ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: العنكبوت
آية:
 

العنكبوت

الٓمٓ
“Alif-Lâm-Mîm.
التفاسير العربية:
أَحَسِبَ ٱلنَّاسُ أَن يُتۡرَكُوٓاْ أَن يَقُولُوٓاْ ءَامَنَّا وَهُمۡ لَا يُفۡتَنُونَ
“Kodi anthu akuganiza kuti adzasiyidwa popanda kuyesedwa ndi masautso pakungonena kuti: “Takhulupirira?” (Iyayi, ayenera kuyesedwa ndithu ndi masautso osiyanasiyana pa matupi pawo ndi pachuma chawo kuti adziwike woona ndi wachiphamaso).
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ فَتَنَّا ٱلَّذِينَ مِن قَبۡلِهِمۡۖ فَلَيَعۡلَمَنَّ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ صَدَقُواْ وَلَيَعۡلَمَنَّ ٱلۡكَٰذِبِينَ
“Ndipo ndithu tidawayesa amene adalipo patsogolo pawo. Ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zoona, ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zabodza.
التفاسير العربية:
أَمۡ حَسِبَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلسَّيِّـَٔاتِ أَن يَسۡبِقُونَاۚ سَآءَ مَا يَحۡكُمُونَ
“Kodi amene akuchita zoipa akuganiza kuti atipambana (kotero kuti sitingawalange)? Ndichiweruzo choipa chimene akuweruzacho.
التفاسير العربية:
مَن كَانَ يَرۡجُواْ لِقَآءَ ٱللَّهِ فَإِنَّ أَجَلَ ٱللَّهِ لَأٓتٖۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
“Amene akuyembekezera kukumana ndi Allah, (agwire ntchito yabwino pamoyo wake kuti akakumane Naye ndi zabwino), pakuti ndithu nthawi ya Allah (tsiku la chimaliziro) ikudza (popanda chikaiko). Ndipo Iye Ngwakumva (zonena za akapolo Ake), Ngodziwa (zachinsinsi chawo).
M’ndime iyi akufotokoza kuti adalenga anthu kuchokera m’madzi ofooka. Ndipo kuchokera pamenepo chilengedwe chimasinthasintha pokhala khanda, mnyamata kenako nkukhala wamkulu wanyongazake ndipo mapeto ake nkukhala nkhalamba ya imvi, yofooka. Zonsezi zimachitika mwa chifuniro cha Allah popanda munthu kuikapo dzanja.
التفاسير العربية:
وَمَن جَٰهَدَ فَإِنَّمَا يُجَٰهِدُ لِنَفۡسِهِۦٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ لَغَنِيٌّ عَنِ ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Ndipo amene akuchita khama (polimbana ndi Akafiri, kapena pogonjetsa mtima wake kuti utsatire malamulo a Allah), ndithu zabwino za khamalo zili pa iye mwini. Ndithu Allah siwosaukira chilichonse kwa zolengedwa Zake.
التفاسير العربية:

وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّـٰلِحَٰتِ لَنُكَفِّرَنَّ عَنۡهُمۡ سَيِّـَٔاتِهِمۡ وَلَنَجۡزِيَنَّهُمۡ أَحۡسَنَ ٱلَّذِي كَانُواْ يَعۡمَلُونَ
“Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, Tidzawafafanizira zoipa zawo, ndipo tidzawalipira zabwino kuposa zomwe amachita.
التفاسير العربية:
وَوَصَّيۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ بِوَٰلِدَيۡهِ حُسۡنٗاۖ وَإِن جَٰهَدَاكَ لِتُشۡرِكَ بِي مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٞ فَلَا تُطِعۡهُمَآۚ إِلَيَّ مَرۡجِعُكُمۡ فَأُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Ndipo tamulamula munthu kuchitira zabwino makolo ake. Koma ngati atakukakamiza (makolo ako) kuti undiphatikize Ine ndi (zinthu zina) zomwe iwe sukuzidziwa, usawamvere. Kwa Ine ndiko kobwerera kwanu, ndipo ndidzakuuzani zimene mumachita.
Ndime iyi ikufotokozera kuti anthu ochita zoipa akadzaukitsidwa m’manda ndi kuona zoopsa zothetsa nzeru, adzaganiza kuti pamoyo wa padziko lapansi sadakhale nthawi yaitali koma ola limodzi basi. Izi nchifukwa chamavuto omwe adzakumana nawo patsiku limenelo.
التفاسير العربية:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّـٰلِحَٰتِ لَنُدۡخِلَنَّهُمۡ فِي ٱلصَّـٰلِحِينَ
“Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, tidzawalowetsa m’gulu la anthu abwino.
التفاسير العربية:
وَمِنَ ٱلنَّاسِ مَن يَقُولُ ءَامَنَّا بِٱللَّهِ فَإِذَآ أُوذِيَ فِي ٱللَّهِ جَعَلَ فِتۡنَةَ ٱلنَّاسِ كَعَذَابِ ٱللَّهِۖ وَلَئِن جَآءَ نَصۡرٞ مِّن رَّبِّكَ لَيَقُولُنَّ إِنَّا كُنَّا مَعَكُمۡۚ أَوَلَيۡسَ ٱللَّهُ بِأَعۡلَمَ بِمَا فِي صُدُورِ ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Ndipo alipo ena mwa anthu omwe akunena: “Takhulupirira mwa Allah.” Koma akavutitsidwa chifukwa cha Allah, amawachita masautso a anthu monga chilango cha Allah, (sapirira; iwowa ndi achinyengo (achiphamaso). Ndipo chikadza chipulumutso chochokera kwa Mbuye wako amanena: “Ndithu ife tidali pamodzi ndi inu.” (Koma chikhalirecho akunena zonama). Kodi Allah sadziwa zomwe zili m’zifuwa za zolengedwa?
Malembo awa akudziwitsa kuti Qur’an idalembedwa mwachidule chomveka ndi kulozera kuti bukuli lomwe ilo anthu anzeru zakuya akulephera kulemba, lapangika kuchokera m’malembo amenewa omwe anthu akuwadziwa ndi kugwiritsa ntchito. Ngati iwo ali ndi chipeneko kuti silidachokere kwa Allah, koma kuti Muhammad (s.a.w) adangolilemba yekha ngakhale kuti adali wosadziwa kulemba, alembe buku lawo longa ili. Malembo a bukuli ndi omwenso iwo amawadziwa. Komatu sangathe kulemba buku longa ili ngakhale anthu onse a m’dziko lapansi atathandizana. Uwu ndi umboni waukulu umene ukusonyeza kuti bukuli lidachokera kwa Allah.
التفاسير العربية:
وَلَيَعۡلَمَنَّ ٱللَّهُ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَلَيَعۡلَمَنَّ ٱلۡمُنَٰفِقِينَ
“Ndipo ndithu Allah awaonetsera poyera amene akhulupirira (moona), ndiponso awaonetsera poyera achiphamaso (achinyengo).
التفاسير العربية:
وَقَالَ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ لِلَّذِينَ ءَامَنُواْ ٱتَّبِعُواْ سَبِيلَنَا وَلۡنَحۡمِلۡ خَطَٰيَٰكُمۡ وَمَا هُم بِحَٰمِلِينَ مِنۡ خَطَٰيَٰهُم مِّن شَيۡءٍۖ إِنَّهُمۡ لَكَٰذِبُونَ
“Ndipo amene sadakhulupirire adanena kwa okhulupirira: “Tsatani njira yathu; (musatsate njira ya Muhammad). Ife tidzakusenzerani machimo anu (kuti chilichonse chisakupezeni). Koma sadzasenza chilichonse cha machimo awo, ndithu iwo ngabodza.
التفاسير العربية:
وَلَيَحۡمِلُنَّ أَثۡقَالَهُمۡ وَأَثۡقَالٗا مَّعَ أَثۡقَالِهِمۡۖ وَلَيُسۡـَٔلُنَّ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَمَّا كَانُواْ يَفۡتَرُونَ
“Ndipo ndithudi, adzasenza mitolo ya machimo ndi mitolo yina yamachimo (ya omwe adawasokeretsa) poiphatikiza ku mitolo yawo ya machimo. (Nawonso osokezedwa, adzasenzanso mitolo ya machimo chifukwa cha kutsatira kwawo anthu owasokezawo). Ndipo pa tsiku la Qiyâma (chimaliziro,) ndithu adzafunsidwa pa zimene amapeka.
التفاسير العربية:
وَلَقَدۡ أَرۡسَلۡنَا نُوحًا إِلَىٰ قَوۡمِهِۦ فَلَبِثَ فِيهِمۡ أَلۡفَ سَنَةٍ إِلَّا خَمۡسِينَ عَامٗا فَأَخَذَهُمُ ٱلطُّوفَانُ وَهُمۡ ظَٰلِمُونَ
“Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake ndipo adakhala nawo zaka chikwi chimodzi kupatulapo zaka makumi asanu. (Koma m’nthawi yonseyi sadatsatire ulaliki wake). Choncho chigumula chidawapeza (ndipo adamira onse), uku ali odzichitira zoipa.
M’ndime iyi Allah akutifotokozera kuti adalenga thambo monga lilili m’kukula kwake ndi m’kuphanuka kwake ndi kulimba kwake popanda mizati yolichirikiza. Ndipo inu anthu mukuliona mmene lili lopanda chilichonse choligwira koma mphamvu za Allah Wamkulu Wapamwambamwamba.
Ndipo m’nthaka adaikamo mapiri akuluakulu kuti nthaka isamagwedezeke ndi kumakusowetsani mtendere, kapena kumakugumulirani nyumba zanu. Ndipo Allah adafalitsa padziko zamoyo zochuluka ndi kumeretsa mbewu zosiyanasiyana. Zonsezi zikusonyeza mphamvu Zake zoopsa.
التفاسير العربية:

فَأَنجَيۡنَٰهُ وَأَصۡحَٰبَ ٱلسَّفِينَةِ وَجَعَلۡنَٰهَآ ءَايَةٗ لِّلۡعَٰلَمِينَ
“Tidampulumutsa iye (ndi anthu ake) a m’chombo; ndipo tidachita ichi kuti likhale phunziro kwa zolengedwa.
التفاسير العربية:
وَإِبۡرَٰهِيمَ إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱتَّقُوهُۖ ذَٰلِكُمۡ خَيۡرٞ لَّكُمۡ إِن كُنتُمۡ تَعۡلَمُونَ
“Ndipo (akumbutse nkhani ya) Ibrahim pamene adawauza anthu ake: “Mpembedzeni Allah ndi kumuopa. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati mukudziwa (kusiyana kwa chabwino ndi choipa).”
التفاسير العربية:
إِنَّمَا تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡثَٰنٗا وَتَخۡلُقُونَ إِفۡكًاۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ تَعۡبُدُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ لَا يَمۡلِكُونَ لَكُمۡ رِزۡقٗا فَٱبۡتَغُواْ عِندَ ٱللَّهِ ٱلرِّزۡقَ وَٱعۡبُدُوهُ وَٱشۡكُرُواْ لَهُۥٓۖ إِلَيۡهِ تُرۡجَعُونَ
“Ndithu inu mukupembedza mafano kusiya (kupembedza) Allah ndipo mwadzipangira chonama. Ndithu amene mukuwapembedzawo kusiya Allah, sangakupatseni rizq (madalitso) choncho funani rizq (madalitso) kwa Allah, ndipo mpembedzeni Iye Yekha ndi kumthokoza. Kwa Iye ndikomwe mudzabwerera (tsiku la chimaliziro).
التفاسير العربية:
وَإِن تُكَذِّبُواْ فَقَدۡ كَذَّبَ أُمَمٞ مِّن قَبۡلِكُمۡۖ وَمَا عَلَى ٱلرَّسُولِ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُ ٱلۡمُبِينُ
“Ndipo ngati mutsutsa, ndithu mibadwo ya omwe adalipo patsogolo panu idatsutsanso. Ndipo kwa Mtumiki kulibe udindo wina koma kufikitsa uthenga woonekera poyera, (womveka bwino).
التفاسير العربية:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ كَيۡفَ يُبۡدِئُ ٱللَّهُ ٱلۡخَلۡقَ ثُمَّ يُعِيدُهُۥٓۚ إِنَّ ذَٰلِكَ عَلَى ٱللَّهِ يَسِيرٞ
“Kodi saona momwe Allah ayambitsira zolengedwa, kenako nkuzibwerezanso? Ndithu kwa Allah zimenezo nzosavuta.
التفاسير العربية:
قُلۡ سِيرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ فَٱنظُرُواْ كَيۡفَ بَدَأَ ٱلۡخَلۡقَۚ ثُمَّ ٱللَّهُ يُنشِئُ ٱلنَّشۡأَةَ ٱلۡأٓخِرَةَۚ إِنَّ ٱللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيۡءٖ قَدِيرٞ
“Nena: “Yendani pa dziko ndi kuona momwe Allah adayambitsira chilengedwe; kenako Allah adzaumba, kuumba kwina. Ndithu Allah Ndiwokhoza chilichonse.”
التفاسير العربية:
يُعَذِّبُ مَن يَشَآءُ وَيَرۡحَمُ مَن يَشَآءُۖ وَإِلَيۡهِ تُقۡلَبُونَ
““Amamlanga yemwe wamfuna ndipo amamchitira chifundo amene wamfuna, ndipo kwa Iye nonse mudzabwezedwa.”
التفاسير العربية:
وَمَآ أَنتُم بِمُعۡجِزِينَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَا فِي ٱلسَّمَآءِۖ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ مِن وَلِيّٖ وَلَا نَصِيرٖ
““Ndipo inu simungampambane (Allah) pa dziko ngakhale kumwamba (pomuzemba kuti asakulangeni). Inu mulibe mtetezi kapena mpulumutsi kupatula Allah.”
التفاسير العربية:
وَٱلَّذِينَ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِ ٱللَّهِ وَلِقَآئِهِۦٓ أُوْلَـٰٓئِكَ يَئِسُواْ مِن رَّحۡمَتِي وَأُوْلَـٰٓئِكَ لَهُمۡ عَذَابٌ أَلِيمٞ
“Ndipo amene akana Ayah (ndime) za Allah ndi kukumana Naye amenewo ndiwo ataya mtima pa zakupeza chifundo Changa, ndipo iwowo ndiwo adzapeza chilango chowawa.
التفاسير العربية:

فَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُواْ ٱقۡتُلُوهُ أَوۡ حَرِّقُوهُ فَأَنجَىٰهُ ٱللَّهُ مِنَ ٱلنَّارِۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
“Choncho yankho la anthu ake silidali lina koma adangoti: “Mupheni kapena mtentheni ndi moto.” Koma Allah adampulumutsa ku moto. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu okhulupirira.
التفاسير العربية:
وَقَالَ إِنَّمَا ٱتَّخَذۡتُم مِّن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡثَٰنٗا مَّوَدَّةَ بَيۡنِكُمۡ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ ثُمَّ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يَكۡفُرُ بَعۡضُكُم بِبَعۡضٖ وَيَلۡعَنُ بَعۡضُكُم بَعۡضٗا وَمَأۡوَىٰكُمُ ٱلنَّارُ وَمَا لَكُم مِّن نَّـٰصِرِينَ
“Ndipo adanena: “Ndithu inu mwasankha mafano kukhala milungu kusiya Allah, ndipo mukukondana pakati panu m’moyo wa pa dziko; (pokhalirana pamodzi ndi kupitiriza kupembedza mafanowo mwachimvano). Koma tsiku la Qiyâma, mudzakanana wina ndi mnzake, komanso mudzatembelerana wina ndi mnzake, malo anu adzakhala ku Moto, ndipo simudzapeza okupulumutsani.”
التفاسير العربية:
۞فَـَٔامَنَ لَهُۥ لُوطٞۘ وَقَالَ إِنِّي مُهَاجِرٌ إِلَىٰ رَبِّيٓۖ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
“Choncho (Mneneri) Luti adamkhulupirira iye. Ndipo (Mneneri Ibrahim) adanena: “Ndithu ine ndikusamukira kwa Mbuye wanga (ku dziko lomwe wandilamulira). Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.”
التفاسير العربية:
وَوَهَبۡنَا لَهُۥٓ إِسۡحَٰقَ وَيَعۡقُوبَ وَجَعَلۡنَا فِي ذُرِّيَّتِهِ ٱلنُّبُوَّةَ وَٱلۡكِتَٰبَ وَءَاتَيۡنَٰهُ أَجۡرَهُۥ فِي ٱلدُّنۡيَاۖ وَإِنَّهُۥ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ لَمِنَ ٱلصَّـٰلِحِينَ
“Ndipo tidampatsa (Mneneri Ibrahim) Ishâq ndi Ya’qub, ndipo tidaika uneneri ndi buku pa mbumba yake, ndipo tidampatsa malipiro ake pa dziko lapansi; ndithu iye pa tsiku la chimaliziro adzakhala mwa anthu abwino.
M’ndime izi 14 mpaka 15 Allah akulamula munthu kuti achitire zabwino makolo ake powamvera ndi kuwathandiza ngati ali osowa. Izi nchifukwa cha kuti makolo ake adazunzika kwambiri pomulera iye makamaka mayi wake ndi amene adazunzika kwambiri kuyambira pamene adatenga mimba yake kufikira pamene adamusiyitsa kuyamwa. Choncho mverani makolo anu pazimene akukulangizani zomwe sizili zolakwira Allah. Koma ngati akukulangizani zolakwira Allah, musatsatire malangizo awowo, koma khalani nawoni mwa ubwino.
التفاسير العربية:
وَلُوطًا إِذۡ قَالَ لِقَوۡمِهِۦٓ إِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلۡفَٰحِشَةَ مَا سَبَقَكُم بِهَا مِنۡ أَحَدٖ مِّنَ ٱلۡعَٰلَمِينَ
“Ndipo (akumbutse nkhani ya Mneneri) Luti pamene adawauza anthu ake: “Ndithu inu mukuchita zadama; palibe amene adakutsogolerani kuzichita (zadamazo) mwa zolengedwa.”
التفاسير العربية:
أَئِنَّكُمۡ لَتَأۡتُونَ ٱلرِّجَالَ وَتَقۡطَعُونَ ٱلسَّبِيلَ وَتَأۡتُونَ فِي نَادِيكُمُ ٱلۡمُنكَرَۖ فَمَا كَانَ جَوَابَ قَوۡمِهِۦٓ إِلَّآ أَن قَالُواْ ٱئۡتِنَا بِعَذَابِ ٱللَّهِ إِن كُنتَ مِنَ ٱلصَّـٰدِقِينَ
““Kodi inu mukuchita amuna anzanu ukwati ndi kutseka njira (pakuchita chifwamba) ndi kuchita zoipa m’mabwalo anu osonkhanirana?” Koma yankho la anthu ake silidali lina koma kunena kuti: “Tidzere ndi chilango cha Allah cho ngati uli mmodzi wa owona.”
التفاسير العربية:
قَالَ رَبِّ ٱنصُرۡنِي عَلَى ٱلۡقَوۡمِ ٱلۡمُفۡسِدِينَ
“Iye adati: “Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu oononga.”
التفاسير العربية:

وَلَمَّا جَآءَتۡ رُسُلُنَآ إِبۡرَٰهِيمَ بِٱلۡبُشۡرَىٰ قَالُوٓاْ إِنَّا مُهۡلِكُوٓاْ أَهۡلِ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةِۖ إِنَّ أَهۡلَهَا كَانُواْ ظَٰلِمِينَ
“Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Ibrahim ndi nkhani yabwino (yoti abereka Mneneri Ishaq), adanenanso: “Ndithu tiwaononga eni mudzi uwu (wa Sodom); ndithu iwowo ngochimwa.”
التفاسير العربية:
قَالَ إِنَّ فِيهَا لُوطٗاۚ قَالُواْ نَحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَن فِيهَاۖ لَنُنَجِّيَنَّهُۥ وَأَهۡلَهُۥٓ إِلَّا ٱمۡرَأَتَهُۥ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ
“(Mneneri Ibrahim) adati: “Koma mmenemo muli Luti.” Iwo adati: “Ife ndife odziwa kwambiri za omwe ali m’menemo; ndithu timpulumutsa iye ndi banja lake kupatula mkazi wake; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”
التفاسير العربية:
وَلَمَّآ أَن جَآءَتۡ رُسُلُنَا لُوطٗا سِيٓءَ بِهِمۡ وَضَاقَ بِهِمۡ ذَرۡعٗاۖ وَقَالُواْ لَا تَخَفۡ وَلَا تَحۡزَنۡ إِنَّا مُنَجُّوكَ وَأَهۡلَكَ إِلَّا ٱمۡرَأَتَكَ كَانَتۡ مِنَ ٱلۡغَٰبِرِينَ
“Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Luti, adawadandaulira ndi kuwadera nkhawa; (ndipo iwo) adati: “Usaope ndipo usadandaule. Ndithu ife tikupulumutsa ndi banja lako kupatula mkazi wako; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”
التفاسير العربية:
إِنَّا مُنزِلُونَ عَلَىٰٓ أَهۡلِ هَٰذِهِ ٱلۡقَرۡيَةِ رِجۡزٗا مِّنَ ٱلسَّمَآءِ بِمَا كَانُواْ يَفۡسُقُونَ
““Ndithu ife tiwatsitsira chilango choipa kuchokera kumwamba eni mudzi uwu chifukwa cha kuchimwa kwawo (ndi kuukira malamulo a Allah).”
التفاسير العربية:
وَلَقَد تَّرَكۡنَا مِنۡهَآ ءَايَةَۢ بَيِّنَةٗ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ
“Ndipo ndithu tidasiya chizindikiro mmenemo choonekera kwa anthu anzeru.
التفاسير العربية:
وَإِلَىٰ مَدۡيَنَ أَخَاهُمۡ شُعَيۡبٗا فَقَالَ يَٰقَوۡمِ ٱعۡبُدُواْ ٱللَّهَ وَٱرۡجُواْ ٱلۡيَوۡمَ ٱلۡأٓخِرَ وَلَا تَعۡثَوۡاْ فِي ٱلۡأَرۡضِ مُفۡسِدِينَ
“Ndipo ku Madiyan (tidatumako) m’bale wawo Shuaib, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah ndipo opani tsiku lachimaliziro musanke mu ononga pa dziko.”
التفاسير العربية:
فَكَذَّبُوهُ فَأَخَذَتۡهُمُ ٱلرَّجۡفَةُ فَأَصۡبَحُواْ فِي دَارِهِمۡ جَٰثِمِينَ
“Koma adamutsutsa. Ndipo kugwedezeka kwa nthaka kudawachotsa moyo wawo, ndipo kudawachera ali gwadegwade m’nyumba zawo (atafa).
التفاسير العربية:
وَعَادٗا وَثَمُودَاْ وَقَد تَّبَيَّنَ لَكُم مِّن مَّسَٰكِنِهِمۡۖ وَزَيَّنَ لَهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ أَعۡمَٰلَهُمۡ فَصَدَّهُمۡ عَنِ ٱلسَّبِيلِ وَكَانُواْ مُسۡتَبۡصِرِينَ
“Nawonso Âdi ndi Asamudu (tidawaononga). Ndipo mokhala mwawo mukudziwika kwa inu. Ndipo satana adawakometsera zochita zawo (zoipa), ndipo adawatsekereza ku njira (zabwino) chikhalirecho adali openya (anzeru zawo).
التفاسير العربية:

وَقَٰرُونَ وَفِرۡعَوۡنَ وَهَٰمَٰنَۖ وَلَقَدۡ جَآءَهُم مُّوسَىٰ بِٱلۡبَيِّنَٰتِ فَٱسۡتَكۡبَرُواْ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَمَا كَانُواْ سَٰبِقِينَ
“Momwemonso Kaaruni, Farawo ndi Hamana (adaonongedwa). Ndithu adawadzera Mûsa ndi zozizwitsa (zooneka), koma adadzikweza pa dziko. Komatu sadathe kumpambana (Allah pomulepheretsa kuwalanga).
التفاسير العربية:
فَكُلًّا أَخَذۡنَا بِذَنۢبِهِۦۖ فَمِنۡهُم مَّنۡ أَرۡسَلۡنَا عَلَيۡهِ حَاصِبٗا وَمِنۡهُم مَّنۡ أَخَذَتۡهُ ٱلصَّيۡحَةُ وَمِنۡهُم مَّنۡ خَسَفۡنَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ وَمِنۡهُم مَّنۡ أَغۡرَقۡنَاۚ وَمَا كَانَ ٱللَّهُ لِيَظۡلِمَهُمۡ وَلَٰكِن كَانُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ يَظۡلِمُونَ
“Choncho aliyense wa iwo tidamlanga ndi machimo ake. Ena a iwo tidawatumizira chimphepo chamiyala; ena a iwo udawaononga mkuwe; ena a iwo tidawadidimiza m’nthaka, ndipo ena a iwo tidawamiza (m’madzi). Si Allah amene adawachitira zoipa, koma adadzichitira okha zoipa.
التفاسير العربية:
مَثَلُ ٱلَّذِينَ ٱتَّخَذُواْ مِن دُونِ ٱللَّهِ أَوۡلِيَآءَ كَمَثَلِ ٱلۡعَنكَبُوتِ ٱتَّخَذَتۡ بَيۡتٗاۖ وَإِنَّ أَوۡهَنَ ٱلۡبُيُوتِ لَبَيۡتُ ٱلۡعَنكَبُوتِۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
“Fanizo la amene adzipangira milungu yabodza kusiya Allah, lili ngati fanizo la kangaude (yemwe) wadzipangira nyumba (kuti imsunge, pomwe nyumbayo siingathe kumsunga m’nyengo yozizira kapena yotentha), ndithu nyumba yomwe ili yofooka kwambiri ndi nyumba ya kangaude, akadakhala akudziwa.
E inu anthu! Ndithu Allah Wolemekezeka adakupangirani zonse zili kumwamba monga dzuwa mwezi, nyenyezi kuti muthandizike nazo. Ndipo adakupangirani zonse zomwe zili m’nthaka monga mapiri, mitengo, zipatso, mitsinje, ndi zina zambiri zosawerengeka kuti zonsezi zigonjere inu ndikuti muthandizike nazo.
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱللَّهَ يَعۡلَمُ مَا يَدۡعُونَ مِن دُونِهِۦ مِن شَيۡءٖۚ وَهُوَ ٱلۡعَزِيزُ ٱلۡحَكِيمُ
“Ndithu Allah akudziwa kupembedza kwawo zinthu zina kusiya Iye, Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
التفاسير العربية:
وَتِلۡكَ ٱلۡأَمۡثَٰلُ نَضۡرِبُهَا لِلنَّاسِۖ وَمَا يَعۡقِلُهَآ إِلَّا ٱلۡعَٰلِمُونَ
“Ndipo amenewa ndimafanizo (omwe) tikuwaponyera anthu. Sangawazindikire kupatula odziwa.
التفاسير العربية:
خَلَقَ ٱللَّهُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ بِٱلۡحَقِّۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَأٓيَةٗ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ
“Allah adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi; ndithu; m’menemo muli zizindikiro kwa okhulupirira.
التفاسير العربية:
ٱتۡلُ مَآ أُوحِيَ إِلَيۡكَ مِنَ ٱلۡكِتَٰبِ وَأَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَۖ إِنَّ ٱلصَّلَوٰةَ تَنۡهَىٰ عَنِ ٱلۡفَحۡشَآءِ وَٱلۡمُنكَرِۗ وَلَذِكۡرُ ٱللَّهِ أَكۡبَرُۗ وَٱللَّهُ يَعۡلَمُ مَا تَصۡنَعُونَ
“Werenga zimene zavumbulutsidwa kwa iwe (za) m’buku, ndipo pemphera Swala moyenera; ndithu Swala (ikapempheredwa moyenera) imamtchinjiriza (woipempherayo) ku zinthu zauve ndi zoipa. Ndipo kukumbukira Allah, ndi chinthu chachikulu. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita.
التفاسير العربية:

۞وَلَا تُجَٰدِلُوٓاْ أَهۡلَ ٱلۡكِتَٰبِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ إِلَّا ٱلَّذِينَ ظَلَمُواْ مِنۡهُمۡۖ وَقُولُوٓاْ ءَامَنَّا بِٱلَّذِيٓ أُنزِلَ إِلَيۡنَا وَأُنزِلَ إِلَيۡكُمۡ وَإِلَٰهُنَا وَإِلَٰهُكُمۡ وَٰحِدٞ وَنَحۡنُ لَهُۥ مُسۡلِمُونَ
“۞ Ndipo musatsutsane ndi anthu a buku koma kutsutsana kwabwino kupatula amene achita zoipa mwa iwo. Ndipo nenani: “Takhulupirira zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa inu, ndipo Mulungu wathu ndi Mulungu wanu ndi Mmodzi; ndipo ife ndife ogonjera Iye.”
التفاسير العربية:
وَكَذَٰلِكَ أَنزَلۡنَآ إِلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَۚ فَٱلَّذِينَ ءَاتَيۡنَٰهُمُ ٱلۡكِتَٰبَ يُؤۡمِنُونَ بِهِۦۖ وَمِنۡ هَـٰٓؤُلَآءِ مَن يُؤۡمِنُ بِهِۦۚ وَمَا يَجۡحَدُ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَّا ٱلۡكَٰفِرُونَ
“Ndipo umo ndimomwe takuvumbulutsira buku (ili la Qur’an). Choncho amene tidawapatsa buku, (ili lisadadze, monga Taurat ndi Injili), akulikhulupirira; akulikhulupiriranso ena mwa awa (Arabu omwe sitidawapatse buku). Ndipo sangawakane ma Ayah Athu kupatula osakhulupirira.
التفاسير العربية:
وَمَا كُنتَ تَتۡلُواْ مِن قَبۡلِهِۦ مِن كِتَٰبٖ وَلَا تَخُطُّهُۥ بِيَمِينِكَۖ إِذٗا لَّٱرۡتَابَ ٱلۡمُبۡطِلُونَ
“Ndipo iwe sumawerenga buku lililonse, ili lisanadze; ndipo sudalilembe ndi dzanja lako lakumanja. Zikadatero ndiye kuti anthu achabe akadakaikira.
Ndime iyi ikufotokoza kuti mawu a Allah ngochuluka. Mitengo yonse pa dziko lapansi itakhala ngati mapensulo ndipo nyanja zonse pa dziko lapansi, nkuwonjezanso nyanja zina, zikadakhala inki, zonse zikadatha koma mawu a Allah alipobe.
التفاسير العربية:
بَلۡ هُوَ ءَايَٰتُۢ بَيِّنَٰتٞ فِي صُدُورِ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَۚ وَمَا يَجۡحَدُ بِـَٔايَٰتِنَآ إِلَّا ٱلظَّـٰلِمُونَ
“Koma izi ndi Ayah zoonekera poyera zomwe zili m’zifuwa za amene apatsidwa nzeru. Ndipo sangazikane Ayah (ndime) zathu koma achinyengo.
التفاسير العربية:
وَقَالُواْ لَوۡلَآ أُنزِلَ عَلَيۡهِ ءَايَٰتٞ مِّن رَّبِّهِۦۚ قُلۡ إِنَّمَا ٱلۡأٓيَٰتُ عِندَ ٱللَّهِ وَإِنَّمَآ أَنَا۠ نَذِيرٞ مُّبِينٌ
“Ndipo akunena: “Kodi bwanji sizinatsitsidwe kwa iye zozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah; ndipo ine ndine mchenjezi woonekera, (ndilibe mphamvu zokudzetserani zozizwitsa koma pokhapo Allah atafuna).”
التفاسير العربية:
أَوَلَمۡ يَكۡفِهِمۡ أَنَّآ أَنزَلۡنَا عَلَيۡكَ ٱلۡكِتَٰبَ يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَرَحۡمَةٗ وَذِكۡرَىٰ لِقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
“Kodi sizidawakwanire kuti takuvumbulutsira buku (ili) lomwe likuwerengedwa kwa iwo? Ndithu mmenemo muli chifundo ndi phunziro kwa anthu okhulupirira.
التفاسير العربية:
قُلۡ كَفَىٰ بِٱللَّهِ بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡ شَهِيدٗاۖ يَعۡلَمُ مَا فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ بِٱلۡبَٰطِلِ وَكَفَرُواْ بِٱللَّهِ أُوْلَـٰٓئِكَ هُمُ ٱلۡخَٰسِرُونَ
“Nena: “Allah akukwana kukhala mboni pakati panga ndi inu; akudziwa za kumwamba ndi zapansi ndipo amene akukhulupirira zachabe ndi kukana Allah, iwowo ndiwo otayika.”
التفاسير العربية:

وَيَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَلَوۡلَآ أَجَلٞ مُّسَمّٗى لَّجَآءَهُمُ ٱلۡعَذَابُۚ وَلَيَأۡتِيَنَّهُم بَغۡتَةٗ وَهُمۡ لَا يَشۡعُرُونَ
“Ndipo akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; kukadapanda kuti kudaikidwa nthawi yodziwika, chilango chikadawadzera. Ndipo ndithu chidzawadzera mwadzidzidzi asakudziwa.
التفاسير العربية:
يَسۡتَعۡجِلُونَكَ بِٱلۡعَذَابِ وَإِنَّ جَهَنَّمَ لَمُحِيطَةُۢ بِٱلۡكَٰفِرِينَ
“Akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; ndithu Jahannam idzawazinga osakhuiupirira.
التفاسير العربية:
يَوۡمَ يَغۡشَىٰهُمُ ٱلۡعَذَابُ مِن فَوۡقِهِمۡ وَمِن تَحۡتِ أَرۡجُلِهِمۡ وَيَقُولُ ذُوقُواْ مَا كُنتُمۡ تَعۡمَلُونَ
“Tsiku limene chidzawavindikira chilango kuchokera pamwamba pawo ndi pansi pa miyendo yawo; ndipo adzanena: “Lawani (chilango cha) zomwe munkachita.”
التفاسير العربية:
يَٰعِبَادِيَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّ أَرۡضِي وَٰسِعَةٞ فَإِيَّـٰيَ فَٱعۡبُدُونِ
“E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Ndithu nthaka Yanga njophanuka; (mukhoza kupita dziko lina ngati m’dziko lanulo simukupeza mwayi wopembedza Allah mokwanira); ndipo Ine ndekha ndipembedzeni.
التفاسير العربية:
كُلُّ نَفۡسٖ ذَآئِقَةُ ٱلۡمَوۡتِۖ ثُمَّ إِلَيۡنَا تُرۡجَعُونَ
“Chamoyo chilichonse chidzalawa imfa. Kenako mudzabwezedwa kwa Ife.
التفاسير العربية:
وَٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّـٰلِحَٰتِ لَنُبَوِّئَنَّهُم مِّنَ ٱلۡجَنَّةِ غُرَفٗا تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَاۚ نِعۡمَ أَجۡرُ ٱلۡعَٰمِلِينَ
“Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndithudi tidzawakhazika m’zipinda za ku Munda wamtendere, momwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Taonani kukhala bwino malipiro a ochita zabwino!
التفاسير العربية:
ٱلَّذِينَ صَبَرُواْ وَعَلَىٰ رَبِّهِمۡ يَتَوَكَّلُونَ
“Amene adapirira ndipo kwa Mbuye wawo amatsamira.
التفاسير العربية:
وَكَأَيِّن مِّن دَآبَّةٖ لَّا تَحۡمِلُ رِزۡقَهَا ٱللَّهُ يَرۡزُقُهَا وَإِيَّاكُمۡۚ وَهُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
“Ndinyama zingati zomwe sizidzipezera rizq lake. Allah akuzipatsa izo pamodzi ndi inunso. Ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa.
التفاسير العربية:
وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّنۡ خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ وَسَخَّرَ ٱلشَّمۡسَ وَٱلۡقَمَرَ لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۖ فَأَنَّىٰ يُؤۡفَكُونَ
“Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndi kugonjetsa dzuwa ndi mwezi?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nanga akutembenuzidwira kuti?
التفاسير العربية:
ٱللَّهُ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ مِنۡ عِبَادِهِۦ وَيَقۡدِرُ لَهُۥٓۚ إِنَّ ٱللَّهَ بِكُلِّ شَيۡءٍ عَلِيمٞ
“Allah amamtambasulira rizq amene wamfuna mwa akapolo Ake, ndi kumchepetsera (amene wamfunanso). Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri za chilichonse.
التفاسير العربية:
وَلَئِن سَأَلۡتَهُم مَّن نَّزَّلَ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مَآءٗ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ مِنۢ بَعۡدِ مَوۡتِهَا لَيَقُولُنَّ ٱللَّهُۚ قُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِۚ بَلۡ أَكۡثَرُهُمۡ لَا يَعۡقِلُونَ
“Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani amene akutsitsa madzi kuchokera ku mitambo ndi kuiukitsa nthaka ndi madziwo pambuyo pakufa kwake?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sazindikira.
التفاسير العربية:

وَمَا هَٰذِهِ ٱلۡحَيَوٰةُ ٱلدُّنۡيَآ إِلَّا لَهۡوٞ وَلَعِبٞۚ وَإِنَّ ٱلدَّارَ ٱلۡأٓخِرَةَ لَهِيَ ٱلۡحَيَوَانُۚ لَوۡ كَانُواْ يَعۡلَمُونَ
“Ndipo moyo uwu wa pa dziko lapansi suli kanthu, koma chibwana ndi masewera. Ndipo ndithu nyumba ya tsiku la chimaliziro, ndiwo moyo weniweni, akadakhala akudziwa.
التفاسير العربية:
فَإِذَا رَكِبُواْ فِي ٱلۡفُلۡكِ دَعَوُاْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ فَلَمَّا نَجَّىٰهُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ إِذَا هُمۡ يُشۡرِكُونَ
“Ndipo akakwera m’chombo (ndi kukumana ndi zoopsa), amampempha Allah modzipereka ndikumuyeretsera pempho. Koma akawapulumutsa ndi kuwafikitsa ku ntunda, iwo amayambanso kumuphatikiza ndi mafano.
التفاسير العربية:
لِيَكۡفُرُواْ بِمَآ ءَاتَيۡنَٰهُمۡ وَلِيَتَمَتَّعُواْۚ فَسَوۡفَ يَعۡلَمُونَ
“Posathokoza zimene tawapatsa. Aleke asangalale (ndi zoipa zawozo); posachedwa adzadziwa.
التفاسير العربية:
أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّا جَعَلۡنَا حَرَمًا ءَامِنٗا وَيُتَخَطَّفُ ٱلنَّاسُ مِنۡ حَوۡلِهِمۡۚ أَفَبِٱلۡبَٰطِلِ يُؤۡمِنُونَ وَبِنِعۡمَةِ ٱللَّهِ يَكۡفُرُونَ
“Kodi saona kuti dziko lawo (mzinda wa Makka) talichita kukhala lopatulika, lamtendere pomwe anthu ena akutsompholedwa m’mphepete mwawo? Kodi akukhulupirira zachabe ndi kuukana mtendere wa Allah?
التفاسير العربية:
وَمَنۡ أَظۡلَمُ مِمَّنِ ٱفۡتَرَىٰ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبًا أَوۡ كَذَّبَ بِٱلۡحَقِّ لَمَّا جَآءَهُۥٓۚ أَلَيۡسَ فِي جَهَنَّمَ مَثۡوٗى لِّلۡكَٰفِرِينَ
“Kodi wachinyengo wamkulu ndani woposa amene akupekera bodza Allah, kapena kutsutsa choona chikamdzera? Kodi si mu Jahannam momwe mudzakhala malo a osakhulupirira?
التفاسير العربية:
وَٱلَّذِينَ جَٰهَدُواْ فِينَا لَنَهۡدِيَنَّهُمۡ سُبُلَنَاۚ وَإِنَّ ٱللَّهَ لَمَعَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ
“Ndipo amene akulimbikira m’njira yathu, (polimbana ndi satana, ndi mzimu woipa ndi zilakolako zoipa zam’thupi, ndi cholinga chofuna kukondweretsa Allah) ndithu tiwaongolera ku njira Zathu. Ndipo ndithu Allah ali pamodzi ndi ochita zabwino.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: العنكبوت
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق