ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الجن   آية:

الجن

قُلۡ أُوحِيَ إِلَيَّ أَنَّهُ ٱسۡتَمَعَ نَفَرٞ مِّنَ ٱلۡجِنِّ فَقَالُوٓاْ إِنَّا سَمِعۡنَا قُرۡءَانًا عَجَبٗا
Nena (iwe Mtumiki (s.a.w), kwa anthu ako): “Kwavumbulutsidwa kwa ine kuti gulu la ziwanda lidamvetsera (kuwerenga kwanga kwa Qur’an) ndipo lidanena (kumtundu wawo): ndithu tamvetsera Qur’an yodabwitsa (ikuwerengedwa).
التفاسير العربية:
يَهۡدِيٓ إِلَى ٱلرُّشۡدِ فَـَٔامَنَّا بِهِۦۖ وَلَن نُّشۡرِكَ بِرَبِّنَآ أَحَدٗا
Ikuitanira kuchilungamo, ndipo taikhulupirira. Ndipo sitimphatikiza aliyense ndi Mbuye wathu, (pa mapemphero).
التفاسير العربية:
وَأَنَّهُۥ تَعَٰلَىٰ جَدُّ رَبِّنَا مَا ٱتَّخَذَ صَٰحِبَةٗ وَلَا وَلَدٗا
Ndipo ndithu ukulu ndi ulemelero wa Mbuye wathu watukuka; sadadzipangire mkazi kapena mwana.
التفاسير العربية:
وَأَنَّهُۥ كَانَ يَقُولُ سَفِيهُنَا عَلَى ٱللَّهِ شَطَطٗا
Ndipo ndithu mbuli za mwa ife zakhala zikunenera Allah mawu abodza (okhala kutali ndi choonadi).
التفاسير العربية:
وَأَنَّا ظَنَنَّآ أَن لَّن تَقُولَ ٱلۡإِنسُ وَٱلۡجِنُّ عَلَى ٱللَّهِ كَذِبٗا
Ndipo ndithu ife tinkaganiza kuti anthu ndi ziwanda sangamnenere Allah zabodza (zosayenera ulemelero Wake).
التفاسير العربية:
وَأَنَّهُۥ كَانَ رِجَالٞ مِّنَ ٱلۡإِنسِ يَعُوذُونَ بِرِجَالٖ مِّنَ ٱلۡجِنِّ فَزَادُوهُمۡ رَهَقٗا
Ndipo ndithu padali amuna a mu wanthu amapempha chitetezo kwa amuna amziwanda, ndipo adawaonjezera (amuna amziwanda) kupitiriza machimo (awo, kupulikira ndi kuchenjelera anthu).
التفاسير العربية:
وَأَنَّهُمۡ ظَنُّواْ كَمَا ظَنَنتُمۡ أَن لَّن يَبۡعَثَ ٱللَّهُ أَحَدٗا
Ndipo ndithu iwo amaganiza monga momwe mumaganizira inu kuti Allah sadzaukitsa aliyense.
التفاسير العربية:
وَأَنَّا لَمَسۡنَا ٱلسَّمَآءَ فَوَجَدۡنَٰهَا مُلِئَتۡ حَرَسٗا شَدِيدٗا وَشُهُبٗا
Ndithu ife tidafuna kukafika kumwamba; tidakupeza kutadzala alonda (angelo) amphamvu ndi zenje za moto.
التفاسير العربية:
وَأَنَّا كُنَّا نَقۡعُدُ مِنۡهَا مَقَٰعِدَ لِلسَّمۡعِۖ فَمَن يَسۡتَمِعِ ٱلۡأٓنَ يَجِدۡ لَهُۥ شِهَابٗا رَّصَدٗا
Ndithu ife tidali kukhala m’menemo (kale) mokhala momvetsera; (mobera nkhani zakumwamba). Koma amene afune kumvetsera tsopano apeza chenje cha moto chikudikilira (kuti chimgwere iye ndi kumuononga).
التفاسير العربية:
وَأَنَّا لَا نَدۡرِيٓ أَشَرٌّ أُرِيدَ بِمَن فِي ٱلۡأَرۡضِ أَمۡ أَرَادَ بِهِمۡ رَبُّهُمۡ رَشَدٗا
Ndithu ife sitikudziwa chilango chimene akuwafunira a m’dziko (polondera kumwamba, kuletsa kumvetsera nkhani zakumeneko); kapena Mbuye wawo akuwafunira zabwino ndi chilungamo (pa zimenezo)!
التفاسير العربية:
وَأَنَّا مِنَّا ٱلصَّٰلِحُونَ وَمِنَّا دُونَ ذَٰلِكَۖ كُنَّا طَرَآئِقَ قِدَدٗا
Ndithu ena mwa ife ndi abwino koma ena sali choncho. Tili njira zosiyanasiyana.
التفاسير العربية:
وَأَنَّا ظَنَنَّآ أَن لَّن نُّعۡجِزَ ٱللَّهَ فِي ٱلۡأَرۡضِ وَلَن نُّعۡجِزَهُۥ هَرَبٗا
Ndithu ife tidadziwa kuti Allah sitingathe kumlepheretsa (lamulo Lake pa ife paliponse tingakhale) pa dziko lapansi, ndipo sitingamlepheretsenso pomzemba ndi kuthawira (kumwamba).
التفاسير العربية:
وَأَنَّا لَمَّا سَمِعۡنَا ٱلۡهُدَىٰٓ ءَامَنَّا بِهِۦۖ فَمَن يُؤۡمِنۢ بِرَبِّهِۦ فَلَا يَخَافُ بَخۡسٗا وَلَا رَهَقٗا
Ndipo ife pamene tachimva chiongoko (Qur’an) tachikhulupirira ndipo amene ati akhulupirire mwa Mbuye wake saopa kumchepetsera (chabwino kapena kumuonjezera machimo ake).
التفاسير العربية:
وَأَنَّا مِنَّا ٱلۡمُسۡلِمُونَ وَمِنَّا ٱلۡقَٰسِطُونَۖ فَمَنۡ أَسۡلَمَ فَأُوْلَٰٓئِكَ تَحَرَّوۡاْ رَشَدٗا
Ndithu mwa ife alipo Asilamu ndiponso mwa ife alipo opatuka (mu njira ya chilungamo); amene walowa m’Chisilamu, iwowo ndi amene alunjika njira ya choonadi.
التفاسير العربية:
وَأَمَّا ٱلۡقَٰسِطُونَ فَكَانُواْ لِجَهَنَّمَ حَطَبٗا
Koma opatuka (kunjira ya chilungamo) adzakhala nkhuni za Jahannam.”
التفاسير العربية:
وَأَلَّوِ ٱسۡتَقَٰمُواْ عَلَى ٱلطَّرِيقَةِ لَأَسۡقَيۡنَٰهُم مَّآءً غَدَقٗا
Ndithu (anthu ndi ziwanda) akadalungama panjira ya chilungamo tikadawamwetsa madzi ambiri (okwanira nyengo zonse).
التفاسير العربية:
لِّنَفۡتِنَهُمۡ فِيهِۚ وَمَن يُعۡرِضۡ عَن ذِكۡرِ رَبِّهِۦ يَسۡلُكۡهُ عَذَابٗا صَعَدٗا
Kuti tiwayese ndi zimenezo (mmene angamyamikire Allah pa mtendere Wake pa iwo). Koma amene anyozera kupembedza Mbuye wake, amlowetsa ku chilango chovuta (chimene sangathe kupirira nacho).
التفاسير العربية:
وَأَنَّ ٱلۡمَسَٰجِدَ لِلَّهِ فَلَا تَدۡعُواْ مَعَ ٱللَّهِ أَحَدٗا
Ndithu misikiti ndi ya Allah yekha! Choncho, musapembedze aliyense pamodzi ndi Allah.
التفاسير العربية:
وَأَنَّهُۥ لَمَّا قَامَ عَبۡدُ ٱللَّهِ يَدۡعُوهُ كَادُواْ يَكُونُونَ عَلَيۡهِ لِبَدٗا
Ndipo ndithu pamene adaima kapolo wa Allah (Muhammad{s.a.w}, pa Swala yake) uku akumpembedza (Allah), ziwanda zidatsala pang’ono kumgwera (chifukwa cha kuchuluka kwawo ndi kumzinga podabwa ndi zimene adaziona ndi kuzimva).
التفاسير العربية:
قُلۡ إِنَّمَآ أَدۡعُواْ رَبِّي وَلَآ أُشۡرِكُ بِهِۦٓ أَحَدٗا
Nena: “Ndikumpembedza Mbuye wanga M’modzi (Yekha) ndipo sindingamphatikize ndi aliyense (m’mapemphero Ake).”
التفاسير العربية:
قُلۡ إِنِّي لَآ أَمۡلِكُ لَكُمۡ ضَرّٗا وَلَا رَشَدٗا
Nena: “Ine ndilibe udindo wokupatsani mavuto kapena chilungamo (ndi zabwino).”
التفاسير العربية:
قُلۡ إِنِّي لَن يُجِيرَنِي مِنَ ٱللَّهِ أَحَدٞ وَلَنۡ أَجِدَ مِن دُونِهِۦ مُلۡتَحَدًا
Nena: “Ine palibe anganditeteze ku chilango cha Allah (ngati nditamnyoza) sindingapeze malo (othawira kuchilango Chake) kupatula kwa Iye.”
التفاسير العربية:
إِلَّا بَلَٰغٗا مِّنَ ٱللَّهِ وَرِسَٰلَٰتِهِۦۚ وَمَن يَعۡصِ ٱللَّهَ وَرَسُولَهُۥ فَإِنَّ لَهُۥ نَارَ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدًا
“Koma (mphamvu imene ndili nayo) ndikufikitsa uthenga wa Allah umene adanditumizira; ndithu amene anyoza Allah ndi Mtumiki Wake (ndi kupatuka pa chipembedzo cha (Allah) ndithu moto wa Jahannam ndi wake, akakhala m’menemo muyaya.”
التفاسير العربية:
حَتَّىٰٓ إِذَا رَأَوۡاْ مَا يُوعَدُونَ فَسَيَعۡلَمُونَ مَنۡ أَضۡعَفُ نَاصِرٗا وَأَقَلُّ عَدَدٗا
Mpaka pomwe adzaziona zimene alonjezedwa ndipamene adzadziwa (kuti) kodi ndani mwini mthandizi wofooka ndiponso wochepekedwa mchiwerengero (cha omtsatira, iwo kapena Asilamu).”
التفاسير العربية:
قُلۡ إِنۡ أَدۡرِيٓ أَقَرِيبٞ مَّا تُوعَدُونَ أَمۡ يَجۡعَلُ لَهُۥ رَبِّيٓ أَمَدًا
Nena (kuti): “Sindikudziwa ngati zomwe mukulonjezedwa (za chilango) zili pafupi, kapena Mbuye wanga azitalikitsa.”
التفاسير العربية:
عَٰلِمُ ٱلۡغَيۡبِ فَلَا يُظۡهِرُ عَلَىٰ غَيۡبِهِۦٓ أَحَدًا
“(Iye) ndi wodziwa zobisika; sazionetsa zobisika Zake kwa aliyense (mzolengedwa Zake),”
التفاسير العربية:
إِلَّا مَنِ ٱرۡتَضَىٰ مِن رَّسُولٖ فَإِنَّهُۥ يَسۡلُكُ مِنۢ بَيۡنِ يَدَيۡهِ وَمِنۡ خَلۡفِهِۦ رَصَدٗا
“Kupatula Mtumiki (Wake) amene wamuyanja; (iyeyo amamdziwitsa zobisikazo) ndipo ndithu amamuikira alonda kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake (omulonda).”
التفاسير العربية:
لِّيَعۡلَمَ أَن قَدۡ أَبۡلَغُواْ رِسَٰلَٰتِ رَبِّهِمۡ وَأَحَاطَ بِمَا لَدَيۡهِمۡ وَأَحۡصَىٰ كُلَّ شَيۡءٍ عَدَدَۢا
“Kuti adziwe ngati afikitsa uthenga wa Mbuye wawo, ndipo wawazungulira (podziwa zonse zili kwa iwo) ndipo wadziwa kuchuluka kwa zinthu zonse zimene zilipo; (palibe chobisika kwa Iye).”
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني سورة: الجن
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق