Check out the new design

Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala * - Translations’ Index


Translation of the meanings Surah: Yūsuf   Ayah:
قَالَ يَٰبُنَيَّ لَا تَقۡصُصۡ رُءۡيَاكَ عَلَىٰٓ إِخۡوَتِكَ فَيَكِيدُواْ لَكَ كَيۡدًاۖ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ لِلۡإِنسَٰنِ عَدُوّٞ مُّبِينٞ
(Bambo wake) adati: “E iwe mwana wanga! Usawasimbire abale ako maloto ako (kuopa kuti) angakuchitire chiwembu; ndithu satana kwa munthu, ndi mdani woonekera.”[228]
[228] Sibwino munthu kufotokozera anthu chisomo chako chonse ngati palibe zofunikira kutero. Dziwani kuti mwini madalitso ngochitiridwa dumbo.
Arabic explanations of the Qur’an:
وَكَذَٰلِكَ يَجۡتَبِيكَ رَبُّكَ وَيُعَلِّمُكَ مِن تَأۡوِيلِ ٱلۡأَحَادِيثِ وَيُتِمُّ نِعۡمَتَهُۥ عَلَيۡكَ وَعَلَىٰٓ ءَالِ يَعۡقُوبَ كَمَآ أَتَمَّهَا عَلَىٰٓ أَبَوَيۡكَ مِن قَبۡلُ إِبۡرَٰهِيمَ وَإِسۡحَٰقَۚ إِنَّ رَبَّكَ عَلِيمٌ حَكِيمٞ
“Ndipo momwemo Mbuye wako akusankha komanso akuphunzitsa kumasulira nkhani (za maloto) ndi kukwaniritsa mtendere Wake pa iwe, ndi pa mbumba ya Ya’qub monga momwe adakwaniritsira kwa makolo ako kale, Ibrahim ndi Ishaq. Ndithu Mbuye wako Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.”
Arabic explanations of the Qur’an:
۞ لَّقَدۡ كَانَ فِي يُوسُفَ وَإِخۡوَتِهِۦٓ ءَايَٰتٞ لِّلسَّآئِلِينَ
Ndithu mwa Yûsuf ndi abale ake, muli malingaliro ambiri kwa ofunsa (zinthu kuti adziwe).
Arabic explanations of the Qur’an:
إِذۡ قَالُواْ لَيُوسُفُ وَأَخُوهُ أَحَبُّ إِلَىٰٓ أَبِينَا مِنَّا وَنَحۡنُ عُصۡبَةٌ إِنَّ أَبَانَا لَفِي ضَلَٰلٖ مُّبِينٍ
Kumbuka pamene (abale a Yûsuf) adati: “Ndithu Yûsuf ndi m’bale wake (Binyamini) ngokondeka zedi kwa bambo wathu kuposa ife pomwe ife ndife gulu lamphamvu. Ndithu bambo wathu ali mkusokera koonekera (sadziwa yemwe ali ndi chithandizo chokwanira).”
Arabic explanations of the Qur’an:
ٱقۡتُلُواْ يُوسُفَ أَوِ ٱطۡرَحُوهُ أَرۡضٗا يَخۡلُ لَكُمۡ وَجۡهُ أَبِيكُمۡ وَتَكُونُواْ مِنۢ بَعۡدِهِۦ قَوۡمٗا صَٰلِحِينَ
“Mupheni Yûsuf kapena mukamponye ku dziko (lakutali), kuti nkhope ya bambo wanu ikutembenukireni (pakuti nthawi imeneyo Yûsuf sadzakhalapo, yemwe akumkonda kwambiriyo); ndipo pambuyo pake (mutalapa tchimoli) mdzakhala abwino, (kwa Allah).”[229]
[229] Dyera loipa kwambiri ndiko kunena koti: “Tandisiyani ndichite machimo, kenako ndidzalapa.” Dziwani kuti machimo omwe Allah angawakhululuke ngomwe munthu wawachita mosazindikira kapena kuti popanda kuwafunafuna, osati owachita mwadaladala ncholinga choti adzalapa pambuyo pake monga momwe abale ake a Yusuf ankaganizira.
Arabic explanations of the Qur’an:
قَالَ قَآئِلٞ مِّنۡهُمۡ لَا تَقۡتُلُواْ يُوسُفَ وَأَلۡقُوهُ فِي غَيَٰبَتِ ٱلۡجُبِّ يَلۡتَقِطۡهُ بَعۡضُ ٱلسَّيَّارَةِ إِن كُنتُمۡ فَٰعِلِينَ
Adanena wonena mwa iwo: “Musamuphe Yûsuf, koma mponyeni m’chitsime chakuya; adzamtola ena a paulendo ngati inu mwalingadi kutelo.”
Arabic explanations of the Qur’an:
قَالُواْ يَٰٓأَبَانَا مَا لَكَ لَا تَأۡمَ۬نَّا عَلَىٰ يُوسُفَ وَإِنَّا لَهُۥ لَنَٰصِحُونَ
(Pambuyo pogwirizana paganizo lomuponya m’chitsime chakuya adapita kwa bambo wawo) anati: “E bambo wathu! Kodi bwanji simutikhulupirira pa Yûsuf, pomwe ife timamfunira zabwino?”
Arabic explanations of the Qur’an:
أَرۡسِلۡهُ مَعَنَا غَدٗا يَرۡتَعۡ وَيَلۡعَبۡ وَإِنَّا لَهُۥ لَحَٰفِظُونَ
Mperekeni mawa pamodzi ndi ife (kubusa) kuti akadye mokondwa ndi kusewera; ndithudi, ife tikamsamala.”
Arabic explanations of the Qur’an:
قَالَ إِنِّي لَيَحۡزُنُنِيٓ أَن تَذۡهَبُواْ بِهِۦ وَأَخَافُ أَن يَأۡكُلَهُ ٱلذِّئۡبُ وَأَنتُمۡ عَنۡهُ غَٰفِلُونَ
(Bambo wawo) adati: “Ndithu zikundidandaulitsa zakuti mupite naye; ndikuopa kuti angajiwe ndi mimbulu pomwe inu simukulabadira za iye.”
Arabic explanations of the Qur’an:
قَالُواْ لَئِنۡ أَكَلَهُ ٱلذِّئۡبُ وَنَحۡنُ عُصۡبَةٌ إِنَّآ إِذٗا لَّخَٰسِرُونَ
(Iwo) adati: “Ngati mimbulu itamudya pomwe ife ndife gulu lanyonga kwambiri, ndiye kuti tidzakhala otaika.”
Arabic explanations of the Qur’an:
 
Translation of the meanings Surah: Yūsuf
Surahs’ Index Page Number
 
Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala - Translations’ Index

Translated by Khalid Ibrahim Betala

close