ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا * - فهرس التراجم


ترجمة معاني سورة: الأعلى
آية:
 

الأعلى

سَبِّحِ ٱسۡمَ رَبِّكَ ٱلۡأَعۡلَى
“Lemekeza dzina la Mbuye wako Wapamwambamwamba (ndikuliyeretsa ku zinthu zosayenera).
Tanthauzo la “kukondweretsedwa ndi zochita zawo’’ ndikuti anthu abwino adzakondwera ndi ntchito zawo zabwino zomwe adazichita pa dziko lapansi akadzakhala ndi malipiro abwino pa tsiku lachimaliziro.
التفاسير العربية:
ٱلَّذِي خَلَقَ فَسَوَّىٰ
“Amene adalenga (chilichonse) ndikuchikonza bwinobwino (mkalengedwe kolingana).
التفاسير العربية:
وَٱلَّذِي قَدَّرَ فَهَدَىٰ
“Amene adalamuliratu (chilichonse zochita zake) ndi kuchiongolera.
(Ndime 12-16) Zosangalatsa zenizeni za tsiku lachimaliziro monga momwe adatiuzira Mneneri (s.a.w) kuti ku Jannah kuli zinthu zimene diso silidapenyepo ngakhale khutu silidamvepo ndipo sizidapitepo m’maganizo a munthu. Choncho zokondweretsa izi zimene Allah watiuza apa akungofanizira ndi zinthu zomwe tikuzidziwa.
التفاسير العربية:
وَٱلَّذِيٓ أَخۡرَجَ ٱلۡمَرۡعَىٰ
“Ndi Yemwenso akumeretsa msipu.
التفاسير العربية:
فَجَعَلَهُۥ غُثَآءً أَحۡوَىٰ
“Ndipo nausandutsa kukhala wouma ndi wodera.
التفاسير العربية:
سَنُقۡرِئُكَ فَلَا تَنسَىٰٓ
“Tikulakatulira (chivumbulutso Chathu) ndipo siuyiwala.
(Ndime 17-20) Allah akuwauza kuti ayang’ane chilengedwe cha ngamira, thambo, mapiri ndi nthaka. Pambuyo pake alingalire, aone kuti amene adalenga zimenezo ngotha kuchita chilichonse monga kuukitsa anthu m’manda. Cholinga cha Allah potchula zinthu zimenezi, ngakhale kuti malangizowa nga munthu aliyense, koma adali kuwauza akafiri a pa Makka amene zinthu zimenezi maso awo ankaziona nthawi ndi nthawi.
التفاسير العربية:
إِلَّا مَا شَآءَ ٱللَّهُۚ إِنَّهُۥ يَعۡلَمُ ٱلۡجَهۡرَ وَمَا يَخۡفَىٰ
“Kupatula chimene wafuna Allah (kuti uchiiwale); ndithu Iye amadziwa zoonekera ndi zimene zimabisika.
التفاسير العربية:
وَنُيَسِّرُكَ لِلۡيُسۡرَىٰ
“Ndipo tikufewetsera (njira yochitira zinthu) zabwino.
Ayah iyi ikukwana kuwatsutsa adani a Chisilamu amene akunena kuti, “chipembedzo cha Chisilamu chidafala ndi lupanga.” Kutanthauza kuti ankawakakamiza anthu kuti achivomere chipembedzochi. Sichodabwitsa kuona adani a Chisilamu akuchinyoza chipembedzochi, koma chodabwitsa nchakuti mawu onamawa nkumatulukanso mkamwa mwa anthu omwe amadzitcha kuti ndi Asilamu. Nzoona alipo ena mwa anthu odziwa za chipembedzo (ma Ulama) amene adanena kuti chipembedzo cha Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga. Koma simonga momwe akutanthauzilira adani amene sadziwa za Chisilamu nkumangotsatira mabodza a akuluakulu awo. Cholinga cha ma Ulama ponena kuti “Chisilamu chidatetezedwa ndi lupanga” kumeneko ndi kudziteteza kwa adani omwe adafuna kuchithetsa, osati kuwakakamiza anthu kulowa mchipembedzo. Kukakamiza anthu kulowa mChisilamu nkosaloledwa. Amene akudziwa mbiri ya Chisilamu, akudziwa kuti Asilamu sadalamulidwe kuchita Jihâd mpaka pamene akafiri adali kuwazunza. Pali nkhani zambiri za Maswahaba (otsatira Mneneri) (s.a.w) ku Madina pamene adafuna kuwakakamiza ana awo kulowa m’Chisilamu, koma Mneneri adawakaniza kutero. Basi, munthu amene akunena zoterezo mwina akutero pa chifukwa chosadziwa za chipembedzo cha Chisilamu, mwinanso nkukhala misala basi.
التفاسير العربية:
فَذَكِّرۡ إِن نَّفَعَتِ ٱلذِّكۡرَىٰ
“Choncho akumbutse (wanthu powalalikira) ngati kukumbutsa kuthandiza.
Tanthauzo la Ayah iyi ndi masiku khumi olemekezeka omwe ali mkhumi loyamba la mwezi wa Thul-Hijjah umene ndi mwezi wa 12 pa kalendala ya Chisilamu. Amenewa ndi masiku olemekezeka kuposa masiku onse ngakhale masiku a Ramadan kupatula usiku wa LAILA-TUL-QADR, ndi masiku khumi omaliza a mwezi wa Ramadan. Choncho ndi bwino kuchulukitsa mapemphero m’masiku amenewa.
التفاسير العربية:
سَيَذَّكَّرُ مَن يَخۡشَىٰ
“(Palibe chikaiko ulalikiwo) aukumbukira (ndikuthandizidwa nawo) amene akuopa Allah.
التفاسير العربية:

وَيَتَجَنَّبُهَا ٱلۡأَشۡقَى
“Ndipo wamavuto ambiri, (wamakani ndi wokanira), adzitalikitsa ndi ulalikiwo.
Shafi ndi nambala yotheka kugawa ndi 2 (even number) Witri ndi nambala yosatheka kuigawa ndi 2 (odd number). Cholinga cha Allah pamenepa ndi kuzilumbilira zinthu zonse zimene adazilenga, zowerengedwa mnjira zonse ziwiri.
التفاسير العربية:
ٱلَّذِي يَصۡلَى ٱلنَّارَ ٱلۡكُبۡرَىٰ
“Amene adzalowa ku moto waukulu (umene wakonzedwa kuti udzakhale malipiro ake).
التفاسير العربية:
ثُمَّ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحۡيَىٰ
“Ndipo sakafa m’menemo (ndikupumula kumazunzo), ndiponso sakakhala ndi moyo (wamtendere).
التفاسير العربية:
قَدۡ أَفۡلَحَ مَن تَزَكَّىٰ
“Ndithu wapambana amene wadziyeretsa (ku machimo),
(Ndime 7-9) Âdi aku Irama ndi mtundu wa Mneneri Hud. Adali akuluakulu matupi a mphamvu kwambiri mwakuti ankanena kuti: “Ndani wamphamvu kuposa ife!” Thamudu (Samudu) ndi mtundu wa Mneneri Swaleh. Iwowa adali kukhala ku mpoto kwa chilumba cha Arabia.
التفاسير العربية:
وَذَكَرَ ٱسۡمَ رَبِّهِۦ فَصَلَّىٰ
“Ndikukumbukira dzina la Mbuye wake (ndi mtima wake, ndi lirime lake) uku akumapemphera.
التفاسير العربية:
بَلۡ تُؤۡثِرُونَ ٱلۡحَيَوٰةَ ٱلدُّنۡيَا
“Koma inu mukukonda kwambiri moyo wa dziko lapansi.
التفاسير العربية:
وَٱلۡأٓخِرَةُ خَيۡرٞ وَأَبۡقَىٰٓ
“Pamene moyo wa tsiku lachimaliziro ndiwabwino kwambiri ndiponso wamuyaya.
التفاسير العربية:
إِنَّ هَٰذَا لَفِي ٱلصُّحُفِ ٱلۡأُولَىٰ
“Ndithu izi (mukuuzidwa m’Qur’an) zilipo m’mabuku oyamba, akale,
Mzinthu zoipa zimene Farawo adachita, ndi kudzitcha kuti iye ndi mulungu, kupha ana achimuna popanda chilungamo, ndi kuwazunza Aisraeli.
التفاسير العربية:
صُحُفِ إِبۡرَٰهِيمَ وَمُوسَىٰ
“Mabuku a Ibrahim ndi Mûsa.
التفاسير العربية:

 
ترجمة معاني سورة: الأعلى
فهرس السور رقم الصفحة
 
ترجمة معاني القرآن الكريم - الترجمة الشيشيوا - فهرس التراجم

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

إغلاق