Check out the new design

Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala * - Sadržaj prijevodā


Prijevod značenja Sura: Eš-Šura   Ajet:
وَتَرَىٰهُمۡ يُعۡرَضُونَ عَلَيۡهَا خَٰشِعِينَ مِنَ ٱلذُّلِّ يَنظُرُونَ مِن طَرۡفٍ خَفِيّٖۗ وَقَالَ ٱلَّذِينَ ءَامَنُوٓاْ إِنَّ ٱلۡخَٰسِرِينَ ٱلَّذِينَ خَسِرُوٓاْ أَنفُسَهُمۡ وَأَهۡلِيهِمۡ يَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِۗ أَلَآ إِنَّ ٱلظَّٰلِمِينَ فِي عَذَابٖ مُّقِيمٖ
Udzawaona (osalungama) akusonyezedwa ku Moto ali okhumata chifukwa chakunyozeka uku akuyang’ana (Moto) mkayang’anidwe kobisa (kotsinzina). Ndipo amene adakhulupirira adzanena pa tsiku la Qiyâma: “Ndithu otaika ndi amene adadzitaya okha pamodzi ndi maanja awo.” Dziwani kuti osalungama adzakhala mchilango chamuyaya.
Tefsiri na arapskom jeziku:
وَمَا كَانَ لَهُم مِّنۡ أَوۡلِيَآءَ يَنصُرُونَهُم مِّن دُونِ ٱللَّهِۗ وَمَن يُضۡلِلِ ٱللَّهُ فَمَا لَهُۥ مِن سَبِيلٍ
Ndipo sadzakhala ndi athangati owapulumutsa (kuchilango cha Moto) kupatula Allah. Ndipo amene Allah wamusiya kuti asokere (chifukwa cha zochita zake zoipa) sangapeze njira (yopezera kulungama.)
Tefsiri na arapskom jeziku:
ٱسۡتَجِيبُواْ لِرَبِّكُم مِّن قَبۡلِ أَن يَأۡتِيَ يَوۡمٞ لَّا مَرَدَّ لَهُۥ مِنَ ٱللَّهِۚ مَا لَكُم مِّن مَّلۡجَإٖ يَوۡمَئِذٖ وَمَا لَكُم مِّن نَّكِيرٖ
Muyankheni Mbuye wanu lisadadze tsiku losapeweka lochokera kwa Allah; tsiku limenelo simudzapeza pothawira, ndipo simudzakhala ndi njira (yokanira zimene mudzachitidwa).
Tefsiri na arapskom jeziku:
فَإِنۡ أَعۡرَضُواْ فَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ حَفِيظًاۖ إِنۡ عَلَيۡكَ إِلَّا ٱلۡبَلَٰغُۗ وَإِنَّآ إِذَآ أَذَقۡنَا ٱلۡإِنسَٰنَ مِنَّا رَحۡمَةٗ فَرِحَ بِهَاۖ وَإِن تُصِبۡهُمۡ سَيِّئَةُۢ بِمَا قَدَّمَتۡ أَيۡدِيهِمۡ فَإِنَّ ٱلۡإِنسَٰنَ كَفُورٞ
Ngati anyalanyaza (Allah awalanga) sitidakutume kwa iwo kukhala muyang’aniri. Udindo wako ndikufalitsa uthenga. Ndipo ndithu tikamulawitsa munthu mtendere wochokera kwa Ife, akuunyadira (modzikweza), koma choipa chikawapeza kupyolera mzoipa zimene manja awo adatsogoza, pompo munthuyo sathokoza (Allah).
Tefsiri na arapskom jeziku:
لِّلَّهِ مُلۡكُ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۚ يَخۡلُقُ مَا يَشَآءُۚ يَهَبُ لِمَن يَشَآءُ إِنَٰثٗا وَيَهَبُ لِمَن يَشَآءُ ٱلذُّكُورَ
Ufumu wakumwamba ndi pa dziko lapansi ngwa Allah; amalenga zimene wafuna; amene wam’funa amampatsa ana achikazi (okhaokha) ndiponso amene wamfuna amampatsa ana achimuna (okhaokha).
Tefsiri na arapskom jeziku:
أَوۡ يُزَوِّجُهُمۡ ذُكۡرَانٗا وَإِنَٰثٗاۖ وَيَجۡعَلُ مَن يَشَآءُ عَقِيمًاۚ إِنَّهُۥ عَلِيمٞ قَدِيرٞ
Kapena kuphatikiza (ana) achimuna ndi achikazi, ndipo amene wam’funa amamchita kukhala chumba. Ndithu Iye Ngodziwa, Wokhoza (chilichonse).
Tefsiri na arapskom jeziku:
۞ وَمَا كَانَ لِبَشَرٍ أَن يُكَلِّمَهُ ٱللَّهُ إِلَّا وَحۡيًا أَوۡ مِن وَرَآيِٕ حِجَابٍ أَوۡ يُرۡسِلَ رَسُولٗا فَيُوحِيَ بِإِذۡنِهِۦ مَا يَشَآءُۚ إِنَّهُۥ عَلِيٌّ حَكِيمٞ
Nkosayenera kwa munthu kuti Allah alankhule naye koma kupyolera mkumzindikiritsa, kapena kuchokera kuseri kwa chotsekereza, kapena pomtuma mtumiki (Jiburil) kuti amvumbulutsire zimene Iye akufuna mwa chilolezo Chake. Ndithu Iye Ngwapamwamba, Ngwanzeru zakuya.
Tefsiri na arapskom jeziku:
 
Prijevod značenja Sura: Eš-Šura
Indeks sura Broj stranice
 
Prijevod značenja časnog Kur'ana - Prijevod na čeva jezik - Halid Ibrahim Betala - Sadržaj prijevodā

Halid Ibrahim Bejtala je preveo.

Zatvaranje