للإطلاع على الموقع بحلته الجديدة

ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الأعراف   آية:
قُل لَّآ أَمۡلِكُ لِنَفۡسِي نَفۡعٗا وَلَا ضَرًّا إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۚ وَلَوۡ كُنتُ أَعۡلَمُ ٱلۡغَيۡبَ لَٱسۡتَكۡثَرۡتُ مِنَ ٱلۡخَيۡرِ وَمَا مَسَّنِيَ ٱلسُّوٓءُۚ إِنۡ أَنَا۠ إِلَّا نَذِيرٞ وَبَشِيرٞ لِّقَوۡمٖ يُؤۡمِنُونَ
Nena: “Ine ndekha ndilibe mphamvu yodzibweretsera chabwino kapena kudzichotsera choipa, koma chimene Allah wafuna. Ndikadakhala kuti ndikudziwa za mseri, ndikadadzichulukitsira zabwino, ndipo choipa sichikadandikhudza. Ine sindili chilichonse koma mchenjezi ndi wouza anthu okhulupirira nkhani zabwino.”
التفاسير العربية:
۞ هُوَ ٱلَّذِي خَلَقَكُم مِّن نَّفۡسٖ وَٰحِدَةٖ وَجَعَلَ مِنۡهَا زَوۡجَهَا لِيَسۡكُنَ إِلَيۡهَاۖ فَلَمَّا تَغَشَّىٰهَا حَمَلَتۡ حَمۡلًا خَفِيفٗا فَمَرَّتۡ بِهِۦۖ فَلَمَّآ أَثۡقَلَت دَّعَوَا ٱللَّهَ رَبَّهُمَا لَئِنۡ ءَاتَيۡتَنَا صَٰلِحٗا لَّنَكُونَنَّ مِنَ ٱلشَّٰكِرِينَ
Iye ndi Yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu mmodzi, napanga mwa iye mkazi wake kuti adzikhala naye. Pamene adamkumbatira, adakhala ndi pakati popepuka nayenda napo (mosalemedwa). Koma pamene (pakatipo) padalemera (patangotsala pang’ono kuti abereke) anampempha Allah, Mbuye wawo (kuti): “Ngati mutipatsa mwana wabwino, ndithu tidzakhala mwa othokoza kwambiri.”
التفاسير العربية:
فَلَمَّآ ءَاتَىٰهُمَا صَٰلِحٗا جَعَلَا لَهُۥ شُرَكَآءَ فِيمَآ ءَاتَىٰهُمَاۚ فَتَعَٰلَى ٱللَّهُ عَمَّا يُشۡرِكُونَ
Choncho, pamene adawapatsa mwana wabwino (yemwe adapempha) adamchitira Allah anzake (mafano) pa chimene adawapatsacho. Koma Allah watukuka kuzimene akumphatikiza nazozo.
التفاسير العربية:
أَيُشۡرِكُونَ مَا لَا يَخۡلُقُ شَيۡـٔٗا وَهُمۡ يُخۡلَقُونَ
Kodi akumphatikiza (Allah) ndi zinthu zomwe sizilenga chilichonse pomwe izo zikulengedwa?
التفاسير العربية:
وَلَا يَسۡتَطِيعُونَ لَهُمۡ نَصۡرٗا وَلَآ أَنفُسَهُمۡ يَنصُرُونَ
Ndipo sizingathe kuwathandiza ngakhale kudzithandiza zokha (podzibweretsera zabwino ndi kudzichotsera zoipa).
التفاسير العربية:
وَإِن تَدۡعُوهُمۡ إِلَى ٱلۡهُدَىٰ لَا يَتَّبِعُوكُمۡۚ سَوَآءٌ عَلَيۡكُمۡ أَدَعَوۡتُمُوهُمۡ أَمۡ أَنتُمۡ صَٰمِتُونَ
Ngati (milungu yamafanoyo) mutaiitanira ku chiongoko, siingakutsatireni (chifukwa chakuti siimva kapena kuzindikira chilichonse). Nchimodzimodzi kwa inu kuiitana kapena kukhala chete (palibe chimene ingadziwe).
التفاسير العربية:
إِنَّ ٱلَّذِينَ تَدۡعُونَ مِن دُونِ ٱللَّهِ عِبَادٌ أَمۡثَالُكُمۡۖ فَٱدۡعُوهُمۡ فَلۡيَسۡتَجِيبُواْ لَكُمۡ إِن كُنتُمۡ صَٰدِقِينَ
Ndithu amene mukuwapembedza kusiya Allah, ndi akapolo monga inu. (Koma inu muposa iwo). Choncho aitaneni ndipo akuyankheni ngati inu mulidi owona (pa zimene mukunenazi).
التفاسير العربية:
أَلَهُمۡ أَرۡجُلٞ يَمۡشُونَ بِهَآۖ أَمۡ لَهُمۡ أَيۡدٖ يَبۡطِشُونَ بِهَآۖ أَمۡ لَهُمۡ أَعۡيُنٞ يُبۡصِرُونَ بِهَآۖ أَمۡ لَهُمۡ ءَاذَانٞ يَسۡمَعُونَ بِهَاۗ قُلِ ٱدۡعُواْ شُرَكَآءَكُمۡ ثُمَّ كِيدُونِ فَلَا تُنظِرُونِ
Kodi iwo ali nayo miyendo yoyendera? Kapena ali nawo manja ogwilira. Kapena ali nawo maso openyera? Kapena ali nawo makutu omvelera? Nena: “Aitaneni aphatikizi anuwo, ndipo kenako ndichitireni chiwembu ndipo musandipatse nthawi.”
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني سورة: الأعراف
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - خالد إبراهيم بتيالا - فهرس التراجم

ترجمها خالد إبراهيم بيتالا.

إغلاق