Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa * - Índice de traducciones


Traducción de significados Capítulo: Sura Al-Bayyina   Versículo:

Sura Al-Bayyina

لَمۡ يَكُنِ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ وَٱلۡمُشۡرِكِينَ مُنفَكِّينَ حَتَّىٰ تَأۡتِيَهُمُ ٱلۡبَيِّنَةُ
Amene adakanira (Allah ndi Mthenga Wake) mwa omwe adapatsidwa buku ndi opembedza mafano sadali olekana (ndi umbuli wawo ndi kusalabadira kwawo choona) mpaka pomwe chidawadzera chisonyezo choonekera poyera.[466]
[466] “Akafiri” omwe adapatsidwa buku, ndi Ayuda ndi Akhristu. “Amushirikina” ndi omwe adali kupembedza mafano. Tanthauzo la ma Ayah awa 1- 4 ndikuti asadatulukire Muhammad (s.a.w), Ayuda ndi Akhristu omwe adali ku Madina, pamene adali kuwauza opembedza mafano kuti: “Yayandikira nthawi yotulukira Mneneri. Ife tidzamtsatira, tidzakhala pamodzi ndi iye. Tidzakumenyani nkhondo mpaka kukugonjetsani.” Adali kuyembekezera kuti Mneneriyo adzakhala mwa iwo. Pamene adali kumva izi, opembedza mafano aja, adali odandaula. Iwonso adali kuyembekezera Mneneriyo; limeneli ndilo tanthauzo la mawu aja oti: “Sadali olekana mpaka pomwe chidawadzera chisonyezo choonekera poyera.”
Apa ndiye kuti fuko lililonse mwa mafuko atatu aja lidali ndi mtima wopitiriza zipembedzo zawo, osaleka mpaka chiwafikire chisonyezo. Tanthauzo la “chisonyezo,” apa ndi Muhammad (s.a.w) monga Ayah yachiwiri yafotokozera.
Pamene adafika Mneneri, opembedza mafano aja ndiwo adayamba kumukhulupilira, koma Ayuda ndi Akhristu pamene adaona kuti Mneneri sali wochokera mwa iwo monga m’mene adali kuyembekezera adakhumudwa; ena mwa iwo adamkhulupilira pomwe ena sadamkhulupirire. Ili ndilo tanthauzo lakuti, “sadalekane omwe adapatsidwa mabuku mpaka pomwe chidawafikira chisonyezo.”
Las Exégesis Árabes:
رَسُولٞ مِّنَ ٱللَّهِ يَتۡلُواْ صُحُفٗا مُّطَهَّرَةٗ
(Yemwe ndi) Mtumiki wochokera kwa Allah akuwawerengera makalata oyeretsedwa (ku zonama).[467]
[467] Tanthauzo la “Makalata oyeretsedwa kuzonama” ndi Qur’an.
Las Exégesis Árabes:
فِيهَا كُتُبٞ قَيِّمَةٞ
Omwe mkati mwake muli malamulo oongoka (ofotokoza za choona).[468]
[468] Kapena kuti “mkati mwake muli mabuku olingana,” ndiye kuti m’Qur’an muli zophunzitsa za mabuku onse omwe Allah adavumbulutsa kwa Aneneri onse akale.
Las Exégesis Árabes:
وَمَا تَفَرَّقَ ٱلَّذِينَ أُوتُواْ ٱلۡكِتَٰبَ إِلَّا مِنۢ بَعۡدِ مَا جَآءَتۡهُمُ ٱلۡبَيِّنَةُ
Sadalekane omwe adapatsidwa mabuku mpaka pomwe chidawafikira chisonyezo (chosonyeza kuti Muhammad (s.a.w) ndi mthenga wa Allah yemwe adalonjezedwa mmabuku awo).
Las Exégesis Árabes:
وَمَآ أُمِرُوٓاْ إِلَّا لِيَعۡبُدُواْ ٱللَّهَ مُخۡلِصِينَ لَهُ ٱلدِّينَ حُنَفَآءَ وَيُقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَيُؤۡتُواْ ٱلزَّكَوٰةَۚ وَذَٰلِكَ دِينُ ٱلۡقَيِّمَةِ
Ndipo sadalamulidwe (china) koma kuti ampembedze Allah (Mmodzi yekha) ndikuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona (ndi kusiya njira zonama) ndi kuti asunge Swala ndiponso apereke chopereka (cha pachuma chawo); chimenecho (ndicho) chipembedzo choongoka.[469]
[469] Tanthauzo lake ndikuti “Mneneri uyu” sadadze ndi chinthu cha chilendo chakuti ndikumukanira. Koma iye akulamula za kupembedza Allah Mmodzi ndi kumuyeretsera chipembedzo Chake; kuima ndi kupemphera, kupereka chopereka ndi zina zotero. Zoterezi ndizonso adali kuphunzitsa aneneri onse omwe adadza ndi zipembedzo zoongoka.
Las Exégesis Árabes:
إِنَّ ٱلَّذِينَ كَفَرُواْ مِنۡ أَهۡلِ ٱلۡكِتَٰبِ وَٱلۡمُشۡرِكِينَ فِي نَارِ جَهَنَّمَ خَٰلِدِينَ فِيهَآۚ أُوْلَٰٓئِكَ هُمۡ شَرُّ ٱلۡبَرِيَّةِ
Ndithu amene sadakhulupirire (Mneneri) (s.a.w) pakati pa anthu a mabuku ndi opembedza mafano adzalowetsedwa ku Jahannam ndikukhala m’menemo nthawi yaitali; iwowo ndiwo zolengedwa zoipa.
Las Exégesis Árabes:
إِنَّ ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ وَعَمِلُواْ ٱلصَّٰلِحَٰتِ أُوْلَٰٓئِكَ هُمۡ خَيۡرُ ٱلۡبَرِيَّةِ
Ndithu amene akhulupirira (mwa Allah ndi Mthenga Wake) ndikumachita zabwino, iwo ndiwo zolengedwa zabwino.
Las Exégesis Árabes:
جَزَآؤُهُمۡ عِندَ رَبِّهِمۡ جَنَّٰتُ عَدۡنٖ تَجۡرِي مِن تَحۡتِهَا ٱلۡأَنۡهَٰرُ خَٰلِدِينَ فِيهَآ أَبَدٗاۖ رَّضِيَ ٱللَّهُ عَنۡهُمۡ وَرَضُواْ عَنۡهُۚ ذَٰلِكَ لِمَنۡ خَشِيَ رَبَّهُۥ
Malipiro awo kwa Mbuye wawo, ndi minda yamuyaya momwe ikuyenda pansi pake mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya. Allah adzawayanja nawonso adzamuyanja (chifukwa cha zomwe adzawapatse); zimenezo ndi za yemwe awope Mbuye wake (Allah).
Las Exégesis Árabes:
 
Traducción de significados Capítulo: Sura Al-Bayyina
Índice de Capítulos Número de página
 
Traducción de los significados del Sagrado Corán - Traducción al Chewa - Índice de traducciones

Traducción del significado del Corán al chewa por Khaled Ibrahim Betala (ed.2020)

Cerrar