Check out the new design

Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala * - Translations’ Index


Translation of the meanings Surah: Yūsuf   Ayah:
فَلَمَّا سَمِعَتۡ بِمَكۡرِهِنَّ أَرۡسَلَتۡ إِلَيۡهِنَّ وَأَعۡتَدَتۡ لَهُنَّ مُتَّكَـٔٗا وَءَاتَتۡ كُلَّ وَٰحِدَةٖ مِّنۡهُنَّ سِكِّينٗا وَقَالَتِ ٱخۡرُجۡ عَلَيۡهِنَّۖ فَلَمَّا رَأَيۡنَهُۥٓ أَكۡبَرۡنَهُۥ وَقَطَّعۡنَ أَيۡدِيَهُنَّ وَقُلۡنَ حَٰشَ لِلَّهِ مَا هَٰذَا بَشَرًا إِنۡ هَٰذَآ إِلَّا مَلَكٞ كَرِيمٞ
Ndipo (mkazi wa nduna) pamene adamva kunyogodola kwawo, adawaitana (kuti adzaone kukongola kwa Yûsuf kuti adziwe kuti yemwe wathedwa nzeru polakalaka Yûsuf ngosayenera kudzudzulidwa). Ndipo adawakonzera phwando ndikupatsa aliyense wa iwo mpeni; kenaka adamuuza (Yûsuf): “Tuluka ndi kubwera pamaso pa iwo.” Choncho pamene (akazi aja) adamuona, adaona kuti nchinthu chachikulu zedi ndipo adadzicheka manja awo (ndi mipeni ija. Sadazindikire kuti akudzicheka chifukwa cha chidwi ndi kukongola kwa Yûsuf), ndipo adati: “Hasha Lillah! (tikudzitchinjiriza kwa Allah) uyu simunthu, uyu sichina koma ndi mngelo wolemekezeka.”
Arabic explanations of the Qur’an:
قَالَتۡ فَذَٰلِكُنَّ ٱلَّذِي لُمۡتُنَّنِي فِيهِۖ وَلَقَدۡ رَٰوَدتُّهُۥ عَن نَّفۡسِهِۦ فَٱسۡتَعۡصَمَۖ وَلَئِن لَّمۡ يَفۡعَلۡ مَآ ءَامُرُهُۥ لَيُسۡجَنَنَّ وَلَيَكُونٗا مِّنَ ٱلصَّٰغِرِينَ
(Mkazi wa nduna) adati: “Uyu ndi amene mumandidzudzula naye. Ndithudi ndidamulakalaka pomwe iye samandifuna ndipo anadziteteza. Ndipo ngati sachita chimene ndikumulamula, ndithu amangidwa ndipo ndithu akhala m’gulu la onyozeka!”
Arabic explanations of the Qur’an:
قَالَ رَبِّ ٱلسِّجۡنُ أَحَبُّ إِلَيَّ مِمَّا يَدۡعُونَنِيٓ إِلَيۡهِۖ وَإِلَّا تَصۡرِفۡ عَنِّي كَيۡدَهُنَّ أَصۡبُ إِلَيۡهِنَّ وَأَكُن مِّنَ ٱلۡجَٰهِلِينَ
(Yûsuf) adati: “E Mbuye wanga! Ndende ndi yabwino kwa ine kuposa izi akundiitanira. Ngati simundichotsera ndale zawo ndiye kuti ndiwacheukira ndikukhala mmodzi mwa mbuli.”[232]
[232] Akazi aja atamuona Yûsuf tsiku limenelo nawonso anadzazidwa ndi chikondi chachikulu nayamba kumtumizira mithenga ndi makalata. Ndipo Yûsuf adaganiza kuti ndibwino angopita kundende poopa kuti akaziwo angamulakwitse.
Arabic explanations of the Qur’an:
فَٱسۡتَجَابَ لَهُۥ رَبُّهُۥ فَصَرَفَ عَنۡهُ كَيۡدَهُنَّۚ إِنَّهُۥ هُوَ ٱلسَّمِيعُ ٱلۡعَلِيمُ
Ndipo Mbuye wake adamuyankha (pempho lake) ndikumchotsera ndale zawo. Ndithudi, Iye Ngwakumva, Ngodziwa.
Arabic explanations of the Qur’an:
ثُمَّ بَدَا لَهُم مِّنۢ بَعۡدِ مَا رَأَوُاْ ٱلۡأٓيَٰتِ لَيَسۡجُنُنَّهُۥ حَتَّىٰ حِينٖ
Kenako kudaoneka kwa iwo, (nduna ndi anthu ake) pambuyo poona zizindikiro (zonse zakuyeretsedwa kwa Yûsuf) kuti akamponye kundende kwa nthawi yochepa (pofuna kumusungira ulemu mkazi wa nduna).
Arabic explanations of the Qur’an:
وَدَخَلَ مَعَهُ ٱلسِّجۡنَ فَتَيَانِۖ قَالَ أَحَدُهُمَآ إِنِّيٓ أَرَىٰنِيٓ أَعۡصِرُ خَمۡرٗاۖ وَقَالَ ٱلۡأٓخَرُ إِنِّيٓ أَرَىٰنِيٓ أَحۡمِلُ فَوۡقَ رَأۡسِي خُبۡزٗا تَأۡكُلُ ٱلطَّيۡرُ مِنۡهُۖ نَبِّئۡنَا بِتَأۡوِيلِهِۦٓۖ إِنَّا نَرَىٰكَ مِنَ ٱلۡمُحۡسِنِينَ
Ndipo anyamata awiri adalowa m’ndende pamodzi ndi iye. Mmodzi mwa iwo adati (kumuuza Yûsuf): “Ndithu ine ndalota ndikufulula mowa.” Ndipo wina adati: “Ndithu ine ndalota ndikusenza mikate pamutu panga yomwe idali kudyedwa ndi mbalame. Tiuze tanthauzo lake. Ndithu ife tikukuona iwe kuti ndiwe mmodzi wa anthu abwino.”
Arabic explanations of the Qur’an:
قَالَ لَا يَأۡتِيكُمَا طَعَامٞ تُرۡزَقَانِهِۦٓ إِلَّا نَبَّأۡتُكُمَا بِتَأۡوِيلِهِۦ قَبۡلَ أَن يَأۡتِيَكُمَاۚ ذَٰلِكُمَا مِمَّا عَلَّمَنِي رَبِّيٓۚ إِنِّي تَرَكۡتُ مِلَّةَ قَوۡمٖ لَّا يُؤۡمِنُونَ بِٱللَّهِ وَهُم بِٱلۡأٓخِرَةِ هُمۡ كَٰفِرُونَ
(Yûsuf) adati: “(Kupyolera mu uneneri umene ndapatsidwa ndingathe kukumasulirani maloto anuwa ndi zinthu zina zobisika kwa inu), sichikudzerani chakudya cha mtundu uliwonse choti mungapatsidwe koma ndikhala nditakumasulirani tanthauzo lake chisanakufikeni; (ngati mukufunadi ndikuchitirani zimenezi). Izi ndi zina mwa zomwe Mbuye wanga wandiphunzitsa. Ndithudi, ine ndasiya njira za anthu osakhulupirira Allah ndiponso omwe akukana za tsiku la chimaliziro.”
Arabic explanations of the Qur’an:
 
Translation of the meanings Surah: Yūsuf
Surahs’ Index Page Number
 
Translation of the Meanings of the Noble Qur'an - Chewa translation - Khaled Ibrahim Batyala - Translations’ Index

Translated by Khalid Ibrahim Betala

close