“Akukufunsa za chuma cholandidwa pa nkhondo (mmene chingagawidwire). Nena: “Chuma cholanda pa nkhondo ndi cha Allah ndi Mtumiki (ndiamene ali olamula kagawidwe kake); choncho, muopeni Allah ndipo yanjanani mwachibale pakati panu. Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ngati mulidi okhulupirira.”
Munthu ngati akuopa Allah moona mtima, ndiye kuti Allah amutsekulira makomo amadalitso pano pa dziko lapansi ndi pa tsiku la chimaliziro.
“Ndithu okhulupirira, enieni ndi amene akuti Allah akatchulidwa mitima yawo imadzadzidwa ndi mantha; pamenenso Ayah Zake zikuwerengedwa kwa iwo zimawaonjezera chikhulupiliro, ndipo amayadzamira kwa Mbuye wawo Yekha basi; (sakhulupirira nyanga ndi mizimu ya anthu akufa).
Apa pakutchulidwa ziwembu za Aquraish zomwe adamchitira Mtumiki (s.a.w) asanasamuke ku Makka. Iwo adasonkhana m’nyumba yochitiramo upo nayamba kukambirana za chomwe angachite naye Mneneri Muhammad, chimene chingamuonongeretu. Ena anapereka maganizo akuti akamponye m’ndende konko ku Makka popanda kumpatsa chakudya. Kapena ampatse chakudya chochepa kwambiri kufikira afe ndi njala. Ndipo ena adati koma amtseke maso ndi milomo ndi kumnjata goli m’manja kenako kumkweza pa ngamira nkukamtaya kuchipululu chamchenga kuti akafere konko.
Ena amapereka ganizo oti asankhe anyamata ochokera m’mafuko amfulu kuti onse pamodzi akammenye ndi kumupha. Ganizoli ndi lomwe anavomerezana. Koma usiku omwe adapangana kuti amuphe, ndi umene Mtumiki (s.a.w) adasamuka kunka ku Madina. potero adalephera kumupha.
“Awa (okhala ndi makhalidwe otere) ndi amene ali okhulupirira mwachoonadi. Iwo adzapeza ulemelero (wapamwamba) kwa Mbuye wawo, ndi chikhululuko ndi zopatsidwa zaulemu.
“(Kumbukirani, E inu okhulupirira!) Pamene Allah anakulonjezani gulu limodzi mwa magulu awiri kuti likhale lanu (kuti mumenyane nalo). Koma inu mukufuna lopanda mphamvu kuti likhale lanu (kuti ndilo mumenyane nalo). Koma Allah akufuna kuchitsimikiza choonadi ndi mawu Ake ndi kudula mizu ya osakhulupirira, (pomenyana ndi gulu lamphamvulo, omwe ndi ankhondo a Chikuraishi).
“Ndipo Allah sadachite ichi koma kuti chikhale nkhani yabwino (yosangalatsa), ndi kuti mitima yanu ikhazikike ndi chimenecho. Ndipo palibe chipulumutso (chothandiza) koma chimene chachokera kwa Allah. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
M’chaka chachisanu nchimodzi (6) chakusamuka, Mtumiki (s.a.w) pamodzi ndi omtsatira ake ochuluka zedi adapita ku Makka ncholinga chokachita mapemphero a Umra. Koma Aquraish adamuletsa kulowa mu mzinda wa Makka podziganizira kuti iwo ndiwo oyang’anira Kaaba.
“Izi ndi chifukwa chakuti iwo anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki wake (iwo podziika mbali ina kusiya komwe kudali Allah). Amene anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu Allah ndi wolanga kwambiri (amalanga ndi chilango choopsa).
“Ndipo amene adzawatembenuzire msana kuthawa pa tsikulo - osati kutembenuka (kwa ndale) kofuna kumenyana kapena kukalowa m’gulu (la Asilamu ena) - ndiye kuti adziitanira mkwiyo wochokera kwa Allah; ndipo malo ake ndi ku Jahannam, kumeneko ndi ku malo koipa kubwererapo.
“Inu simudawaphe (ndi mphamvu zanu) koma Allah ndi Yemwe anawapha; siudawagende pamene udagenda koma Allah ndi amene anawagenda (pofikitsa mchenga m’maso mwawo, wachita zimenezi) kuti awachitire zabwino Asilamu powapatsa dalitso labwino lochokera kwa Iye. Ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa.
M’ndime iyi mwatchulidwa gulu lankhondo la Asilamu ndi gulu lankhondo la Aquraish ndi aulendo a chuma chamalonda a Aquraish. Aquraish adavutitsa Asilamu mu Mzinda wa Makka m’nyengo yazaka khumi ndi zitatu powalanda zinthu zawo ndi kuwamenya ndi kuwapha kumene. Pambuyo pake Asilamu adathawira ku Madina nkusiya chuma chawo chonse ku Makka. Chumacho chidatengedwa ndi anthu osakhulupilira Allah a Chikuraishi. Ndipo kuonjezera pa zimenezi Akafiri (Aquraish) adali kudza ku Madina usiku kudzaononga zinthu zambiri, pambuyo pake nkuthawa. Ndipo mwa zomwe adachita ndi monga kutentha nyumba ndi ziweto. Ankachitanso zifwamba zambiri.
Patapita zaka khumi ndi zisanu, Asilamu akuvutitsidwabe, Allah adawapatsa chilolezo kuti amenyane ndi Akafiriwo monga momwe iwo adali kuwamenyera. Ndiponso kuti awalande chilichonse chimene Asilamu angathe kulanda kuti abweze zinthu zawo zomwe adawalanda. Choncho Mtumiki (s.a.w) adamva kuti pali ulendo wa Aquraish umene wanyamula chuma chambiri ndipo udzadutsa pafupi ndi mzinda wa Madina. Tero, adawakhwirizira omtsatira ake (Maswahaba) kuti apite pamodzi naye nkukauthira nkhondo ulendowo, nkuulanda chumacho.
Choncho anthu adamtsata okwana mazana atatu popanda kutenga zida zaukali za nkhondo poti sadalinge kukamenya nkhondo yeniyeni koma adalinga kukalanda chumacho basi, chomwe chidali m’manja mwa anthu ochepa a paulendo; ndipo sadalinge kukawapha. Koma wotsogolera ulendo wamalondawo, mwamwayi adamva kuti Mtumiki ndi omtsatira ake akumufunafuna kuti amulande chumacho. Pompo adasintha njira natsata njira ina yomwe siinkayendedwa kuti asakumane ndi Mtumiki.
Ndipo anatuma mthenga ku Makka kuti akawauze anthu a m’Makka kuti iwo anthu amalonda athiridwa nkhondo. Aquraish ku Makka atamva nkhani iyi, adasangalala. Adaona kuti apeza mwayi womumaliziratu Mtumiki Muhammad (s.a.w) ndi omtsatira ake. Choncho adatuluka atakonzeka bwinobwino za nkhondo. Osati momwe Mtumiki ndi omtsatira ake adakonzekera. Mtumiki ndi omtsatira ake sadadziwe kuti aulendo amene iwo adali kuwadikilira awadutsa kale, ndi kuti gulu lalikulu lankhondo la Aquraish likuwadzera kudzawathira nkhondo, ndipo lafika kale pafupi nawo. Adadziwa za nkhaniyo pomwe iwo (Mtumiki ndi gulu lake) adali kutali ndi mzinda wawo wa Madina. Ndipo nkhaniyi itadziwika kwa omtsatira ake, padabuka mkangano pakati pawo. Ena adali ndi maganizo akuti alithawe gulu lankhondo la Aquraishwo, nkupitiriza kutsatira gulu lamalonda lija, pakuti adali ndi chitsimikizo chonse kuti akawagonjetsa amalondawo. Koma gulu lankhondo la Aquraish adalibe nalo chiyembekezo choligonjetsa naona kuti sikwabwino kudziika okha pachionongeko. Koma mwamwayi adakumana nalo gulu lankhondo la Aquraish mosayembekezera pomwe aulendo wa malonda aja adali kutali nawo.
Tero ili ndilo tanthauzo la Ayah ya 42.
“E inu amene mwakhulupirira muvomereni Allah (pa zimene akukulamulani) ndiponso muvomereni Mtumiki Wake pamene akukuitanirani ku chimene chingakupatseni moyo (wabwino wa pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro). Ndipo dziwani kuti Allah amatchinga pakati pa munthu ndi mtima wake (amautembenula mmene akufunira). Ndipo dziwani kuti kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.
(Ndime 1-2) Omasulila Qur’an adati Arabu adali kuswa mapangano amene adamanga pamodzi ndi Mtumiki wa Allah. Potero, Allah adalamula Mtumiki Wake kuti awaponyere mapangano awo. Choncho, Mtumiki adatuma Abubakari (r.a) kukhala mtsogoleri wa anthu kumapemphero a Hajj. Ndipo adamtsatanso Ali (r.a) kumeneko ndi nkhani yokhayokhayo kuti akawawerengere anthu kuti Allah ndi Mtumiki Wake atulukamo m’mapangano okhalirana mwa mtendere ndi Amushirikina sadzaloledwa kuyandikira Nyumba Yopatulika chaka chotsatiracho, ndikutinso sadzaloledwa kuzungulira Nyumba yopatulikayo uku ali maliseche.
“Ndipo muope mazunzo (a Allah a pano pa dziko lapansi) omwe sangagwere okhawo amene adzichitira zoipa mwa inu (koma adzawagweranso amene akusiya kuletsa zoipa) ndipo dziwani kuti Allah Ngolanga kwambiri.
Allah akuti kodi mungapangane nawo mapangano anthu oti akapeza mwawi wokugonjetsani inu sasunga chibale chomwe chidali pakati panu ngakhale pangano? Iwo amakunenerani mawu otsekemera ngati uchi pomwe mitima yawo ndi yodzadzidwa ndi mkwiyo ndi inu.
“Ndipo dziwani kuti chuma chanu ndi ana anu ndimayesero (oyesedwa ndi Allah kuti aone mmene mungagwiritsire nazo ntchito). Ndi kuti kwa Allah kuli malipiro aakulu.
“E inu amene mwakhulupirira! Ngati muopa Allah, adzakupatsani chilekanitso (cholekanitsa pakati pa choonadi ndi chachabe), ndiponso akufafanizirani zoipa zanu ndi kukukhululukirani. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino waukulu.
Mu Ayah iyi, Allah akuchenjeza amene akusonkhanitsa chumacho nkumangochiunjika m’nkhokwe popanda kutulutsamo chopereka (Zakaat). Akawalanga nacho pa tsiku la chimaliziro ndi chilango cha moto. Tero, tulutsamoni Zakaat m’chuma chanu. Musanyozere lamulo la Allah.
“Ndipo (kumbukira) pamene adati: “E Inu Allah! Ngati ichi (chimene wadza nacho Muhammad {s.a.w}) chili choonadi chochokera kwa Inu, tivumbwitsireni mvula ya miyala yochokera kumwamba, kapena mutibweretsere chilango chowawa kwambiri.”
Kuichedwetsa miyezi yopatulika, kapena ina mwa iyo ndi kuichotsa mu mndondomeko wake umene Allah adaiika monga momwe ankachitira anthu am’nyengo ya umbuli, kumawaonjezera kusakhulupilira anthu osakhulupilira mwa Allah. Arabu m’nyengo ya umbuli amauyesa mwezi wopatulika kukhala wosapatulika akafuna kuti achite nkhondo m’mweziwo. Ndipo mwezi wosapatulika amauyesa wopatulika ncholinga choti akwaniritse chiwerengero cha miyezi yopatulika yomwe Allah adaipatula. Zonsezi zimachitika pofuna kukwaniritsa zilakolako zawo zoipa.
“Kuti Allah alekanitse oipa ndi abwino, ndi kuti awayike ena mwa oipawo pamwamba pa anzawo, potero nkuwaunjika oipawo mulu umodzi, kenako nawaponya ku Jahannam. Iwowa ndi anthu otaika.
“Nena kwa osakhulupirira kuti: “Ngati asiya (zochita zawo zoipa), adzakhululukidwa zimene zidatsogola. Koma ngati abwereza (kuwazunza Asilamu, tiwalanga) ndithudi njira ya Allah yomwe idachitika kwa anthu akale inadutsa (powalanga akasiya kutsata malamulo a Allah).
“۞ Ndipo dziwani kuti chilichonse chimene mwapeza monga chuma cholanda ku nkhondo, gawo limodzi mwa magawo asanu ndi cha Allah ndi Mtumiki, ndi a chibale (a Mtumiki), amasiye, masikini ndi munthu wa pa ulendo (amene asowedwa choyendera pa ulendo. Tsatilani malamulowa) ngatidi mwakhulupirira Allah ndi chimene tachivumbulutsa kwa kapolo Wathu pa tsiku lachilekanitso (lolekanitsa pakati pa choona ndi chabodza), tsiku limene magulu awiri adakumana (tsiku la nkhondo ya Badr, gulu la nkhondo la Asilamu ndi gulu la nkhondo la osakhulupirira). Ndipo Allah Ngokhoza kuchita chilichonse.
“(Kumbukirani) pamene mudali mbali ya chigwa yoyandikira (mzinda wa Madina) pomwe iwo (ankhondo a Chikuraishi) adali mbali ya kutali ya tsidya lina (la chigwacho) pomwe aulendo amalonda adali cha kumunsi kwanu. Ngati mukadapangana nthawi yokumanirana (kuti mukumane nthawi yakutiyakuti), mukadasiyana posunga chipangano (chifukwa cha kuopa kuchuluka kwa adani anuwo). Koma (mwakumana mosayembekezera ndi ankhondo a adaniwo) kuti Allah akwaniritse chinthu chomwe nchofunika kuti chichitike, kuti awonongeke amene waonongeka (posankha kusakhulupirira) ndi umboni woonekera (umene adaukana kuutsata), ndi kuti akhale ndi moyo amene wakhala ndi moyo (amene watsata njira ya Chisilamu) ndi umboninso woonekera. Ndithudi Allah Ngwakumva zonse, Ngodziwa kwambiri.
M’ndime iyi Allah akutifotokozera magulu a anthu amene ngoyenera kuwagawira chuma cha Zakaat. Iwo ndi awa:- 1. Osauka amene sangagwire ntchito nkudzipezera okha chakudya (mafukara). 2. Osauka amene alibe zokwanira pa zofunikira pa moyo wawo (Masikini). 3. Amene akusonkhetsa chuma cha Zakaat cho omwe ntchito yawo ndiyokhayo. 4. Amene angolowa kumene m’Chisilamu omwe akuyembekezedwa kuti akapatsidwa adzalimbikitsidwa mitima yawo pa chipembedzochi. 5. Amene afuna kudziombola ku ukapolo. 6. Amene akulephera kulipira ngongole ya choonadi. 7. Amene akuchita Jihâd panjira ya Allah. 8. Wapaulendo amene alibe choyendera (ndalama zoyendera).
“Ndipo mumvereni Allah ndi Mtumiki Wake, musakangane (kuopera kuti) mungakhale olephera (ndi kutaya mtima), ndikuchoka mphamvu zanu. Koma pitirizani kupirira. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi anthu opirira.
“Ndipo musakhale ngati anthu amene anatuluka m’nyumba zawo modzikweza ndi modzionetsera kwa anthu, ndikuwasekereza anthu kuyenda pa njira ya Allah. Koma Allah ndi Wodziwa kwambiri zimene akuchita.
“(Kumbukirani) pamene achiphamaso ndi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo amanena: “Anthu awa chipembedzo chawo (cha Chisilamu) chawanyenga.” Komatu amene akuyadzamira kwa Allah ndithudi Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya.
““Izo ndi chifukwa cha (machimo) amene manja anu anawatsogoza, ndipo Allah sali opondereza akapolo (Ake).”
Anthu achinyengo (achiphamaso) adakana kupita naye limodzi Mtumiki (s.a.w) ku nkhondo namasangalalira kukhala kwawoko. Ndipo apa Allah akuwauza kuti asangalale ndi kuseka pang’ono. Koma adzalira ndi kukukuta mano nthawi yaitali.
“(Khalidwe lawo awa lili ) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi omwe adalipo patsogolo pawo. Anazikana zizindikiro za Allah, choncho Allah anawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndithudi Allah Ngwamphamvu, Wolanga moopsa.
“Ndipo akonzekereni mmene mungathere ndi mphamvu zanu (zonse zomenyera nkhondo), ndiponso poikiratu mahatchi odikira nkhondo kuti muwaopseze nazo adani a Allah ndi adani anu (amene mukuwadziwa) ndiponso (ndi) ena omwe (inu) simukuwadziwa. Koma Allah akuwadziwa. Ndipo chilichonse mungapereke pa njira ya Allah chidzalipidwa kwa inu modzadza ndipo simuzaponderezedwa.
“Ngati afuna kukunyenga pa chimvanochi, ndithudi, Allah akukwanira kwa iwe (kukuteteza). Iye ndi Yemwe anakuthangata ndi chipulumutso chake ndi okhulupirira.
“Ndipo (Allah) analuzanitsa pakati pa mitima yawo (poika chikondi pakati pawo). Ngati ukanapereka zonse za m’dziko lapansi (ncholinga choti uwaluzanitse mitima yawo mwa iwe wekha) sukadatha kuluzanitsa pakati pa mitima yawo. Koma Allah adaluzanitsa pakati pawo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.
“Sichoyenera kwa Mneneri kukhala ndi akayidi mpaka amenye nkhondo (kwambiri) ndi kugonjetseratu maiko molimba (ndi pamene atha kukhala ndi akayidi). Mukufuna zinthu za m’dziko pomwe Allah akufuna (mupeze mphoto ya) tsiku lachimaliziro! Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.
“Pakadapanda lamulo la Allah limene linatsogolera kale (lokulolezani chuma chopeza ku nkhondo), chilango chachikulu chikanakugwerani, chifukwa cha zimene munatenga (ku-nkhondo ya Badri).
“Ndithu anthu amene anakhulupirira nasamuka kwawo ndi kumenyana pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi moyo wawo; ndiponso amene anawalandira (iwo) ndi kuwapatsa malo ndi kuwathandiza, awa ndiabale otchinjirizana wina ndi mnzake. Ndipo anthu amene akhulupirira koma nasiya kusamuka (kudza ku Madina), palibe udindo pa inu wa kuwateteza kufikira nawonso atasamuka (kudza ku Madina). Ngati atakupemphani chithandizo cha chipembedzo athandizeni, kupatula (akaputana ndi anthu) amene pakati panu ndi iwo pali chipangano, (pamenepo musawathandize pomenyana ndi osakhulupirirawo omwe muli nawo chipangano). Ndipo Allah Ngowoona zomwe muchita.
“Amene akhulupirira nasamuka, namenya nkhondo panjira ya Allah (pamodzi nanu), ndiponso amene anawalandira (osamukawo), nawapatsa malo ndi kuwathandiza, iwo ndi omwe ali okhulupirira mwa choonadi. Iwo adzapeza chikhululuko ndi zopatsidwa za ulemu.
“Ndipo aja akhulupirira pambuyo (pa Amuhajirina ndi Answari), nawonso nasamukira (ku Madina kukakhala pamodzi ndi Mtumiki ndi Asilamu anzawo), namenyanso nkhondo pamodzi nanu, iwo ndi amene ali mwa inu. Koma achibale chakubadwana, ndiamene ali oyenera (kulowerana mmalo pa chuma) ena ndi ena, mmene zilili) m’buku la Allah. Ndithudi, Allah Ngodziwa chilichonse.
بوابة إلكترونية لنشر ترجمات مجانية وموثوقة ومتطورة لمعاني وتفاسير القرآن الكريم بلغات العالم، تم تجهيزها بإشراف ورعاية وتطوير جهات متخصصة ومترجمين ثقات، يتاح الوصول إليها وأخذ نسخ منها وإعادة نشرها لعموم الجهات والأفراد بكل يسر وسهولة، من خلال جميع وسائل النشر والتواصل الإلكتروني.
أهداف الموسوعة:
إيجاد مرجعية إلكترونية مجانية موثوقة لترجمات معاني القرآن الكريم وفق منهج أهل السنة والجماعة لتكون بديلاً عن المرجعيات الإلكترونية غير الموثوقة الشائعة في الفضاء الإلكتروني.
توفير صيغ إلكترونية متنوعة للترجمات تتناسب مع تطور الأجهزة الذكية والتطبيقات والأنظمة الإلكترونية.
تعميم النفع بالترجمات الموثوقة وإتاحتها مجاناً، وتسهيل الوصول إليها من خلال محركات البحث ومصادر المعلومات العالمية.
تطوير مستمر للترجمات من خلال إشراك عموم المختصين والمهتمين بمراجعة وتقييم وتصحيح الترجمة المتعلقة بكل آية من خلال خدمات إلكترونية للتقييم والمشاركة في تصحيح الترجمات.
مراحل العمل في الموسوعة:
مرحلة حصر الترجمات الموثوقة
وذلك بحصر أفضل ترجمات معاني وتفاسير القرآن الكريم الموثوقة المتوفرة في الساحة، والحصول على حقوق نشرها لإتاحتها مجاناً بكافة الصيغ.
مرحلة تجهيز محتوى الترجمات:
إدخال ترجمات معاني القرآن الكريم المختارة من خلال التحويل النصي وتدقيق الإدخال ليسهل حفظها واسترجاعها ونشرها إلكترونياً، وستستمر المراجعة وتصحيح الملاحظات على الترجمات -إن شاء الله-.
مرحلة الإتاحة والنشر الإلكتروني للترجمات:
وذلك من خلال نشر مجموعة كبيرة من ترجمات معاني وتفاسير القرآن الكريم على هذه البوابة، وإتاحة الوصول إليها من خلال جميع أنواع الأنظمة والأجهزة الذكية والشبكات الإلكترونية.
ضوابط العمل في الموسوعة:
العمل على أسس شرعية علمية وفق منهج أهل السنة والجماعة.
المخرجات والأصول لجميع جوانب المشروع وقف مجاني لعموم المسلمين.
تحقيق العمل الجماعي التشاركي خلال مراحل البناء ومرحلة التطوير.
الاتقان في العمل عن علم ومعلومات وافية والرجوع إلى أهل العلم والمتخصصين.
التطوير المستمر ومواكبة المستجدات التقنية لاستثمار فرص نشر ترجمات معاني كتاب الله.
4. إبقاء معلومات نسخة الترجمة الموجودة داخل المستند.
5. إفادة المصدر (QuranEnc.com) بأي ملاحظة على الترجمة.
6. تطوير الترجمات وفق النسخ الجديدة الصادرة من المصدر (QuranEnc.com).
API specs
Endpoints:
Sura translation
GET / https://quranenc.com/api/translation/sura/{translation_key}/{sura_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified sura (by its number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114)
Returns:
json object containing array of objects, each object contains the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".
GET / https://quranenc.com/api/translation/aya/{translation_key}/{sura_number}/{aya_number} description: get the specified translation (by its translation_key) for the speicified aya (by its number sura_number and aya_number)
Parameters: translation_key: (the key of the currently selected translation) sura_number: [1-114] (Sura number in the mosshaf which should be between 1 and 114) aya_number: [1-114] (Aya number in the sura which should be between 1 and 286)
Returns:
json object containing the "sura", "aya", "translation" and "footnotes".