsa Zathu zonse (zimene zidadza kupyolera m’manja mwa aneneri Athu). Choncho tidawalanga, kulanga kwa Wamphamvu (Wosapambanidwa), Wokhoza.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
أَكُفَّارُكُمۡ خَيۡرٞ مِّنۡ أُوْلَٰٓئِكُمۡ أَمۡ لَكُم بَرَآءَةٞ فِي ٱلزُّبُرِ
Kodi osakhulupirira anuwa ndi abwino kuposa iwo (kotero kuti sadzaonongedwa)? Kapena zalembedwa m’mabuku kuti inu mdzasiyidwa (sadzakuonongani monga momwe adawaonongera akale?)
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
أَمۡ يَقُولُونَ نَحۡنُ جَمِيعٞ مُّنتَصِرٞ
Kapena akunena kuti: “Ife ndiochuluka titha kudziteteza (palibe angatipambane)?”
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
سَيُهۡزَمُ ٱلۡجَمۡعُ وَيُوَلُّونَ ٱلدُّبُرَ
(Auze): Gululo ligonjetsedwa ndipo athawa ndi kutembenuza misana.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
بَلِ ٱلسَّاعَةُ مَوۡعِدُهُمۡ وَٱلسَّاعَةُ أَدۡهَىٰ وَأَمَرُّ
Koma lonjezo la chilango chawo ndi tsiku la chiweruziro, ndipo tsiku la chiweruziro ndi latsoka lalikulu, lowawa kwabasi (kwa osakhulupirira).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّ ٱلۡمُجۡرِمِينَ فِي ضَلَٰلٖ وَسُعُرٖ
Ndithu oipa (mwa awa ndi aja) ali nkusokera ndi misala.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
يَوۡمَ يُسۡحَبُونَ فِي ٱلنَّارِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ ذُوقُواْ مَسَّ سَقَرَ
Tsiku limene adzakokedwera ku Moto ndi nkhope zawo, (kudzanenedwa kwa iwo:) “Lawani zowawa za Jahena (ndi kutentha kwake)!
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّا كُلَّ شَيۡءٍ خَلَقۡنَٰهُ بِقَدَرٖ
Ndithu Ife tachilenga chinthu chilichonse ndi muyeso (kulingana ndi zolinga).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَمَآ أَمۡرُنَآ إِلَّا وَٰحِدَةٞ كَلَمۡحِۭ بِٱلۡبَصَرِ
Ndipo silili lamulo Lathu (pa chinthu tikachifuna) koma liwu limodzi, (timangoti kwa chinthucho: “Chitika.” Ndipo chimachitika mwachangu) ngati kuphethira kwa diso.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَلَقَدۡ أَهۡلَكۡنَآ أَشۡيَاعَكُمۡ فَهَلۡ مِن مُّدَّكِرٖ
Ndipo ndithu tidawaononga anzanu (onga inu osakhulupirira): Kodi alipo wokumbuka?
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَكُلُّ شَيۡءٖ فَعَلُوهُ فِي ٱلزُّبُرِ
Ndipo chinthu chilichonse adachichita iwowo (pa dziko lapansi) chili mkaundula.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
وَكُلُّ صَغِيرٖ وَكَبِيرٖ مُّسۡتَطَرٌ
Ndipo ntchito iliyonse, yaing’ono kapena yaikulu, idalembedwa; (palibe chimene chingamsowe).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
إِنَّ ٱلۡمُتَّقِينَ فِي جَنَّٰتٖ وَنَهَرٖ
Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda ya ulemelero waukulu ndi Mitsinje (yosiyanasiyana).
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
فِي مَقۡعَدِ صِدۡقٍ عِندَ مَلِيكٖ مُّقۡتَدِرِۭ
Pokhala pabwino pachoonadi, (popanda mawu achabe ndi machimo), kwa Mfumu yokhoza chilichonse.
የአረብኛ ቁርኣን ማብራሪያ:
 
የይዘት ትርጉም ምዕራፍ: አል ቀመር
የምዕራፎች ማውጫ የገፅ ቁጥር
 
የቅዱስ ቁርዓን ይዘት ትርጉም - የቺቼዋኛ ትርጉም - ኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ - የትርጉሞች ማዉጫ

በኻሊድ ኢብራሂም ቢታላ ተተረጎመ

መዝጋት