Prijevod značenja časnog Kur'ana - الترجمة الشيشيوا * - Sadržaj prijevodā


Prijevod značenja Sura: Sura el-Isra   Ajet:

Sura el-Isra

سُبۡحَٰنَ ٱلَّذِيٓ أَسۡرَىٰ بِعَبۡدِهِۦ لَيۡلٗا مِّنَ ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡحَرَامِ إِلَى ٱلۡمَسۡجِدِ ٱلۡأَقۡصَا ٱلَّذِي بَٰرَكۡنَا حَوۡلَهُۥ لِنُرِيَهُۥ مِنۡ ءَايَٰتِنَآۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡبَصِيرُ
۞ Ulemelero ngwa Yemwe adayendetsa kapolo Wake usiku (umodzi) kuchokera mu Msikiti Wopatulika (wa Makka) kupita ku Msikiti wakutali (wa Baitul-Muqaddas), womwe tidazidalitsa zomwe zauzungulira. (Tidampititsa kumeneko) kuti timsonyeze zina mwa zisonyezo Zathu; ndithu Iye (Allah) Ngwakumva, Ngowona ( chilichonse).[253]
[253] Mneneri Muhammad (s.a.w) pamene adakwezedwa kumwamba adaona zisonyezo zikuluzikulu za Allah monga Munda wa mtendere, Moto, mtengo wotchedwa Sidratul- Muntaha, Angelo, Aneneri ndi zina zododometsa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَءَاتَيۡنَا مُوسَى ٱلۡكِتَٰبَ وَجَعَلۡنَٰهُ هُدٗى لِّبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ أَلَّا تَتَّخِذُواْ مِن دُونِي وَكِيلٗا
Ndipo Mûsa tidampatsa buku (la Taurat) tidaliika kukhala chiongoko kwa ana a Israyeli (Allah adawauza): “Musadzipangire atetezi kusiya Ine.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
ذُرِّيَّةَ مَنۡ حَمَلۡنَا مَعَ نُوحٍۚ إِنَّهُۥ كَانَ عَبۡدٗا شَكُورٗا
(Ndiponso adawauza kuti: “E inu) Mbumba ya amene tidawanyamula pamodzi ndi Nuh! (Khalani othokoza monga tate wanu.) Ndithu iye adali kapolo wothokoza kwambiri.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقَضَيۡنَآ إِلَىٰ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ لَتُفۡسِدُنَّ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَّتَيۡنِ وَلَتَعۡلُنَّ عُلُوّٗا كَبِيرٗا
Ndipo tidawazindikiritsa ana a Israyeli m’bukulo, kuti: “Ndithu inu muononga pa dziko kawiri, ndipo mudzapyola malire pochita zoipa, kupyola malire kwakukulu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ أُولَىٰهُمَا بَعَثۡنَا عَلَيۡكُمۡ عِبَادٗا لَّنَآ أُوْلِي بَأۡسٖ شَدِيدٖ فَجَاسُواْ خِلَٰلَ ٱلدِّيَارِۚ وَكَانَ وَعۡدٗا مَّفۡعُولٗا
Ndipo likadzafika lonjezo (lakupatsidwa chilango chakuononga) koyamba mkuononga kuwiriko, tidzawakhwirizira pa inu anthu athu, eni kumenya nkhondo mwaukali, adzakhala akuzungulira mkatikati mwa nyumba (zanu), ndipo lidali lonjezo lochitika.
Tefsiri na arapskom jeziku:
ثُمَّ رَدَدۡنَا لَكُمُ ٱلۡكَرَّةَ عَلَيۡهِمۡ وَأَمۡدَدۡنَٰكُم بِأَمۡوَٰلٖ وَبَنِينَ وَجَعَلۡنَٰكُمۡ أَكۡثَرَ نَفِيرًا
Kenako tidakubwezerani kupambana pa iwo (omwe adakugonjetsani poyamba); ndipo tidakupatsani chuma ndi ana, ndi kukudalitsani kukhala ndi gulu lochuluka.
Tefsiri na arapskom jeziku:
إِنۡ أَحۡسَنتُمۡ أَحۡسَنتُمۡ لِأَنفُسِكُمۡۖ وَإِنۡ أَسَأۡتُمۡ فَلَهَاۚ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ ٱلۡأٓخِرَةِ لِيَسُـُٔواْ وُجُوهَكُمۡ وَلِيَدۡخُلُواْ ٱلۡمَسۡجِدَ كَمَا دَخَلُوهُ أَوَّلَ مَرَّةٖ وَلِيُتَبِّرُواْ مَا عَلَوۡاْ تَتۡبِيرًا
(Tidati kwa iwo): “Ngati muchita bwino (pomumvera Allah), ubwino ngwanu (pa dziko lapansi ndi pa tsiku la Chimaliziro); ngati muipitsa (ponyoza Allah), kuipako kuli pa inu nokha. Choncho pamene idadza nthawi ya lonjezo lachilango chomaliza, (tidakutumizirani adani anu) kuti apereke kunyozeka pa nkhope zanu, ndikutinso alowe mu Nsikiti monga adalowera mnthawi yoyamba, ndikuti aononge chilichonse chimene achigonjetsa; kuononga kwakukulu.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
عَسَىٰ رَبُّكُمۡ أَن يَرۡحَمَكُمۡۚ وَإِنۡ عُدتُّمۡ عُدۡنَاۚ وَجَعَلۡنَا جَهَنَّمَ لِلۡكَٰفِرِينَ حَصِيرًا
“(Koma ngati mudzalungama mzochita zanu), Mbuye wanu adzakuchitirani chifundo; ndipo ngati mudzabwereranso (ku machitidwe anu okhota), tidzabwereranso (kukulangani). Ndipo taikonza Jahannam kukhala ndende ya osakhulupirira.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
إِنَّ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانَ يَهۡدِي لِلَّتِي هِيَ أَقۡوَمُ وَيُبَشِّرُ ٱلۡمُؤۡمِنِينَ ٱلَّذِينَ يَعۡمَلُونَ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أَنَّ لَهُمۡ أَجۡرٗا كَبِيرٗا
Ndithu iyi Qur’an ikuongolera ku njira yoongoka ndi kuwasangalatsa okhulupirira omwe akuchita zabwino, kuti ndithu iwo adzalandira malipiro aakulu (pa tsiku la chiweruziro);
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَأَنَّ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡتَدۡنَا لَهُمۡ عَذَابًا أَلِيمٗا
Ndikutinso omwe sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro tawakonzera chilango chowawa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَيَدۡعُ ٱلۡإِنسَٰنُ بِٱلشَّرِّ دُعَآءَهُۥ بِٱلۡخَيۡرِۖ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ عَجُولٗا
Ndipo munthu amafulumira kupempha zoipa monga momwenso amafulumilira kupempha zabwino; ndithu munthu ngwaphuma (mzochita zake).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَجَعَلۡنَا ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَ ءَايَتَيۡنِۖ فَمَحَوۡنَآ ءَايَةَ ٱلَّيۡلِ وَجَعَلۡنَآ ءَايَةَ ٱلنَّهَارِ مُبۡصِرَةٗ لِّتَبۡتَغُواْ فَضۡلٗا مِّن رَّبِّكُمۡ وَلِتَعۡلَمُواْ عَدَدَ ٱلسِّنِينَ وَٱلۡحِسَابَۚ وَكُلَّ شَيۡءٖ فَصَّلۡنَٰهُ تَفۡصِيلٗا
Ndipo tapanga usiku ndi usana (mkusinthana-sinthana kwake) monga zisonyezo ziwiri (zosonyeza umodzi wa Allah ndi mphamvu Zake zoposa); ndipo tidachifafaniza chisonyezo cha usiku (kuti chisakhale ndi kuunika) ndipo chisonyezo cha usana tidachipanga kuti chikhale ndi kuunika; kuti mufunefune ubwino wochokera kwa Mbuye wanu, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka ndichiwerengero (cha miyezi ndi masiku); ndipo chinthu chilichonse (chofunika pa chipembedzo ndi za m’dziko), tachilongosola bwinobwino, mwatsatanetsatane.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَكُلَّ إِنسَٰنٍ أَلۡزَمۡنَٰهُ طَٰٓئِرَهُۥ فِي عُنُقِهِۦۖ وَنُخۡرِجُ لَهُۥ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ كِتَٰبٗا يَلۡقَىٰهُ مَنشُورًا
Ndipo munthu aliyense tammangilira mkhosi mwake zochita zake; ndipo tsiku la Qiyâma tidzamtulutsira kaundula (momwe muli zochita zake), adzampeza wovundukulidwa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
ٱقۡرَأۡ كِتَٰبَكَ كَفَىٰ بِنَفۡسِكَ ٱلۡيَوۡمَ عَلَيۡكَ حَسِيبٗا
(Kudzanenedwa kwa iye:) “Werenga kaundula wako (kupyolera m’mphamvu za Allah ngakhale pa dziko lapansi siunkatha kuwerenga); mzimu wako ukwanira lero kudziwerengera.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
مَّنِ ٱهۡتَدَىٰ فَإِنَّمَا يَهۡتَدِي لِنَفۡسِهِۦۖ وَمَن ضَلَّ فَإِنَّمَا يَضِلُّ عَلَيۡهَاۚ وَلَا تَزِرُ وَازِرَةٞ وِزۡرَ أُخۡرَىٰۗ وَمَا كُنَّا مُعَذِّبِينَ حَتَّىٰ نَبۡعَثَ رَسُولٗا
Amene waongoka (potsatira njira ya choonadi) ndithu wadzipindulira yekha, ndipo amene wapotoka (ku njira ya choonadi) ndithu wadzitaya iye mwini. Ndipo msenzi wosenza machimo sadzasenza mtolo wa machimo a wina. Ndipo Ife siolanga (zolengedwa) kufikira titatumiza mtumiki (kuti azidziwitse choonadi. Zikakana ndipomwe timazilanga).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِذَآ أَرَدۡنَآ أَن نُّهۡلِكَ قَرۡيَةً أَمَرۡنَا مُتۡرَفِيهَا فَفَسَقُواْ فِيهَا فَحَقَّ عَلَيۡهَا ٱلۡقَوۡلُ فَدَمَّرۡنَٰهَا تَدۡمِيرٗا
Ndipo tikafuna kuononga mudzi (pamene eni mudziwo akuchita zoipa), timawalamula opeza bwino a m’menemo (kuti asiye zoipa). Koma akapitiriza kuononga kwawo m’menemo, apo ndipo liwu (la kuwaononga) limatsimikizidwa pa iwo ndipo timauononga, kuononga kwakukulu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَكَمۡ أَهۡلَكۡنَا مِنَ ٱلۡقُرُونِ مِنۢ بَعۡدِ نُوحٖۗ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ بِذُنُوبِ عِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا
Ndimibadwo ingati imene tidaiononga pambuyo pa Nuh! Ndipo akukwanira Mbuye wako kudziwa bwinobwino ndi kuona bwinobwino uchimo wa akapolo Ake. (Palibe chobisika kwa Iye m’zochitachita za anthu).
Tefsiri na arapskom jeziku:
مَّن كَانَ يُرِيدُ ٱلۡعَاجِلَةَ عَجَّلۡنَا لَهُۥ فِيهَا مَا نَشَآءُ لِمَن نُّرِيدُ ثُمَّ جَعَلۡنَا لَهُۥ جَهَنَّمَ يَصۡلَىٰهَا مَذۡمُومٗا مَّدۡحُورٗا
Amene afuna zachangu (zosangalatsa za m’dziko ndikumaikirapo mtima pa izo), timpatsiratu mwachangu pa dziko lapansi chimene tikufuna kwa amene tafuna (kumpatsa;) koma (tsiku la chimaliziro) tamkonzera Jahannam adzailowa ali wonyozeka, wopirikitsidwa apa ndi apo.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَمَنۡ أَرَادَ ٱلۡأٓخِرَةَ وَسَعَىٰ لَهَا سَعۡيَهَا وَهُوَ مُؤۡمِنٞ فَأُوْلَٰٓئِكَ كَانَ سَعۡيُهُم مَّشۡكُورٗا
Ndipo amene afuna tsiku la chimaliziro (mzochita zake) ndikuligwilira ntchito yake yeniyeni uku ali okhulupirira, iwowo khama lawo lidzakhala lolandiridwa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
كُلّٗا نُّمِدُّ هَٰٓؤُلَآءِ وَهَٰٓؤُلَآءِ مِنۡ عَطَآءِ رَبِّكَۚ وَمَا كَانَ عَطَآءُ رَبِّكَ مَحۡظُورًا
Onse awa, (abwino ndi oipa), timawapatsa awa ndi awa mwazopatsa za Mbuye wako; ndipo zopatsa za Mbuye wako sizotsekerezedwa (kuti zisamfike kapolo Wake).
Tefsiri na arapskom jeziku:
ٱنظُرۡ كَيۡفَ فَضَّلۡنَا بَعۡضَهُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۚ وَلَلۡأٓخِرَةُ أَكۡبَرُ دَرَجَٰتٖ وَأَكۡبَرُ تَفۡضِيلٗا
Taona (ndi diso lolingalira) m’mene tawasiyanitsira mkupeza bwino, ena nkukhala pamwamba pa anzawo (pa chuma ndi pa moyo wangwiro); ndipo pa tsiku la chimaliziro kusiyana kwawo pa masitepe ndi ulemelero, nkwakukulu kwabasi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
لَّا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتَقۡعُدَ مَذۡمُومٗا مَّخۡذُولٗا
Usadzipangire mulungu wina ndi kumphatika kwa Allah; kuti ungadzakhale wodzudzulidwa (kwa Allah) ndikusiidwa wopanda m’thandizi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
۞ وَقَضَىٰ رَبُّكَ أَلَّا تَعۡبُدُوٓاْ إِلَّآ إِيَّاهُ وَبِٱلۡوَٰلِدَيۡنِ إِحۡسَٰنًاۚ إِمَّا يَبۡلُغَنَّ عِندَكَ ٱلۡكِبَرَ أَحَدُهُمَآ أَوۡ كِلَاهُمَا فَلَا تَقُل لَّهُمَآ أُفّٖ وَلَا تَنۡهَرۡهُمَا وَقُل لَّهُمَا قَوۡلٗا كَرِيمٗا
Ndipo walamula Mbuye wako kuti musapembedze (wina) koma Iye Yekha, ndi kuti muchitire zabwino makolo (anu). Ngati m’modzi wa iwo afika msinkhu waukalamba uli naye, kapena onse awiri, usawanenere mawu amnyozo, ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu.[254]
[254] M’ndimeyi Allah akulamula anthu Ake kuti apembedze Iye Yekha; asapembedze china chake cholengedwa monga miyala, mitengo, dzuwa, mwezi, nkhalango zowilira, mizimu ya anthu akufa ndi ziwanda. Koma chikhulupiliro chathu chikhale mwa Allah yekha. Tikafuna kudziteteza tidziteteze ndi Allah. Ndiponso Allah watilamula kuchitira zabwino makolo. Tisawanenere mawu amwano ndiponso tisawakalipire. Koma tiwanenere mau aulemu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَٱخۡفِضۡ لَهُمَا جَنَاحَ ٱلذُّلِّ مِنَ ٱلرَّحۡمَةِ وَقُل رَّبِّ ٱرۡحَمۡهُمَا كَمَا رَبَّيَانِي صَغِيرٗا
Ndipo afungatire ndi phiko lodzichepetsa powachitira chisoni, ndipo nena: “Mbuye wanga achitireni chisoni (makolo anga) monga momwe ankandilelera ku ubwana.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَا فِي نُفُوسِكُمۡۚ إِن تَكُونُواْ صَٰلِحِينَ فَإِنَّهُۥ كَانَ لِلۡأَوَّٰبِينَ غَفُورٗا
Mbuye wanu akudziwa kwambiri zomwe zili m’maganizo mwanu; ngati muli ofuna kuchita zabwino, (kwa makolo anu Iye akudziwa. Ndipo ngati mutawalakwira, kenako ndikulapa), ndithu Iye ndi Mwini kukhululukira otembenukira kwa Iye.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَءَاتِ ذَا ٱلۡقُرۡبَىٰ حَقَّهُۥ وَٱلۡمِسۡكِينَ وَٱبۡنَ ٱلسَّبِيلِ وَلَا تُبَذِّرۡ تَبۡذِيرًا
Ndipo mnansi wako, masikini ndi wapaulendo (yemwe alibe choyendera) mpatse gawo lake (la chuma chako) ndipo usamwaze (chuma chako) mosakaza.
Tefsiri na arapskom jeziku:
إِنَّ ٱلۡمُبَذِّرِينَ كَانُوٓاْ إِخۡوَٰنَ ٱلشَّيَٰطِينِۖ وَكَانَ ٱلشَّيۡطَٰنُ لِرَبِّهِۦ كَفُورٗا
Ndithu omwaza chuma mosakaza ndiabale a satana (otsatira satana), ndipo satana ngosathokoza kwa Mbuye wake.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِمَّا تُعۡرِضَنَّ عَنۡهُمُ ٱبۡتِغَآءَ رَحۡمَةٖ مِّن رَّبِّكَ تَرۡجُوهَا فَقُل لَّهُمۡ قَوۡلٗا مَّيۡسُورٗا
Ndipo ngati ukuwapewa opempha (pamene ulibe chowapatsa) pamene ukufunafuna chifundo cha Mbuye wako chomwe ukuchiyembekezera, nena kwa iwo mau ofewa (ponena kuti: “Ndikapeza chokupatsani, ndikuninkhani.”)
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَا تَجۡعَلۡ يَدَكَ مَغۡلُولَةً إِلَىٰ عُنُقِكَ وَلَا تَبۡسُطۡهَا كُلَّ ٱلۡبَسۡطِ فَتَقۡعُدَ مَلُومٗا مَّحۡسُورًا
Ndipo mkono wako usaukhalitse ngati kuti wamangidwa kukhosi kwako, ndiponso usautambasule mosayenera, ungadzakhale wodzudzulidwa ndiwosowa.[255]
[255] Tanthauzo la ndime iyi nkuti mkono wako usakhale wofumbata posiya kugawira ena zomwe ulinazo; ndikutinso usatambasule popatsa mosakaza koma kuchita zapakatikati; osachita umbombo ndiponso osasakaza. Anthu aumbombo ndi osakaza chuma, ndi abale a satana.
Tefsiri na arapskom jeziku:
إِنَّ رَبَّكَ يَبۡسُطُ ٱلرِّزۡقَ لِمَن يَشَآءُ وَيَقۡدِرُۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا
Ndithu Mbuye wako amamtambasulira rizq amene wamfuna, ndikulichepetsa (kwa amene wamfuna). Ndithu Iye Ngodziwa bwino; wopenya bwino za akapolo Ake.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَا تَقۡتُلُوٓاْ أَوۡلَٰدَكُمۡ خَشۡيَةَ إِمۡلَٰقٖۖ نَّحۡنُ نَرۡزُقُهُمۡ وَإِيَّاكُمۡۚ إِنَّ قَتۡلَهُمۡ كَانَ خِطۡـٔٗا كَبِيرٗا
Ndipo musaphe ana anu poopa umphawi. Ife ndi amene tikuwapatsa iwo ndi inu. Ndithu kupha anawo ndi tchimo lalikulu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَا تَقۡرَبُواْ ٱلزِّنَىٰٓۖ إِنَّهُۥ كَانَ فَٰحِشَةٗ وَسَآءَ سَبِيلٗا
Ndipo musachiyandikire chiwerewere; ndithu (icho) ndi uve (chonyansa chachikulu), ndiponso ndi njira yoipa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَا تَقۡتُلُواْ ٱلنَّفۡسَ ٱلَّتِي حَرَّمَ ٱللَّهُ إِلَّا بِٱلۡحَقِّۗ وَمَن قُتِلَ مَظۡلُومٗا فَقَدۡ جَعَلۡنَا لِوَلِيِّهِۦ سُلۡطَٰنٗا فَلَا يُسۡرِف فِّي ٱلۡقَتۡلِۖ إِنَّهُۥ كَانَ مَنصُورٗا
Ndipo musaphe munthu amene Allah waletsa (kumupha) koma mwachoonadi (poweruza oweruza zakuphedwa ngati utam’gwera mulandu woyenera kuphedwa). Ndipo amene waphedwa mopanda chilungamo, tapereka mphamvu kwa mlowammalo wake (wa wophedwayo atafuna angamuphenso kapena kumsiya ndikulandirapo dipo); koma asapyole malire mukuphako. Ndithu iye ngothandizidwa ndi Shariya.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَا تَقۡرَبُواْ مَالَ ٱلۡيَتِيمِ إِلَّا بِٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُ حَتَّىٰ يَبۡلُغَ أَشُدَّهُۥۚ وَأَوۡفُواْ بِٱلۡعَهۡدِۖ إِنَّ ٱلۡعَهۡدَ كَانَ مَسۡـُٔولٗا
Ndipo musachiyandikire chuma cha wamasiye (pochidya mosayenera) koma pokhapokha m’njira yomwe ili yabwino, kufikira atakula, (apo tsono apatsidwe chumacho); ndipo kwaniritsani lonjezo, popeza lonjezo lidzafunsidwa (tsiku la Qiyâma).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَأَوۡفُواْ ٱلۡكَيۡلَ إِذَا كِلۡتُمۡ وَزِنُواْ بِٱلۡقِسۡطَاسِ ٱلۡمُسۡتَقِيمِۚ ذَٰلِكَ خَيۡرٞ وَأَحۡسَنُ تَأۡوِيلٗا
Ndipo kwaniritsani mlingo pamene mulinga, ndipo yesani ndi sikelo zabwino, zimenezo ndi zabwino (kwa inu) ndiponso mathero (ake) ngabwino.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَا تَقۡفُ مَا لَيۡسَ لَكَ بِهِۦ عِلۡمٌۚ إِنَّ ٱلسَّمۡعَ وَٱلۡبَصَرَ وَٱلۡفُؤَادَ كُلُّ أُوْلَٰٓئِكَ كَانَ عَنۡهُ مَسۡـُٔولٗا
Ndipo usazitsate (pongoziyankhulayankhula kapena kuzichita) zomwe sukuzidziwa; ndithu makutu, maso ndi mtima zonsezo zidzafunsidwa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَا تَمۡشِ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَرَحًاۖ إِنَّكَ لَن تَخۡرِقَ ٱلۡأَرۡضَ وَلَن تَبۡلُغَ ٱلۡجِبَالَ طُولٗا
Ndipo usayende padziko modzitukumula; ndithu iwe sungang’ambe nthaka ndiponso sungalifikire phiri m’kutalika.
Tefsiri na arapskom jeziku:
كُلُّ ذَٰلِكَ كَانَ سَيِّئُهُۥ عِندَ رَبِّكَ مَكۡرُوهٗا
Zonsezi kuipa kwake nkonyansidwa kwa Mbuye wako.
Tefsiri na arapskom jeziku:
ذَٰلِكَ مِمَّآ أَوۡحَىٰٓ إِلَيۡكَ رَبُّكَ مِنَ ٱلۡحِكۡمَةِۗ وَلَا تَجۡعَلۡ مَعَ ٱللَّهِ إِلَٰهًا ءَاخَرَ فَتُلۡقَىٰ فِي جَهَنَّمَ مَلُومٗا مَّدۡحُورًا
Izi ndi zina mwa za nzeru zomwe Mbuye wako wakuvumbulutsira. Usakhale ndi mulungu wina ndi kumphatikiza kwa Allah, kuti ungadzaponyedwe ku Jahannam uli wodzudzulidwa ndi wopirikitsidwa apa ndi apo.
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَفَأَصۡفَىٰكُمۡ رَبُّكُم بِٱلۡبَنِينَ وَٱتَّخَذَ مِنَ ٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ إِنَٰثًاۚ إِنَّكُمۡ لَتَقُولُونَ قَوۡلًا عَظِيمٗا
Kodi Mbuye wanu wakusankhirani ana aamuna, ndipo mwini wadzipangira ana aakazi achingelo? Ndithu inu mukunena liwu lalikulu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لِيَذَّكَّرُواْ وَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا نُفُورٗا
Ndipo ndithu talongosola lamulo la chinthu chilichonse mwatsatanetsatane m’Qur’an iyi kuti akumbukire, ndipo (oipa) siikuwaonjezera (china) koma kuida ndi kuithawa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُل لَّوۡ كَانَ مَعَهُۥٓ ءَالِهَةٞ كَمَا يَقُولُونَ إِذٗا لَّٱبۡتَغَوۡاْ إِلَىٰ ذِي ٱلۡعَرۡشِ سَبِيلٗا
Nena: “Pakadakhala milungu ina pamodzi ndi Allah, monga momwe akunenera, ikadafuna njira yomufikira (Mbuye) Mwini Arsh (Mpando wa chifumu, ndi kumthira nkhondo).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
سُبۡحَٰنَهُۥ وَتَعَٰلَىٰ عَمَّا يَقُولُونَ عُلُوّٗا كَبِيرٗا
Wayera ndipo watukuka Allah ku zimene akunenazo; kutukuka kwakukulu (kwabasi).
Tefsiri na arapskom jeziku:
تُسَبِّحُ لَهُ ٱلسَّمَٰوَٰتُ ٱلسَّبۡعُ وَٱلۡأَرۡضُ وَمَن فِيهِنَّۚ وَإِن مِّن شَيۡءٍ إِلَّا يُسَبِّحُ بِحَمۡدِهِۦ وَلَٰكِن لَّا تَفۡقَهُونَ تَسۡبِيحَهُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ حَلِيمًا غَفُورٗا
Zonse zakumitambo isanu ndi iwiri ndi nthaka ndi zam’menemo, zikulemekeza Iye; ndipo palibe chilichonse koma chikumlememekeza ndi kumtamanda; koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo! Ndithudi Iye (Allah) Ngodekha, Ngokhululuka.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِذَا قَرَأۡتَ ٱلۡقُرۡءَانَ جَعَلۡنَا بَيۡنَكَ وَبَيۡنَ ٱلَّذِينَ لَا يُؤۡمِنُونَ بِٱلۡأٓخِرَةِ حِجَابٗا مَّسۡتُورٗا
Ndipo ukamawerenga Qur’an (zikukhala ngati) taika chotchinga chosaonekera pakati pako ndi pakati pa amene sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَجَعَلۡنَا عَلَىٰ قُلُوبِهِمۡ أَكِنَّةً أَن يَفۡقَهُوهُ وَفِيٓ ءَاذَانِهِمۡ وَقۡرٗاۚ وَإِذَا ذَكَرۡتَ رَبَّكَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِ وَحۡدَهُۥ وَلَّوۡاْ عَلَىٰٓ أَدۡبَٰرِهِمۡ نُفُورٗا
Ndipo (ngati) taika zitsekelero m’mitima mwawo kuti angaizindikire, ndipo (ngati) mmakutu mwawo muli kulemera kwa ugonthi. Ndiponso ukamtchula m’Qur’an Mbuye wako Yekha, iwo akutembenuka ndi misana yawo moipidwa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
نَّحۡنُ أَعۡلَمُ بِمَا يَسۡتَمِعُونَ بِهِۦٓ إِذۡ يَسۡتَمِعُونَ إِلَيۡكَ وَإِذۡ هُمۡ نَجۡوَىٰٓ إِذۡ يَقُولُ ٱلظَّٰلِمُونَ إِن تَتَّبِعُونَ إِلَّا رَجُلٗا مَّسۡحُورًا
Ife tikudziwa chifukwa chomwe akuimvetsera (Qur’an), pamene akukumvetsera ndi pamene akunong’onezana awo achinyengo, pamene akunena awo oyipa (kuuza Asilamu kuti): “Inu simutsatira (wina) koma munthu wolodzedwa.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
ٱنظُرۡ كَيۡفَ ضَرَبُواْ لَكَ ٱلۡأَمۡثَالَ فَضَلُّواْ فَلَا يَسۡتَطِيعُونَ سَبِيلٗا
Ona momwe akukufanizira ndi mafanizo abodza. (Nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa, nthawi zina akuti ndiwe mfiti!) Choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yeniyeni).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقٗا جَدِيدٗا
Ndipo akunena: “Kodi tikadzakhala mafupa odukaduka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”
Tefsiri na arapskom jeziku:
۞ قُلۡ كُونُواْ حِجَارَةً أَوۡ حَدِيدًا
Nena: “Khalani miyala kapena zitsulo.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَوۡ خَلۡقٗا مِّمَّا يَكۡبُرُ فِي صُدُورِكُمۡۚ فَسَيَقُولُونَ مَن يُعِيدُنَاۖ قُلِ ٱلَّذِي فَطَرَكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٖۚ فَسَيُنۡغِضُونَ إِلَيۡكَ رُءُوسَهُمۡ وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هُوَۖ قُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ قَرِيبٗا
“Kapena cholengedwa chilichonse mwa zomwe zikuoneka kuti nzovuta kwambiri m’mitima mwanu (m’maganizo mwanu), (ngakhale mutakhala zimenezo, mudzaukitsidwa).” Pamenepo anena: “Ndani adzatibweza?” Nena: “Yemwe adakulengani pachiyambi.” Pamenepo adzakupukusira mitu yawo ndi kunena: “Zichitika liti zimenezo?” Nena: “Mwina zili pafupi!”
Tefsiri na arapskom jeziku:
يَوۡمَ يَدۡعُوكُمۡ فَتَسۡتَجِيبُونَ بِحَمۡدِهِۦ وَتَظُنُّونَ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلٗا
“(Zidzakhala) pa tsiku lomwe adzakuitanani (Allah), ndipo inu mudzayankha momuyamikira, ndipo mudzaganizira kuti simudakhale (pa dziko lapansi) koma (kwa) nthawi yochepa.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقُل لِّعِبَادِي يَقُولُواْ ٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ يَنزَغُ بَيۡنَهُمۡۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلۡإِنسَٰنِ عَدُوّٗا مُّبِينٗا
Ndipo auze akapolo Anga kuti (nthawi zonse) azinena zomwe zili zabwino; chifukwa satana amakhwirizira mikangano pakati pawo; ndithu satana kwa munthu, ndi m’dani woonekera.
Tefsiri na arapskom jeziku:
رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِكُمۡۖ إِن يَشَأۡ يَرۡحَمۡكُمۡ أَوۡ إِن يَشَأۡ يُعَذِّبۡكُمۡۚ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ وَكِيلٗا
Mbuye wanu akukudziwani bwino. Ngati afuna akuchitirani chisoni (mukatembenukira kwa Iye), ndipo ngati afuna, akulangani (mukapitiriza kumnyoza); ndipo sitidakutumize kuti ukhale muyang’anili wawo.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَرَبُّكَ أَعۡلَمُ بِمَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَلَقَدۡ فَضَّلۡنَا بَعۡضَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ عَلَىٰ بَعۡضٖۖ وَءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ زَبُورٗا
Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino onse ali kumwamba ndi pansi, ndithu tawapatsa ulemelero wambiri aneneri ena kuposa ena. Ndipo Daud tidampatsa Zaburi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُلِ ٱدۡعُواْ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُم مِّن دُونِهِۦ فَلَا يَمۡلِكُونَ كَشۡفَ ٱلضُّرِّ عَنكُمۡ وَلَا تَحۡوِيلًا
Nena: “Aitaneni amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Iye (Allah) kuti akuchotsereni masautso, sadzatha kukuchotserani vuto lililonse ngakhale kulisintha (kuti likhale chabwino).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ يَبۡتَغُونَ إِلَىٰ رَبِّهِمُ ٱلۡوَسِيلَةَ أَيُّهُمۡ أَقۡرَبُ وَيَرۡجُونَ رَحۡمَتَهُۥ وَيَخَافُونَ عَذَابَهُۥٓۚ إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ كَانَ مَحۡذُورٗا
Iwo amene akuwapempha (naonso) akufunafuna njira yoziyandikitsira kwa Mbuye wawo (ngakhale) omwe ali pafupi mwa iwo (ndi Allah, monga angelo); naonso akuyembekezera chifundo chake ndi kuopa chilango chake; ndithu chilango cha Mbuye wako, nchoopedwa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِن مِّن قَرۡيَةٍ إِلَّا نَحۡنُ مُهۡلِكُوهَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَوۡ مُعَذِّبُوهَا عَذَابٗا شَدِيدٗاۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَسۡطُورٗا
Ndipo sipadzapezeka mudzi uliwonse koma Ife tidzauphwasula tsiku la Qiyâma lisanadze, kapena tidzaulanga ndi chilango chaukali (ngati uli woyenerana ndi zimenezo). Izi zidalembedwa m’buku.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَمَا مَنَعَنَآ أَن نُّرۡسِلَ بِٱلۡأٓيَٰتِ إِلَّآ أَن كَذَّبَ بِهَا ٱلۡأَوَّلُونَۚ وَءَاتَيۡنَا ثَمُودَ ٱلنَّاقَةَ مُبۡصِرَةٗ فَظَلَمُواْ بِهَاۚ وَمَا نُرۡسِلُ بِٱلۡأٓيَٰتِ إِلَّا تَخۡوِيفٗا
Ndipo palibe chimene chikutiletsa kutumiza zizizwa (zomwe akuzipempha) koma kuti anthu akale adazitsutsa. Asamuda tidawapatsa ngamira yaikazi kuti ikhale chizindikiro choonekera (chozizwitsa) koma adaichitira zosayenera; ndipo sititumiza zizizwa ndi cholinga china, koma kuchenjeza.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِذۡ قُلۡنَا لَكَ إِنَّ رَبَّكَ أَحَاطَ بِٱلنَّاسِۚ وَمَا جَعَلۡنَا ٱلرُّءۡيَا ٱلَّتِيٓ أَرَيۡنَٰكَ إِلَّا فِتۡنَةٗ لِّلنَّاسِ وَٱلشَّجَرَةَ ٱلۡمَلۡعُونَةَ فِي ٱلۡقُرۡءَانِۚ وَنُخَوِّفُهُمۡ فَمَا يَزِيدُهُمۡ إِلَّا طُغۡيَٰنٗا كَبِيرٗا
Ndipo (kumbuka) pamene tidakuuza kuti ndithu Mbuye wako wawazungulira anthu (mowadziwa bwinobwino;) ndipo sitidawachite maloto omwe tidakuonetsa koma kuti akhale mayeso kwa anthu, (kuti kodi akhulupirira kapena sakhulupirira), ndiponso (kutchula kwa) rntengo wotembeleredwa m’Qur’an (ndimayetseronso kwa iwo;) ndipo tikuwachenjeza, koma (machenjezo athu) sakuwaonjezera china koma kulumpha malire kwakukulu basi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِذۡ قُلۡنَا لِلۡمَلَٰٓئِكَةِ ٱسۡجُدُواْ لِأٓدَمَ فَسَجَدُوٓاْ إِلَّآ إِبۡلِيسَ قَالَ ءَأَسۡجُدُ لِمَنۡ خَلَقۡتَ طِينٗا
Ndipo (akumbutse) pamene tidauza angelo kuti: “Mugwadireni Adam.” Ndipo adamugwadira kupatula Iblis (iye) adati: “Kodi ndimugwadire yemwe mwamlenga ndi dongo?”
Tefsiri na arapskom jeziku:
قَالَ أَرَءَيۡتَكَ هَٰذَا ٱلَّذِي كَرَّمۡتَ عَلَيَّ لَئِنۡ أَخَّرۡتَنِ إِلَىٰ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ لَأَحۡتَنِكَنَّ ذُرِّيَّتَهُۥٓ إِلَّا قَلِيلٗا
Adatinso (kwa Allah): “Kodi mukuona uyu amene mwampatsa ulemelero kuposa ine? Ngati mundipatsa nthawi mpaka tsiku la Qiyâma, ndithu ndiononga mbumba yake (yonse) kupatula ochepa basi.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
قَالَ ٱذۡهَبۡ فَمَن تَبِعَكَ مِنۡهُمۡ فَإِنَّ جَهَنَّمَ جَزَآؤُكُمۡ جَزَآءٗ مَّوۡفُورٗا
(Allah) adati: “Choka! Amene adzakutsata mwa iwo, ndithu Jahannam ndiyo mphoto yanu mphoto yokwanira.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَٱسۡتَفۡزِزۡ مَنِ ٱسۡتَطَعۡتَ مِنۡهُم بِصَوۡتِكَ وَأَجۡلِبۡ عَلَيۡهِم بِخَيۡلِكَ وَرَجِلِكَ وَشَارِكۡهُمۡ فِي ٱلۡأَمۡوَٰلِ وَٱلۡأَوۡلَٰدِ وَعِدۡهُمۡۚ وَمَا يَعِدُهُمُ ٱلشَّيۡطَٰنُ إِلَّا غُرُورًا
Ndipo apusitse amene ungawathe mwa iwo ndi liwu lako; ndipo asonkhanitsire gulu lako la nkhondo la okwera akavalo ndi loyenda ndi miyendo; tenga gawo lako pa chuma chawo ndi ana awo; ndipo alonjeze (malonjezo abodza).” Koma satana salonjeza china koma chinyengo basi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
إِنَّ عِبَادِي لَيۡسَ لَكَ عَلَيۡهِمۡ سُلۡطَٰنٞۚ وَكَفَىٰ بِرَبِّكَ وَكِيلٗا
“Ndithu akapolo Anga, ulibe nyonga pa iwo.” Ndipo Mbuye wako akukwanira kukhala mtetezi (wawo).
Tefsiri na arapskom jeziku:
رَّبُّكُمُ ٱلَّذِي يُزۡجِي لَكُمُ ٱلۡفُلۡكَ فِي ٱلۡبَحۡرِ لِتَبۡتَغُواْ مِن فَضۡلِهِۦٓۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِكُمۡ رَحِيمٗا
Mbuye wanu ndi yemwe amakuyendetserani zombo pa nyanja kuti munke mufunafuna ubwino Wake. Ndithu Iye Ngwachisoni kwa inu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِذَا مَسَّكُمُ ٱلضُّرُّ فِي ٱلۡبَحۡرِ ضَلَّ مَن تَدۡعُونَ إِلَّآ إِيَّاهُۖ فَلَمَّا نَجَّىٰكُمۡ إِلَى ٱلۡبَرِّ أَعۡرَضۡتُمۡۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ كَفُورًا
Ndipo akakupezani masautso pa nyanja, amasowa amene mumakhala mukuwapembedza kupatula Iye (Allah). Koma akakupulumutsirani kumtunda, mukutembenuka ndi kunyoza Allah. Ndithu munthu ndi wokana (mtendere wa Allah sayamika.)
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَفَأَمِنتُمۡ أَن يَخۡسِفَ بِكُمۡ جَانِبَ ٱلۡبَرِّ أَوۡ يُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ حَاصِبٗا ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ وَكِيلًا
Kodi mukudziika pa chitetezo ndi chilango cha Allah (mukafika pa ntunda) kuti Allah sangakulowetseni pansi mbali iliyonse ya pa ntunda, kapena sangakutumizireni chigumula chamchenga (kapena miyala) kenako inu simudzapeza mtetezi (wokupulumutsani ku chilangocho)?
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَمۡ أَمِنتُمۡ أَن يُعِيدَكُمۡ فِيهِ تَارَةً أُخۡرَىٰ فَيُرۡسِلَ عَلَيۡكُمۡ قَاصِفٗا مِّنَ ٱلرِّيحِ فَيُغۡرِقَكُم بِمَا كَفَرۡتُمۡ ثُمَّ لَا تَجِدُواْ لَكُمۡ عَلَيۡنَا بِهِۦ تَبِيعٗا
Kapena mwadziika pachitetezo kuti (Allah) sadzakubwezeraninso m’nyanjamo kachiwiri ndipo nkudzakutumizirani chimphepo chaukali ndikukumizani chifukwa cha kusakhulupirira (ndi kusathokoza kwanu,) kenako inu nkusapeza wokutetezani kwa Ife?
Tefsiri na arapskom jeziku:
۞ وَلَقَدۡ كَرَّمۡنَا بَنِيٓ ءَادَمَ وَحَمَلۡنَٰهُمۡ فِي ٱلۡبَرِّ وَٱلۡبَحۡرِ وَرَزَقۡنَٰهُم مِّنَ ٱلطَّيِّبَٰتِ وَفَضَّلۡنَٰهُمۡ عَلَىٰ كَثِيرٖ مِّمَّنۡ خَلَقۡنَا تَفۡضِيلٗا
Ndipo ndithu tawalemekeza ana a Adam; ndipo tawapatsa zokwera pa ntunda ndi pa nyanja; tawapatsa zopatsa zabwino kwambiri; ndipo tawapatsa ulemelero kuposa zambiri m’zomwe tidalenga; ulemelero waukulu kwabasi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
يَوۡمَ نَدۡعُواْ كُلَّ أُنَاسِۭ بِإِمَٰمِهِمۡۖ فَمَنۡ أُوتِيَ كِتَٰبَهُۥ بِيَمِينِهِۦ فَأُوْلَٰٓئِكَ يَقۡرَءُونَ كِتَٰبَهُمۡ وَلَا يُظۡلَمُونَ فَتِيلٗا
(Akumbutse za) tsiku lomwe tidzaitana anthu onse m’dzina la mneneri wawo; choncho, amene adzapatsidwe akaundula awo ndi dzanja lamanja iwo adzawerenga akaundula awowo (mwachisangalalo), ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pa (kachinthu kakang’ono monga) kaulusi ka mkati mwa njere ya kanjeza.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَمَن كَانَ فِي هَٰذِهِۦٓ أَعۡمَىٰ فَهُوَ فِي ٱلۡأٓخِرَةِ أَعۡمَىٰ وَأَضَلُّ سَبِيلٗا
Ndipo amene ali wakhungu pano (pa dziko lapansi posapenya zizindikiro) adzakhalanso wakhungu pa tsiku la chimaliziro, ndipo adzakhala wosokera kwambiri njira (kumeneko).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِن كَادُواْ لَيَفۡتِنُونَكَ عَنِ ٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ لِتَفۡتَرِيَ عَلَيۡنَا غَيۡرَهُۥۖ وَإِذٗا لَّٱتَّخَذُوكَ خَلِيلٗا
Ndipo ndithu adatsala pang’ono kukusokoneza pa zimene tavumbulutsa kwa iwe kuti utipekere zina zake m’malo mwa izi; pamenepo, akadakusankha kukhala bwenzi (lawo).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَوۡلَآ أَن ثَبَّتۡنَٰكَ لَقَدۡ كِدتَّ تَرۡكَنُ إِلَيۡهِمۡ شَيۡـٔٗا قَلِيلًا
Ndipo tikadapanda kukulimbikitsa, ukadapendekera kwa iwo, kupendekera kwa pang’ono.
Tefsiri na arapskom jeziku:
إِذٗا لَّأَذَقۡنَٰكَ ضِعۡفَ ٱلۡحَيَوٰةِ وَضِعۡفَ ٱلۡمَمَاتِ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ عَلَيۡنَا نَصِيرٗا
Tero ndithu tikadakulawitsa chilango chachikulu cha moyo (wa pa dziko lapansi) ndi chilango chachikulu utafa; kenako siukadapeza mthandizi wokupulumutsa kwa Ife.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِن كَادُواْ لَيَسۡتَفِزُّونَكَ مِنَ ٱلۡأَرۡضِ لِيُخۡرِجُوكَ مِنۡهَاۖ وَإِذٗا لَّا يَلۡبَثُونَ خِلَٰفَكَ إِلَّا قَلِيلٗا
Ndipo padatsala pang’ono kuti akusowetse mtendere m’dziko ili (la Makka) kuti akutulutse m’menemo; koma pambuyo pako sakadakhala (ndi moyo) kupatula (nthawi) yochepa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
سُنَّةَ مَن قَدۡ أَرۡسَلۡنَا قَبۡلَكَ مِن رُّسُلِنَاۖ وَلَا تَجِدُ لِسُنَّتِنَا تَحۡوِيلًا
Chimenechi ndi chikhalidwe cha omwe tidawatuma patsogolo pako mwa atumiki Athu, ndipo supeza kusintha pachikhalidwe Chathu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَقِمِ ٱلصَّلَوٰةَ لِدُلُوكِ ٱلشَّمۡسِ إِلَىٰ غَسَقِ ٱلَّيۡلِ وَقُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِۖ إِنَّ قُرۡءَانَ ٱلۡفَجۡرِ كَانَ مَشۡهُودٗا
Pemphera Swala (za Farazi), dzuwa likapendeka mpaka mu mdima wausiku (zomwe ndi Swala za Dhuhri, Asri, Maghrib ndi Isha), ndipo pempheranso Swala ya Fajir: ndithu Swala ya Fajir amaichitira umboni (angelo).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَمِنَ ٱلَّيۡلِ فَتَهَجَّدۡ بِهِۦ نَافِلَةٗ لَّكَ عَسَىٰٓ أَن يَبۡعَثَكَ رَبُّكَ مَقَامٗا مَّحۡمُودٗا
Ndipo pakati pa usiku, dzuka mtulo ndi kupemphera Swala; ilo ndipemphero loonjezera pa iwe, kuti Mbuye wako akakuimike pamalo pa ulemu potamandidwa (ndi zolengedwa zonse pa tsiku la Qiyâma.)
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقُل رَّبِّ أَدۡخِلۡنِي مُدۡخَلَ صِدۡقٖ وَأَخۡرِجۡنِي مُخۡرَجَ صِدۡقٖ وَٱجۡعَل لِّي مِن لَّدُنكَ سُلۡطَٰنٗا نَّصِيرٗا
Ndipo nena (mawu awa pomwe ukupemphera): “Mbuye wanga! Ndilowetseni, kulowetsa kwabwino (paliponse pamene ndikulowa), ndiponso nditulutseni, kutulutsa kwabwino (paliponse pamene ndikutuluka); ndipatseni mphamvu zochokera kwa Inu zondithandiza ndi kugonjetsera adani.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقُلۡ جَآءَ ٱلۡحَقُّ وَزَهَقَ ٱلۡبَٰطِلُۚ إِنَّ ٱلۡبَٰطِلَ كَانَ زَهُوقٗا
Ndipo nena: “Choonadi chafika, ndipo chachabe chachoka; ndithu chachabe ndichochoka (ngakhale patapita nthawi yaitali).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَنُنَزِّلُ مِنَ ٱلۡقُرۡءَانِ مَا هُوَ شِفَآءٞ وَرَحۡمَةٞ لِّلۡمُؤۡمِنِينَ وَلَا يَزِيدُ ٱلظَّٰلِمِينَ إِلَّا خَسَارٗا
Ndipo tikuivumbulutsa Qur’an yomwe imachiritsa (matenda a mmitima) ndiponso ndi chifundo kwa okhulupirira. Komabe osalungama siikuwaonjezera (kanthu kena) koma kutayika.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَإِذَآ أَنۡعَمۡنَا عَلَى ٱلۡإِنسَٰنِ أَعۡرَضَ وَنَـَٔا بِجَانِبِهِۦ وَإِذَا مَسَّهُ ٱلشَّرُّ كَانَ يَـُٔوسٗا
Ndipo tikampatsa chisomo munthu, (monga moyo wangwiro ndikupeza bwino), amatembenuka (ndikusiya kutikumbukira ndikutipempha), ndipo amadziika kutali (ndi Ife chifukwa chakudzitama ndikudzikuza), koma masautso akamkhudza, (monga matenda ndi umphawi) amataya mtima kwambiri.
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُلۡ كُلّٞ يَعۡمَلُ عَلَىٰ شَاكِلَتِهِۦ فَرَبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِمَنۡ هُوَ أَهۡدَىٰ سَبِيلٗا
Nena (iwe Mneneri, kwa osakhulupirira a Chikuraishi,): “Aliyense (wa ife ndi inu) akuchita ntchito (zake ndikuyenda panjira yake) ndipo Mbuye wanu Ngodziwa kwambiri za yemwe ali panjira yolondola (potsatira choonadi).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَيَسۡـَٔلُونَكَ عَنِ ٱلرُّوحِۖ قُلِ ٱلرُّوحُ مِنۡ أَمۡرِ رَبِّي وَمَآ أُوتِيتُم مِّنَ ٱلۡعِلۡمِ إِلَّا قَلِيلٗا
Ndipo akukufunsa (iwe, Muhammad (s.a.w), anthu ako mokhwiriziridwa ndi Ayuda) za Mzimu. Nena: “Mzimu ndi chinthu chomwe akuchidziwa Mbuye wanga Yekha; ndipo inu simudapatsidwe nzeru (zozindikilira zinthu) koma pang’ono chabe, (poyerekeza ndi nzeru za Allah).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَئِن شِئۡنَا لَنَذۡهَبَنَّ بِٱلَّذِيٓ أَوۡحَيۡنَآ إِلَيۡكَ ثُمَّ لَا تَجِدُ لَكَ بِهِۦ عَلَيۡنَا وَكِيلًا
Ndipo tikadafuna kufufuta Qur’an (pachifuwa chako) yomwe takuvumbulutsira, (tikadatha kutero). Kenako sukadapeza kwa Ife wokuimilira ndi kukupulumutsa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
إِلَّا رَحۡمَةٗ مِّن رَّبِّكَۚ إِنَّ فَضۡلَهُۥ كَانَ عَلَيۡكَ كَبِيرٗا
Koma (taisiya mu mtima mwako) chifukwa cha chifundo chochokera kwa Mbuye wako; ndithu ubwino Wake pa iwe ngwaukulu.
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُل لَّئِنِ ٱجۡتَمَعَتِ ٱلۡإِنسُ وَٱلۡجِنُّ عَلَىٰٓ أَن يَأۡتُواْ بِمِثۡلِ هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ لَا يَأۡتُونَ بِمِثۡلِهِۦ وَلَوۡ كَانَ بَعۡضُهُمۡ لِبَعۡضٖ ظَهِيرٗا
Nena: “Ngakhale atasonkhana anthu ndi ziwanda (mothandizana) kuti abwere ndi buku longa ili la Qur’an (mukayalidwe ka mawu ndi matanthauzo ake), sangathe kubweretsa longa ilo, ngakhale atathandizana wina ndi mnzake.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَقَدۡ صَرَّفۡنَا لِلنَّاسِ فِي هَٰذَا ٱلۡقُرۡءَانِ مِن كُلِّ مَثَلٖ فَأَبَىٰٓ أَكۡثَرُ ٱلنَّاسِ إِلَّا كُفُورٗا
Ndipo ndithu tawalongosolera anthu, m’Qur’an iyi; mkulongosola kwa njira zosiyanasiyana ndikupereka fanizo lamtundu uliwonse. Ndipo anthu ambiri akukana (zonsezo) koma kusakhulupirira basi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقَالُواْ لَن نُّؤۡمِنَ لَكَ حَتَّىٰ تَفۡجُرَ لَنَا مِنَ ٱلۡأَرۡضِ يَنۢبُوعًا
Ndipo (pamene adalephera kubwera ndi Qur’an yawo,) adati: “Sitingakukhulupirire mpaka utatitulutsira kasupe wosaphwa m’dziko (lathu ili la Makka).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَوۡ تَكُونَ لَكَ جَنَّةٞ مِّن نَّخِيلٖ وَعِنَبٖ فَتُفَجِّرَ ٱلۡأَنۡهَٰرَ خِلَٰلَهَا تَفۡجِيرًا
Kapena ukhale ndi munda wazipatso za kanjedza ndi mphesa (kuno ku Makka), ndipo utulutse mitsinje yambiri pakati pa mundapo.
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَوۡ تُسۡقِطَ ٱلسَّمَآءَ كَمَا زَعَمۡتَ عَلَيۡنَا كِسَفًا أَوۡ تَأۡتِيَ بِٱللَّهِ وَٱلۡمَلَٰٓئِكَةِ قَبِيلًا
Kapena utigwetsere zidutswa za thambo pa mitu yathu monga momwe umatiopsezera, apo ayi, um’bweretse Allah ndi angelo (kuti) tionane nawo nkhope kwa nkhope (mwamasomphenya.)”
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَوۡ يَكُونَ لَكَ بَيۡتٞ مِّن زُخۡرُفٍ أَوۡ تَرۡقَىٰ فِي ٱلسَّمَآءِ وَلَن نُّؤۡمِنَ لِرُقِيِّكَ حَتَّىٰ تُنَزِّلَ عَلَيۡنَا كِتَٰبٗا نَّقۡرَؤُهُۥۗ قُلۡ سُبۡحَانَ رَبِّي هَلۡ كُنتُ إِلَّا بَشَرٗا رَّسُولٗا
Kapena ukhale ndi nyumba ya golide, kapena ukwere kumwamba. Ndipo sitikukhulupirira kukwera kwako pokhapokha utatibweretsera buku (lochokera kwa Allah lomwe likulongosola za kuona kwako), kuti tidziliwerenga.” Nena (kwa iwo): “Mbuye wanga alemekezeke ndikupatukana ndi mbiri zopunguka! Ine sindine kanthu koma munthu, mtumiki (monga atumiki ena).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَمَا مَنَعَ ٱلنَّاسَ أَن يُؤۡمِنُوٓاْ إِذۡ جَآءَهُمُ ٱلۡهُدَىٰٓ إِلَّآ أَن قَالُوٓاْ أَبَعَثَ ٱللَّهُ بَشَرٗا رَّسُولٗا
Ndipo palibe chimene (Amushirikina a m’Makka) chawaletsa kukhulupirira choona pamene chiongoko chawadzera, koma kunena kwawo (kwa umbuli) kwakuti: “Kodi Allah amatuma munthu kukhala Mtumiki (Wake)?
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُل لَّوۡ كَانَ فِي ٱلۡأَرۡضِ مَلَٰٓئِكَةٞ يَمۡشُونَ مُطۡمَئِنِّينَ لَنَزَّلۡنَا عَلَيۡهِم مِّنَ ٱلسَّمَآءِ مَلَكٗا رَّسُولٗا
Nena: “Padziko pakadakhala angelo omayendayenda ndi okhazikika (m’malo awo ndi m’nyumba zawo), tikadawatsitsira m’ngelo monga mtumiki kuchokera kumwamba.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُلۡ كَفَىٰ بِٱللَّهِ شَهِيدَۢا بَيۡنِي وَبَيۡنَكُمۡۚ إِنَّهُۥ كَانَ بِعِبَادِهِۦ خَبِيرَۢا بَصِيرٗا
Nena: “(Ngati mukutsutsa uthenga wanga) Allah wakwanira kukhala Mboni (ndi Muweruzi) pakati panga ndi pakati panu (zakuona kwa uthenga wanga kwa inu). Ndithu Iye Ngodziwa za akapolo Ake (zilakolako zawo) Ngowona (zochita zawo).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَمَن يَهۡدِ ٱللَّهُ فَهُوَ ٱلۡمُهۡتَدِۖ وَمَن يُضۡلِلۡ فَلَن تَجِدَ لَهُمۡ أَوۡلِيَآءَ مِن دُونِهِۦۖ وَنَحۡشُرُهُمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ عَلَىٰ وُجُوهِهِمۡ عُمۡيٗا وَبُكۡمٗا وَصُمّٗاۖ مَّأۡوَىٰهُمۡ جَهَنَّمُۖ كُلَّمَا خَبَتۡ زِدۡنَٰهُمۡ سَعِيرٗا
Ndipo yemwe Allah wamuongola, (chifukwa cha kukonzeka kwake kwa ubwino), iyeyo ndi amene waongoka; ndipo amene wamulekelera kusokera, (chifukwa cha kuipa kwa khalidwe lake), simungampezere athandizi kupatula Iye (Allah). Ndipo pa tsiku la chiweruziro tidzawasonkhanitsa uku akukokedwa ndi nkhope zawo ali osapenya, osalankhula ndi osamva. Malo awo okhala ndi ku Jahannam. Nthawi iliyonse (Motowo) ukatotobwa, tidzauonjezera kwa iwo kuyaka mwaukali.
Tefsiri na arapskom jeziku:
ذَٰلِكَ جَزَآؤُهُم بِأَنَّهُمۡ كَفَرُواْ بِـَٔايَٰتِنَا وَقَالُوٓاْ أَءِذَا كُنَّا عِظَٰمٗا وَرُفَٰتًا أَءِنَّا لَمَبۡعُوثُونَ خَلۡقٗا جَدِيدًا
(Chilango) chimenecho ndiyo mphoto yawo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo zisonyezo (zomwe tidasonyeza kwa iwo), ndi kunena kwawo koti: “Kodi tikadzakhala mafupa ndi zidutswa zonyenyekanyenyeka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”
Tefsiri na arapskom jeziku:
۞ أَوَلَمۡ يَرَوۡاْ أَنَّ ٱللَّهَ ٱلَّذِي خَلَقَ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضَ قَادِرٌ عَلَىٰٓ أَن يَخۡلُقَ مِثۡلَهُمۡ وَجَعَلَ لَهُمۡ أَجَلٗا لَّا رَيۡبَ فِيهِ فَأَبَى ٱلظَّٰلِمُونَ إِلَّا كُفُورٗا
Kodi (onyalanyaza) sadadziwebe kuti Allah Yemwe adalenga thambo ndi nthaka Ngokhoza kulenga ena onga iwo? Ndipo wawaikira nthawi (yodziwika) yopanda chikaiko, (yowaukitsira ku imfa). Koma achinyengo akukana (zonsezi) koma kusakhulupirira basi.
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُل لَّوۡ أَنتُمۡ تَمۡلِكُونَ خَزَآئِنَ رَحۡمَةِ رَبِّيٓ إِذٗا لَّأَمۡسَكۡتُمۡ خَشۡيَةَ ٱلۡإِنفَاقِۚ وَكَانَ ٱلۡإِنسَٰنُ قَتُورٗا
Nena (kwa opembedza mafano): “Mukadakhala kuti muli nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wanga, mukadachita umbombo (posagawira ena) kuopa umphawi. Ndipo munthu ali ndi khalidwe loumira.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَلَقَدۡ ءَاتَيۡنَا مُوسَىٰ تِسۡعَ ءَايَٰتِۭ بَيِّنَٰتٖۖ فَسۡـَٔلۡ بَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ إِذۡ جَآءَهُمۡ فَقَالَ لَهُۥ فِرۡعَوۡنُ إِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰمُوسَىٰ مَسۡحُورٗا
Ndipo ndithu tidampatsa Mûsa zizizwa zoonekera zisanu ndi zinayi (komabe osakhulupirira sadazikhulupirire). Afunse ana a Israyeli pamene adawadzera (Musayo), Farawo adati kwa iye (Mûsa): “Ndithu ine ndikukuona iwe Mûsa kuti walodzedwa.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
قَالَ لَقَدۡ عَلِمۡتَ مَآ أَنزَلَ هَٰٓؤُلَآءِ إِلَّا رَبُّ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ بَصَآئِرَ وَإِنِّي لَأَظُنُّكَ يَٰفِرۡعَوۡنُ مَثۡبُورٗا
(Mûsa) adati: “Ndithu wadziwa kuti palibe amene watumiza (mitsutso) iyi kupatula Mbuye wathambo ndi nthaka kuti zikhale chiphanula maso. Koma ine ndikukuona iwe Farawo kuti waonongeka.”
Tefsiri na arapskom jeziku:
فَأَرَادَ أَن يَسۡتَفِزَّهُم مِّنَ ٱلۡأَرۡضِ فَأَغۡرَقۡنَٰهُ وَمَن مَّعَهُۥ جَمِيعٗا
Choncho (Farawo) adafuna kuwatulutsa m’dziko (la Iguputo Mûsa ndi ana a Israyeli) koma tidammiza iye ndi onse omwe adali naye.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقُلۡنَا مِنۢ بَعۡدِهِۦ لِبَنِيٓ إِسۡرَٰٓءِيلَ ٱسۡكُنُواْ ٱلۡأَرۡضَ فَإِذَا جَآءَ وَعۡدُ ٱلۡأٓخِرَةِ جِئۡنَا بِكُمۡ لَفِيفٗا
(Mûsa ndi anthu ake tidawapulumutsa). Ndipo tidati, kwa ana a Israyeli, pambuyo pake (pommiza Farawo): “Khalani m’dziko (loyera la Shami); ndipo likazadza lonjezo la moyo winawo, tidzakubweretsani nonsenu (muli m’chipwirikiti.)”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَبِٱلۡحَقِّ أَنزَلۡنَٰهُ وَبِٱلۡحَقِّ نَزَلَۗ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ إِلَّا مُبَشِّرٗا وَنَذِيرٗا
Ndipo chifukwa chobweretsa choonadi pa dziko tidaitumiza (Qur’an); ndipo mwachoonadi, yavumbulutsidwa. Ndipo sitidakutume (ndi china) koma kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino, ndi wochenjeza (osakhulupirira).
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقُرۡءَانٗا فَرَقۡنَٰهُ لِتَقۡرَأَهُۥ عَلَى ٱلنَّاسِ عَلَىٰ مُكۡثٖ وَنَزَّلۡنَٰهُ تَنزِيلٗا
Ndipo Qur’an iyi taigawa (m’zigawo zosiyanasiyana poivumbulutsa pang’onopang’ono) kuti uwawerengere anthu mwa chifatse ndipo taivumbulutsa pang’onopang’ono.
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُلۡ ءَامِنُواْ بِهِۦٓ أَوۡ لَا تُؤۡمِنُوٓاْۚ إِنَّ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡعِلۡمَ مِن قَبۡلِهِۦٓ إِذَا يُتۡلَىٰ عَلَيۡهِمۡ يَخِرُّونَۤ لِلۡأَذۡقَانِۤ سُجَّدٗاۤ
Nena (kwa osakhulupirira a m’Makka mowachenjeza): “Ikhulupirireni (iyi Qur’an) kapena musaikhulupirire, (zonse zili m’chifuniro chanu.) Ndithu amene adapatsidwa nzeru kale (yozindikira za m’mabuku a Allah Qur’an isanadze) ikamalakatulidwa kwa iwo (Qur’aniyi) amagwa ndi zibwano zawo molambira.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَيَقُولُونَ سُبۡحَٰنَ رَبِّنَآ إِن كَانَ وَعۡدُ رَبِّنَا لَمَفۡعُولٗا
Ndipo amanena: “Mbuye wathu Ngoyera! Ndithu lonjezo la Mbuye wathu ndi lokwaniritsidwa!”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَيَخِرُّونَ لِلۡأَذۡقَانِ يَبۡكُونَ وَيَزِيدُهُمۡ خُشُوعٗا۩
Ndipo amagwa ndi zibwano zawo uku akulira, ndipo (Qur’an) imawaonjezera kudzichepetsa.
Tefsiri na arapskom jeziku:
قُلِ ٱدۡعُواْ ٱللَّهَ أَوِ ٱدۡعُواْ ٱلرَّحۡمَٰنَۖ أَيّٗا مَّا تَدۡعُواْ فَلَهُ ٱلۡأَسۡمَآءُ ٱلۡحُسۡنَىٰۚ وَلَا تَجۡهَرۡ بِصَلَاتِكَ وَلَا تُخَافِتۡ بِهَا وَٱبۡتَغِ بَيۡنَ ذَٰلِكَ سَبِيلٗا
Nena (kwa Amushirikina): “Mpempheni Allah, m’dzina la Allah kapena mpempheni m’dzina la Rahman; (dzina) lililonse, limene mungamtchulire (zithandizabe); Iye ali nawo maina abwino. Ndipo usawerenge (Qur’an) pa Swala yako ndi mawu okweza, ndiponso usatsitse mawu kwambiri, koma tsata njira yolingana pakati pa zimenezo (pokweza kwambiri kapena kutsitsa zedi).”
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَقُلِ ٱلۡحَمۡدُ لِلَّهِ ٱلَّذِي لَمۡ يَتَّخِذۡ وَلَدٗا وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ شَرِيكٞ فِي ٱلۡمُلۡكِ وَلَمۡ يَكُن لَّهُۥ وَلِيّٞ مِّنَ ٱلذُّلِّۖ وَكَبِّرۡهُ تَكۡبِيرَۢا
Ndipo nena: “Kutamandidwa kwabwino nkwa Allah, yemwe saadadzipangire mwana, ndipo alibe m’phatikizi mu ufumu (Wake); ndipo alibe mthandizi (womthandiza) mkufooka; ndipo mkuzeni, kumkuza kwakukulu!”
Tefsiri na arapskom jeziku:
 
Prijevod značenja Sura: Sura el-Isra
Indeks sura Broj stranice
 
Prijevod značenja časnog Kur'ana - الترجمة الشيشيوا - Sadržaj prijevodā

ترجمة معاني القرآن الكريم إلى اللغة الشيشيوا، ترجمها خالد إبراهيم بيتالا. نسخة عام 2020م.

Zatvaranje