ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني آية: (11) سورة: الأعلى
وَيَتَجَنَّبُهَا ٱلۡأَشۡقَى
Ndipo wamavuto ambiri, (wamakani ndi wokanira), adzitalikitsa ndi ulalikiwo.[422]
[422] “Wamavuto ambiri” apa, ndiko kuzunzika ndi matsoka. Allah akumutcha kafiri kuti “Wamavuto ambiri” chifukwa chakuti ali ndi mavuto padziko lino lapansi mpaka pa tsiku lachimaliziro. Mazunzo a tsiku lachimaliziro monga momwe tidziwira ndi chilango cha Moto chomwe chikumuyembekeza. Tsono “chilango cha padziko lapansi” ndiko kuti alibe chinthu chomutonthoza likampeza tsoka kapena vuto lililonse. Msilamu likampeza vuto amadzitonthoza ndi chikhulupiliro chake chakuti moyo wa munthu suwonjezeka ndiponso suchepa, ndikuti munthu amamwalira akamaliza moyo wake. Koma kafiri saganiza choncho; amangokukuta zala ndi kuwatukwana ma dokotala kuti sadziwa kanthu akadachita mwakutimwakuti munthuyo sakadafa. Msilamu kukampeza kusauka amadzitonthoza ndi kupilira pamodzi ndi chikhulupiliro choti “chilichonse chimachitika mchifuniro cha Allah.” Ndipo amakhala woyembekezera kuti lero kapena mawa, Allah amupatsa chisomo Chake. Koma anthu opanda chikhulupiliro amangoona kuti aponderezedwa; amayesetsa kufunafuna chuma mnjira zosayenera, ndipo akalephera amadzudzula uyu kapena kumenyana ndi uyu, ndipo amangodziona ngati wonyozeka kwambiri pa maso pa munthu wolemera.
Kotero kuti atauzidwa kuti amulambire wolemera uja kuti amupatse ndalama akhoza kuchita zotero. Ndipo tsiku lililonse njiru imamuondetsa; mwina amangodzipha monga momwe tionera masiku ano. Palibe mazunzo aakulu kuposa amenewa. Ngati muyang’ana ma Ayah 16 ndi 17 muona kuti akuthilira umboni pa zimene talongosolazi.
التفاسير العربية:
 
ترجمة معاني آية: (11) سورة: الأعلى
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق